Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 12/8 tsamba 8-11
  • Dziko Lapansi—Mphatso Yathu ya kwa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Lapansi—Mphatso Yathu ya kwa Mulungu
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Dziko Lapansi—Lodabwitsa Ndiponso Lokongola
  • Anthu Osayamika Osayenera Mphatso ya Mulungu
  • Pamene Mphatso ya Mulungu Idzayamikiridwa
  • Kodi Dziko Lapansi Lidzawonongedwa?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Anthu Apitiriza Kuwononga Dzikoli N’kufika Poti Silingakonzedwenso?
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Kodi Planeti Dziko Lapansi Lidzakhala Chiyani?
    Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Pulaneti Lokhala ndi Zamoyo
    Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa?
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 12/8 tsamba 8-11

Dziko Lapansi—Mphatso Yathu ya kwa Mulungu

“PACHIYAMBI Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Ananenanso kuti dziko lapansi linali ‘labwino ndithu.’ (Genesis 1:1, 31) Kunalibe miyulu ya zinyalala zimene zinaliwononga; kunalibe madzala amene analiipitsa. Mphatso yokongolayo inaperekedwa monga choloŵa kwa anthu: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana anthu.”—Salmo 115:16.

Pa Yesaya 45:18, iye amatchula chifuno chake ponena za dziko lapansi kuti: “Atero Yehova amene Analenga kumwamba, iye ndiye Mulungu [woona, NW] amene Anaumba dziko lapansi, Nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; iye analiumba akhalemo anthu; ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.”

Amasonyeza kwenikweni thayo la munthu kulinga ku dziko lapansi—‘kulilima ndi kuliyang’anira.’—Genesis 2:15.

Yehova amapereka chitsanzo chabwino. Amalisamalira dziko lapansi. Njira ina imene amachitira zimenezo ndi mwa kubwezeretsa makonzedwe ofunika kwambiri a dziko lapansi, zinthu zimene zamoyo zonse zimadalirapo. Kope lapadera la Scientific American linali ndi nkhani yokhudza zingapo za njira zimenezi, zimene zimaphatikizapo njira yopatsa dziko lapansi nyonga, njira yobwezeretsa nyonga m’zamoyo, kayendedwe ka madzi, kayendedwe ka oxygen, kayendedwe ka carbon, kayendedwe ka nitrogen, ndi kayendedwe ka maminero.

Dziko Lapansi—Lodabwitsa Ndiponso Lokongola

Katswiri wazamoyo wotchuka kwambiri Lewis Thomas, analemba motamanda kwambiri dziko lapansi m’magazini a sayansi otchedwa Discover motere:

“Dziko lapansi ndilo chinthu chodabwitsa kwambiri, chachilendo zedi chimene tikuchidziŵa pakali pano m’chilengedwe chonse, chinthu chozizwitsa kopambana m’sayansi ya chilengedwe, chovuta kuchidziŵa bwino pa kuyesayesa kwathu konse. Tangoyamba kumene kumvetsa mmene lilili lachilendo ndi lokongola, mmene limachititsira chidwi, chinthu chokongola koposa chomazungulira dzuŵa, chokhala ndi mlengalenga wake wa bluu, chomapanga ndi kutulutsa okosijeni yakeyake, kuloŵetsa nitrogen yakeyake m’nthaka yake kuchokera mumpweya, chomakonza machedwe akeake m’nkhalango zake za mvula, chomapanga chodzichinjiriza nacho mwa kugwiritsira ntchito zotsala za zinthu zomwe zinali zamoyo: mapiri achoko, mitandadza ya makorali, zotsala za zamoyo zoyambirira zomwe tsopano zili zophimbika ndi zamoyo zatsopano kuzungulira dziko lonse.”

Ameneŵa ndi makonzedwe ochepa chabe amene Yehova wakonza kuti dziko lapansi lipitirize monga mphatso yokongola kwa anthu, mudzi wolengedwa kuti akhaleko kosatha kaamba ka anthu ndi zolengedwa zina miyandamiyanda. Salmo 104:5 limati: “Anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka ku nthaŵi yonse.” Mboni ina youziridwa inachirikiza kukhalitsa kumeneku kwa dziko lapansi kuti: “Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse.”—Mlaliki 1:4.

Opita m’mlengalenga ozungulira dziko lapansi ananena zochuluka pa mbulunga yokongola yofuna chisamaliro imeneyi, yomayenda mumpita mwake kuzungulira dzuŵa ndipo anena kuti anthu afunika kuyamikira kukongola kwake ndi kulisamalira. Wopita m’mlengalenga wina Edgar Mitchell, pamene anayang’ana dziko lapansi nthaŵi yoyamba ali m’mlengalenga, anatumiza uthenga pawailesi ku Houston kuti: “Likuoneka ngati juwelo lonyezimira la bluu ndi loyera . . . lokutidwa ndi mitambo yoyera yoyenda pang’onopang’ono mozungulira . . . , monga ngale yaing’ono m’nyanja yaikulu yakuda bi yosafotokozeka.” Wopita m’mlengalenga wina Frank Borman anati: “Tili ndi pulaneti yokongola kwambiri. . . . Zimene zimandidabwitsa kwambiri nzakuti nchifukwa ninji sitimayamikira zimene tili nazo.” Mmodzi wa opita m’mlengalenga paulendo wa Apollo 8 wopita kumwezi anati: “Kulikonse kumene tinayang’ana m’chilengedwe chonse, kumene kunali maonekedwe pang’ono ndi ku dziko lapansi chabe. Kumeneko tinaona maonekedwe a nyanja abluu waulemerero, kufiirira ndi kudera kwa nthaka, ndi kuyera kwa mitambo. . . . Linali chinthu chokongola koposa kuona, m’miyamba yonse. Anthu pansi pano sadziŵa zimene ali nazo.”

Maumboni akusonyeza kuti mawu amenewo ali oona—anthu sadziŵa chuma chimene ali nacho. M’malo mosamalira mphatso imeneyi yochokera kwa Mulungu, anthu akuiipitsa ndi kuiwononga. Opita m’mlengalenga aonanso zimenezi. Paul Weitz, mtsogoleri wa ulendo woyamba wa chombo cha m’mlengalenga chotchedwa Challenger, ananena kuti ngati uli m’mlengalenga “nzowopsa” kuona mmene munthu wawonongera mpweya wokuta dziko lapansi. “Mwatsoka, dzikoli likukhala pulaneti lotumbuluka mofulumira.” Anawonjezanso kuti: “Kodi zimenezi zikutiuza chiyani? Kuti tikuipitsa mudzi wathu.” Ndipo kuwononga kumeneku kwachitika mofulumira kowopsa makamaka mu “masiku otsiriza” ano. Yehova walengeza chiweruzo chake pa awo owononga dziko lapansi, kuti, ‘adzawononga iwo akuwononga dziko lapansi.’—Chivumbulutso 11:18.

Anthu Osayamika Osayenera Mphatso ya Mulungu

Anthu okonda chuma apondereza miyezo yauzimu kuti achite ntchito za thupi mosadziletsa. Zitsogozo zogwira ntchito zimene Yehova anapatsa anthu kaamba ka moyo wachimwemwe ndi wokhutiritsa zakankhidwira pambali ndi mzimu wa ine choyamba umene ulipo m’nthaŵi yathu.

Timoteo Wachiŵiri 3:1-5 amafotokoza bwino lomwe nthaŵi zowopsa zimene tikukhalamo kuti: “Zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiŵembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.”

Malonda amakulitsa mzimu wokonda kugula zopambanitsa, ndipo kusatsa malonda ndiko chiŵiya chake. Kusatsa malonda kwina kochuluka nkoyenera; komanso kwina kochuluka nkosayenera. Komalizaku kukugwirizana ndi zonena za Eric Clark mu The Want Makers: “Kusatsa malonda sikumangothandizira kugulitsa zinthu zolakwika kwa anthu amene sangazikwanitse, komanso kumatero pamitengo yokwera mosayenera.” Alan Durning wa World Watch akuti: “Zimene osatsa malonda amagulitsa si zinthu koma makhalidwe, kaonedwe ka zinthu, maloto, akumagwirizanitsa katundu wawo ndi zolakalaka zosatha za mtima.” Cholinga cha kusatsa malonda ndicho kutikhalitsa osakhutira ndi zimene tili nazo ndi kukhumbira zimene sitifunikira. Kumadzutsa chilakolako chachikulu; kumachititsa anthu kungogula zinthu mwadyera; kumachititsa madzala ochuluka oipitsa dziko lapansi. Chikoka chake chonyenga chimaloŵa pang’onopang’ono ngakhale m’mitima ya aja aumphaŵi wadzaoneni. Ambiri osatsa malonda amalimbikira kugulitsa katundu wodziŵika kuti amapha anthu kapena kuwadwalitsa.

Chinthu chofunika ndicho kaimidwe kathu ndi Mulungu, malinga ndi kunena kwa Mlaliki 12:13 kuti: “Mawu atha; zonse zamveka zatha; opa[ni] Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.” Awo amene amatero adzayenerera moyo m’Paradaiso woyera wa Yehova! Yesu analonjeza kuti: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.”—Yohane 5:28, 29.

Pamene Mphatso ya Mulungu Idzayamikiridwa

Ndipotu dziko lapansi limenelo lidzakhala lokongola modabwitsa chotani nanga! Yehova watifotokozera za ilo mochititsa chidwi kuti: “[Ine Yohane] ndinaona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kunalibenso nyanja. [Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:1, 4.

Ndipo sipadzakhalanso zinthu zoyamba zonga madzala, zotayidwa zapoizoni, ndi aja amene amakatayira zinthu zawo zotha ntchito kwa ena. Ndiyeno anthu okha amene adzakhala pa dziko lapansi ndi aja amene amakonda anansi awo monga iwo eni, amene amatamanda Yehova chifukwa cha mphatso yake ya dziko lapansi, ndi amene amafuna kulisamalira ndi kulisunga mumkhalidwe wa paradaiso.—Mateyu 22:37, 38; 2 Petro 3:13.

[Bokosi patsamba 11]

Kupanda Pake Kwa Kukonda Chuma

Yesu analankhula choonadi chosabisa pamene anachenjeza kuti: “Yang’anirani, mudzisungire kupeŵa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” (Luka 12:15) Zimene tili nazo sindizo zofunika ayi; chimene ife tili ndicho chofunika. Nzosavuta kutanganitsidwa ndi zochita za moyo—kupanga ndalama, kukundika chuma, kususukira zokondweretsa zonse zomwe thupi limalakalaka—tikumaganiza kuti tili ndi moyo wokhutiritsa, wosasoŵa kanthu, pamene tingakhale tikusoŵa kanthu kabwino koposa kamene moyo ungapereke.

Timayamba kuzindikira zimene tataya kokha pamene moyo ulikutha. Timazindikira kuona kwa zimene Baibulo limanena: Moyo ngwaufupi kwambiri—ndiwo nkhungu imene imazimiririka, utsi umene umafuka, mpweya, mthunzi umene umapitirira, udzu umene umanyala, duŵa limene limafota. Kodi wapita kuti? Kodi takwaniritsa chiyani? Nchifukwa ninji tinali ndi moyo? Kodi ndi zokhazi basi? Kodi nzachabechabe, kungothamangitsa mphepo?—Yobu 14:2; Salmo 102:3, 11; 103:15, 16; 144:4; Yesaya 40:7; Yakobo 4:14.

Munthu amene alikufa m’chipatala, akuyang’ana pazenera, kuona phiri dzuŵa lili nde, chigawo chomera udzu ndi namsongole, maluŵa angapo otsala, timba akupalapasa m’fumbi kufuna timbewu—zinthu zosachita nazo chidwi kwenikweni. Koma kwa munthu yemwe alikufayo, nzokongola. Chisoni chachikulu chimgwira, poganiza za tinthu tosangalatsa timene waphonya, tinthu tating’ono tofunika kwambiri. Tonseto tikumapita msanga!

Malemba Achigiriki a Baibulo amafotokoza bwino zimenezo motere: “Sitinatenga kanthu poloŵa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.” (1 Timoteo 6:7, 8) Malemba Achihebri amafotokoza molunjika kwambiri: “Monga anatuluka m’mimba ya amake, adzabweranso kupita wamaliseche, monga anadza osatenga kanthu pa ntchito zake, kakunyamula m’dzanja lake.”—Mlaliki 5:15.

[Mawu a Chithunzi patsamba 8]

Chithunzithunzi cha NASA

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena