Kudziŵa Zizindikiro za Kupsinjika Maganizo mwa Mwana Wanu
“Malingaliro akupsinjika samangochitika okha: Iwo kaŵirikaŵiri amachititsidwa ndi zochitika zina kapena mikhalidwe.”—Dr. Lilian G. Katz.
KODI ndimotani mmene woyendetsa ndege angaonere kumene akupita ngati akuyendetsa ndege m’nthaŵi yausiku wamdima ndi wokhala ndi nkhungu? Kuyambira pamene inyamuka mpaka pamene itera, iye amadalira pazizindikiro. Pamakhala zipangizo zoposa zana limodzi pamalo okhalapo woyendetsa wake m’ndenge yaikulu, chizindikiro chilichonse chikumapereka chidziŵitso chofunika chodziŵitsa woyendetsayo za mavuto othekera kubuka.
Kukulira m’dziko lodzaza ndi zipsinjo kuli ngati kuuluka ndi ndege kupyola m’chimphepo cha namondwe. Kodi ndimotani mmene makolo angatheketsere kuulukako kochokera paubwana kufikira pauchikulire kukhala kwabwinobwino? Popeza kuti ana ambiri samalankhula ponena za zipsinjo zawo, makolo ayenera kuphunzira kudziŵa zizindikiro.
Thupi “Limalankhula”
Kupsinjika maganizo kwa mwana kaŵirikaŵiri kumawonekera kupyolera m’thupi. Mavuto ochititsidwa ndi maganizo, kuphatikizapo kupweteka m’mimba, kudwala mutu, kutopa, kubalalika kwa tulo, ndi kusapita kuchimbudzi, zingakhale zizindikiro zakuti chinachake sichili bwino.a
Kuleka kumva kwa Sharon kunachititsidwa ndi kusungulumwa kwakukulu kumene kunali kutafika pachimake. Pamene Amy anapita kusukulu, kupweteka m’mimba kwake kunachititsidwa ndi mantha akutalikirana ndi amake. Kubindikira m’mimba kwa John kunachititsidwa ndi kuvutika maganizo kwake pamene ankaona kumenyana kwachiwawa kwa makolo ake.
Kugonedwa paubwana kunali ndi ziyambukiro zakuthupi pa Ashley wa zaka khumi. “Ndikukumbukira kuti ndinalephera kupita kusukulu kwa sabata lonse [pamene anagonedwa mwakugwidwa] chifukwa chakuti ndinadwala,” iye akukumbukira motero. Buku lakuti When Your Child Has Been Molested limafotokoza kuti: “Vuto la kukumbukira za kugonedwa kokakamiza likhoza kupsinja maganizo a mwana ndi kumchititsa kudwala.” Zizindikiro zina za kupsinjika maganizo koteroko ndizo tizilonda m’thupi, kupweteka pokodza ndi kuchimbudzi, kudwaladwala m’mimba, mutu wobwerezabwereza, ndi kupweteka kwa mafupa ndi minofu kosadziŵika bwinobwino.
Pamene nthenda iwoneka kukhala yochititsidwa ndi maganizo, makolo ayenera kuwona chizindikirocho mwamphamvu. “Zilibe kanthu kaya mwanayo akungonamizira kapena akunena zenizeni,” akutero Dr. Alice S. Honig. “Chimene chili chofunika ndicho vuto lenilenilo lochititsa zimenezo.”
Machitidwe Amanena Zomveka Kuposa Mawu
Kusintha kwadzidzidzi kwa makhalidwe a mwana kaŵirikaŵiri kumakhala chizindikiro chakuti pakufunikira chithandizo. Buku lakuti Giving Sorrow Words likunena kuti: “Pamene mwana wanzeru ayamba kupeza magiredi otsika, zimenezo zimafunikira chisamaliro, chimodzimodzinso ndi mwana amene kale anali wovuta koma mwadzidzidzi nkukhala wofatsa kwambiri.”
Kuyamba kunama kwadzidzidzi kwa Timmy wa zaka zisanu ndi chimodzi zakubadwa kunayamba pamene amake anakhala otanganitsidwa kotheratu m’ntchito yawo. Mkhalidwe wamwano wamwadzidzidzi wa Adam wa zaka zakubadwa zisanu ndi chimodzi unachititsidwa ndi malingaliro a kusakhoza kwake kusukulu. Kuyambanso kukodzera pabedi kwa Carl wa zaka zisanu ndi ziŵiri kunali chizindikiro chakuti anali kufuna chisamaliro cha makolo, chimene tsopano chinawoneka kuti chinapita kwa mlongo wake wachichepere.
Makhalidwe akudzivulaza ali makamaka ovutitsa. Kudzipweteka kwa kaŵirikaŵiri kwa Sara wa zaka khumi ndi ziŵiri kunaonedwa kuti sikunali kaamba ka kusasamala pochita zinthu. Chiyambire pamene makolo ake anasudzulana, kudzivulaza kunali njira imene mosadziŵa anakumbukirira chikondi cha atate ake amene tsopano panalibe. Kaya kukhale kwakung’ono monga kudzivulaza kapena kwakukulu monga kuyesa kudzipha, mkwiyo wobisidwa mkati ndi machitidwe akudzivulaza uli chizindikiro cha kupsinjika maganizo kwakukulu.
Kulankhula Zakukhosi
“Mkamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima,” anatero Yesu Kristu. (Mateyu 12:34) Mtima wodzazidwa ndi zopweteka kaŵirikaŵiri umawoneka ndi zimene mwana amanena.
“Ana amene amafika panyumba ndi kunena kuti ‘Palibe munthu amene amandikonda,’ kwenikweni akukuuzani kuti iwo amadzida okha,” akutero Dr. Loraine Stern. Zingakhalenso zofanana ponena za kudzitama. Ngakhale kuti kumawoneka kukhala kusonyeza kukwezeka kwa munthu, kudzitama ponena za chinthu chenicheni kapena chongolingaliridwa kungakhale kuyesayesa kugonjetsa malingaliro akudziona kukhala wolephera.
Zowona, ana onse amadwala, amapulupudza nthaŵi zina, ndipo amadzigwiritsa mwala iwo okha panthaŵi zina. Koma pamene mavuto oterowo akhazikika popanda chifukwa chenicheni chowoneka, makolo ayenera kupenda tanthauzo la zizindikirozo.
Atapenda njira za makhalidwe a achichepere asanu ndi mmodzi amene anayambitsa chiwawa choipitsitsa, Mary Susan Miller anati: “Panali zizindikiro zokhutiritsa. Anyamatawo akhala akuzisonyeza kwa zaka zambiri, koma palibe amene anasamala. Achikulire anaona, koma anangozinyalanyaza.”
Tsopano kuposa ndi kale lonse, makolo ayenera kukhala maso kwambiri kuti adziŵe zizindikiro za kupsinjika kwa mwana ndi kuchitapo kanthu.
[Mawu a M’munsi]
a Mosiyana ndi zopweteka zongolingalira chabe, zimene zimaphatikizapo matenda ongoyerekezera, kudwala kochititsidwa ndi maganizo kuli kwenikweni. Komabe, chochititsa chake chimakhala chamalingaliro osati chathupi.
[Bokosi patsamba 25]
Kupsinjika Maganizo Ali m’Mimba?
Ngakhale mwana wosabadwa akhoza kuzindikira kupsinjika maganizo, mantha, ndi nkhaŵa zimene amake amapereka kupyolera m’masinthidwe a makemikolo oyenda m’mwazi mwawo. “Mwana wosabadwa womakulayo amamva kupweteka kulikonse kumene mkazi wokhala ndi pathupiyo amakhala nako,” akulemba motero Linda Bird Francke m’buku lake lakuti Growing Up Divorced. “Ngakhale kuti dongosolo la mitsempha la mwana wosabadwa ndi la mkaziyo sizolumikizana mwachindunji, pali unansi wina pakati pa aŵiriwo umene sungaswedwe.” Zimenezi zingafotokoze chifukwa chake, malinga nkunena kwa magazini a Time, kuyerekezera kwa 30 peresenti ya makanda a miyezi 18 ndi ocheperapo amakhala ndi mavuto ochititsidwa ndi kupsinjika maganizo kwa kusakondwa ndipo ngakhale nkhaŵa zosadziŵika bwino. “Makanda obadwa kwa akazi opanda chimwemwe ndi opsinjika maganizo nawonso kaŵirikaŵiri amakhala opanda chimwemwe ndi opsinjika maganizo,” akumaliza motero Francke.
[Bokosi patsamba 27]
Pamene Mwana Ayesa Kudzipha
“Kodi chingachitike nchiyani ngati ndigona tulo kwa zaka zana limodzi?” Lettie anafunsa atate ake zimenezo. Atate akewo anangonyalanyaza funsolo kukhala laubwana chabe. Koma Lettie anali wotsimikiza. Pambuyo pamasiku oŵerengeka anagonekedwa m’chipatala chifukwa chakuti anameza botolo lonse la mibulu yogoneka tulo.
Kodi muyenera kuchitanji ngati mwana wanu alingalira za kudzipha kapena ngati ayesadi kutero? “Mwamsanga funani chithandizo chaukatswiri,” likusonkhezera motero buku lakuti Depression—What Families Should Know. “Kuchiritsa anthu ofuna kudzipha sikuli ntchito ya anthu wamba, ngakhale awo osamalira kwambiri munthu wopsinjikayo. Mungaganize kuti mwalankhula naye ndipo mwachotsa mwa iye malingaliro akufuna kudzipha pamene kuli kwakuti iye wangokhala chete kufikira pamene malingalirowo adzabukanso ndi zotsatirapo zowopsa.”
Ndi chithandizo choyenera, kungakhale kothekera kuchiritsa malingaliro akuyesa kudzipa mwa mwana. “Anthu ochuluka amene amayesa kudzipha, kwenikweni samafuna kudzipha,” limatero buku logwidwa mawu pamwambalo. “Iwo amangofuna kuthetsa zovuta zawo. Zochita zawo zili kwenikweni chiitano cha chithandizo.” Mumpingo Wachikristu, makolo amene sangathe kusamalira zikhoterero zofuna kudzipha angalandire chichilikizo chachikondi ndi uphungu wa Malemba wochokera kwa akulu.