“Ukwati wa Mwambo” ku Ghana
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU GHANA
UKWATI—anthu zikwi mazana ambiri amaloŵa mu unansi umenewu chaka chilichonse padziko lonse. Iwo amachita motero malinga ndi mwambo wa ukwati umene uli wofala kumene amakhala.
Ku Ghana mtundu wofala kwambiri wa ukwati ndiwo umene umatchedwa kuti ukwati wa mwambo. Umenewu umaphatikizapo kulipira malowolo kochitidwa ndi akuchimuna kwa akuchikazi. Ukwati wa mwambo umachitidwa ndi anthu m’mbali yaikulu ya Afirika ndi kumalo onga Hong Kong, Papua New Guinea, ndi ku Solomon Islands ndiponso pakati pa Aindiya achigoajiro kumpoto cha kummaŵa kwa Colombia ndi kumpoto cha kumadzulo kwa Venezuela, kungotchulapo oŵerengeka.
Malipiro a malowolo anali mwambo mu nthaŵi za Baibulo. (Genesis 34:11, 12; 1 Samueli 18:25) Lingaliro lake la nthaŵi zakale ndi lamakono nlakuti malowolo ndiwo chobwezera kwa makolo a msungwana chifukwa chotayikidwa mautumiki ake ndi nthaŵi, nyonga, ndi chuma zimene anawononga pa maphunziro ake ndi kumlera asanakwatiwe.
Thayo la Makolo
Kale, ku Ghana kunalibe kuyendera pamodzi ndi kupalana chibwenzi pakati pa achinyamata. Makolo ndiwo anali kulinganiza maukwati a ana awo amene akula atapendetsetsa mnyamata ndi msungwana wokhoza kuloŵa mu ukwati m’mudzi mwawo. Makolo ena ku Ghana adakachitabe zimenezi.
Makolo a mnyamata amalingalira zinthu zonga umunthu wa msungwana; mbiri yake ndi ya banja lakwawo; nthenda yobadwa nayo imene amadwala m’banja lakwawo; ndipo ponena za Mboni za Yehova, mkhalidwe wake wauzimu. Ngati akhutiritsidwa, makolowo amafikira makolo a msungwanayo ndi kufunsira ukwati.
Makolo a msungwanayo tsopano amafufuza za khalidwe la mnyamatayo ndi la banja lakwawo. Kuwonjezera pa zinthu zimene zatchulidwa pamwambapa, amalingaliranso za kukhoza kwa mnyamatayo kusamalira mkazi—kodi iye amagwira ntchito kapena ndi lova? Ngati makolo a msungwanayo akhutiritsidwa, nawonso amadziŵitsa makolo a mnyamatayo, ndiyeno makolowo pamodzi amalinganiza mmene ukwatiwo ungayendere, mnyamata ndi msungwanayo atauvomereza.
Kodi nchifukwa ninji makolo ena amasenza thayo la kupeza okwatirana nawo a ana awo okula msinkhu? Mkazi wina ku India amene makolo ake anamlinganizira ukwati anati: “Kodi munthu wachichepere angakhoze bwanji kupanga chosankha cholemera chimenecho? Kuli bwino kwambiri kusiya nkhaniyo kwa awo amene ali okhoza kudziŵa chosankha chanzeru koposa chifukwa cha msinkhu ndi chidziŵitso.” Ndemanga yakeyo ikusonyezanso lingaliro la Aafirika ambiri.
Komabe, nthaŵi zikusintha ku Ghana. Kuyendera pamodzi ndi kupalana chibwenzi zikuwanda kwambiri. Nthaŵi yoyenera itafika pa chibwenzicho, aŵiriwo amadziŵitsa makolo za malingaliro awo. Makolo awo ataonana ndiponso makolo atakhutira kuti iwowo akuyenerana, mabanjawo amapitiriza kuchita mwambo umene anthu ambiri m’zinenero zosiyanasiyana za ku Ghana amaudziŵa kuti kugogoda pa khomo, khomo la ukwati.
Mwambo wa Kugogoda pa Khomo
Makolo a aŵiriwo amadziŵitsa a m’mabanjamo za tsiku ndi chifuno cha kukumana. Liwulo “a m’mabanja” limanena za banja lapachibale lachiafirika limene limaphatikizapo amalume, azakhali, asuwani ndi abale, ndi agogo a aŵiriwo. Pa tsiku loikika, oimira mabanja aŵiriwo amasonkhana kaamba ka mwambowo. Mkwati angakhalepo ngati akufuna. Zotsatirazi ndizo chitsanzo chachidule kwambiri cha zimene zinachitika pa mwambo wina wa kugogoda pa khomo.
Woimira msungwana (WM): [Alankhula kwa oimira akuchimuna] Tikudziŵa chomwe mwafikira, koma malinga ndi mwambo tifunsebe, Mwadzatani?
Woimira mnyamata (WMN): Mwana wathu Kwasi anali kudutsa panyumba panu pano ndipo anaona duŵa lokongola ndipo akufuna chilolezo chanu choti alithyole.
WM: [Ngati sakudziŵa kanthu] Panyumba pano palibe duŵa. Tatifotokozerani bwino.
WMN: Mwana wathuyu walondola ndithu. Tikunenetsa kuti m’nyumba muno muli duŵa lokongola. Dzina la duŵalo ndilo Afi.
WM: Ndiye kuti munena duŵa la munthu. Chabwino, Afi amakhala pano.
WMN: Tikufuna kugogoda pa khomo ndi kupempha kuti mupereke Afi kwa mwana wathu Kwasi kuti akwatirane.
Tsopano akuchimuna apereka zinthu, monga ngati zakumwa ndi ndalama. Malinga ndi mtundu, zinthu zoperekedwazo ndi kuchuluka kwake zimasiyanasiyana. Mwambo umenewu umafananako ndi chikole cha kumaiko a Kumadzulo, ndipo m’zochitika zina pamafunika mphete ya chikole.
Tsopano woimira mkazi amafunsa mnsungwana pamaso pa oonerera ngati angalandire zinthu zimene zabweretsedwazo. Mwa kuvomera kwake, onse amene alipo amakhala mboni za kufuna kwake kukwatiwa. Mabanja aŵiriwo amamvana za deti lowakomera la phwando la ukwati. Amamaliza mwambowo ndi zakumwa zoziziritsa kukhosi.
Mwambo wa Ukwati
Chiŵerengero cha anthu amene amasonkhana kuti apezekepo pa kulipiridwa kwa malowolo panyumba ya msungwanayo kapena panyumba ya woimira wosankhidwa, chochitika chimene chimakhala ukwati, kaŵirikaŵiri chimakhala chachikulu kuposa cha anthu amene anali pa mwambo wa kugogoda pa khomo. Zimenezi zimachitika chifukwa chakuti mabwenzi ambiri tsopano amakhala alipo.
Mkhalidwe wake umakhala wachikondwerero. Anyamata ndi asungwana osakwatiwa amafunitsitsa kuona zimene abweretsera mkwatibwi. Koma mkhalidwe wachimwemwewo umasintha pamene akuchikazi adandaula kuti zinthu zamalowolozo nzosakwanira. Anthu ena omvetsera amada nkhaŵa pamene akuchikazi aoneka kuti akuumitsa zinthu. Mneneri wakuchimuna amakambirana nawo mwaluso kuti akuchikaziwo awakomere mtima. Anthu amamasuka pamene akuchikazi afeŵetsa zinthu. Mkhalidwewo ukusinthanso. Tsopano pakhalanso chikondwerero, ndipo zakumwaimwa ziperekedwa.
Kuti ayambe mwambo wa ukwati, mneneri wakuchikazi amatontholetsa osonkhanawo ndi kulonjera onse. Amafunsa oimira akuchimuna chimene adzera. Mneneri wakuchimuna amafotokoza chifukwa chimene adzera, akumakumbutsa osonkhanawo kuti anagogoda kale pakhomo ndi kuti analoledwa kuloŵa.
Pamenepo mneneri wa banja lililonse amadziŵikitsa achibale apafupi a m’banjamo kwa osonkhana, kuphatikizapo munthu amene akupereka mnsungwanayo mu ukwati ndiponso munthu amene akuchirikiza mnyamata kuloŵa mu ukwati. Mwambowo umapitiriza.
WM: [Alankhula kwa oimira akuchimuna] Tulutsani tsono zinthu zaukwati zimene tinakupemphani.
Mneneri wakuchikazi amatchula zinthu zamalowolo chimodzi ndi chimodzi kuti onse atsimikizire kuti zilipo. Ngati oimira akuchimuna alingalira kuti akuchikazi achulukitsa zimene akufuna, amakambirana nkhaniyo mwamtseri tsiku la ukwati lisanafike. Komabe, akuchimuna amafika pa mwambowo ali okonzekera kudzakambirana za kuchepetsa zinthu zina zowonjezereka ngati akuchikazi ena akhala ovuta. Kulikonse kumene munthu amakhala, malowolo ofunika—kaya akhale okwera kapena otsika—ayenera kulipiridwa onse.
Mabanja ena amafuna zinthu zonga zakumwa, zovala, ndendele, ndolo, ndi zinthu zina za akazi. Kumpoto kwa Ghana, malowolo angaphatikizepo mchere, mtedza wa kola, nkhanga, nkhosa, ndipo ngakhale ng’ombe. Nthaŵi zonse malowolowo amaphatikizapo ndalama.
Pamene kukambiranako kukupitiriza, mkwatibwi samakhalapo koma amakhala ali pafupi, akumaonerera. Mkwati angakhalepo ngati akufuna. Motero, munthu wokhala kutali angapatse mphamvu makolo ake ya kulinganiza ukwati wake. Komabe, pa chochitika chimene chafotokozedwa pano, mkwati amakhalapo. Tsopano akuchimuna amanena chofuna chawo.
WMN: Takwaniritsa zonse zimene munafuna kwa ife, komano sitinaone mpongozi wathu.
Mwambo wa ukwatiwo sumangokhala wakukambirana; umakhalanso nthaŵi yachisangalalo. Tsopano akuchikazi amayankha pempho la akuchimuna la kuona mkwatibwi.
WM: Tikanakonda kuti mkwatibwiyo akhale pano. Mwatsoka, iye wapita kunja kwa dziko ndipo tilibe mapasipoti kapena maviza oyendera ulendo kukamtenga.
Aliyense amadziŵa tanthauzo la zimenezo. Nthaŵi yomweyo, akuchimuna amapereka ndalama—ndalama zilizonse zimene mkwati angathe kupereka—ndipo pompo! mapasipoti ndi maviza oyerekezera amakonzeka. Ndipo mkwatibwi amakhala atabwerako ku ulendo wake!
Kuwonjezera pa chikondwererocho, mitundu ina imalinganiza kuti mabwenzi a mkwatibwi aloŵe m’malo mwake. Woloŵa m’malo mwake aliyense amakanidwa ndi khamu lonse kufikira, pakati pa mfuu yaikulu, mkwatibwi weniweniyo aperekedwa. Ndiyeno amapemphedwa ndi mneneri wake kuti aone zinthu zosiyanasiyana za malowolo ake. Iyeyo amafunsidwa ngati ayenera kulandira zimene mkwati wabweretsa. Pamakhala bata pamene aliyense akuyembekezera yankho. Asungwana ena ngamantha ndipo ena ngolimba mtima, koma nthaŵi zonse yankho lake limakhala lakuti inde, motsatiridwa ndi mfuu yaikulu ndi kuomba manja.
Ngati mkwati alipo, akuchikazi amafuna kumdziŵa. Chikondwererocho chimapitiriza mosadukiza ngati analinganiza kuti mmodzi wa mabwenzi a mnyamatayo amloŵe m’malo. Bwenzi lakelo monyada limaimirira, komano amaliwowoza kuti likhale pansi.
Makolo a mkwatibwi amapempha kuona mkamwini wawo. Tsopano mkwati weniweni amaimirira, akumwetulira. Akuchikazi amalola mnsungwanayo kugwirizana ndi mwamuna wake, amene amamuveka mphete kuchala ngati mpheteyo ifunika kukhala mbali ya malowolo. Mphete ili chinthu chatsopano chochokera ku maiko a Kumadzulo. Nayenso mnsungwanayo amaveka mnyamata mphete kuchala. Mafuno abwino ndi chisangalalo zimakula. Kaamba ka nthaŵi ndi chuma, ena aphatikiza mwambo wa kugogoda pa khomo ndi ukwati pa tsiku limodzimodzilo.
Anthu achidziŵitso a m’mabanja aŵiri onsewo ndi ena tsopano amapatsa uphungu kwa okwatirana chatsopanowo wonena za mmene angapangitsire ukwati wawo kuyenda bwino kufikira imfa itawalekanitsa. Pomaliza tsikulo, amapereka zakumwa.
Mwambo wa ukwatiwo watha! Ku Ghana, kuyambira tsikulo, aŵiriwo amaonedwa ndi anthu kukhala okwatirana mwalamulo. Ngati pali akuchikazi ena alionse amene sanathe kufika pa mwambowo kaamba ka chifukwa china, amawatumizira zina za zakumwa zimene zaperekedwazo kuti akatsimikizire za kumangidwa kwa ukwatiwo. Ngati mkwati ndi mkwatibwi ali Mboni za Yehova, nthaŵi zina Mbonizo zimalinganiza nkhani ya Baibulo yoti ikambidwe, zoziziritsa kukhosi zikumatsatira pambuyo pake.
Ku Ghana anyamata ndi asungwana ena amatsatira mwambo wa ukwati wa maiko a Kumadzulo, umene kunoko umatchedwa kuti ukwati wa kuboma, kapena ukwati walamulo. Umenewu ungamangitsidwe ndi chivomerezo cha makolo kapena ayi malinga ngati aŵiriwo ali ausinkhu wololedwa ndi lamulo. Mu ukwati wamwambo makolo ayenera kuvomereza.
Mu ukwati wa kuboma aŵiriwo amachita ziŵindo. Koma mu ukwati wamwambo mulibe ziŵindo. Boma limafuna kuti maukwati onse amwambo alembetsedwe, ndipo Mboni za Yehova zimachita mogwirizana ndi zimenezo. (Aroma 13:1) Ndiyeno amapatsidwa mtchato.
Kuyambira m’nthaŵi zakale kufikira pamene Gold Coast, tsopano Ghana, anakhala dziko loyang’aniridwa ndi Abritishi, ukwati wamwambo ndiwo wokha unali mtundu wa ukwati m’dzikomo. Ndiyeno Abritishi anayambitsa ukwati wa maiko a Kumadzulo kaamba ka nzika zawo zimene zinali kukhala kuno. Eni dzikoli nawonso anali kuloledwa kumanga mtundu umenewu wa ukwati, ndipo tsopano kwa zaka zambiri, maukwati a maiko a Kumadzulo ndi amwambo akhala akuchitidwa pamodzi. Ku Ghana aŵiri onsewo ali ovomerezedwa mwalamulo, nchifukwa chake Mboni za Yehova zimawavomereza. Munthu ndiye amene amadzisankhira mtundu umene akufuna.
M’maiko ena a mu Afirika, maukwati amwambo amafunikira kulembetsedwa aŵiriwo asanalingaliridwe kukhala okwatirana mwalamulo. Komabe, ku Ghana, ukwati wamwambo monga momwe taonera uli wovomerezedwa mwalamulo popanda kulembetsa, aŵiriwo amaonedwa kukhala okwatirana mwalamulo pamene amangitsa ukwati wamwambo. Pambuyo pake, ukwati wamwambo umalembetsedwa kaamba ka kaundula wa boma chabe.
Ukwati ulidi mphatso yachikondi ya Mulungu ku mtundu wa anthu, mphatso yapadera imene ngakhale angelo sanapatsidwe. (Luka 20:34-36) Ndiyo unansi wamtengo wapatali woyenerera kusungidwa kaamba ka ulemerero wa Wouyambitsa wake, Yehova Mulungu.
[Chithunzi patsamba 14]
Avekana mphete