Kodi Nyimbo Zingakuvulazenidi?
TAYEREKEZERANI izi: Mnzanu wakuntchito wakuitanani kupita kunyumba kwake kuchakudya chamadzulo. Mwavomera kupitako. Ndiyeno, mukucheza madzulowo, mukuzindikira zinthu zingapo zochititsa mantha ponena za wocherezayo. Iye ali ndi chibadwa chankhalwe, akusonyeza malingaliro ofuna kudzipha, akutukwana, ndipo akuchilikiza kulambira Mdyerekezi. Tsopano, kodi mungafune kudzacheza nayenso madzulo ena? Muyankha kuti “Ayi!”
Ndiponso, bwanji ngati mnzanuyo ajambula zikhulupiriro ndi malingaliro ake oipawo usikuwo ndi kukupatsani tepiyo? Kodi mukadziika pangozi mwakuliza mobwerezabwereza? Mwachiwonekere ayi.
Komabe, mfundo njakuti mamiliyoni ambiri lerolino akudziika pangozi mwanjira imeneyi. Chotsatirapo nchakuti, ambiri amene amamvetsera nyimbo zimenezi amatengera kulingalira ndi khalidwe limene nyimbozo zimalimbikitsa.
Kodi ndinyimbo zotani zimene tikunena? Ziyambukiro zoluluzika zingapezeke pafupifupi mu mtundu uliwonse wa nyimbo. Kaya wina amakonda nyimbo za classical, jazz, kapena mtundu wina, nkofunika kukhala wochenjera ndi wosankha.
Komabe, pali mitundu ina ya nyimbo zimene zimafotokoza nkhani zoipa kwambiri mosabisa. Zimenezi zimachititsa vuto lalikulu. U.S.News & World Report ikufotokoza mutu weniweni wa nyimbo za heavy metal kukhala “kupanduka kwa achichepere, kodzaza kotheratu ndi kugonana kwachiwawa ndi kulingalira kamodzikamodzi za kudzipha.” Dr. David Elkind akunena za magulu ena a rock amene “ali opandukiratu ndi kutukwana ndi makhalidwe oipa kwakuti amapereka chithunzi choipa pa nyimbo zonse za rock.” M’malo ena pazikuto za malekodi ndi matepi anyimbo pamalembedwa mawu ochenjeza za zinthu zoipa zamkati mwake.
Kodi anthu akungonena zoipitsa kwambiri nyimbozo chifukwa chakuti samazikonda, kapena kodi pali chifukwa chenicheni chokhalira wodera nkhaŵa? Tiyeni tipende mosamalitsa zina za nyimbo za rock zimene zikufikira anthu ambiri m’malekodi, mavidiyo anyimbo pa wailesi yakanema, ndi makonsati. Mupende kuti anthu amayambukiridwa nazo motani. Ndiyeno munene nokha kuti kaya zosangulutsa zimenezi nzosavulaza kapena ndipaizoni yamaganizo. Kodi ndizinthu zimene inuyo kapena banja lanu muyenera kusunga kapena ngakhale kumvetsera?