Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 12/8 tsamba 23-25
  • Nyengo ya Kuchira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nyengo ya Kuchira
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchira
  • Pasakhale Mitima Yosungulumwa
  • Mabanja Afunikira Chichirikizo
  • Kudziŵa Zizindikiro Zake ndi Kuchitapo Kanthu
    Galamukani!—1996
  • Kupambana Nkhondo Yolimbana ndi Kuchita Tondovi
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Mungapeze Chimwemwe m’Dziko Lochititsa Tondovi!
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kuyamikira Chichilikizo CHosalekeza cha Yehova
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 12/8 tsamba 23-25

Nyengo ya Kuchira

PAMBUYO pa kudwala mtima, nkwachibadwa kwa munthu kuchita mantha ndi kuda nkhaŵa. Kodi ndidzadwalanso? Kodi ndidzalemala kapena kulephera kuchita zambiri chifukwa cha kuŵaŵa ndi kutaya nyonga ndi mphamvu?

John, wotchulidwa m’nkhani yathu yachiŵiri, anaganiza kuti m’kupita kwa nthaŵi, kusamva bwino kwake tsiku ndi tsiku ndi kupweteka m’chifuŵa zidzatha. Koma patapita miyezi ingapo, iye anati: “Kufikira lero sizinathe. Zimenezo, limodzi ndi kutopa msanga ndi kuthamanga kwa mtima wanga, zimandichititsa kudzifunsa ndekha nthaŵi zonse kuti, ‘Kodi ndikufuna kudwalanso mtima?’”

Jane, wa ku United States, amene anali mkazi wamasiye wachichepere pamene anadwala mtima, anavomereza kuti: “Ndinaganiza kuti sindidzakhalanso ndi moyo kapena kuti ndidzadwalanso mtima ndi kufa. Ndinatekeseka, pakuti ndinali ndi ana atatu owasamalira.”

Hiroshi, wa ku Japan, anasimba kuti: “Zinandimyula mtima atandiuza kuti mtima wanga sudzagwiranso ntchito monga momwe unkachitira; liŵiro lake la kupopa linali litatsika ndi 50 peresenti. Ndinali wotsimikiza zedi kuti ndinafunikira kuchepetsa zochita zanga monga mtumiki wa Mboni za Yehova, pakuti ndinangochita theka la zimene ndinkachita.”

Pamene wina ali ndi nyonga yochepa, tondovi ndi malingaliro akuti iyeyo ali wopanda pake zingayambe. Marie, Mwausitileliya wazaka 83 amene anadzipereka nthaŵi zonse pantchito yolalikira ya Mboni za Yehova, anadandaula kuti: “Kulephera kwanga kuchita changu monga kale kunandikhumudwitsa. M’malo mothandiza ena, ine ndine amene ndinafuna thandizo tsopano.” Ku South Africa, Harold anati: “Sindinathe kugwira ntchito kwa miyezi itatu. Zimene ndinakhoza kuchita panthaŵiyo ndi kungoyendayenda m’maluŵa. Zimenezo zinali zogwiritsa mwala!”

Pamene Thomas wa ku Australia anadwalanso mtima, anafunikira opaleshoni ya bypass. Iye anati: “Zimandivuta kupirira kupweteka, ndipo kulingalira za kuchitidwa opaleshoni yaikulu kunandivuta kwambiri.” Jorge, wa ku Brazil, anati pambuyo pa opaleshoni ya mtima: “Chifukwa cha kusauka kwanga, ndinada nkhaŵa kuti ndidzamsiya yekha mkazi wanga popanda chomthandiza. Ndinaganiza kuti sindidzakhala ndi moyo nthaŵi yaitali.”

Kuchira

Kodi nchiyani chathandiza ambiri kuchira ndi kukhalanso ndi maganizo okhazikika? Jane anati: “Pamene ndinatekeseka, ndinkapita kwa Yehova nthaŵi zonse m’pemphero ndi kumsenza nkhaŵa zanga ndi kumsiyira.” (Salmo 55:22) Pemphero limathandiza munthu kupezanso nyonga ndi mtendere wa maganizo zofunika kwambiri pamene ali ndi nkhaŵa.—Afilipi 4:6, 7.

John ndi Hiroshi anatenga mbali m’machitachita ochiritsa. Kudya bwino ndi maseŵero olimbitsa thupi zinalimbitsa mitima yawo, kotero kuti onse aŵiri anayambanso ntchito. Ndipo iwo anati anakhalanso anyonga m’maganizo ndi mumtima chifukwa cha mphamvu yochirikiza ya mzimu wa Mulungu.

Mwa chichirikizo cha abale ake achikristu, Thomas analimbika mtima napirira ndi opaleshoni. Iye anati: “Ndisanapite kuopaleshoni, woyang’anira wina anadzandiona ndipo anapemphera nane. Mochonderera kwambiri, anapempha Yehova kundilimbitsa. Usikuwo ndinasinkhasinkha pemphero lake ndipo ndinaganiza kuti ndine wodala pokhala ndi akulu onga iyeyo amene chifundo chawo panyengo zovuta chilinso mbali ya kuchiritsa.”

Anna, wa ku Italy, anapirira tondovi motere: “Nditapsinjika, ndimaganiza za madalitso onse amene ndalandira kale monga mmodzi wa atumiki a Mulungu ndi za madalitso amene adzakhalako mu Ufumu wa Mulungu. Zimenezi zimandithandiza kupezanso mtendere.”

Marie akuthokoza Yehova pomthandiza. Banja lake lamchirikiza, ndipo akuti: “Abale ndi alongo anga auzimu, yense atasenza katundu wakewake, anapatula nthaŵi ya kudzandiona, kundiimbira telefoni, kapena kunditumizira makhadi. Kodi ndikanakhala bwanji wachisoni posonyezedwa chikondi chonsecho?”

Pasakhale Mitima Yosungulumwa

Pali mawu akuti mtima womachira usakhale mtima wosungulumwa. Chichirikizo cha banja ndi mabwenzi chimathandiza kwambiri pakuchira kwa awo amene mitima yawo iyenera kuchira mwakuthupi ndi mophiphiritsira.

Michael, wa ku South Africa, anati: “Nzovuta kuti ufotokozere ena mmene kusukidwa kumamvekera. Koma pamene ndiloŵa m’Nyumba ya Ufumu, nkhaŵa imene abale amasonyeza njokhudza mtima kwambiri ndipo imandilimbikitsa.” Henry, wa ku Australia, nayenso analimbitsidwa ndi chikondi chachikulu ndi chifundo chimene mpingo wake unasonyeza. Anati: “Ndinafunikiradi mawu achifundo amenewo ndi olimbikitsa.”

Jorge anayamikira nkhaŵa yaikulu imene ena anasonyeza mwa kuthandiza banja lake ndi ndalama kufikira atayambanso kugwira ntchito. Momwemonso, Olga, wa ku Sweden, anayamikira thandizo limene iye ndi banja lake anapatsidwa ndi abale ambiri auzimu ndi alongo. Ena anakamgulira zinthu, pamene ena anayeretsa nyumba yake.

Nthaŵi zambiri, odwala mtima ayenera kuchepetsa zochita zawo zimene amakonda kwambiri. Sven, wa ku Sweden, anati: “Nthaŵi zina ndimapeŵa kutengamo mbali mu utumiki pamene kuli mphepo kwambiri kapena kuzizira, pakuti zimachititsa mitsempha kutukula. Ndimayamikira Mboni zinzanga zambiri pondimvetsa pankhani imeneyi.” Ndipo pamene ali wobindikira mumbedi, Sven amakhoza kumvetsera misonkhano chifukwa abale mwachikondi amaijambula patepi. “Amandidziŵitsa zimene zikuchitika mumpingo, ndipo zimandipangitsa kumva ngati nanenso ndikutengamo mbali.”

Marie, wobindikira mumbedi, akuganiza kuti ali wodala popeza awo amene amaphunzira nawo Baibulo amadza kwa iye. Mwa njira imeneyi, iye atha kupitiriza kukambitsirana nawo za mtsogolo mwabwino kwambiri mmene iye akuyembekezera. Thomas akuyamikira kaamba ka nkhaŵa imene amamsonyeza: “Akulu akhala achifundo kwambiri ndipo achepetsa magawo amene amandipatsa.”

Mabanja Afunikira Chichirikizo

Mkhalidwe ungakhale wovuta kwambiri kwa apabanja monga momwenso ulili kwa wodwalayo. Amapsinjika kwambiri ndi kuchita mantha. Ponena za nkhaŵa ya mkazi wake, Alfred, wa ku South Africa, anati: “Pamene ndinafika kunyumba kuchokera ku chipatala, mkazi wanga anandidzutsa nthaŵi zambiri usiku kuti aone ngati ndinali bwino, ndipo anali kuumirira kuti ndikaonane ndi dokotala patapita miyezi itatu iliyonse kuti akandipime.”

Miyambo 12:25 imati “nkhaŵa iŵeramitsa mtima.” Carlo, wa ku Italy, akunena kuti kuchokera pamene anadwala mtima, mkazi wake wachikondi ndi womchirikiza “wakhala akuchita tondovi.” Lawrence, wa ku Australia, anati: “Zina zimene uyenera kusamala nazo nzakuti mnzako akusamaliridwa. Mnzako angapsinjike kwambiri.” Chotero, tiyenera kukumbukira zimene onse m’banja akufuna, kuphatikizapo ana. Mkhalidwewo ungawachititse kupsinjika mtima ndi kudwala.

James, wotchulidwa m’nkhani yathu yachiŵiri, anasiya kulankhulana ndi aliyense atate wake atadwala mtima. Anati: “Ndinaganiza kuti sindikanasangulukanso chifukwa choganiza kuti ndikatero, padzachitika chinthu choipa.” Pamene anafotokozera atate wake za mantha ake nalimbikira kuti ayambitsenso kulankhulana kwabwino ndi ena, zinamthandiza kuchepetsa nkhaŵa yake. Mkati mwa nthaŵiyo James anachita zina zimene zinasintha moyo wake kwambiri. Anati: “Ndinayamba kuchita kwambiri phunziro laumwini la Baibulo ndi kukonzekera misonkhano yathu yachikristu.” Patapita miyezi itatu iye anapatulira moyo wake kwa Yehova nasonyeza zimenezo mwa ubatizo wa m’madzi. “Kuyambira pamenepo,” iye akutero, “ndakhala ndi unansi wapafupi kwambiri ndi Yehova. Ndimthokoza kwambiri pa zimene wachita.”

Nyengo ya kudwala mtima itapita, munthu amakhala ndi nthaŵi ya kupendanso moyo wake. Mwachitsanzo, maganizo a John anasintha. Iye anati: “Umaona kupanda pake kwa ntchito zadziko ndi kuzindikira kuti chikondi cha banja ndi mabwenzi nchofunika kwambiri ndi kuti Yehova amatiŵerengera kwambiri. Unansi wanga ndi Yehova, banja langa, ndi abale anga auzimu ndi alongo ngwofunika koposa tsopano.” Pokumbukira kuzunzika kwake, anawonjezera kuti: “Ndiganiza kuti sindikanapirira popanda chiyembekezo chathu cha nthaŵi pamene zinthu zimenezi zidzawongoleredwa. Ndikapsinjika, ndimalingalira za mtsogolo, ndipo zimene zikuchitika tsopano lino zimaoneka ngati zosanunkha kanthu.”

Pamene akumana ndi zovuta za panyengo ya kuchira, opulumuka nthenda ya mtima ameneŵa amazika chiyembekezo chawo molimba pa Ufumu umene Yesu Kristu anatiphunzitsa kuti tiupempherere. (Mateyu 6:9, 10) Ufumu wa Mulungu udzapatsa anthu moyo wosatha waungwiro padziko lapansi la paradaiso. Ndiyeno nthenda ya mtima ndi kulemala kwa mtundu uliwonse kudzathetsedwa kosatha. Dziko latsopano limenelo lili pafupi kwambiri. Inde, moyo wabwino koposa udakali mtsogolo!—Yobu 33:25; Yesaya 35:5, 6; Chivumbulutso 21:3-5.

[Chithunzi patsamba 25]

Chichirikizo cha banja ndi mabwenzi chimathandiza pakuchira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena