Linawathandiza Kuleka Ndeu
Mnyamata wazaka 11 wa ku California, U.S.A., analembera kalata yotsatirayi Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York:
“Mabuku anu ndimawakonda, makamaka buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Tisanapeze bukulo, ine ndi mlongo wanga timangoyambana nthaŵi zonse. Tsiku lina tinaganiza zophunzira bukuli, ndipo tinazindikira kuti sitinali kuchita zimene Mulungu amafuna kuti tizichita.
“Bukuli linatithandiza kwambiri. Ndikuliyamikira, ndipo ndikulimbikitsa mabanja ena kuti aliŵerenge chifukwa ndi labwino. Likuthandizanso banja lathu kukhala mwamtendere ndi mwachimwemwe.”
Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja ndi buku lamasamba 192 limene lili ndi nkhani zothandiza zonga ngati “Tetezerani Banja Lanu ku Zisonkhezero Zowononga,” “Sungani Mtendere m’Banja Mwanu,” ndi “Mukhoza Kulaka Mavuto Owononga Banja.”
Ngati mungakonde kuti munthu wina azidzachita nanu phunziro la Baibulo la panyumba laulere, lemberani kalata ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malaŵi, kapena ku keyala yoyenerera yomwe ili patsamba 5.