Kodi Ngozi Yake Ingachepetsedwe Motani?
NTHENDA ya mtsempha wa mtima (CAD) imachititsidwa ndi zinthu zambiri za majini, malo, ndi moyo wa munthu. CAD ndi nthenda ya mtima zingayambe pambuyo pa zaka, ngakhale zaka makumi ambiri, za kukhalapo kwa zinthu zangozi zochititsidwa ndi chinthu chimodzi kapena zambiri za zimenezo.
Msinkhu, Umuna Kapena Ukazi, ndi Chibadwa
Kukula msinkhu kumakhala ndi ngozi yaikulu ya kudwala mtima. Pafupifupi 55 peresenti ya nthenda za mtima zimachitika mwa anthu oposa zaka 65. Pafupifupi 80 peresenti ya amene amafa ndi nthenda ya mtima ali ndi zaka 65 kapena kuposapo.
Amuna osakwanitsa zaka 50 ali pangozi kwambiri kuposa akazi a msinkhu umodzimodziwo. Atapyola nyengo yoleka kusamba, mkazi amakhala pangozi yaikulu chifukwa cha kutsika kwambiri kwa homoni yotetezera ya estrogen. Malinga ndi kunena kwa ena, machiritso obwezera estrogen angachepetse kuthekera kwa nthenda ya mtima mwa akazi ndi 40 peresenti kapena kuposapo, ngakhale kuti angakhale pangozi yaikulu ya kudwala makansa ena.
Choloŵa chingakhale chochititsa chachikulu. Awo amene makolo awo anadwalapo asanakwanitse zaka 50 ali pangozi yaikulu ya kudwala. Ngakhale ngati makolo anadwala atakwanitsa zaka 50, amakhalabe pangozi yaikulu. Ngati banja lili ndi mbiri ya nthenda ya mtima, nzothekera kwambiri kuti ana adzakhala ndi zovuta zofananazo.
Zimene Cholesterol Imachita
Cholesterol, mtundu wa lipid, ngwofunika kwambiri pa moyo. Chiŵindi chimaipanga, ndipo mwazi umaipereka ku maselo, m’mamolekyu otchedwa lipoproteins. Mitundu yake iŵiri ndi low-density lipoproteins (LDL cholesterol) ndi high-density lipoproteins (HDL cholesterol). Cholesterol imasonkhezera kwambiri CAD pamene LDL cholesterol ichulukitsa m’mwazi.
HDL imalingaliridwa kuti imapereka chitetezo mwa kuchotsa cholesterol m’minofu ndi kuibwezera m’chiŵindi, mmene imasinthidwa ndi kuchotsedwa m’thupi. Atapima ndi kupeza kuti LDL ili yokwera ndi kuti HDL ili yotsika, ndiye kuti nthenda ya mtima ili yothekera kwambiri. Kutsitsa mlingo wa LDL kungachepetsa ngoziyo kwambiri. Kusamalira kadyedwe ndiko chinthu chofunika kwambiri pa kuchira ndipo maseŵero olimbitsa thupi angathandize. Mankhwala amitundumitundu angathandizenso, koma ena ali ndi zotulukapo zoipa.a
Chakudya chosachuluka cholesterol ndi mafuta nchabwino. Kudya chakudya chamafuta ochepa m’malo mwa chamafuta ochuluka, monga mafuta a canola kapena a azitona m’malo mwa butter, kungatsitse LDL ndi kusunga HDL. Komanso, American Journal of Public Health ikunena kuti mafuta a ndiwo zamasamba okhala ndi hydrogen wambiri kapena pang’ono opezeka m’majarini ochuluka ndi mafuta oika mu ndiwo zamasamba angachulukitse LDL ndi kuchepetsa HDL. Kuchepetsa kudya nyama zamafuta kwambiri ndi kumadya nyama ya nkhuku kapena nkhukundembo yochepa mafuta nkwabwinonso.
Kufufuza kwasonyeza kuti vitameni E, beta-carotene, ndi vitameni C zingachedwetse atherosclerosis m’nyama. Kufufuza kwina kunasonyeza kuti zimenezi zingachepetsenso nthenda ya mtima mwa anthu. Kudya ndiwo zamasamba masiku onse ndi zipatso zokhala ndi beta-carotene yambiri ndi ma carotenoid ena ndi vitameni C, monga matimati, ndiwo zamasamba zobiriŵira kwambiri, tsabola, makaroti, mbatata, ndi mavwendi zingatetezere wina ku CAD.
Ndiponso amati vitameni B6 ndi magnesium nzothandiza kwambiri. Dzinthu dzathunthu monga balere ndi ma oat ndi nyemba zomwe, mphodza, ndi mbewu zina ndi mtedza zingathandize. Ndiponso, kumalingaliridwa kuti kudya nsomba monga chambo, mackerel, herring, kapena tuna mwina kaŵiri pamlungu kungachepetse ngozi ya CAD, pakuti zimenezi zili ndi maasidi ochuluka amafuta a mtundu wa omega-3 amene alibe misanganizo yochuluka ya mafuta.
Moyo Wongokhala Popanda Chochita
Anthu amene amangokhala popanda chochita ali pangozi yaikulu ya kudwala mtima. Nthaŵi yaikulu patsiku samachita kanthu kolimba ndipo sachita maseŵero olimbitsa thupi nthaŵi zonse. Anthu oterewa amadwala mtima kaŵirikaŵiri atachita ntchito zolimba monga kulimirira kwambiri maluŵa, kuthamanga, kunyamula zolemera, kapena kufoshola chipale chofeŵa. Koma awo amene amachita maseŵero olimbitsa thupi nthaŵi zonse samadwaladwala.
Kuyenda mwamphamvu mphindi 20 kapena 30 katatu kapena kanayi pamlungu kungachepetse ngozi ya kudwala. Maseŵero olimbitsa thupi anthaŵi zonse amalimbitsa mphamvu ya mtima ya kupopa, kuthandizira kuwonda, ndipo angachepetse mlingo wa cholesterol ndi kutsitsa BP.
Hypertension, Kunenepetsa, ndi Matenda a Shuga
BP (hypertension) ingawononge mitsempha ndi kuloŵetsa LDL cholesterol m’muyalo wa mkati mwa mtsempha ndi kusonkhezera kuti plaque ipangike. Pamene nsenga za plaque ziwonjezeka, mwazi umakanika kuyenda chotero BP imakwera.
BP iyenera kupimidwa nthaŵi zonse, pakuti mwina sipangakhale zizindikiro zakunja za vutolo. Kutsika ndi nambala imodzi kulikonse kwa diastolic pressure (nambala yapansi) kungachepetse ngozi ya kudwala mtima ndi 2 kapena 3 peresenti. Mankhwala otsitsa BP angathandizenso. Kusamala kadyedwe, ndipo nthaŵi zina kuchepetsako mchere, limodzi ndi maseŵero olimbitsa thupi anthaŵi zonse ochepetsako kunenepa zingathandize kuchepetsa BP.
Kunenepetsa kumasonkhezera BP ndi kusokoneza lipid. Kupeŵa kunenepa kwambiri kapena kukuchiritsa ndiko njira yaikulu yoletsera nthenda ya shuga. Nthenda ya shuga imafulumiza CAD ndi kuwonjezera ngozi ya nthenda ya mtima.
Kusuta
Kusuta fodya kumathandizira kwambiri kuti CAD iyambe. Ku United States, kusuta kumachititsa pafupifupi 20 peresenti ya imfa za nthenda ya mtima ndi pafupifupi 50 peresenti ya nthenda za mtima mwa akazi osakwanitsa zaka 55. Kusuta fodya kumakweza BP ndi kuloŵetsa m’mwazi mankhwala akupha onga chikonga ndi carbon monoxide. Mankhwala ameneŵa amawononganso mitsempha.
Osuta amaikanso pangozi awo amene amapuma utsi wawo. Kufufuza kukusonyeza kuti osasuta amene amakhala ndi osuta ali pangozi yaikulu ya kudwala mtima. Chifukwa chake, mwa kuleka kusuta, munthu angachepetse ngozi yake ndipo mwina angapulumutse moyo wa okondedwa ake osasuta.
Kupsinjika
Atapsinjika mtima kapena maganizo kwambiri, awo amene ali ndi CAD amakhala pangozi yaikulu kwambiri ya kudwala mtima ndi kufa kuposa anthu amene ali ndi mitsempha yabwino. Malinga ndi kufufuza kwina, kupsinjika kungachititse mitsempha yodzala ndi plaque kupanikizika, ndipo zimenezi zimachepetsa kayendedwe ka mwazi ndi 27 peresenti. Kupanikizika kwakukulu kunaoneka ngakhale m’mitsempha imene inali bwino pang’ono. Kufufuzanso kwina kunasonyeza kuti kupsinjika kwambiri kungapereke mpata wakuti plaque yokhala m’mitsempha iphulike ndi kuyambitsa nthenda ya mtima.
Consumer Reports on Health ikuti: “Anthu ena amachita ngati amangokhala ndi moyo ali ndi maganizo oipa. Amakhala onyumwa, okwiya, ndi amtima wapachala. Pamene kuli kwakuti anthu ochuluka amaiŵala zowakhumudwitsa zazing’ono, anthu audani amakhumudwa koposa.” Mkwiyo ndi udani waukulu umakweza BP, kuwonjezera kugunda kwa mtima, ndi kusonkhezera chiŵindi kuloŵetsa cholesterol m’mwazi. Zimenezi zimawononga mitsempha ya mtima ndi kuyambitsa CAD. Mkwiyo amati umawonjezera ngozi ya nthenda ya mtima kuŵirikiza kaŵiri, ndipo ngoziyo imakhalapobe kwa maola osachepera aŵiri. Kodi chingathandize nchiyani?
Malinga ndi kunena kwa The New York Times, Dr. Murray Mittleman anati anthu amene amayesa kukhala odekha atakhumudwa angakhoze kuchepetsa ngozi yawo ya kudwala mtima. Zimenezi zikumveka ngati mawu olembedwa m’Baibulo zaka mazana ambiri zapitazo: “Mtima wabwino [“wodekha,” NW] ndi moyo wa thupi.”—Miyambo 14:30.
Mtumwi Paulo anadziŵa mmene kupsinjika kumakhalira. Analankhula za nkhaŵa zimene zinampanikiza tsiku ndi tsiku. (2 Akorinto 11:24-28, NW) Koma analandira thandizo kwa Mulungu nalemba kuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 4:6, 7.
Ngakhale kuti pali zinthu zina zochititsa zovuta za mtima, zimene zafotokozedwa munomo zingathandize munthu kuzindikira ngozi kuti achitepo kanthu moyenerera. Komabe, ena sadziŵa mmene zinthu zimakhalira kwa awo amene ayenera kupirira ndi zotulukapo za nthenda ya mtima. Kodi angachire kufikira pati?
[Mawu a M’munsi]
a Galamukani! samalimbikitsa machiritso a mankhwala, maseŵero olimbitsa thupi, kapena kadyedwe koma amapereka chidziŵitso chofufuzidwa bwino kwambiri. Munthu aliyense ayenera kusankha zimene iye mwini adzachita.
[Chithunzi patsamba 20]
Kusuta, kukwiya msanga, kudya zakudya zamafuta ochuluka, ndi kumangokhala popanda chochita kumawonjezera kuthekera kwa nthenda ya mtima