Kudziŵa Zizindikiro Zake ndi Kuchitapo Kanthu
PAMENE zizindikiro za nthenda ya mtima zionekera, nkofunika kwambiri kupeza thandizo la madokotala nthaŵi yomweyo, pakuti ngozi ya imfa imakhala yaikulu koposa mu ola loyamba uwo utaima. Machiritso a mwamsanga angapulumutse minofu ya mtima kuti isawonongekeretu. Ngati minofu yambiri ya mtima ipulumutsidwa, mtima udzapopa mwazi bwino kwambiri utayambanso.
Komabe, kudwala mtima kwina kumakhala kobisika, kosasonyeza zizindikiro zakunja. Zikatere, munthu sangadziŵe kuti ali ndi nthenda ya mtsempha wa mtima (CAD). Mwachisoni, kwa ena kudwala kwambiri kungakhale chizindikiro choyamba cha mavuto a mtima. Pamene cardiac arrest ichitika (mtima umaleka kugunda), mwaŵi wa kupulumuka umakhala wochepa ngati gulu lopulumutsa siliitanidwa nthaŵi yomweyo ndipo cardiopulmonary resuscitation (CPR) (kutsitsimutsa mtima ndi mapapu) siiperekedwa ndi winawake nthaŵi yomweyo.
Ponena za ambiri amene ali ndi zizindikiro za CAD, ikutero Harvard Health Letter, okwanira ngati theka safuna kupeza thandizo la mankhwala nthaŵi yomweyo. Chifukwa? “Nthaŵi zambiri chifukwa sadziŵa tanthauzo la zizindikiro zawo kapena samaziona monga nkhani yowopsa.”
John,a wodwala mtima ndipo mmodzi wa Mboni za Yehova, akuchonderera kuti: “Mutazindikira kuti simuli bwino, musazengereze kupita kwa dokotala chifukwa choganiza kuti adzakuonani ngati wokuza nkhani pachabe. Ndikadataya moyo wanga chifukwa chosachitapo kanthu msanga.”
Zimene Zinachitika
John akufotokoza kuti: “Chaka chimodzi ndi theka ndisanadwale mtima, dokotala anandichenjeza za kuchuluka kwa cholesterol yanga, chochititsa chachikulu cha CAD. Koma ndinanyalanyaza nkhaniyo, poganiza kuti ndinali wamng’ono—wosafika zaka 40—ndi wathanzi. Ndimachita chisoni kwambiri kuti sindinachitepo kanthu panthaŵiyo. Ndinali ndi zizindikiro zina zondichenjeza—kuvutika kupuma, zopweteka zimene ndinaganiza kuti zinali chifukwa cha kusapukusika kwa chakudya ndipo, miyezi ingapo kudwalako kusanayambe, kutopa kwambiri. Ndinati chinachititsa zochuluka za zimenezi chinali kugona tulo tosakwanira ndi kupsinjika kwambiri ndi ntchito. Masiku atatu nthenda yanga ya mtima isanayambe, m’chifuŵa mwanga munachita ngati kuti minofu inali kutukula. Kunali kudwala pang’ono, kwakukulu kusanachitike pambuyo pa masiku atatu.”
Kupweteka m’chifuŵa kapena kupanikizika, kotchedwa angina, kumapereka chenjezo kwa theka la anthu odwala mtima. Zizindikiro za ena zimakhala kulephera kupuma bwino kapena kutopa ndi kufooka, kusonyeza kuti mtima sukulandira oxygen yokwanira chifukwa cha kutsekeka kwa mtsempha wake. Zizindikiro zochenjeza zimenezi ziyenera kupititsa munthu kwa dokotala kuti akampime mtima. Dr. Peter Cohn akuti: “Angina itachiritsidwa, sipamakhala chitsimikizo chakuti nthenda ya mtima idzaletsedwa, koma pamakhalako mwaŵi wakuti kudwalako sikudzachitika msanga.”
Kudwalako
John akupitiriza kuti: “Tsikulo tinali kukaseŵera mpira wa softball. Pamene ndinali kudya hamburger ndi mbatata zokazinga masana, ndinanyalanyaza kusapeza bwino, nseru, ndi kumangika m’mimba chapamwamba. Koma titafika kubwalo la mpira ndi kuyamba kuseŵera, ndinadziŵa kuti sindinali bwino. Masana amenewo, ndinayamba kusamva bwino pang’ono ndi pan’ono.
“Nthaŵi zingapo, ndinagona pabenchi ya oseŵera, chagada, ndi kuyesa kunyololotsa minofu ya m’chifuŵa mwanga, koma inapitiriza kumangika. Poseŵera, ndinadzilankhuza ndekha kuti, ‘Mwina ndili ndi chimfine,’ pakuti nthaŵi zina ndinamva kuipa ndi kufooka. Pothamanga, aliyense akanaona kuti ndinali kulephera kupuma bwino. Ndinagonanso pabenchi. Nditakhala, sindinakayikire konse kuti ndinali m’mavuto aakulu. Ndinakuwa kuuza mwana wanga James kuti: ‘Ndifuna kupita kuchipatala TSOPANO LINO!’ Ndinamva ngati kuti chifuŵa changa chaloŵa mkati. Ndinamva kupweteka kwambiri kwakuti sindinathe kunyamuka. Ndinaganiza kuti, ‘Imeneyi singakhale nthenda ya mtima. Ndili ndi zaka 38 zokha!’”
Mwana wa John, amene panthaŵiyo anali ndi zaka 15, akusimba kuti: “Panapita mphindi zingapo zokha kuti atate afooke, kwakuti anafunikira kuwanyamula kuti tipite nawo ku galimoto. Mnzanga anayendetsa galimoto pamene anali kufunsa Atate mafunso kuti iwo apirire ndi mkhalidwe wawo. Potsirizira, Atate sanayankhe. ‘A John!’ mnzangayo anawaitana. Koma atate sanayankhenso. Ndiyeno Atate anatsalima ali mumpando wawo, akumapalapata ndi kusanza. Ndinafuula mobwerezabwereza kuti: ‘Atate! Ndimakukondani! Musafe chonde!’ Ataleka kutsalima, anangoti lephethe pampandowo. Ndinaganiza kuti afa.”
Kuchipatala
“Tinathamangira m’chipatala kufuna thandizo. Panali patapita mphindi ziŵiri kapena zitatu kuchokera pamene ndinaganiza kuti Atate afa, koma ndinaganiza kuti adzatsitsimuka. Ndinadabwa kupeza Mboni za Yehova zinzathu pafupifupi 20, zimene zinali kubwalo la mpira, zili m’chipinda choyembekezera. Zinandichititsa kumva bwino ndi kuti zimandikonda, zimene zinathandiza kwambiri panthaŵi yoipa ngati imeneyo. Patapita pafupifupi mphindi 15, dokotala wina anafika ndi kufotokoza kuti: ‘Takhoza kutsitsimutsa atate wako, koma adwala mtima kwambiri. Tikukayikira ngati adzakhala ndi moyo.’
“Ndiyeno anandilola kukaona Atate kwakanthaŵi. Chikondi chimene Atate anasonyeza banja lathu chinandilasa mtima. Alikumva kupweteka kwakukulu, anati: ‘Mwananga, ndimakukonda. Uzikumbukira nthaŵi zonse kuti Yehova ndiye munthu wofunika koposa m’moyo wathu. Osasiya kumtumikira, ndipo uthandize amako ndi abale ako kuti asasiye kumtumikira. Tili ndi chiyembekezo cholimba cha chiukiriro, ndipo ngati ndifa, ndikufuna kudzakuonani nonsenu nditakhalanso ndi moyo.’ Aŵirife tinali kulira chifukwa cha chikondi, mantha, ndi chiyembekezo.”
Mkazi wa John, Mary, anafika patapita ola limodzi. “Pamene ndinaloŵa m’chipinda cha imejensi, dokotala anati: ‘Amuna anu adwala mtima kwambiri.’ Ndinazunguzika. Anafotokoza kuti mtima wa John anauchita defibrillate kasanu ndi katatu. Njira ya mwamsanga imeneyi imaphatikizapo kugwiritsira ntchito mphamvu ya magetsi kuletsa mtima kugunda mosokonezeka ndi kuyambanso kugunda bwino. Limodzi ndi CPR, kuwapatsa oxygen, ndi mankhwala kudzera m’mitsempha, defibrillation ili njira yopita patsogolo yopulumutsa moyo.
“Pamene ndinaona a John, mtima wanga unapweteka. Anali otumbuluka kwambiri, ndipo thupi lawo linalunzanitsidwa ku makina ndi machubu ambiri ndi mawaya. Ndinapemphera kwa Yehova mwakachetechete kuti andipatse nyonga yopiririra ndi chiyeso chimenechi chifukwa cha ana athu aamuna atatu, ndipo ndinapempha chitsogozo chake kuti ndipange zosankha zanzeru pa zimene zinali kudza. Poyandikira mbedi wa a John, ndinaganiza kuti, ‘Kodi unganenenji kwa wokondedwa wako panthaŵi ngati imeneyi? Kodi tilidi okonzekera mkhalidwe wotere wowopsa motere?’
“‘Che Dale,’ a John anatero, ‘ukudziŵa kuti mwina sindidzapulumuka. Koma nkofunika kuti iweyo ndi anyamata mukhale okhulupirika kwa Yehova chifukwa posachedwa dongosolo ili lidzatha ndipo sikudzakhalanso matenda ndi imfa. Ndikufuna kudzadzuka m’dongosolo latsopanolo ndi kudzaona iweyo ndi anyamata athu mmenemo.’ Misozi inali kugwa m’maso mwathu.”
Dokotalayo Afotokoza
“Pambuyo pake dokotalayo anandiitana nandifotokozera kuti kupima kwawo kunasonyeza kuti a John anadwala mtima chifukwa cha kutsekekeratu kwa mtsempha wakutsogolo wotsikira kumtima. Mtsempha winanso unali wotsekeka. Dokotalayo anandiuza kuti ndisankhe machiritso amene akanayenera a John. Pa zimene ndinayenera kusankhapo panalinso zinthu ziŵiri, mankhwala ndi angioplasty. Iye anaganiza kuti yotherayi inali bwino, chotero tinasankha angioplasty. Koma madokotala sanatilonjeze kuti zonse zidzayenda bwino, pakuti ochuluka samapulumuka mtundu umenewu wa nthenda ya mtima.”
Angioplasty ndi opaleshoni imene catheter (chubu) yokhala ndi kabaluni imaloŵetsedwa mumtsempha wa mtima ndiyeno kuivutira kuti itsegule potsekekapo. Njira imeneyi imathandiza kwambiri kuyambitsanso mwazi kuyenda. Pamene mitsempha ingapo ili yotsekeka kowopsa, nthaŵi zambiri amasankha kuchita opaleshoni ya bypaass.
Mkhalidwe Wake Wokayikitsa
Itatha angioplasty, moyo wa John unapitiriza kukhala wakayakaya kwa maola ena 72. Potsirizira pake, mtima wake unayamba kutakasuka. Koma mtima wa John unali kupopa ndi theka lokha la mphamvu yake yoyamba, ndipo mbali yake yaikulu inali italimba, chotero panali kuthekera kwakukulu kwakuti adzakhala wolemala mtima.
Pokumbukira zimene zinachitika, John akulangiza kuti: “Tili ndi thayo kwa Mlengi wathu, mabanja athu, abale ndi alongo athu auzimu, ndi pa ife eni la kulabadira machenjezo ndi kusamalira thanzi lathu—makamaka ngati tili pangozi. Kwenikweni, tingakhale ochititsa chimwemwe kapena chisoni. Zili kwa ife.”
Nthenda ya John inali yowopsa ndipo inafunikira chisamaliro cha mwamsanga. Koma sikuti onse amene amamva chilungulira ayenera kuthamangira kwa dokotala. Komabe, zimene zinamchitikira zili chenjezo, ndipo awo amene aganiza kuti ali ndi zizindikiro zake ayenera kukapimidwa.
Kodi chingachitidwe nchiyani kuti ngozi ya nthenda ya mtima ichepe? Nkhani yotsatira idzalongosola zimenezo.
[Mawu a M’munsi]
a Maina m’nkhaniyi asinthidwa.
[Bokosi patsamba 18]
Zizindikiro za Nthenda ya Mtima
• Kumva kupanikizika, kufasa, kapena kuŵaŵa m’chifuŵa kwamphindi zochuluka. Nthaŵi zina mungaganize kuti ndi chilungulira chachikulu
• Kuŵaŵa kumene kungafalikire—kapena kumene kungakhale kokha—m’nsagwada, khosi, m’mapeŵa, m’mikono, zigongono, kapena kudzanja lamanzere
• Kuŵaŵa kwanthaŵi yaitali m’mimba pafupi ndi liŵezani
• Kulephera kupuma bwino, chizwezwe, kukomoka, kuchita thukuta, kuchita nyatinyati utadzikhudza
• Kulema—kungachitike milungu ingapo nthendayo isanayambe
• Nseru kapena kusanza
• Kudwala angina kaŵirikaŵiri yosachititsidwa ndi kugwiritsa ntchito
Zizindikiro zingakhale zosiyanasiyana zikumakhala zamphamvu pang’ono kapena zamphamvu kwambiri ndipo si zonse zimene zimaonekera pa nthenda ya mtima iliyonse. Koma ngati zingapo za zimenezi zitsatizana, fulumirani kufuna thandizo. Komabe, nthaŵi zina sipamakhala zizindikiro zilizonse; zimenezi zimatchedwa nthenda ya mtima yobisika.
[Bokosi patsamba 19]
Zochita Kuti Mupulumuke
Ngati inuyo kapena wina amene mudziŵa asonyeza zizindikiro za nthenda ya mtima:
• Dziŵani zizindikiro zake.
• Siyani zonse zimene mukuchita ndi kukhala pansi kapena kugona.
• Ngati zizindikirozo zipitiriza kwa mphindi zochuluka, imbirani foni panambala yakwanu ya imejensi. Uzani wotumidwayo kuti mukuganiza kuti mwadwala mtima, ndipo mpatseni chidziŵitso chofunikira kuti akupezeni.
• Ngati mutha kupereka wodwalayo kuchipatala ku chipinda cha imejensi mwamsanga mwa kuyendetsa galimoto inu mwini kupita kumeneko, chitani zimenezo. Ngati muganiza kuti mwadwala mtima, pemphani wina kuti akupititseni kumeneko pa galimoto.
Ngati mukuyembekezera madokotala aimejensi:
• Masulani zovala zothina, kuphatikizapo lamba kapena taye. Thandizani wodwalayo kuti apeze bwino, kumuikira mitsamiro ngati kuli kofunika.
• Dekhani, kaya ndinu wodwalayo kapena wothandiza. Nthumanzi ingawonjezere kwambiri ngozi ya arrhythmia imene ingatayitse moyo. Pemphero lingathandize kwambiri kukupatsani nyonga yakuti mukhale wodekha.
Ngati wodwalayo aoneka ngati waleka kupuma:
• Mokweza mawu funsani kuti, “Kodi mukundimva?” Ngati sakuyankha, ngati mtima sukugunda, ndipo ngati wodwalayo sakupuma, yambani kutsitsimutsa mtima ndi mapapu (CPR).
• Kumbukirani njira zitatu zazikulu za CPR:
1. Kwezani chibwano cha wodwalayo, kuti pakhosi patseguke.
2. Pakhosi patatseguka, uzirani mpweya kaŵiri m’kamwa mwake pang’onopang’ono, mutapana mphuno ya wodwalayo, kufikira chifuŵa chake chitatundumuka.
3. Msindikizeni pachifuŵa pakati pa maŵere nthaŵi 10 kapena 15 kuti mutulutse mwazi mumtima ndi m’chifuŵa. Masekondi 15 alionse, bwerezani kuuzira mpweya kaŵiri ndiyeno kusindikiza nthaŵi 15 kufikira mtima utayamba kugunda ndipo atayambanso kupuma kapena madokotala aimejensi atafika.
CPR ichitidwe ndi munthu wophunzitsidwa. Koma ngati palibe aliyense wophunzitsidwa, “ndi bwino kuchita CPR iliyonse kuposa kusaichita nkomwe,” akutero Dr. R. Cummins, mkulu wa madokotala a mtima aimejensi. Ngati wina sayamba njira zimenezi, kupulumuka kumakhala kokayikitsa kwambiri. CPR imasunga munthu wamoyo kufikira thandizo litafika.
[Chithunzi patsamba 17]
Chisamaliro chofulumira munthu atadwala mtima chingapulumutse moyo ndi kuletsa mtima kuwonongeka kwambiri