Nkhuni—Kodi Mtsogolo Mukuwonongedwa?
Ndi mtola nkhani wa Galamukani! mu Nigeria
DZUWA likuloŵa ndi kufiiritsa thambo la mu Afirika. Sampa akuphikira mwamuna wake ndi ana awo mpunga. Iye akutunga madzi mumtsuko ndi kuthira m’sufuliya yodetsedwa ndi utsi. Pansi pa mphikawo pakuthetheka moto wochepa, wosonkhezeredwa ndi nkhuni zazikulu zitatu.
Zounjikidwa chapafupipo ndizo nkhuni zina. Sampa amazigula kwa amuna amene amabwera nazo palole kuchokera kumapiri. Nkhunizo nzofunika. Popanda nkhuni sipangakhale moto. Popanda moto sungaphike mpunga.
Mwana wamwamuna wachisamba wa Sampa akuti: “Tikasowa nkhuni, sitimadya.” Iye akuloza kunyumba za okhuphuka cha paphiripo. “M’nyumba zija, muli magetsi. Muli zitofu zimene zimagwira ntchito ndi magetsi ndi zitofu zina zimene zimagwira ntchito ndi gasi.” Akutembenukira ku moto, akunyakula mapeŵa, ndi kuti: “Ife timagwiritsira ntchito nkhuni.”
Pali ambiri amene ali mumkhalidwe wofanana ndi wa banja la Sampa. Mwa anthu 4 alionse m’maiko osatukuka, 3 amadalira pa nkhuni monga magwero awo okha okolezera moto wophikira ndi kuwotha. Koma pali kupereŵera kwakukulu kwa nkhuni.
Malinga ndi FAO (Food and Agriculture Organization la UN), mlingo wa vuto la nkhuni ngwowopsadi kwambiri. Pafupifupi anthu mamiliyoni chikwi chimodzi m’maiko osatukuka akuyang’anizana ndi kupereŵera kwa nkhuni. Ngati mkhalidwe ulipowu upitirizabe, chiŵerengerochi chikatha kuŵirikiza kaŵiri mosavuta pakutha kwa zaka za zanali. Woimira gulu la FAO anafotokoza kuti: “Nkosapindulitsa kugaŵira chakudya anjala a padziko ngati alibe njira yochiphikira.”
Kodi Nchifukwa Ninji Kupereŵerako?
Kuyambira m’nthaŵi zamakedzana, mtundu wa anthu wagwiritsira ntchito nkhuni kukolezera moto. Chifukwa ninji? Nkhuni nzothandiza kwambiri. Sutofunikira chiŵiya chokwera mtengo kapena luso lazopangapanga kuti ukaziteme. Kusiyapo ngati zagwiritsiridwa ntchito mopambanitsa, izo zingapezekebe mwa kukula kwa mitengo yatsopano. Kuphika ndi kuwotha moto wankhuni sikufunikiritsa zitofu ndi mbaula zamagetsi. Ndiponso mothandiza, nkhuni nzaulere ndipo zimapezeka mosavuta mofanana ndi mtengo wapafupi. Mwakhala kokha m’zaka mazana aŵiri zapitazo pamene mitundu yolemera koposerapo yadziko yatembenukira kumtundu wina wokolezera moto, wonga gasi, malasha, ndi mafuta. Otsalawo apitirizabe ndi nkhuni.
Akatswiri ena akunena kuti chochititsa chachikulu cha vutolo ndicho kuwonjezereka kwankhaninkhani kwa chiŵerengero cha anthu. Pamene anthu akuwonjezereka m’chiŵerengero, ndipamenenso nkhalango zimasengedwa kuwonjezera midzi, kukulitsa minda, ndi kupezera maindasitale matabwa ndiponso nkhuni. Nkhalango zimatha pakufutukuka kwa pafupifupi dziko lirilonse. Maiko a North America ndi Ulaya analoŵa mumkhalidwe woterowo.
Koma chiŵerengero cha anthu cha lerolino chikukula pamlingo wowopsa. Pakali pano, pali kale anthu mamiliyoni zikwi zisanu ndi theka paplaneti lino. M’maiko osatukuka, ziŵerengero za anthuzo zimaŵirikiza kaŵiri m’zaka 20 kufikira 30 zirizonse. Pamene chiŵerengero cha anthu chiwonjezereka, kufunika kwa nkhuni kumateronso. Kuli monga ngati kuti chiŵerengero cha anthu chakhala chilombo chachikulu kwadzawoneni, chodya nkhalango chokhala ndi njala yosatha, chilombo chimene chimamka nichikulakulabe ndi kukhala chanjala mowonjezereka tsiku lirilonse. Chotero mitengo ya nkhuni ikudyedwa isanaloŵedwe mmalo. Malinga ndi FAO, anthu oposa mamiliyoni zana limodzi m’maiko 26 ali kale osakhoza kupeza mitengo yankhuni yosamalira ngakhale zosoŵa zawo zazikulu koposa.
Komabe, sionse amene amakhala m’maiko okhala ndi kusoŵa kwakukulu amene amayambukiridwa mofanana. Awo amene angathe amangotembenukira kumitundu ina yokolezera moto, yonga parafini kapena gasi. Vuto lankhuni ndivuto la amphaŵi, amene akumka nawonjezereka m’chiŵerengero.
Chiyambukiro pa Anthu
M’zaka zaposachedwapa mtengo wogulira nkhuni waŵirikiza kaŵiri kapena katatu ndipo m’madera ena kuŵirikiza kanayi. Lerolino, mitengoyo ikupitirizabe kukwera pamene madera ozungulira mizinda akukhwaulidwa kukhala apululu. Mizinda yambiri m’Asia ndi Afirika tsopano yazunguliridwa ndi madera amene ali pafupifupi opandiratu mitengo. Mizinda ina iyenera kukatema nkhuni kutali kufikira makilomitala 160.
Mitengo yomakwerakwera imawonjezera mtolo wa awo amene ali kale amphaŵi kwambiri. Mapendedwe asonyeza kuti m’mbali za Amereka Wapakati ndi Kumadzulo kwa Afirika, mabanja ogwira ntchito amalipilira pafupifupi 30 peresenti ya chiwonkhetso cha ndalama zawo zolandiridwa kaamba ka nkhuni. Kanthu kena kalikonse—chakudya, zovala, nyumba, zoyendera, maphunziro—ziyenera kupatulidwa pa zimene zatsala. Kwa iwo mawuwo ngowona akuti “zimene zimaloŵa pansi pamphika nzokwera mtengo koposa zimene zimaloŵa mumphika.”
Kodi iwo amachita motani? Kumene nkhuni ziri zosawonekawoneka kapena ziri zokwera mtengo, anthu amachepetsa chakudya chotentha chimene amadya. Amagula chakudya chotsika mtengo kapena chakudya chochepa, zikumapangitsa kudya chakudya chosakwanira. Iwo amaphikanso mwapang’ono chakudya chawo. Tizilombo tobweretsa matenda ndi tina sitimafa, ndipo chakudya cholimbikitsa thupi chochepa chimatsopedwa ndi thupi. Iwo amalephera kuŵiritsa madzi awo akumwa. Amangotola kanthu kalikonse kamene kadzayaka.
Anthu mamiliyoni ambiri atembenukira kuzokolezera moto zotsika mtengo, zonga matsatsa, mapesi, kapena ndoŵe yazinyama. Kumene nkhuni ziri zokwera mtengo ndipo ndoŵe siiri, kumawonekera kukhala kosungitsa ndalama moyenera kusonkhezera moto ndi ndoŵe koposa kuika m’munda. Kaŵirikaŵiri sangachitire mwina. Koma chotulukapo nchakuti nthaka imamanidwa zinthu zochititsa nthaka kukhala yachonde. M’kupita kwanthaŵi nthakayo imasukuluka ndi kuuma.
Ngakhale kuti awo okhala m’madera akumidzi kaŵirikaŵiri satofunikira kugula nkhuni zawo, kusoŵeka kumawonjezera kwambiri nthaŵi yotheredwa pokazitema. M’mbali za South America, akazi amathera 10 peresenti ya tsiku lawo kutema nkhuni. M’maiko ena a mu Afirika, kukatema nkhuni kwatsiku lathunthu kumapezetsa zokwanira masiku atatu okha. Nthaŵi zina mabanja amasankha mwana mmodzi kukagwira ntchito nthaŵi yonse kufunafuna zokolezera moto.
Mwakaŵirikaŵiri kwambiri, madera akumidzi amagwiritsiridwa ntchito kufikira zifunsiro za mzinda. Mitengo imadulidwa ndi kugulitsidwa mwamsanga kwambiri koposa mmene imakulira. Chotero imachepachepa, ndipo mabanjawo mwina amasamukira kumizinda kapena amathera nthaŵi yowonjezereka kudzitemera nkhuni.
Chotero, anthu mamiliyoni ambiri amataya nthaŵi ndi ndalama zambiri kuti afikire zosoŵa zawo zazikulu za zokolezera moto. Kodi njira zina nziti? Kwa amphaŵi, zimatanthauza kudya mochepera, kukhala ozizidwa, ndi kukhala popanda nyale usiku.
Zimene Zikuchitidwa
Zaka zingapo zapitazo ukulu wa vuto la nkhuni unayamba kuzindikiridwa ndi maiko onse. Bungwe la World Bank ndi magulu ena anathera ndalama m’maprojekiti olima nkhalango. Ngakhale kuti sionse a maprojekiti ameneŵa amene anapambana, zambiri zinaphunziridwa. Chidziŵitso chodziwonera chinasonyeza kuti chothetsera vuto la nkhuni sichinali kokha kungobzala mitengo yowonjezereka. Vuto lina linali lakuti olinganiza nthaŵi zina analephera kulingalira malingaliro a anthu a m’malowo. Chotero, m’dziko lina la Kumadzulo kwa Afirika, anthu apamudzi anawononga mbewu zamitengo chifukwa chakuti zinabzalidwa pamabusa achikhalire.
Vuto lina linali lakuti kulimanso nkhalango kumatenga nthaŵi yaitali. Kungatenge zaka zofikira ku 25 mitengo isanakhoze kukhala nkhuni zosatha. Zimenezi zimatanthauza kuchedwa kwa phindu loyenera kupezedwa m’zolimidwazo. Zimatanthauzanso kuti kubzala sikumathandizira kufikira zosowa zatsopano.
Maprojekiti obzalanso nkhalango akuchitika m’maiko ambiri. Koma kodi adzafikira zosoŵa zamtsogolo? Akatswiri a nkhalango amati ayi. Mitengo ikulikhidwa mofulumira kwambiri koposa imene ikubzalidwa. Wofufuza wa gulu lotchedwa Worldwatch Institute akulemba kuti: “Mwachisoni, chitsimikizo chandale zadziko ndi kudziyesa athayo pazinthu zofunikira kuthetsera mkhalidwe wochititsidwa ndi kutha kwa nkhalango zikusoŵeka mu ambiri a Maiko Osatukuka otenthawo. Pakali pano, “[hekitala] imodzi ya mitengo ndiyo imene inabzalidwa pa [mahekitala] khumi alionse a mitengo yolikhidwa. Mpatawo ngwaukulu kwambiri mu Afirika, kumene mitengo yolikhidwa makumi aŵiri mphambu asanu ndi anayi iriyonse pamabzalidwa umodzi. Kupezedwa kwa nkhuni zofunikazo kolinganizidwa m’Maiko Osatukuka podzafika [m’chaka cha] 2000 kukafunikira chiwonjezeko choŵirikiza nthaŵi khumi ndi zitatu pamlingo watsopano wa kubzala mitengo yosagwiritsiridwa ntchito m’maindasitale.”
Ziyembekezo Zamtsogolo
Lerolino anthu owona mtima ambiri akuphatikizidwa mokangalika m’kuyesayesa kuthetsa vuto la kupereŵera kwa nkhuni. Chikhalirechobe, kuyerekezera kwawo kwamtsogolo kaŵirikaŵiri nkosakondweretsa. Ofufuza openda dziko lapansi akulemba m’bukhu lawo lakuti Fuelwood—The Energy Crisis That Won’t Go Away kuti: “Masitepe onsewo pamodzi [a kugonjetsa vuto la nkhuni] sangachepetse mokwanira mtolo wa kusoŵeka kwa zokolezera moto ndi mitengo yomakwerakwera yogulira nkhuni zimene zidzaikidwa pa amphaŵi.” Bukhu lophunzitsira la FAO lakuti The Fuelwood Crisis and Population—Africa likufotokoza kuti: “Kuyesayesa kulikonse kudzakhala ndi kuthekera kochepa kwambiri kwa chipambano kufikira pamene kukula kwa chiŵerengero cha anthu kwalamuliridwa.” Komabe, bukhu limodzimodzilo, limasonyeza kuti chiŵerengero cha anthu chidzakulakulabe “chifukwa chakuti makolo amaŵa ngochuluka kwambiri koposa makolo alero. Makolo amaŵa abadwa kale.”
Mosiyana ndi kuneneratu kosakondweretsa koteroko, ulosi Wabaibulo umasonyeza bwino lomwe kuti Mulungu Wamphamvuyonse akulinganiza kubwezeretsa kotheratu Paradaiso padziko lapansili. (Luka 23:43) Iye sangalephere kuthetsa mavuto ocholoŵana a nkhuni, chiŵerengero cha anthu, ndi umphaŵi.—Yesaya 65:17-25.
Kodi Mtsogolo Mukuwonongedwa? Kutalitali! Mwamsanga ulosi wonena za Mlengi wathu wachikondi udzakwaniritsidwa wakuti: “Muwolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.”—Salmo 145:16.
[Mawu Otsindika patsamba 19]
‘Nkosapindulitsa kwambiri kuŵagaŵira chakudya ngati alibe njira yochiphikira’