Kodi Mankhwala Ake Nchiyani?
“PALI chikhulupiriro chomakula chakuti thanzi la anthu, ndipo mwinamwake ngakhale kukhalapo kwathu monga mtundu wa zamoyo, kudzadalira pa kukhoza kwathu kuzindikira matenda omwe akubuka. . . . Kodi tikanakhala kuti lero ngati HIV ikanakhala kachilombo koyenda ndi mphepo? Ndipo pali umboni wotani wakuti nthenda yonga imeneyo singadzatero mtsogolo?” anatero D. A. Henderson— amene anathandiza kwambiri pa kuthetsa nthomba—kwa gulu la asayansi ku Geneva, Switzerland, mu 1993.
Kodi matenda omwe akubuka angazindikiridwe motani? Njira yoyambirira yochenjeza za miliri ya matenda a m’madera otentha ndiyo malaboletale 35 apadziko lonse ogwirira ntchito pamodzi amene amadziŵitsa bungwe la World Health Organization (WHO). Komabe, kufufuza komwe kunachitidwa pa malaboletale ameneŵa kunasonyeza kuti ochepera theka la iwo ndiwo anali okhoza kuzindikira encephalitis yachijapani, ma hantavirus, ndi malungo a Rift Valley—onsewo ndi matenda akupha. Okwanira 56 peresenti okha ndiwo anakhoza kuzindikira yellow fever, vairasi yonyamulidwa ndi udzudzu imene imachititsa kusanza, chiŵindi kulephera kugwira ntchito, ndi kukha mwazi mkati mwa thupi. Mu 1992 anthu osachepera 28 anafa ku Kenya ndi yellow fever madokotala asanapeze chochititsa nthendayo. Kwa miyezi isanu ndi umodzi iwo anaganiza kuti anali kulimbana ndi malungo.
Vuto lina la maprogramu ofufuza nlakuti iwo satha kuzindikira matenda amavairasi omwe akubuka obwera pang’onopang’ono. Mwachitsanzo, HIV imabisala mwa munthu, kufalikira kwa ena, ndiyeno kudzatulukira monga AIDS mwina patapita zaka khumi. Mliri wa AIDS womwe ulipo unabuka pafupifupi nthaŵi imodzi pamakontinenti atatu ndipo mosataya nthaŵi unaloŵa m’maiko ena 20. Mwachionekere, panalibe chenjezo lake loyambirira!
Ngakhale kuti pali mavutowo, asayansi ambiri akuyang’anabe kutsogolo ndi chidaliro, akumalankhula motsimikiza za zinthu zazikulu zimene adzapeza ndi zipambano zawo zimene zidzakhalakodi zaka zakutsogolo. International Herald Tribune ikusimba kuti: ‘Chiyembekezo chachikulu cha zipambano zenizeni, amatero asayansi ambiri, chili pa biotechnology, kusanduliza majini m’maselo amoyo. Asayansi m’mabungwe a biotechnology akhulupirira kuti adzapanga maselo otulutsa zinthu zakupha tizilombo ta matenda, ndiko kuti, mtundu watsopano wa mankhwala opangidwa ndi genetic engineering.’
Komabe, zimenezi zili ndi kuipa kwake. Genetic engineering yatheketsa kuika majini m’vairasi yabwino kuti vairasiyo ipereke majiniwo mwa anthu. Tekinoloji imeneyi ingagwiritsiridwe ntchito bwino, mwinamwake kutheketsadi kupangidwa kwa otchedwa mankhwala opangidwa ndi genetic engineering. Komanso tekinoloji imeneyi ingagwiritsiridwenso ntchito pazifuno zoipa.
Mwachitsanzo, majini a Ebola angakhoze kuikidwa mwangozi kapena mwadala m’vairasi, monga ya fuluwenza kapena chikuku. Ndiyeno vairasi yakupha imeneyo ingafalikire mwa kutsokomola kapena kuyetsemula. Dr. Karl Johnson, amene wathera moyo wake pa kufufuza mavairasi onga Machupo ndi Ebola, anati posapita nthaŵi zingachitike kuti ‘munthu wamisala wokhala ndi makina ogulidwa madola zikwi zoŵerengeka amenenso ali ndi maphunziro apakoleji mu biology angapange tizilombo towopsa kuposa Ebola.’ Akatswiri ena a biology ali ndi nkhaŵa imodzimodziyo.
Mankhwala Ake
Kuthetsa mavuto a matenda oyambukira sikuli chabe nkhani yopanga mankhwala atsopano. Kumaphatikizapo kuthetsa mavuto a umphaŵi, nkhondo, othaŵa kwawo, anamgoneka, kuchulukitsa kwa anthu m’mizinda, moyo woipa, kuipitsa, ndi kuwononga malo okhala amene amachirikiza matenda. Ganizanipo moona mtima. Kodi mulingalira kuti anthu adzakhoza kuthetsa mavuto aakulu ameneŵa?
Mawu a Mulungu amachenjeza kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” Nanga ndani amene tiyenera kukhulupirira? Lembalo likupitiriza: “Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake; amene Analenga zakumwamba ndi dziko lapansi.” Yehova yekha, Mlengi wa anthu, ndiye adzachotsa zothetsa nzeru zimene anthu akuyang’anizana nazo.—Salmo 146:3-6.
Mawu ouziridwa a Yehova, Baibulo, ponena za ulosi waukulu wa Yesu wa “chizindikiro cha . . . mathedwe a nthaŵi ya pansi pano,” analosera za masautso a matenda amene akukantha mbadwo wathu. Yesu anati: ‘Kudzakhala . . . miliri m’malo akutiakuti.’—Mateyu 24:3-8; Luka 21:10, 11.
Komabe, Baibulo limanenanso za nthaŵi ya mtsogolo padziko lapansi mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu pamene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24; Mateyu 6:9, 10) Chotero aja okhulupirira Yehova ali ndi chifukwa champhamvu chokhulupiririra kuti anthu omvera posachedwapa adzalandira chimasuko chosatha osati ku matenda akupha okha amene akantha anthu komanso ku mavuto amene amachirikiza matenda. Akristu oona amayamikira kuyesayesa kwa odziŵa za mankhwala pankhondo yovuta yolimbana ndi tizilombo takupha ta matenda. Komabe, amadziŵa kuti mankhwala achikhalire a matenda ndi imfa ali ndi Mulungu, amene ‘achiritsa nthenda zako zonse.’—Salmo 103:1-3; Chivumbulutso 21:1-5; 22:1, 2.
[Chithunzi patsamba 28]
Baibulo linalonjeza za nthaŵi imene munthu aliyense sadzati, “Ine ndidwala”