Nthenda ya Mtima Moyo Uli Pangozi
CHAKA chilichonse amuna ndi akazi miyandamiyanda padziko lonse amadwala mtima. Ambiri amapulumuka ali ndi zotulukapo zake zingapo. Ena samapulumuka. Komabe, ena mtima wawo umawonongeka kwambiri kwakuti “kumakhala kokayikitsa ngati adzachitanso ntchito zothandiza,” dokotala wa mtima Peter Cohn akutero, akumawonjezera kuti: “Chifukwa chake, tiyenera kuletsa nthenda ya mtima isanakule pamene kuli kotheka.”
Mtima ndi mnofu umene umapopa mwazi m’thupi lathu lonse. Podwala mtima (myocardial infarction), mbali ina ya minofu ya mtima imafa itamanidwa mwazi. Kuti ukhale wathanzi, mtima umafuna oxygen ndi zinthu zina zomanga thupi zimene mwazi umanyamula. Umalandira zimenezi kudzera m’mitsempha yake, imene imazenenga mtimawo kunja kwake.
Matenda angagwire mbali iliyonse ya mtima. Komabe, nthenda yofala koposa yovuta ndiyo ya mitsempha yake yotchedwa atherosclerosis (kupangika kwa mafuta m’mitsempha ya mtima). Imeneyi itayamba, plaque, kapena mafuta amapangika mkati mwa mtsempha. M’kupita kwa nthaŵi, plaque imaunjikana, kulimba ndi kupanikiza mitsempha, ndipo imaletsa mwazi wambiri kufika kumtima. Ndi coronary artery disease (CAD) (nthenda ya mtsempha wa mtima) imeneyi imene imayambitsa matenda a mtima ochuluka.
Kutsekeka m’mtsempha umodzi kapena yambiri kumasonkhezera kudwalako pamene mtima ulandira oxygen yochepa kuposa imene ukufunikira. Ngakhale m’mitsempha yosapanikizika kwenikweni, plaque younjikana ingasweke ndi kuchititsa mmbulu (thrombus) kupangika. Mitsempha yokhala ndi matenda imakondanso kutukula. Mmbulu ungapangikenso pamene pakutukula, ndi kutulutsa mankhwala amene amapanikizanso mtsempha kwambiri, kuyambitsa kudwalako.
Pamene minofu ina ya mtima imanidwa oxygen kwa nthaŵi yaitali kwambiri, minofu yapafupi nayo ingawonongeke. Mosiyana ndi minofu ina, minofu ya mtima simameranso. Kudwalako kutapitiriza nthaŵi yaitali, mtima umawonongeka kwambiri ndipo imfa imakhala yothekera kwambiri. Ngati njira imene mtima umaperekera mphamvu iwonongeka, kugunda kwabwino kwa mtima kumasokonezeka ndipo mtima ungayambe kuthamanga kwambiri (fibrillate). Chifukwa cha arrhythmia (kusinthasintha m’kugunda kwake) imeneyo, mtima umalephera kupopera mwazi bwino lomwe ku ubongo. M’mphindi khumi ubongo umafa ndiyeno imfa imatsatira.
Chotero, nkofunika kwambiri kuti madokotala odziŵa ayambirire kupereka chisamaliro. Chingapulumutse mtima kuti usapitirize kuwonongeka, chingaletse kapena kuchiritsa arrhythmia, ngakhale kupulumutsa moyo wa munthu.