Lingaliro la Baibulo
Kodi Akristu Ayenera Kukhala Otsutsa Nkhondo?
“Matchalitchi ayenera kuyambanso kutsutsa nkhondo monga mmene anachitira m’zaka za mazana oyambirira zachikristu.”—Hubert Butler, mlembi wachiairishi.
ATACHOKERA kocheza ku Yugoslavia pambuyo pa Nkhondo Yadziko II, Hubert Butler analemba molimba mtima mawu ali pamwambawo m’nkhani yake imene analemba mu 1947 koma imene sinafalitsidwe mpaka chaka chatha chomwechi! Anadabwa kwambiri kuona kuti pankhondo, “Tchalitchi chachikristu chinasonkhezera maupandu osaneneka ndi kutinso chinasiyana kutalitali ndi chiphunzitso cha Kristu.”
Butler sanali kuopa kutsutsa poyera zolinga zoipa kapena magulu a anthu. Pamene anali kutsutsa, nthaŵi zonse analibe womchirikiza. Analankhula mopanda mantha pamene anayerekezera khalidwe la matchalitchi ndi kulimba mtima kwa Mboni za Yehova, zomwe magazini ya The Irish Times inazifotokoza kuti “ndithudi ndilo gulu lachipembedzo lopanda chifukwa ngakhale pang’ono ndipo lilibenso kanthu ndi ndale iyayi.” M’nkhani yake yakuti, “Lipoti la Yugoslavia,” Butler analemba kuti Mboni, zomwe “zinakana machenjera onse amene atsogoleri andale ndi achipembedzo amagwiritsira ntchito polungamitsa nkhondo,” boma la Yugoslavia linazizenga mlandu chifukwa chokana kumenya nkhondo.
Komabe, malinga ndi Malemba, kodi nkolondola kutcha Mboni za Yehova kuti otsutsa nkhondo? Kuti tiimveketse bwino nkhaniyi, choyamba tilongosole chimene liwu lakuti “wotsutsa nkhondo” limatanthauza. Butler anagwiritsira ntchito liwulo potamanda Mboni chifukwa cha kulimba mtima kwawo pakukana kunyamula zida zankhondo, ngakhale kuti anataikiridwa zambiri. Komabe mwachisoni, anthu ambiri amene amakonda nkhondo amamuona wotsutsa nkhondo ngati “wamantha kapena kapirikoni, yemwe amangofuna kuzemba ntchito yotetezera dziko lake” basi. Kodi lingaliro limenelo ndi lolondola?
Kutsutsa Nkhondo Kapena Chiwawa
Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary imati pacifist (wotsutsa nkhondo) ndi munthu amene “amatsutsa kwambiri zokangana ndipo makamaka nkhondo.” Imafotokoza kuti “pacifism” (kutsutsa nkhondo) ndiko “kukana nkhondo kapena chiwawa monga njira yothetsera mikangano; makamaka: kukana kunyamula zida chifukwa nkulakwa kapena kuti chipembedzo chimaletsa.” Kodi mafotokozedwe ameneŵa angayenerane bwanji ndi okhulupirira a mpingo woyamba wachikristu?
Iwo ‘anakana kunyamula zida chifukwa nkulakwa ndipo chipembedzo chinawaletsa’ ndiponso anapeŵa ‘mikangano yonse ndi nkhondo.’ Chifukwa nchiyani? Chifukwa anadziŵa kuti Yesu ananena kuti otsatira ake ‘sanali mbali yadziko lapansi’ ndi kuti “onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” (Yohane 15:19; Mateyu 26:52) M’buku lakuti The Early Church and the World, wolemba mbiri wina akutiuza kuti “Palibe Mkristu yemwe anali kukhala msilikali pambuyo pa ubatizo wake, kufikira ulamuliro wa Marcus Aurelius cha ku ma [161-180 C.E.].” M’buku lakuti The New World’s Foundation in the Old, wina akuti: “Akristu oyamba anaona kuti kumenya nkhondo kunali kulakwa, ndipo sakanaloŵa ntchito m’gulu lankhondo ngakhale ngati Ufumuwo unafuna asilikali.”
Ntchito ya Akristu inali yolalikira uthenga wabwino. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Anadziŵa kuti ntchito imene Mulungu anawapatsa siinali yowathira nkhondo adani ake iyayi, ngati kuti iwo anali olipsira a Mulungu. (Mateyu 5:9; Aroma 12:17-21) Pamene otchedwa Akristuwo ‘akusiyana kutalitali ndi chiphunzitso cha Kristu,’ monga momwe Butler akunenera, mpamene amaloŵerera m’nkhondo zamitundu. Ndiyeno akuluakulu achipembedzo amadalitsa magulu ankhondo kumbali zonse ziŵiri, ndi kuwapempherera kuti apambane. (Yerekezerani ndi Yohane 17:16; 18:36.) Mwachitsanzo, mu zaka mazana zapitazo, Aprotesitanti ndi Akatolika anamenya nkhondo zambiri zokhetsa mwazi kwambiri, zimene “zinachititsa chiwawa choopsa ku Western Europe, a kumbali zonse ziŵiri akumadzitcha kuti anali zipangizo za Mulungu zosonyezera mkwiyo wake,” analemba choncho Kenneth Clark m’buku lake lakuti Civilisation. Cyclopedia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature, ya McClintock ndi Strong, ikuti: zifukwa zawo zolungamitsira mtundu umenewu wankhondo “mwachionekere nzongofuna kukondweretsa boma, ndipo nzosemphaniratu ndi chiphunzitso chachikristu chakale ndi tanthauzo lenileni la Uthenga Wabwino.”—Yakobo 4:4.
Kodi Amatsutsiratu Nkhondo?
Komabe, kodi ‘chiphunzitso chachikristu chakale ndi tanthauzo lenileni la Uthenga Wabwino’ zinalidi zotsutsa nkhondo? Kodi Akristu oyambirira tingawatchedi kuti otsutsa nkhondo, malinga ndi kumasulira komwe kwaperekedwako? Ayi! Kulekeranji? Chifukwa iwo amavomereza kuti Mulungu ali woyenera kumenya nkhondo. (Eksodo 14:13, 14; 15:1-4; Yoswa 10:14; Yesaya 30:30-32) Ndiponso, iwo sanatsutse pamene Mulungu analamula Aisrayeli akale kuti am’menyere nkhondo pamene mtunduwo unali chipangizo chake chokha padziko lapansi.—Salmo 144:1; Machitidwe 7:45; Ahebri 11:32-34.
Mulungu sali woyenera chabe kumenya nkhondo komanso ali ndi udindo wa kuchotsa oipa padziko lapansi chifukwa cha chilungamo chake. Anthu ambiri ochita zoipa azingonyalanyazabe pamene Mulungu akuwadandaulira mobwerezabwereza kuti asinthe khalidwe lawo. (Yesaya 45:22; Mateyu 7:13, 14) Sikuti Mulungu azingolekerera kuipa nthaŵi zonse. (Yesaya 61:2; Machitidwe 17:30) Chotero, Akristu amazindikira kuti potsirizira pake Mulungu adzawachotsa mwa mphamvu yake anthu oipa padziko lapansi. (2 Petro 3:9, 10) Monga momwe Baibulo likuloserera, zimenezi zidzachitika “pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’laŵi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu.”—2 Atesalonika 1:6-9.
Buku lotsiriza la Baibulo likufotokoza kulimbana kumeneku kuti ndiko “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse,” kapena Harmagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Limati Yesu Kristu ndiye adzaitsogolera, likumati “akuchita nkhondo molungama.” (Chivumbulutso 19:11, 14, 15) Moyenerera Yesu Kristu amatchedwa “Kalonga wa mtendere.” (Yesaya 9:6) Koma sali wotsutsa nkhondo. Anamenyapo kale nkhondo kumwamba powachotsako adani onse amene anapandukira Mulungu. (Chivumbulutso 12:7-9) Posachedwapa adzamenyanso nkhondo ina “kuwononga iwo akuwononga dziko.” Komabe, atsatiri ake padziko lapansi sadzatenga mbali pachiweruzo chaumulungu chimenecho.—Chivumbulutso 11:17, 18.
Akristu oona amakonda mtendere. Amakhala chete ndithu pa nkhondo zadziko, ndale, ndi mikangano yautundu. Koma kunena zoona, iwo saali otsutsa nkhondo. Chifukwa nchiyani? Chifukwa akuivomereza nkhondo ya Mulungu imene potsirizira idzakhazikitsa chifuniro chake padziko lapansi—nkhondo imene idzathetsa nkhani ya ufumu wachilengedwe chonse ndiponso onse odana ndi mtendere kuwasesapo padziko lapansi lino kamodzi kwatha.—Yeremiya 25:31-33; Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10.
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
Christ Mocked/The Doré Bible Illustrations/Dover Publications, Inc.