Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Bwanji Ngati Umatamanda Mtundu Wako?
Tanya wazaka 17 anadandaula kuti: “Mnzathu wina kusukulu nthaŵi zonse amanena za mtundu ndi kaonekedwe ka khungu la anthu ena. Pankhani zake zambiri amadzinenerera kuti iye ndi wapamwamba kuposa iwo.”
NKWACHIBADWA kuti munthu amatamanda banja lake, chikhalidwe, chilankhulo, kapena kumene anachokera. “Ndine wa ku Vietnam ndipo ndimanyadira chikhalidwe chathu,” anatero mtsikana wotchedwa Phung wazaka 15.
Komabe, kaŵirikaŵiri, kunyadira mtundu wako kumayendera pamodzi ndi kusankhana mitundu. Kunyadira kumeneku kukhoza kukhala kachilombo kamene kamawononga ubwenzi pang’onopang’ono, ngakhale patamaoneka ngati kuti pali ulemu. Yesu Kristu anati: “Mkamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.” (Mateyu 12:34) Ngati mumtima mwanu munazika malingaliro akuti ndinu apamwamba—kapena malingaliro achipongwe—kaŵirikaŵiri zimadzaonekera ndipo zimakhala zopweteka ndi zoŵaŵa.
Nthaŵi zina kunyadira mtundu kumasanduka chiwawa. M’zaka zaposachedwapa ndiko kwapangitsa nkhondo, ziwawa, ndi “kupululutsana mafuko” mwankhalwe. Komabe, sikuti mpokhapokha mudzaone anthu akuphana kuti mudzaone kuti kunyadira mafuko kwakupangirani zoipa. Mwachitsanzo, kodi simuziona zimenezi kusukulu, pantchito, kapena kumene mumakhala? Wachinyamata wina yemwe ndi Mkristu wotchedwa Melissa, analongosola kuti: “Inde, timazionadi. Anzanga kusukulu amaseka ana amene amalankhula ndi lilime lozoloŵera chilankhulo china, ndipo anzangawo amati ndi apamwambako kuwaposa enawo.” Nayenso Tanya ananena kuti: “Kusukulu ndakhala ndikumva ana ena akuuza anzawo poyera kuti: ‘Ndimakuposa.’” Pa kufufuza kwina komwe kunachitika ku United States., pafupifupi theka la ofunsidwa anati iwo eni anakumanapo ndi tsankho lafuko m’chaka chapita. Natasha anati: “Pasukulu pathu pali kusankhana mitundu kwambiri.”
Tiyerekezere kuti mumakhala m’dziko kapena kumalo kumene mwina mwadzidzidzi chiŵerengero cha obwera chakula mwamsanga, zikumapangitsa zinthu kusintha mwadzidzidzi pasukulu panu, kumene mumakhala, kapena mumpingo wachikristu. Kodi zimenezi zimakunyansani nthaŵi zina? Ndiye kuti mwina chimapangitsa ndi kunyadira fuko m’maganizo mwanu zomwe inu simukuzindikira bwino.
Kunyadira Kwabwino Mosiyana ndi Koipa
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti kunyadira fuko konse nkoipa? Si choncho. Baibulo limasonyeza kuti kunyadira koyenera kuli ndi nthaŵi yake. Pamene mtumwi Paulo analembera Akristu a ku Tesalonika, anati: “Ife tokha tidzitamandira za inu m’Mipingo ya Mulungu.” (2 Atesalonika 1:4) Mofananamo, kudzitamandira pang’ono nkwabwino ndipo nkoyenera. (Aroma 12:3) Motero kutamanda pang’ono fuko, banja, chilankhulo, maonekedwe a khungu, kapena kwanu kobadwira si kulakwa pakokha. Nzoonekeratu kuti Mulungu sangafune kuti tizichita manyazi ndi zimenezo. Pamene mtumwi Paulo anamuyesa mpandu wa ku Aigupto, sanakayike kunena kuti: “Ine ndine munthu Myuda, wa ku Tariso wa m’Kilikiya, mfulu ya mudzi womveka.”—Machitidwe 21:39.
Komabe, kutamanda fuko kumakhala koipa ngati muphatikizapo kudzikweza konyanyira kapena ngati kumpangitsa munthu kuderera ena. Baibulo limanena kuti: “Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m’kamwa mokhota, ndizida.” (Miyambo 8:13) Ndipo Miyambo 16:18 imati: “Kunyada kutsogolera kuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.” Motero kudzitukumula kuti ine ndine wafuko lapamwamba nkoipa pamaso pa Mulungu.—Yerekezerani ndi Yakobo 4:16.
Mmene Kunyadira Fuko Kunayambira
Kodi chimapangitsa anthu kuti azinyadira fuko lawo mopambanitsa nchiyani? Buku lotchedwa Black, White, Other, lolembedwa ndi Lise Funderburg, limati: “Kwa anthu ambiri, maganizo awo oyamba (ndipo okhalitsa) ponena zamafuko amachokera kwa makolo ndi m’banja.” Nzachisoni kuti kaŵirikaŵiri makolo amapereka malingaliro osalongosoka kapena opotoka. Ana ena amauzidwa mwachindunji kuti anthu a fuko lawo ndi apamwamba ndi kuti amafuko ena sali choncho kapena kuti ndi apansi. Komabe, nzofala kwambiri kuti achinyamata amangoona ngati makolo awo sacheza ndi anthu a mafuko ena. Izinso zimasonkhezera mwamphamvu kalingaliridwe kawo. Kufufuza kumasonyeza kuti ngakhale achinyamata sagwirizana ndi makolo awo pa nkhani za zovala kapena nyimbo, achinyamata ambiri amakhala ndi malingaliro ofanana ndi makolo awo pa za mafuko.
Kusakhala ndi malingaliro achikatikati pankhani ya mafuko kukhozanso kuyambika chifukwa cha kutsenderezedwa kapena kuchitidwa nkhanza. (Mlaliki 7:7) Mwachitsanzo, aziphunzitsi anaona kuti ana a anthu amafuko otchedwa kuti ang’onoang’ono sadzilemekeza. Poyesayesa kuwongolera zinthu, aziphunzitsi ena ayambitsa phunziro lophunzitsa ana za mbiri ya fuko lawo. Chodabwitsa nchakuti akatswiri ena amati kuphunzitsa kutamandira fuko kumeneku kumangoyambitsa kusankhana mitundu.
Zomwe munthu unakumana nazo pamoyo wako nazonso zikhoza kukupangitsa kulingalira za fuko molakwika. Ngati munthu wafuko lina sanakuchitire bwino zikhoza kukupangitsa kutsimikiza kuti onse afuko limenelo ndi oipa kapena odzikonda. Kuipidwa ndi fuko lina kukhozanso kubuka pamene ofalitsa nkhani akamba kwambiri za kulimbana kwa mafuko, nkhanza za apolisi, ndi kuguba kwa anthu afuko lina ncholinga chosintha zinthu zina kapena pamene anena zoipa za fuko laling’ono.
Nthanthi Yakuti Fuko Lina ndi Lapamwamba
Bwanji nanga ponena za zomwe ena amanena kuti fuko lawo lili ndi zifukwa zonenera kuti nlapamwamba kuposa ena? Choyamba nchakuti ganizo loti anthu akhoza kugaŵidwadi m’mafuko osiyana kwambiri nlokayikitsa. Nkhani ina mu Newsweek inanena kuti: “Kwa a sayansi omwe analingalirapo za nkhaniyo, ufuko ndi nkhani yovuta imene sitingathe kuilongosola.” Nzoona kuti pangakhale “kusiyana koonekera bwino pa kaonekedwe ka khungu, mmene tsitsi lilili ndiponso mmene maso kapena mphuno zilili.” Komabe, Newsweek inanena kuti “kusiyana kumeneku nkwapakhungu basi—ndipo ngakhale ayesetse chotani, asayansi alephera kupeza kusiyana kwenikweni kosiyanitsa fuko ili ndi linzake. . . . Kwa asayansi omwe amafufuza zimenezi, mfundo njakuti fuko ndi ‘chikhalidwe cha anthu’ basi—mphatikizo woipa wa tsankhu, mwambo ndi nthanthi.”
Ngakhale ngati mwasayansi patapezeka zizindikiro zosiyanitsa mafuko, ganizo lakuti pali fuko “lapalokha” ndi nthanthi chabe. The New Encyclopædia Britannica inati: “Kulibe mafuko apaokha; magulu onse amafuko omwe alipo tsopano ndi oloŵanaloŵana.” Mulimonse mmene zingakhalire, Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu “ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu.” (Machitidwe 17:26) Mosasamala kanthu za kaonekedwe ka khungu, kaya mmene tsitsi lilili, kapena mmene kumaso kuliri, pali chabe fuko limodzi—mtundu wa anthu. Anthu onse ndi paubale mwa kholo lathu Adamu.
Ayuda akale ankazindikira bwino za chiyambi chimodzi cha mafuko a anthu. Koma, ngakhale pamene anakhala Akristu, ena ankaumirirabe chikhulupiriro chakuti iwo anali apamwamba kuposa omwe sanali Ayuda—kuphatikizapo okhulupirira anzawo omwe sanali Ayuda! Mtumwi Paulo anatsutsa chikhulupiriro chakuti fuko lina ndi lapamwamba mwakunena kuti, ‘Ayuda ndi Ahelene omwe, onsewa agwidwa ndi uchimo,’ monga momwe analembera pa Aroma 3:9. Motero palibe fuko lililonse limene linganyade kuti Mulungu amaliyanja. Ndithudi, munthu angakhale paubwenzi ndi Mulungu kokha mwa kukhulupirira Yesu Kristu. (Yohane 17:3) Ndipo Mulungu ‘amafuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.’—1 Timoteo 2:4.
Ngati muzindikira kuti mafuko onse ndi ofanana pamaso pa Mulungu zikhoza kukhudza kwambiri mmene mumadzionera nokha ndi ena. Zikhoza kukupangitsani kumalemekeza ena, kumayamikira ndi kusirira kukhala kwawo osiyana. Mwachitsanzo, wachinyamata wotchedwa Melissa, yemwe tinamtchula poyamba, samagwirizana ndi anzake akusukulu akamaseka ana ena omwe amalankhula ndi lilime lozoloŵera chilankhulo china. Iye anati: “Omwe amalankhula zilankhulo ziŵiri ndimaŵaona monga anzeru. Ine ndimangotha kulankhula chilankhulo chimodzi ngakhale kuti ndimafuna kumalankhulanso chilankhulo china.”
Kumbukiraninso kuti pamene nkosakayikitsa kuti anthu amafuko ndi chikhalidwe chanu ali nazo zambiri zoti nkunyandira, zilinso choncho ndi anthu a mafuko ena. Ndipo ngakhale kuti nkoyenera kunyadira chikhalidwe chanu ndiponso zimene makolo anu akale anachita, nkopindula kwambiri kunyadira zimene inu mwininu mwachita mwa kuyesetsa ndi kugwira ntchito mwakhama! (Mlaliki 2:24) Makamaka, pali chinthu chimodzi chimene muyenera kuchita chimene Baibulo limalimbikitsa kuti muzinyadira. Monga mmene zinanenedwera pa Yeremiya 9:24, Mulungu mwiniyo anati: “Wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziŵa Ine, kuti ndine Yehova.” Kodi mukhoza kudzitamandira choncho?
[Chithunzi patsamba 30]
Kudziŵa mmene Mulungu amaonera mafuko kumatithandiza kugwirizana ndi anthu amafuko ena