Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 3/8 tsamba 10-15
  • Ndinalimbikitsidwa ndi Kukhulupirika kwa Banja Lathu kwa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndinalimbikitsidwa ndi Kukhulupirika kwa Banja Lathu kwa Mulungu
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuzunzidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chathu
  • Kuyesedwa kwa Atate
  • Amayi Agwidwa Chisoni
  • Kuyamba Utumiki Wanthaŵi Zonse
  • Kumangidwa ndi Kuponyedwa m’Ndende
  • Utumiki Pambuyo Potuluka m’Ndende
  • Mwaŵi Wautumiki Wabwino
  • Kudalira Chisamaliro cha Yehova
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Ndingam’bwezere Chiyani Yehova?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kudikirabe Yehova Moleza Mtima Kuyambira Ubwana Wanga
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kusunga Lonjezo Langa Lotumikira Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 3/8 tsamba 10-15

Ndinalimbikitsidwa ndi Kukhulupirika kwa Banja Lathu kwa Mulungu

YOSIMBIDWA NDI HORST HENSCHEL

“Ukalandira kalata iyi usangalale, chifukwa ndapirira kufikira mapeto. Pakangotha maola aŵiri ndinyongedwa.” Awa anali mawu oyamba a kalata yomaliza ya Atate kwa ine. Pa May 10, 1944, ananyongedwa chifukwa chokana kugwira ntchito m’gulu la nkhondo la Hitler. Kukhulupirika kwawo kwa Mulungu, kuphatikizapo kwa amayi ndi mlongo wanga Elfriede, kwakhudza moyo wanga kwambiri.

MU 1932, pafupifupi nthaŵi imene ndinabadwa, Atate anayamba kuŵerenga zofalitsa za Mboni za Yehova. Mwa zina, anaona chinyengo cha atsogoleri achipembedzo. Zotsatira zake, analibenso chidwi ndi tchalitchi.

Itangoyambika Nkhondo Yadziko II m’chaka cha 1939, Atate anawalemba usilikali m’gulu lankhondo la Germany. “Malinga ndi Baibulo, sindiyenera kupita,” iwo anauza Amayi. “Kupha anthu kumeneku si kwabwino.”

Amayi anayankha kuti: “Akuphani ngati simupita, ndiye nanga banja lanu lidzachita bwanji?” Motero Atate anakhala msilikali.

Kenaka Amayi, omwe kufikira panthaŵiyi anali asanaphunzire Baibulo, anayesera kukumana ndi Mboni za Yehova, chinthu changozi kuchichita panthaŵiyo. Anapeza Dora amene mwamuna wake anali kumsasa wachibalo chifukwa cha chikhulupiriro chake. Dora anawapatsa Nsanja ya Olonda, koma anawauza Amayi mwachindunji kuti: “Zindikirani kuti ndikhoza kuphedwa ngati Agestapo (apolisi achinsinsi) azindikira kuti ndinakupatsani.”

Pambuyo pake Amayi analandira zofalitsa zosiyanasiyana za Mboni za Yehova nayamba kuyamikira choonadi cha Baibulo chimene chinali mmenemo. Kenaka, Max Ruebsam, yemwe ankachokera pafupi pa Dresden, anayamba kumadzatichezera panyumba pathu ku Meissen. Anaphunzira nafe Baibulo akumadziika iye mwini pangozi. Ndipodi sipanapite nthaŵi anamangidwa.

Chifukwa cha kuphunzira Baibulo kwa Amayi, anakhala ndi chikhulupiriro mwa Yehova ndipo anapatulira moyo wawo kwa iye, ndipo anasonyeza izi mwaubatizo wa m’madzi m’May 1943. Ine ndi Atate tinabatizidwa miyezi pang’ono pambuyo pake. Mlongo wanga wazaka 20, Elfriede, amene ankagwira ntchito ku Dresden, nayenso anabatizidwa pafupifupi nthaŵi yomweyo. Motero Nkhondo Yadziko II ili mkati, tonse anayi tinapatulira miyoyo yathu kwa Yehova. Mu 1943, Amayi anakhala ndi mwana, mlongo wathu Renate.

Kuzunzidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chathu

Ndisanabatizidwe, ndinatuluka m’gulu la achinyamata lotchedwa Hitler Youth. Pamene ndinakana kupereka moni wa Hitler umene unkafunika tsiku lililonse kusukulu, aphunzitsi anandimenya. Komabe, ndinasangalala kuzindikira kuti ndinakhala wokhulupirika, mothandizidwa ndi makolo anga.

Komabe nthaŵi zina, mwina chifukwa cha mantha kapena chilango, ndinkanenabe kuti “Heil Hitler!” Zikatero ndinkapita kunyumba misozi ili m’maso, ndipo makolo anga ankapemphera nane pamodzi kuti ndikalimbe mtima ndi kukana chiyeso cha mdanicho nthaŵi ina. Ndinalephera kuchita chomwe chinali chabwino nthaŵi zochuluka chifukwa cha mantha, koma Yehova sanandisiye.

Tsiku lina Agestapo anabwera ndi kufufuza m’nyumba yathu. “Kodi ndiwe wa Mboni za Yehova?” mmodzi wa Agestapo anafunsa Amayi. Ndimawaonabe atayedzamira felemu ya chitseko, akunena molimba mtima kuti, “Inde”—ngakhale kuti anadziŵa kuti zimenezi zipangitsa kuti amangidwe.

Masabata aŵiri pambuyo pake, Amayi anali atatangwanika kusamalira Renate yemwe anali asanakwanitse nchaka chomwe, pamene Agestapo anabwera ndi kuwamanga. Amayi anadandaula kuti: “Ndikudyetsa mwana wanga kaye!” Komabe, mayi amene anabwera ndi wapolisiyo ananyamula mwanayo ndikulamula kuti: “Konzeka! Uyenera kunyamuka.” Zinali zovuta kwa Amayi.

Popeza Atate anali asanamangidwe, ine ndi mlongo wanga wamng’ono tinatsala ndi iwo. Mmawa wina patangotha milingu iŵiri kuyambira pamene Amayi anatengedwa, ndinawakumbatira kwambiri Atate ndisanapite kusukulu. Tsiku limenelo Atate anamangidwa chifukwa anakana kubwerera kukagwira ntchito yausilikali. Motero pamene ndinabwera masana, anali atapita, ndipo sindinawaonenso.

Agogo anga ndi abale athu ena—omwe onse ankatsutsa Mboni za Yehova ndipo ena anali mamembala a chipani cha Nazi—anayamba kutisunga ine ndi mlongo wanga wamng’onoyo. Sanandilole kuŵerenga Baibulo. Komabe, pamene mwachinsinsi ndinalipeza kwa mkazi wina woyandikana naye nyumba, ndinali kuŵerenga. Nthaŵi zinanso ndinkagwada pafupi ndi bedi la mlongo wanga wamng’onoyo ndi kupemphera.

Panthaŵi ino nkuti mlongo wanga Elfriede wapirira ziyeso chifukwa cha chikhulupiriro chake. Anakana kupitiriza kugwira ntchito m’fakitale imene inkakonza zida zankhondo ku Dresden, koma anapeza ntchito yosamalira pa paki ndi maluŵa ku Meissen. Akapita ku ofesi kuti akalandire malipiro ake, ankakana kugwiritsira ntchito moni woti “Heil Hitler!” Patapita nthaŵi, iye anamangidwa ndi kuponyedwa m’ndende.

Mwachisoni, Elfriede anadwala zilonda za pakhosi ndiponso scarlet fever ndipo anamwalira milungu yochepa chabe pambuyo pa kumangidwa. Anali ndi zaka 21 zokha. Mu imodzi ya makalata ake omalizira, anagwira mawu Luka 17:10: “Mutachita zonse anakulamulirani, nenani, Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.” Kukhulupirika kwake kwa Mulungu kwakhalabe kolimbikitsa kwa ine.—Akolose 4:11.

Kuyesedwa kwa Atate

Pamene Atate anamangidwa, agogo aamuna—abambo awo a Amayi—anapita kukayesa kuwapangitsa kusintha malingaliro awo. Atate anawabweretsa kumene kunali agogo ali omangidwa manja ndi miyendo. Atate anakana mwamphamvu ganizo lakuti ayambenso usilikali chifukwa cha ana awo. Mmodzi wa osunga ndende anauza Agogo kuti: “Ngakhale ngati munthu uyu akanakhala ndi ana 10, sakanasinthabe malingaliro ake.”

Agogo anabwerera kunyumba atakwiya kwambiri. “Chigaŵenga chimenechi! Munthu wopanda pake! Angathaŵe bwanji ana ake?” Iwo anakalipa. Ngakhale kuti Agogo anakwiya, ndinali wokondwa kudziŵa kuti Atate analimbabe.

Kenaka, Atate anawaweruza kuti aphedwe ndipo anawadula mutu. Patapita nthaŵi, ndinalandira kalata yawo yomalizirayo yomwe anandilembera. Anandilembera ine chifukwa sankadziwa kumene Amayi anakawatsekera. Ndinapita kuchipinda changa pamwamba ndi kuŵerenga mawu oyambawo omwe ndawagwira mawu poyamba nkhani ino. Ndinagwidwa chisoni ndipo ndinalira, koma ndinali wosangalala chifukwa chodziŵa kuti anakhalabe okhulupirika kwa Yehova.

Amayi Agwidwa Chisoni

Amayi anakawaponya m’ndende kummwera kwa Germany kudikirira kuweruzidwa kwa mlandu wawo kukhoti. Tsiku lina msilikali anabwera kuchipinda kwawo, akumanena mwaubwenzi kuti akhale pansi. Koma Amayi anaimirira ndi kunena kuti: “Ndikudziŵa kuti mwamuna wanga waphedwa.” Pambuyo pake, anawatumizira zovala zawo zokhala ndi magazi, umboni wosonyeza mmene anazunzidwira asanafe.

Panthaŵi ina Amayi anawaitanira ku ofesi ya ndende ndipo anawauza modzidzimutsa kuti: “Mwana wako wamkazi anamwalira m’ndende. Kodi ufuna aikidwe motani?” Mawuwa anali odzidzimutsa ndipo osayembekezeka kwakuti poyamba Amayi sanadziŵe zoti anene. Koma chikhulupiriro chawo cholimba mwa Yehova chinawalimbikitsa.

Achibale athu anatisamalira bwino pa zina ndi zina, ine ndi mlongo wanga. Ankatisunga bwino. Ndipo wina mwa iwo anafikira aphunzitsi anga ndi kuwapempha kuti adekhe nane. Motero aziphunzitsi nawonso anakhala aubwenzi ndipo sankandipatsa chilango ndikalephera kuwalonjera ndi mawu akuti “Heil Hitler!” Koma ankasonyeza kukoma mtimako ncholinga chondipatutsa pa chikhulupiriro changa cha m’Baibulo. Ndipo mwachisoni, zinandipatutsakodi.

Miyezi yochepa chabe nkhondo itatsala pang’ono kutha m’May 1945, ndekha mofuna ndinakachita nawo zochita za gulu la Nazi Youth. Ndinawalembera Amayi zimenezi, ndipo anaona m’makalata anga kuti sindinalinso ncholinga chofuna kutumikira Yehova. Kenaka, ananena kuti anali ndi chisoni kwambiri chifukwa cha makalata ameneŵa koposa kumva za imfa ya Atate ndi Elfriede.

Kenaka pambuyo pake nkhondo inatha, ndipo Amayi anabwerako kundende. Ndi chithandizo chawo, ndinalimbanso mwauzimu.

Kuyamba Utumiki Wanthaŵi Zonse

Kumapeto kwa 1949, pambuyo pa zaka zinayi chithere cha Nkhondo Yadziko II, woyang’anira woyendayenda analongosola mawu a m’Baibulo a pa Malaki 3:10 akuti: “Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m’nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu.” Ndinasonkhezereka kulemba fomu yofunsira ntchito ya ulaliki wanthaŵi zonse. Motero, pa January 1 1950, ndinakhala mpainiya, monga mmene atumiki a nthaŵi zonse amatchedwera. Kenaka, ndinasamukira ku Spremberg, kumene kunali kusoŵa kwakukulu kwa apainiya.

Mu August chaka chomwecho, ndinaitanidwa kukatumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Magdeburg, ku East Germany. Komabe, pa August 31, patangotha masiku aŵiri nditafika ine, apolisi anabwera modzidzimutsa pa nyumba pathu, akumanena kuti achifwamba akubisala panyumbapo. Mboni zambiri zinamangidwa ndi kutengedwera ku ndende, koma ndinali ndi mwaŵi wothaŵa ndi kupita ku West Berlin kumene Watch Tower Society inali ndi ofesi. Ndinakawauza kumeneko zimene zinali zitachitika ku Magdeburg. Panthaŵiyonso ndinauzidwa kuti Mboni zambiri zinali kumangidwa mu East Germany yense. Ndipo ndinamva kuti apolisi anali kundifunafuna ku Spremberg!

Kumangidwa ndi Kuponyedwa m’Ndende

Anandigaŵira kuti ndikachite upainiya ku East Berlin. Ndinamangidwa miyezi yoŵerengeka pambuyo pake pamene ndinali kutumikira monga wonyamula mabuku ofotokoza Baibulo kuchokera ku West Berlin kupita nawo ku East Germany, ndipo anapita nane ku mzinda wa Cottbus, kumene anandizenga mlandu ndi kundiweruza kukhala m’ndende zaka 12.

Mwa zina, anandiimba mlandu woti ndinali kufuna kuyambitsa nkhondo. Pamlandu wangawo, ndinati mmawu anga otsiriza: “Kodi zingatheke bwanji kuti ine wa Mboni za Yehova ndiimbidwe mlandu wa kukhala wolimbikitsa nkhondo pamene atate anga anakana kumenya nawo nkhondo chifukwa chakuti anali a Mboni za Yehova ndipo anadulidwa mutu?” Komabe anthu amenewo sankafuna chilungamo.

Pausinkhu wa zaka 19, sizinali zapafupi kulingalira zoti ndikhale m’ndende zaka 12. Komabe ndinazindikira kuti ena ambiri aweruzidwanso choncho. Nthaŵi zina, oyang’anira ndende ankazisiyanitsa Mboni; komabe tinkauza akaidi anzathu choonadi cha m’Baibulo, ndipo ena anakhala Mboni.

Nthaŵi zina, ife Mbonife ankatisunga m’chipinda chimodzi. Ndiye timayesetsa kuphunzira mabaibulo athu kwambiri. Tinali kuloŵeza machaputala a Baibulo pamtima, ngakhale kuyesa kuloŵeza mabuku a m’Baibulo. Tinkadziikira malire a chimene tichite ndi kuphunzira tsiku ndi tsiku. Nthaŵi zina tinkatangwanika kwambiri mwakuti tinkauzana kuti, “Tilibe nthaŵi,” ngakhale kuti tinkatha tsiku lonse m’ndende popanda kupatsidwa ntchito iliyonse kuti tiichite!

Apolisi a chinsinsi anali kutivutitsa ndi mafunso. Nthaŵi zina ankachita zimenezo usana ndi usiku, akumachita chilichonse kutiopseza. Nthaŵi ina, ndinatopa kwambiri ndipo ndinachita mphwayi, zikumapangitsa kukhala kovuta kuti ndipemphere. Patapita masiku aŵiri kapena atatu, popanda chifukwa chenicheni, ndinachotsa pepala pakhoma la ndende limene panalembedwa malamulo a m’ndendemo. Nditalitembenuza, ndinapeza kuti panali polembedwa. Nditalipenyetsa pamene panali kuwala kochepa, ndinaona mawu anali pamenepo: “Musaope opha thupi,” ndi “Ndidzasunga onse okhulupirika monga mwana wa diso langa.” Awa ndi mawu omwe masiku ano ali mbali ya nyimbo nambala 27 m’buku la nyimbo la Mboni za Yehova!

Nzoonekeratu kuti mbale wina yemwe anali m’vuto lokhala ngati lomweli anali m’ndende imeneyi, ndipo Yehova Mulungu anamlimbikitsa. Nthaŵi yomweyo ndinapezanso mphamvu zauzimu ndipo ndinathokoza Yehova chifukwa cha chilimbikitso chimenechi. Sindifuna kuiŵala phunziro limeneli, chifukwa linandiphunzitsa kuti ngakhale sindingathe kulimbana nazo ndekha ndi mphamvu zanga, ndi chithandizo cha Yehova Mulungu, palibe chomwe sichingatheke.

Amayi anali atasamukira ku West Germany motero sankadziŵa kalikonse panthaŵi imeneyi. Komabe panali Hanna, amene anakulira mumpingo wathu womwe nanenso ndinakulira ndipo anazoloŵerana kwambiri ndi banja lathu. Anali kumadzandiona nthaŵi yonse ndinali m’ndende, ndipo anali kumandilembera makalata olimbikitsa ndi kumanditumizira zakudya zamtengo wapatali. Ndinamkwatira nditamasulidwa ku ndende mu 1957, nditagwira ukaidi zaka 6 pa zaka 12 zomwe anandilembera.

Monga mkazi wanga wokondedwa, Hanna watumikira mokhulupirika pamodzi nane m’mautumiki osiyanasiyana ndipo nthaŵi zonse wakhala akumandichirikiza. Zomwe wakhala akundichitira panthaŵi yonse ya utumiki wathu ndi zakuti ndi Yehova Mulungu yekha amene angathe kumbwezera.

Utumiki Pambuyo Potuluka m’Ndende

Ine ndi Hanna tinayamba utumiki wathu wanthaŵi zonse pa ofesi yomwe Watch Tower Society inali kukonzetsa mu West Berlin. Ine ndinagaŵiridwa kukagwira ntchito yomanga kumeneko monga kalipentala. Kenaka, tinayamba kuchita upainiya pamodzi ku West Berlin.

Willi Pohl, amene panthaŵiyo ankayang’anira ntchito yathu ku West Berlin, anandilimbikitsa kupitiriza kuphunzira Chingelezi. “Ndilibe nthaŵi,” ndinayankha motero. Komabe, ndili wokondwa chotani nanga kuti ndinavomera kupitiriza kuphunzira Chingelezi! Zotsatira zake, mu 1962, ndinaitanidwa kukachita kosi ya miyezi khumi ya kalasi la 37 la Sukulu ya Gileadi ku Brooklyn ku New York. Nditabwerera ku Germany pa December 2, 1962, ine ndi Hanna tinatha zaka 16 m’ntchito ya woyang’anira woyendayenda, tikumachezera mipingo m’Germany yense. Kenaka, mu 1978, tinaitanidwa kukatumikira pa ofesi ya nthambi ku Wiesbaden. Pamene ofesi yanthambi inasamukira ku maofesi atsopano okulirapo ku Selters m’ma 1980, tinatumikira pa maofesi okongolawo kwa zaka zingapo.

Mwaŵi Wautumiki Wabwino

Mu 1989 chinthu china chosayembekezeka chinachitika—malire otchedwa Berlin Wall analeka kugwira ntchito, motero Mboni za kumaiko a ku Eastern Europe zinayamba kusangalala ndi mwaŵi wokhala ndi ufulu wolambira. Mu 1992, Ine ndi Hanna anatiitana ku Lviv, ku Ukraine, kukathandiza m’dera lomwe chiŵerengero cha olengeza Ufumu chikuwonjezeka mofulumira.

M’chaka chotsatira tinatumizidwa ku Russia kukathandiza kuyendetsa ntchito ya Ufumu kumeneko. Ku Solnechnoye, mudzi wokhala pamtunda wa makilomita 40 kunja kwa St. Petersburg, kunali kumangidwa ofesi kuti izisamalira ntchito yolalikira mu Russia yense ndiponso m’madera ena a yemwe kale anali Soviet Union. Titafika, anali atayamba kale kumanga nyumba yogonamo kuphatikizaponso ofesi yaikulu ndi nyumba yosungiramo katundu.

Tinali ndi chimwemwe chosaneneka pamene nthambi yathu yatsopanoyo inapatulidwa pa June 21, 1997. Panali osonkhana okwana 1,492 omwe anafika ku Solnechnoye pa programu yapaderayi ochokera m’maiko 42. Tsiku lotsatira, anthu okwana 8,400 anasonkhana mu St. Petersburg Petrovsky Stadium kuti akamvetsere kubwerezanso kwa programu ya kupatulirayo kuphatikizapo malipoti olimbikitsa onenedwa ndi alendo ochokera ku maiko ena.

Ndi chiwonjezeko chotani nanga chimene takhala nacho m’zigawo 15 za yemwe kale anali Soviet Union! Mu 1946, pafupifupi olengeza Ufumu okwana 4,800 anali kulalikira m’chigawo chimenechi. Mu 1985, patapita pafupifupi zaka 40, chiŵerengerocho chinakula kufika 26,905. Lerolino, pali olengeza Ufumu oposa 125,000 m’madera khumi a yemwe kale anali Soviet Union omwe akusamaliridwa ndi ofesi ya nthambi kuno ku Solnechnoye, ndipo oposa 100,000 akulalikira m’madera ena asanu a yemwe kale anali Soviet Union! Tinali okondwa chotani nanga kumva kuti m’zigawo 15 za yemwe kale anali Soviet Union, oposa 600,000 anafika pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu mu March wapitayu!

Ndimasangalala kuona mmene Yehova Mulungu watsogozera ntchito yotuta ndi kusonkhanitsa anthu ake ‘m’masiku otsiriza ano.’ (2 Timoteo 3:1) Monga mmene wamasalmo a m’Baibulo ananenera, Yehova amalangiza atumiki ake, amawalangiza mmene afunikira kuyendera ndipo amatero diso lake lili pa iwo. (Salmo 32:8) Ndimauona kukhala mwaŵi chotani nanga kukhala mmodzi wa m’gulu la padziko lonse la Yehova!

[Chithunzi patsamba 11]

Ndili ndi alongo anga aŵiri, mu 1943

[Chithunzi patsamba 12]

Atate anadulidwa mutu

[Chithunzi patsamba 12]

Amayi anandithandiza kuti ndilimbenso mwauzimu

[Chithunzi patsamba 13]

Ndili ndi mkazi wanga, Hanna

[Chithunzi patsamba 14]

Pankhani ya kupatulira mu Nyumba ya Ufumu ku nthambi ya ku Russia

[Zithunzi patsamba 15]

Panja ndi mawindo ake a chipinda chodyera pa nthambi yathu yatsopano mu Russia

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena