Dziko Lapansi Lopanda Nkhalango—Kodi Chimenecho Nchimene Mtsogolo Mwasunga?
MALO akulu omwe kwa zaka zikwi zingapo anali okutidwa ndi nkhalango za mvula zogundira m’malo otentha masiku ano akukhala zipululu. Amene poyamba anali malo achilengedwe a mbalame zachilendo ndi zinyama zomwe zinathaŵira pansi pa denga la mamiliyoni amitundu yosiyanasiyana ya zomera ndi mitengo, ina ikumatalika mapazi 200 kufika mu mlengalenga, malo okongola, obiriŵira, ogwedera a dziko lapansi amenewa mofulumira akukhala dziko losakazidwa.a
Ndi zokhozetsa kuwononga munthu akuwononga mapiri ndi nkhwangwa, saw, bulldozer, ndi machisa. Akuwachepetsa iwo kukhala malo opanda mitengo, azipsyera, malo otenthedwa a zipululu zosiyidwa. Kuwononga kosagonjetseka kwa nkhalango za kumalo otentha za dziko lapansi kukuikidwa pa liŵiro lochititsa mantha la maekala 50 pa mphindi imodzi, kapena kuposa pa 100,000 square kilometers pa chaka—malo ofanana ndi ukulu wa Austria.b
Podzafika chaka cha 2000, molingana ndi akatswiri ena, chifupifupi 12 peresenti ya nkhalango za kumalo otentha zomwe zinatsala mu 1980 sizidzakhalako—sichidzakhala chokwaniritsa chochepa cha munthu, ngakhale ndi mbiri yake yakuwononga. Zomwe sizidzakhalakonso, zidzakhala mbalame zachilendo, nyama zamthengo, ndi moyo wa zomera zosiyanasiyana zimene sizingapezedwe m’malo ena a dziko lapansi. Munthu akuwononga mbali ya dongosolo locholowanacholowana la kudalirana kwa zamoyo ndi malo ozizinga lomwe liri lofunika koposa ku moyo wake ndi limene limapereka kwa iye mapindu osaŵerengeka.
Loposa theka la mankhwala amene munthu amagwiritsira ntchito amachokera ku zomera, ambiri koposa kuchokera ku zomera za ku malo otentha. Kodi maindastri angachitenji popanda magwero a mpira, turpentine, rattan, msungwi—zonse zopezeka mu nkhalango za kumalo otentha—kuphatikizapo unyinji wa bwazi la mumlalang’amba, maliroliro, utoto, ndi zonunkhiritsa chakudya? Mwa khungu ndi mosasamala, munthu akuwononga chuma cha mtengo waukulu.
Kuchokera ku nkhalango zazikulu zimenezi, unyinji wokulira wa mpweya womwe tipuma wopatsa moyo umapangidwa. Akatswiri a za sayansi, akuchenjeza kuti kuchepetsa kokulira kumeneku kwa nkhalango zopanga mpweya womwe tipuma kungawonjezere chotulukapo chowopedwa cha nkhalango zobiriŵira, kupangitsa malekezero a madzi a m’nyanja kukwera ku utali wodzetsa ngozi.
Kudula mitengo yamkhalango mopambanitsa kwakhala kale ndi chiyambukiro choipitsitsa ndi chamwamsanga pa mbali yaikulu ya dziko. Maiko onga ngati Brazil, Indonesia, ndi Philippines awona kasinthidwe kamwamsanga ka maiko awo kuchokera ku thengo la mitengo yambiri kufikira ku chipululu chopanda mitengo. “Ku Southeast Asia unyinji wa maekala 25 miliyoni omwe kale anali nthaka ya nkhalango tsopano amangobereka mitengo youmirira ndi udzu wopanda ntchito womwe supereka chakudya, mafuta, ngakhale zakudya za ng’ombe,” ikusimba tero World Resources Institute.
Kugwetsa ndi kugulitsa kwa zidutswa zambiri za mitengo kumatsimikizira kudula mitengo kopambanitsa mu Fiji mkati mwa zaka 20, kwa Thailand zidzatero podzafika kumapeto kwa zana limodzi, ndi chigwa cha nkhalango ya kumalo otentha ya ku Philippines zidzatero podzafika mu 1990, ikusimba tero Science Digest. Mu Australia kusakaza kwa nkhalango yake kuli kokulira—magawo aŵiri pa magawo atatu a nkhalango za kumalo otentha kulibiretu! India ikutaya maekala 3.2 miliyoni a nkhalango chaka chirichonse ndi nkhwangwa.
“Ponena za pakati pa ma 1980,” ikusimba tero magazini ya Natural History ya April 1986, “dziko lirilonse mu Africa likutaya kudzazidwa kwa mitengo. Ndithudi kupereŵera kwa nkhalango tsopano kuli lamulo m’Maiko onse Otukuka ozungulira Third World.” M’maiko 63 anthu 1.5 biliyoni akudula mitengo pa liŵiro lokulira kuposa mmene ingakulirenso, kupangitsa kupereŵera komwe kungatsogolere kokha ku kusowa kwa nkhalango ndi nkhuni. Akatswiri akuyembekezera kuti kupereŵera kumeneko kudzaŵirikiza kaŵiri podzafika chaka cha 2000.
Kuwononga nkhalango kumakhudza maziko enieni a kuthekera kwa kukhalapo kwa munthu—ulimi. Choyamba, pamene munthu agwetsa mitengo pamapiri ndi magomo kuti adzalepo mbewu yake, popanda zomera kuti zigwiririre nthaka m’malo ake, nthaka imakokoledwa mwamsanga. Ndiponso, m’maiko mmene nkhuni ziri zosowa, “Chiŵerengero choyerekezedwa pa matani mamiliyoni 400 a ndoŵe amatenthedwa chaka chirichonse . . . Kuotcha kwa feteleza wamphamvu kumeneku kukulingaliridwa kutsendereza kukolola kwa zinthu ndi matani oposa pa mamiliyoni 14.”
Kodi nkhalango zazikulu zadziko lapansi ziri kwenikweni zoweruzidwa ndi mphamvu zosabwezeka m’mbuyo? Kapena kodi mbadwo uno udzasiya chuma chochuluka cha dziko lapansi ndi kukongola kaamba ka ana ake? Umanena zambiri, umalemba m’mapepala, koma umachita zochepera. Chotero, ndi mtsogolo motani momwe udzasiira ana ake? Nthaŵi idzatiwuza, ndipo kwatsala nthaŵi yochepera.
[Mawu a M’munsi]
a 1 ft = 0.3 m.
b 1 a. = 0.4 ha.
[Mawu Otsindika patsamba 7]
M’maiko 63 anthu 1.5 biliyoni akudula mitengo pa liŵiro lokulira kuposa mmene ingakulirenso
[Chithunzi patsamba 7]
Maiko akusintha nkhalango zoti bii kukhala chipululu chopanda ntchito