Dziko Lopanda Upandu Layandikira!
PAMENE tiona mkhalidwe wadziko lerolino, nkoonekeratu kuti nkovuta kwambiri kupeŵa kusonkhezeredwa kuchita zoipa. Ndipotudi, tonsefe timabadwa opanda ungwiro, omafuna kuchita zoipa. (1 Mafumu 8:46; Yobu 14:4; Salmo 51:5) Ndipo popeza kuti Satana Mdyerekezi anachotsedwa kumwamba, akuyesetsa kusiyana ndi kale lonse kuchititsa mavuto.—Chivumbulutso 12:7-12.
Zotulukapo zake zakhala zoopsa. Mwa chitsanzo, kufufuza komwe kunachitidwa pa ana 4,000 a ku Scotland kunasonyeza kuti ana aŵiri mwa atatu alionse a zaka za pakati pa 11 ndi 15 anachitapo kale zaupandu. Kufufuza kochitidwa m’Britain yense kunasonyeza kuti pafupifupi wachinyamata wachitatu aliyense savutika ndi chikumbumtima ngati aba katundu m’sitolo. Ndipo oposa theka anavomera kuti ngati atapatsidwa chenji chochuluka sangabweze ndalama zowonjezerekazo.
Buku la Chitaliyana lakuti Lʹoccasione e lʹuomo ladro (Mwaŵi ndi Mbala) limathandiza kuzindikira chifukwa chake anthu amaba. Bukulo likuti mbala “sizitha kudziletsa kwenikweni” ndikuti akuba “satha kusadzikondweretsa.” Likuwonjezera kuti mbala zambiri si akatakwe akuba koma chabe “anthu ongopezerapo mwaŵi pamikhalidwe yomwe ilipo.”
Chokondweretsa nchakuti bukulo likulongosolanso chifukwa chake anthu ambiri “amakana kuswa malamulo.” Likuti si chifukwa chakuti iwo “amaopa kuti mwalamulo adzalangidwa koma chifukwa chakuti ali ndi makhalidwe abwino amene amawaletsa kutero.” Kodi anthu angawaphunzire kuti makhalidwe abwino oterowo?
Maphunziro Omwe Akufunika
Chabwino, talingalirani zimene anthu amaphunzira mwa njira zambiri zolankhulirana. Mwachitsanzo, kaŵirikaŵiri mavideo ndi mawailesi akanema amasonyeza kuti chiwawa, chiwerewere, ndi khalidwe losayenerera ndi zololedwa. Choncho mposadabwitsa kuti anthu sadziletsa kwenikweni. Mosiyana ndi zimenezo, Baibulo mwanzeru limaphunzitsa kuti: “Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mudzi.”—Miyambo 16:32.
Polingalira za manenanena a masiku ano, siziyenera kutidabwitsa kuti anthu ambiri “satha kusadzikondweretsa.” Kaŵirikaŵiri anthu amamva mawu akuti: “Mungatenge pangongole.” “Uzidzichitira zabwino wekha.” “Ukuyenerera zabwino zedi.” “Uzichita zomwe ufuna.” Kudzikondweretsa kumaonedwa kukhala kwabwino ndiponso koyenerera. Koma kudzikonda koteroko nkosemphana ndi zomwe Baibulo limaphunzitsa kuti “munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.”—Afilipi 2:4.
Kodi simungavomereze kuti anthu ambiri amene ali osaona mtima amangopezera mwaŵi pa mkhalidwe womwe ulipo? Zachisoni, anthu ofuna kuipitsa zinthu kuti iwo apeze bwino akuchulukirachulukirabe. Safunsa ngati mchitidwe wakutiwakuti uli wabwino. Zomwe zimawakhudza nzakuti, ‘kodi ndingazembe?’
Kodi chikufunika nchiyani? Monga kwasonyezedwa kale, chofunika ndi makhalidwe abwino. Adzaletsa anthu kuchita zaupandu, kusalemekeza kupatulika kwa moyo, kusaona ukwati kukhala wopatulika, kupitirira malire pa khalidwe loyenera, ndi kupondereza ufulu wa chibadwidwe wa anthu ena. Amene saphunzira makhalidwe oterowo, “sazindikiranso makhalidwe,” monga mmene Baibulo limanenera. (Aefeso 4:19, NW) Khalidwe laupandu, la anthu opanda umulungu amenewo, nlimene limatilepheretsa kukhala ndi dziko lopanda upandu.
Mmene Dziko Latsopano Lidzafikire
Nzoona kuti anthu ambiri amayesetsa kukhala oona mtima, kulemekeza ndi kulingalira anzawo, ndi kusachita zinthu zosemphana ndi malamulo. Koma tingaphonye ngati titamaganiza kuti munthu aliyense padzikoli adzasintha. Ambiri sadzatero, mofanana ndi anthu ochuluka amene anali ndi moyo m’nthaŵi ya munthu wolungamayo Nowa omwe sanafune kuchita zabwino. M’dziko lachiwawa limenelo, Nowa yekha ndi banja lake anakana khalidwe lopanda umulungu, motero anayanjidwa ndi Mulungu. Mlengi wathu anabweretsa dziko limene kwakanthaŵi linalibe upandu mwa kuchotsa anthu opanda umulungu pa Chigumula cha padziko lonse.
Ndi bwino kumakumbukira kuti nkhani ya m’Baibulo yonena za Chigumula ndi kuwonongedwa kwa anthu opanda umulungu siili chabe nkhani yosangalatsa. Yesu Kristu anafotokoza kuti: “Monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa munthu.” (Luka 17:26; 2 Petro 2:5; 3:5-7) Monga momwe Mulungu anawonongera dziko lachiwawa limenelo Chigumula chisanafike, adzawononganso dziko lodzala upanduli.
Magwero odalirika akutitsimikizira kuti: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse,” monga analongosolera mtumwi wokondedwa wa Yesu, Yohane. (1 Yohane 2:17) Baibulo likutero kuti, kutha kwa dzikoli kudzatsegulira njira dziko latsopano mmene ‘[Mulungu] adzakhalitsa [ndi anthu], ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.’—Chivumbulutso 21:3, 4.
Polongosola mmene dziko latsopano limenelo lidzafikire, Baibulo limatinso: “Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.” (Miyambo 2:22) Pokhala ndi anthu okha oongoka mtima m’dziko, ulosi wa Baibulo uwu udzakwaniritsidwa: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:11.
M’dziko latsopano la Mulungu, ngakhale nyama sizidzakhala zovulaza. Baibulo limaneneratu kuti: “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalungwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choŵeta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera. . . . Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”—Yesaya 11:6-9; 65:17; 2 Petro 3:13.
Dziko Latsopano la Mulungu Lili Pafupi
Nkhani yabwino njakuti mikhalidwe yabwino imeneyo posachedwapa idzakhala padziko lonse lapansi. Kodi tingatsimikize choncho bwanji? Chifukwa cha zimene Yesu analosera kuti zikachitika dzikoli litatsala pang’ono kutha. Mwa zina, analosera kuti: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo akutiakuti.” Anatinso: “Chifukwa cha kuchuluka kwa kusayeruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazirala.”—Mateyu 24:7, 12.
Mtumwi wa Yesu analoseranso kuti: “[M’]masiku otsiriza [a dzikoli] zidzafika nthaŵi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, . . . osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, . . . okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” (2 Timoteo 3:1-5) Tili kukhaladi “[m’]masiku otsiriza” adzikoli! Choncho posachedwapa, ilo lidzaloŵedwa m’malo ndi dziko latsopano lolungama la Mulungu!
Kuphunzira Baibulo kwapangitsa anthu mamiliyoni ochuluka kuzindikira kuti dziko lopanda upandu nlotheka, ndipo iwo akuvomereza chiitano chakuti aphunzitsidwe m’njira za Mlengi wathu, Yehova Mulungu. (Yesaya 2:3) Kodi mungakonde kugwirizana nawo? Kodi muli okonzekera kuti muyesetse kukapeza moyo m’dziko latsopano lopanda upandu?
Yesu anasonyeza chofunika choyamba. Iye anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” Motero, ubwino wanu wosatha wagona pakuti muphunzire Mawu a Mulungu ndi kuchita zimene mumaphunzira.—Yohane 17:3.
[Chithunzi pamasamba 8, 9]
Baibulo limanena za dziko latsopano lopanda upandu ndi mmene tingakhaliremo