Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Nditsanzire Yani Monga Chitsanzo?
“Anali ndi luso lodabwitsa poseŵera maseŵera a mpira wotchedwa basketball. Anzanga onse ankamkonda. Anali chitsanzo kwa ine, ndipo ndinkafuna kukhala ngati iye ndi kumatamandidwa monga iyeyo.”—Ping, mnyamata wa ku Asia.
ANTHU amene ena amawakhumbira ndi kuwatsanzira amatchedwa zitsanzo. Mlembi wotchedwa kuti Linda Nielsen anati: “Achinyamata amatsanzira anthu amene amawadziŵa zomwe amakonda ndi kumvetsa malingaliro awo, amenenso anthu amachita nawo chidwi kapena amene amalandira mphotho zimene achinyamatawo amasirira.” Motero achinyamata amakonda kusirira anzawo amene ali otchuka ndi achikoka. Koma achinyamata ambiri amakonda kwambiri kutsanzira akatswiri a m’kanema, oimba ndi ochita maseŵera.
Komatu, umunthu umene anthu otchuka ambiri amaonetsa kwa anthu wangokhala wopeka, ndipo amachita kuukhalira pansi poukonza ncholinga chakuti abise zophophonya zawo kuti anthu awatame, ndipo koposa zonse, kuti malonda ayende! Ping amene tinamgwira mawu poyambapo, anavomereza kuti: “Ndinagula matepu avidiyo onse a katswiri wanga wa basketball ndipo ndinkavala zovala ndi nsapato zolembedwapo dzina lake.” Achinyamata ena amavala monga akatswiri a pa TV kapena a zamaseŵero omwe iwo amawatama, kumeta tsitsi monga akatswiriwo, ndipo mwina ngakhale kuyenda ndi kulankhula monga iwo.
Zitsanzo—Zabwino ndi Zoipa
‘Koma kodi pali vuto lanji ngati umasirira munthu wina?’ Mukufunsa choncho. Zimadalira ndi amene mukumsirirayo. Baibulo limati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Baibulo silitilimbikitsa kukhala otsatira anthu. (Mateyu 23:10) Komabe limatiuza kuti tiyenera ‘kutsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.’ (Ahebri 6:12) Yemwe analemba mawu amenewo, mtumwi Paulo, anapereka chitsanzo chabwino kwa Akristu oyambirira. Motero anatha kunena kuti: “Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Kristu.”—1 Akorinto 11:1.
Mnyamata wina wotchedwa Timoteo anachitadi zimenezo. Anapanga ubwenzi ndi Paulo pamaulendo a umishonale omwe anayendera pamodzi. (Machitidwe 16:1-4) Paulo anafika pomuona Timoteo monga ‘mwana wake wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye.’ (1 Akorinto 4:17) Ndi chithandizo cha Paulo, Timoteo anakhala mwamuna wapadera wachikristu.—Afilipi 2:19-23.
Koma nanga chingachitike nchiyani ngati musankha munthu woipa kukhala chitsanzo? Wachinyamata wina wotchedwa Richard anati: “Pamene ndinali ndi zaka 15, mnzathu wakusukulu wotchedwa Mario anakhala bwenzi langa lapamtima. Makolo anga anali Akristu, ndipo ankayesetsa kundithandiza pa zauzimu. Koma Mario anali ndi zambiri zosangalatsa—madisiko, mapwando, njinga za moto, ndi zina zotero. Ankachita zonse zomwe afuna, pamene afuna. Koma ine ayi. Motero pamene ndinali ndi zaka 16, ndinawauza makolo anga kuti ndifuna kuleka kukhala Mkristu, ndipo ndinaterodi.”
Kodi pali ngozi yofananayo ngati titenga anthu otchuka ndi akatswiri amaseŵero kukhala zitsanzo zathu? Inde, ilipodi. Ndithudi, palibe cholakwika kungokhumbira luso la katswiri wamaseŵero, kapena wa m’kanema, kaya woimba. Koma dzifunseni kuti, ‘Kodi nchitsanzo chanji chimene anthu ameneŵa amasonyeza pa kakhalidwe kawo?’ Kodi ambiri mwa akatswiri amaseŵera, oimba, ndi ochita zina zosiyanasiyana samadziŵika ndi khalidwe la chiwerewere, kumwa mankhwala osokoneza bongo, ndi moŵa? Kodi si zoona kuti ambiri amakhala osasangalala, osakhutira pamoyo wawo, ngakhale kuti ali ndi ndalama zambiri ndiponso ndi otchuka? Mutapenda muli ndi mfundo zimenezi m’malingaliro, kodi mungapindule chiyani ngati mutsanzira ameneŵa?
Zoonadi, kutengera kasamalidwe ka tsitsi, kavalidwe, kapena kalankhulidwe ka munthu wotchuka zingaoneke ngati si nkhani yaikulu. Koma kungakhale ‘kukupanikizani m’chikombole chake.’ (Aroma 12:2, Phillips) Poyamba chikombolecho chingaoneke chabwino. Koma mukatsatira kwambiri chisonkhezero chake, chingakuumbeni m’njira zimene mosakayika zidzakupangani mdani wa Mulungu. “Ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu,” limatero Baibulo pa Yakobo 4:4.
Mmene Chitsanzo Chabwino Chingakuthandizireni
Komabe kutsanzira munthu wina wachitsanzo chabwino kukhoza kukuthandizani kwambiri pa moyo wanu! Pakati pa abale, Akristu anzanu, mukhoza kupeza ambiri amene ali “chitsanzo . . . m’mawu, m’mayendedwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, m’kuyera mtima.” (1 Timoteo 4:12) Kunena zoona muyenera kuchenjera pamene musankha mabwenzi, ngakhale mumpingo wachikristu. (2 Timoteo 2:20, 21) Komabe sizivuta kuona amenedi “alikuyenda m’choonadi” mumpingo. (2 Yohane 4) Pulinsipulo la pa Ahebri 13:7 limati: “Poyang’anira chitsiriziro cha mayendedwe awo mutsanze chikhulupiriro chawo.” Chifukwa ambiri mwa mabwenzi anu, zakuti kaya khalidwe lawo lidzakhala lotani sizinadziŵikebe. Koma muli akuluakulu mumpingo wanu amene aonetsa kukhulupirika kwawo, ndipo nkwanzeru kuzoloŵerana nawo ameneŵa.
‘Kuzoloŵera akuluakulu?’ mukhoza kufunsa. Inde zingaoneke kukhala zosakondweretsa poyamba. Koma takumbukirani unansi umene Timoteo anali nawo ndi bwenzi lake lachikulirelo, mtumwi Paulo amene anaona kuti Timoteo anali wokhoza kuchita zinthu ndipo anamlimbikitsa ‘kukoleza mphatso ya Mulungu’ inali mwa iye. (2 Timoteo 1:6) Kodi sizingakhale zothandiza kuti wina wake akuthandizeni ndi kukulimbikitsani, akumakuchondererani kuti mukulitse mphatso zanu zopatsidwa ndi Mulungu?
Wachinyamata wina wotchedwa Bryan anaona kuti zimenezi zinalidi zothandiza. Anali kuvutika chifukwa chakudziona monga wopanda pake pamene anayamba kugwirizana ndi mtumiki wotumikira wachikulire, wosakwatira yemwe anali mumpingomo. Bryan anati: “Ndimasirira khalidwe lake lolingalira za ena, kuphatikizapo ine; changu chake pautumiki; ndiponso luso lake pokamba nkhani.” Bryan wayamba kale kupindula chifukwa cha chidwi chimene Mkristu wachikulireyu anali nacho kwa iye. Iye akuvomereza poyera kuti: “Zandithandiza kwambiri kusintha kusiyana ndi mmene ndinalili poyamba—wamanyazi ndi wamphwayi.”
Makolo Monga Chitsanzo
Buku lotchedwa kuti Adolescence—Generation Under Pressure limanena kuti makolo ndi “chida chachikulu cholimbikitsa kapena kupondereza ana pamene akufika panthaŵi yoti nkukhala ndi umunthu wawowawo.” Bukulo likuwonjezera kuti popanda kuwatsogolera bwino ndi kuwathandiza kukhala ndi umunthu wawowawo, achinyamata “amakhala ngati chombo chopanda chiwongolero, chimene chimangosinthasintha koloŵera chikagundidwa ndi funde lililonse.”
Malangizo ameneŵa amangofanana ndi omwe analemba wophunzira Yakobo zaka 1,900 zapitazo, olembedwa pa Yakobo 1:6: “Apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.” Mwinamwake mukudziŵa achinyamata ena otero. Amangokhalira zalero, salingalirapo za maŵa.
Kodi muli ndi makolo oopa Mulungu amene amasonyeza chitsanzo chabwino mumpingo? Ngati zili choncho, kodi inu mumawatsanzira? Kapena mumatsutsana nawo nthaŵi zonse? Kunena zoona, makolo anu si angwiro. Koma musanyalanyaze makhalidwe awo abwino—makhalidwe amene mungachite bwino ngati mutatsanzira. “Ndimasirira kwambiri makolo anga,” analemba motero Mkristu wachinyamata wotchedwa Jarrod. “Changu chawo cha nthaŵi zonse pa utumiki, mmene anapiririra vuto la zachuma, ndiponso mmene ankandilimbikitsira kuti ndichite nawo utumiki wanthaŵi zonse, zonsezo zinandithandiza kwambiri. Nthaŵi zonse ndakhala ndikutsanzira makolo anga.”
Chitsanzo Chabwino Kwambiri
Pamene bungwe lofufuza la Gallup linkafunsa achinyamata ku United States kuti ndani amene ankamganizira kuti ndiye munthu wamkulu koposa m’mbiri, ambiri ankatchula atsogoleri a zandale a ku America. Ndi 6 peresenti yokha yomwe inatchula Yesu Kristu. Komabe Baibulo limatiuza kuti Yesu Kristu anatisiyira ‘chitsanzo [changwiro] kuti tikalondole mapazi ake.’ (1 Petro 2:21; Ahebri 12:3) Amalimbikitsa ophunzira ake kuphunzira kwa iye. (Mateyu 11:28, 29) Koma kodi mungachite motani zimenezo?
Muyenera kudziŵa bwino moyo wa Yesu. Yesani kuŵerenga nkhani zonse zopezeka m’Mauthenga Abwino, limodzi ndi buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako.a Onetsetsani mmene Yesu ankaphunzitsira, mmene ankachitira ndi anthu mwachifundo, ndiponso kulimba mtima kumene ankasonyeza zinthu zikavuta. Mudzaona kuti Yesu ndiye chitsanzo chabwino kwambiri chimene mungatsanzire.
Pamene muzoloŵerana ndi wopereka chitsanzo changwiro ameneyo, mpamenenso simudzalakalaka kwambiri mabwenzi ndi anthu otchuka koma osayenera. Kodi mukukumbukira Ping ndiponso mmene amasirira akatswiri a maseŵera? Mpaka tsopano Ping amaseŵerabe basketball nthaŵi ndi nthaŵi, koma anazindikira kuti kutengera anthu otchuka nkopanda pake.
Nanga bwanji za Richard? Munthu amene anasankha kukhala chitsanzo chake anampangitsa kusiya chikhulupiriro chake chachikristu. Komabe, Richard anadzadziŵana ndi mnyamata wina yemwe anali m’zaka za m’ma 20, wotchedwa Simon, amene anali wa Mboni za Yehova. “Simon anakhala bwenzi langa, ndipo anandithandiza kuona kuti munthu akhoza kumasangalala pa moyo wake popanda kuphwanya mapulinsipulo a Baibulo. Mwamsanga ndinayamba kumlemekeza Simon, ndipo chitsanzo chake chinandithandiza kwambiri kuti ndibwerere mumpingo ndi kupatulira moyo wanga kwa Yehova. Tsopano ndine wosangalala kwambiri, ndipo moyo wanga ndi watanthauzo,” anatero Richard.
Ndithudi, kasankhidwe kanu ka amene muzitsanzira nkofunika kwambiri!
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Inc.
[Chithunzi patsamba 13]
Kuyanjana ndi akuluakulu akhalidwe labwino kukhoza kukuthandizani