April 11, 1998—Tsiku Loyenera Kukumbukira
Usikuwo asanafe, Yesu anapatsa atumwi ake mkate wopanda chotupitsa ndi chikho cha vinyo ndipo anawauza kuti adye ndi kumwa. Komanso anawauza kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.”—Luka 22:19.
Chaka chino kukumbukira zimenezi kudzakhalako Loŵeruka pa April 11, dzuŵa litaloŵa. Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse lapansi zidzasonkhana usiku wapadera umenewu kudzachita Chikumbutso monga mmene Yesu analamulirira. Tikukuitanani kuti mudzakhale nafe kuti mudzaonerere. Chonde funsani Mboni za Yehova zakwanuko za nthaŵi yeniyeni ndi malo kumene kudzakhale msonkhano.