Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 10/8 tsamba 27-29
  • “Chotengera Chofookerapo” Kodi Nkunyoza Akazi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Chotengera Chofookerapo” Kodi Nkunyoza Akazi?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zotengera Zochepa Mphamvu?
  • “Momwemonso, . . . Monga mwa Chidziŵitso”
  • Achitireni Ulemu
  • Oloŵa Nyumba a Moyo
  • Malangizo Anzeru kwa Okwatirana
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kupatsa Ulemu Akazi Mumpingo
    Galamukani!—1992
  • Akazi Achikristu Ayenera Kuchitiridwa Ulemu
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kodi Akazi Ali ndi Tsogolo Lotani?
    Galamukani!—1998
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 10/8 tsamba 27-29

Lingaliro la Baibulo

“Chotengera Chofookerapo” Kodi Nkunyoza Akazi?

“KODI NCHIFUKWA NINJI AKAZI AMAGAMULIDWIRATU PA UKAZI WAWO MMALO MWA CHIDZIŴITSO, LUSO, NDI NZERU YAWO?”​—⁠BETTY A.

“AKAZI AMACHITITSIDWA KUGANIZA KUTI ALI ZOLENGEDWA ZOTSIKIRAPO.”​—⁠LYNN H.

KODI mawu a Baibulo akuti “chotengera chofookerapo” amanyozetsa akazi? Vesi la Baibulo lobutsa funsolo ndilo 1 Petro 3:​7, limene limati: “Amuna inu, khalani nawo monga mwa chidziŵitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera [chofookerapo, NW], monganso woloŵa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.”

Pamene Petro analemba mawu ameneŵa kwa Akristu anzake, akazi anali ndi zoyenera zochepa kwambiri, osati m’dziko lakale lachikunja mokha komanso pakati pa chitaganya Chachiyuda champatuko. Kodi Petro ndi Akristu oyambirira anali kuchirikiza lingaliro lofala la panthaŵiyo ponena za akazi?

Zotengera Zochepa Mphamvu?

Kodi ndimotani mmene oŵerenga mawu a Petro a m’zaka za zana loyamba akanamvera liwulo “chotengera chofookerapo”? Liwu Lachigiriki la chotengera (skeuʹos) linagwiritsiridwa ntchito nthaŵi zambiri m’Malemba Achigiriki ndipo limatanthauza zonyamulira zinthu zosiyanasiyana, zipangizo, ziwiya, ndi zinthu zina zogwiritsira ntchito. Potchula akazi kuti “chotengera chofookerapo,” Petro sanali kunyoza akazi, pakuti mawuwo anapereka lingaliro lakuti amuna nawonso anali chotengera chosalimba kapena chofooka. Mavesi ena a Baibulo amagwiritsira ntchito mawu okuluŵika oterowo ponena za akazi ndi amuna omwe, monga ngati “zotengera zadothi” (2 Akorinto 4:⁠7) ndi “zotengera zachifundo” (Aroma 9:23). Zoonadi, Petro amasonyeza akazi kukhala mtundu “wofookerapo.” Koma Aroma 5:6 amagwiritsira ntchito ‘kufooka’ kosonyezedwa ndi anthu onse​—⁠amuna ndi akazi. Motero, Akristu oyambirira sakanalingalira konse liwulo “chotengera chofookerapo” kukhala mawu onyoza akazi.

Mmalomwake, mawu a Petro akanalingaliridwa kukhala akukweza malo a akazi. M’tsiku la Petro kunalibiretu kulemekeza akazi. Monga momwe Mulungu anali ataoneratu kalekale, kaŵirikaŵiri amuna anapondereza ndi kuchitira nkhanza akazi awo mwakuthupi, mwakugonana, ndi mwamalingaliro. (Genesis 3:16) Motero, uphungu wa Petro kwa amuna Achikristu kwenikweni unatanthauza kuti: Musagwiritsire ntchito mphamvu imene chitaganya cha dziko chapatsa amuna.

Tiyeni tipende mosamalitsa liwulo “chofookerapo.” M’vesi limeneli Petro anali kunena osati za malingaliro, koma za mikhalidwe ya thupi. Amuna ali zotengera zofooka; powayerekeza, akazi ali zotengera zofookerapo. Motani? Mamangidwe a mafupa ndi minyewa ngakuti kaŵirikaŵiri amuna amakhala ndi nyonga yochuluka yakuthupi. Komabe, palibe chisonyezero chakuti Petro anali kuyerekezera za nyonga ya khalidwe, yauzimu, kapena ya maganizo. Kwenikweni, ponena za michitidwe ya malingaliro pa zinthu, mawu ofotokoza bwino kwambiri akazi angakhale akuti iwo ali osiyana ndi amuna, osati kwenikweni kuti ali ofookerapo kapena amphamvupo. Baibulo limalongosola za mkhalidwe wina wamphamvu wa khalidwe, chipiriro, ndi luntha wa akazi amene anatsatira njira ya Mulungu​—⁠onga ngati Sara, Debora, Rute, ndi Estere, kungotchulapo oŵerengeka. Amuna odzichepetsa alibe vuto la kuzindikira kuti akazi angakhale anzeru kwambiri kuposa mmene iwo alili.

Komabe, ena amakhulupirira kuti kutchulidwa kwa akazi kukhala ‘ofookerapo’ kumatanthauza kuti iwo ndi anthu otsikirapo. Komatu lingalirani chitsanzo ichi. Munthu ali ndi zotengera ziŵiri zothandiza. Chimodzi chikumakhala cholimba, chinacho chosalimba kwenikweni. Kodi tingati chotengera chachiŵiricho nchosafunika kwenikweni chifukwa chakuti icho chili chosalimba kwambiri? Ndithudi, chosalimba kwambiricho chimasamaliridwa kwambiri ndiponso mwaulemu koposa cholimbacho. Motero, kodi mkazi ali wosafunika kwambiri chifukwa chakuti ali ndi nyonga yakuthupi yocheperapo kuposa mwamuna? Kutalitali! Petro akugwiritsira ntchito mawuwo “chotengera chofookerapo,” osati kuti anyoze akazi, koma kupereka ulemu.

“Momwemonso, . . . Monga mwa Chidziŵitso”

Petro anafulumiza amuna ‘momwemonso . . . kukhala nawo [akazi awo] monga mwa chidziŵitso.’ “Momwemonso” kwa yani? M’mavesi oyambirira Petro anali kufotokoza za chisamaliro chachikondi cha Kristu kwa otsatira ake, ndipo analangiza amuna kusamalira akazi awo “momwemonso.” (1 Petro 2:​21-25; 3:⁠7) Nthaŵi zonse Kristu anaika ubwino ndi zokonda za ophunzira ake patsogolo pa zikhumbo ndi zokonda zake. Iye anali wokondweretsedwa ndi ubwino wawo wauzimu ndi wakuthupi, ndipo analingalira za zofooka zawo. Amuna ayenera kutsanzira chitsanzo chachikondi cha Kristu, kuchitira akazi awo “momwemonso.”

Ukwati woyenda bwino sumangochitika mwangozi. Mwamuna ndi mkazi yemwe ayenera kudziŵa mmene angachirikizire chipambano mu ukwati wawo. Chifukwa chake, chilangizo cha Petro nchakuti amuna apitirizebe kukhala ndi akazi awo “monga mwa chidziŵitso.” Amuna afunikira kuphunzira mmene Yehova ndi Mwana wake, Yesu Kristu, anachitira ndi akazi. Afunikira kudziŵa za mmene Mulungu amafunira kuti iwo achitire akazi awo.

Ndiponso, amuna afunikira kudziŵa akazi awo bwino lomwe​—⁠malingaliro awo, nyonga, zofooka, zimene amakonda, ndi zimene sakonda. Afunikira kudziŵa mmene angalemekezere nzeru ya akazi awo, chidziŵitso, ndi kulemekezeka. Baibulo limati: “Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda Eklesia, nadzipereka yekha m’malo mwake. Koteronso amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha; pakuti munthu sanadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga.”​—⁠Aefeso 5:​25, 28, 29.

Achitireni Ulemu

Pamene Petro anatchula akazi kukhala “chotengera chofookerapo,” ananenanso kuti amuna ayenera ‘kuwachitira ulemu.’ M’Chigiriki, dzinalo ti·meʹ limapereka lingaliro la ulemu, kukuza, kufunika, kukhala cha mtengo wapatali. Mwa mawu ena, kuchitira ulemu sikuli chabe mchitidwe wa kuyanja koma kuzindikira chimene chili chowayenerera. Paulo analangiza Akristu onse, amuna ndi akazi omwe, motere: “M’chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.”​—⁠Aroma 12:⁠10.

Ndithudi Yehova Mulungu samalingalira akazi kukhala zokometsera chabe. Mu Israyeli, malamulo a Mulungu anagwira ntchito mofanana pa amuna ndi akazi omwe amene anali ndi liwongo la chigololo, kugonana kwapachibale, kugonana ndi nyama, ndi milandu ina. (Levitiko 18:​6-17, 23, 29; 20:​10-12) Akazi ankaphatikizidwa m’zochitika za Masabata, za malamulo a Anaziri, za mapwando, ndi m’makonzedwe ena ambiri a Chilamulo. (Eksodo 20:10; Numeri 6:2; Deuteronomo 12:18; 16:​11, 14) Amayi, ndiponso atate, anayenera kulemekezedwa ndi kumveredwa.​—⁠Levitiko 19:3; 20:9; Deuteronomo 5:16; 27:16; Miyambo 1:⁠8.

Mavesi 10 kufikira 31 a Miyambo chaputala 31 amapereka ulemu kwa “mkazi wangwiro” chifukwa cha kukhulupirika kwake, khama pantchito, ndi nzeru posamalira mathayo ake ambiri. Iye anazindikiridwa moyenerera chifukwa cha phande lake m’kusamalira malonda a banja, ndiponso nkhani zina za ndalama. Ha, zimenezi nzosiyana chotani nanga ndi mkhalidwe wa maganizo wa amuna ena amene amaganiza za akazi kukhala zinthu zokometsera chabe! Pambuyo pake, mu mpingo Wachikristu woyambirira, akazi anapatsidwa mzimu woyera monga mboni za Kristu. (Machitidwe 1:​14, 15; 2:​3, 4; yerekezerani ndi Yoweli 2:​28, 29.) Motero, akazi ena ali ndi mtsogolo mwa kudzakhala oweruza a kumwamba a amuna, akazi, ndipo ngakhale angelo. (1 Akorinto 6:​2, 3) Zoonadi, akazi sanayenere kuphunzitsa pamsonkhano wa mpingo; komabe, panali mikhalidwe ina pamene akazi Achikristu ankapemphera kapena kunenera. Iwo anaikidwa kukhala aphunzitsi a akazi achichepere, ana, ndiponso kwa awo amene anali kunja kwa mpingo.​—⁠Mateyu 24:14; 1 Akorinto 11:​3-6; Tito 2:​3-5; yerekezerani ndi Salmo 68:⁠11.

Chisonyezero china chabwino chonena za zimene Petro anali kuganiza pamene ananena za kuwachitira ulemu chimapezeka pa 2 Petro 1:17. Pamenepo timaŵerenga kuti Yehova analemekeza Yesu mwa kumvomereza pamaso pa ena pamene anati: “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa.” Mofananamo, mwamuna ayenera kusonyeza mwa zochita zake, poyera ndi mwamseri momwe, kuti amachitira ulemu mkazi wake.

Oloŵa Nyumba a Moyo

M’mbiri yonse, kaŵirikaŵiri amuna aona akazi kukhala osafunikira kulemekezedwa kwambiri​—⁠monga akapolo, kapena monga chiwiya chokhutiritsira amuna. Ndithudi lingaliro Lachikristu la kuchitira akazi ulemu limawapatsa malo okwezeka aulemu. Barnes’ Notes on the New Testament imati chilangizo cha Petro “chili ndi choonadi chofunika kwambiri ponena za akazi. Pansi pa dongosolo lililonse la chipembedzo kusiyapo dongosolo Lachikristu, mkazi waonedwa mumkhalidwe uliwonse monga wotsika kwa mwamuna. Chikristu chimaphunzitsa kuti . . . mkazi ali ndi kuyenera kwa kukhala ndi ziyembekezo zonse ndi malonjezo amene chipembedzo chimapereka. . . . Choonadichi chikatulutsa akazi mu mkhalidwe wawo wonyozedwa kulikonse, ndi kuthetseratu nkhanza zina za mtundu wa anthu.”

Popeza kuti Kristu ndiye mwini wa amuna ndi akazi omwe, pali chifukwa chachikulu chimene amuna ayenera kusamalilira akazi awo monga chuma cha Kristu. Atangotchula za akazi kukhala “chotengera chofookerapo,” mawu a Petro akupitiriza kuti: “Monganso woloŵa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.” (1 Petro 3:⁠7b) Petro anasonyeza kuti nkhanza ya mwauna kwa mkazi wake ikawononga unansi wake ndi Mulungu, ikumaletsa mapemphero ake.

Mawu akuti “chotengera chofookerapo” samanyoza akazi konse. Pamene kuli kwakuti Yehova amaika amuna kukhala mutu wabanja, iye samavomereza kuti amuna azichitira akazi mosayenera. Mmalomwake, iye amalangiza kuti mwamuna, pokhala ndi chidziŵitso cha mkazi, ayenera kumpatsa chisamaliro ndi ulemu.

Baibulo limalangiza amuna okwatira ndi osakwatira omwe kuchitira akazi ulemu, osawachitira monga anthu onyozeka. Amuna ndi akazi amene amalambira Mulungu mwakhama ndi amene amalemekezana adzalandira madalitso aakulu ku dzanja la Mulungu.​—⁠Yerekezerani ndi 1 Akorinto 7:⁠16.

[Mawu a Chithunzi patsamba 27]

Miss G. E. K. / Katswiri wojambula: Alice D. Kellogg 1862-1900

Mwa chilolezo cha Joanne W. Bowie

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena