Zimene Odwazika Matenda Angachite
“NTHAŴI zonse ndimadabwa kuona mmene [anthu] amasiyanirana pakukhoza kwawo kupirira,” anatero Margaret, wodziŵa zamankhwala wa ku Australia yemwe kwa zaka zambiri wakhala akugwira ntchito yokhudzana ndi anthu odwala nthenda ya Alzheimer limodzi ndi odwazika matenda. Anapitiriza kuti: “Mabanja ena amalimba nazodi ngakhale zili zovuta zedi, pomwe ena amangolephereratu kungochokera pamene munthuyo wangoyamba kusonyeza zizindikiro zakusintha umunthu wake.”—Mawu ogwidwa m’buku lakuti When I Grow Too Old to Dream.
Kodi nchiyani chimapangitsa anthuwo kusiyana? Chifukwa china chingakhale mgwirizano pakati pa anthuwo kaya anali okondana kapena osakondana matendawo asanayambe. A pabanja okondana amapirira mosavutikira. Ndipo ngati munthu wodwala nthenda ya Alzheimer (AD) akusamalidwa bwino, nthendayo imakhala yosavuta kwenikweni.
Ngakhale kuti amamka akulephera kuchita zinthu, kaŵirikaŵiri odwalawo amayamikira akamasonyezedwa chikondi ndi chifundo mpaka matendawo atafika poipitsitsa. Chikalata chauphungu cha Communication, chochokera ku bungwe la Alzheimer’s Disease Society of London, chinatero kuti “mawu sali njira yokha yolankhulirana.” Njira ina yolankhulirana popanda mawu yomwe njofunika kwa wodwazika matenda ndiyo kumyang’ana mwaubwenzi ndikumlankhula ndi liwu lodekha. China chofunika ndicho kumyang’ana kumaso, ndiponso kulankhula ndi mawu omveka bwino ndi kumamtchula dzina nthaŵi zonse.
A Kathy, omwe tatchula m’nkhani yoyamba ija, anati: “Si kokha kuti kupitirizabe kulankhulana ndi wokondedwa wanu nkotheka, komanso nkofunika. Kumkhudza mwachikondi, mawu odekha, makamakanso kukhalapo kwanu pafupi naye kumamlimbikitsa wokondedwa wanuyo.” Bungwe la Alzheimer’s Disease Society of London linangonena mwachidule kuti: “Chikondi chingakuthandizeni kuyanjana, makamaka pamene kulankhulana kwafikira povuta kwambiri. Kumgwira dzanja munthuyo, kukhala naye pansi mutamgwira papheŵa, kumlankhula ndi mawu otonthoza kapena kumkupatira, zonsezo zili njira zosonyeza kuti mukumsamalabe.”
Ngati wodwazika matenda amagwirizana bwino ndi wodwalayo, kaŵirikaŵiri onse amaseka ngati wina walakwa kanthu kena. Mwachitsanzo, mwamuna wina anakumbukira mmene mkazi wake wosokonekera maganizo anayalira bedi koma nkulakwitsa nkuika bulangete pakati pansalu. Anadzadziŵa pamene anali kugona usiku. Mkaziyo anati: “Maine! Ndalakwitsa pamenepa.” Ndiye onse anangoseka.
Musafune Zambiri Pamoyo Wanu
Anthu odwala AD amamva bwino ngati ali pamalo amene anazoloŵera. Ndipo amafunikira kugwira ntchito imodzi imodzi masiku onse. Njira imene ingathandize kukwanitsa zimenezo ingakhale yakulemba bwino pakalenda yaikulu ntchito zofuna kuchitidwa tsiku ndi tsiku. Dr. Gerry Bennett anafotokoza kuti: “Kumsamutsa munthu pamalo amene anazoloŵera kukhoza kukhala ndi zotsatirapo zoipa. Nkofunika kuti munthu wosokonezeka maganizo azingokhala pamalo amodzimodziwo kuti aziona kuti chilichonse chili monga mwamasiku onse.”
Pamene nthendayo ikukula, odwala AD zimawavuta kwambiri kutsatira malangizo. Malangizowo ayenera kuperekedwa mwanjira yosavuta ndi yomveka bwino. Mwachitsanzo, kuuza wodwalayo kuvala zovala kungakhale kumuuza zinthu zovuta kwambiri. Muyenera kuziika zovalazo chimodzichimodzi ndiye mwina nkumamthandiza wodwalayo kuvala chovala chimodzichimodzi.
Amafunikira Kugwira Ntchito
Anthu ena odwala AD amayendayenda kapena kuchoka panyumba ndiyeno amadzasochera. Kuyendayenda kungakhale njira yabwino yoti wodwalayo azilimbitsa thupi ndipo mwina kungamthandize kuchepetsa kupsinjika maganizo ndipo kungamthandize kugona tulo tabwino. Komabe, kuchoka panyumba kungakhale kwangozi. Buku lakuti Alzheimer’s—Caring for Your Loved One, Caring for Yourself limafotokoza kuti: “Ngati wokondedwa wanu wachoka panyumba, muli mumkhalidwe wangozi, moti mwina nkudzangokhala tsoka. Mawu oyenera kuwakumbukira ngakuti musavutike mtima. . . . Anthu ofunafuna munthu wosochera amafuna kuti muwafotokozere mmene munthu wofunidwayo akuonekera. Sungani zithunzi zaposachedwapa zamaonekedwe achibadwa.”a
Komanso, odwala ena amakhala amphwayi ndipo mwina amangofuna kukhala pansi tsiku lonse. Apangitseni kuchita kanthu kena kamene nonsenu mungakonde. Apangitseni kuimba nyimbo, kuimba mluzi, kapena kuliza chida china choimbira nyimbo. Ena amakonda kuomba m’manja, kugwedeza mutu kapena kuvina nyimbo zimene amakonda. Dr. Carmel Sheridan anafotokoza kuti: “Kaŵirikaŵiri anthu odwala A.D. ntchito imodzi imene angaichite bwino kwambiri ndiyo imene imaphatikizapo nyimbo. A m’banja ena amanena kuti ngakhale kuti achibale awo amaiŵala [zinthu] zina, koma amakumbukirabe nyimbo zakale.”
“Ndinkangofuna Kutero”
Mkazi wina wa ku South Africa yemwe anali ndi mwamuna wodwala AD ndipo itafika poipitsitsa, ankakonda kukhala ndi mwamuna wake masiku onse kunyumba yosungiramo okalamba. Komabe, achibale ake anamdzudzula chifukwa cha zimenezo. Kapena chinali chifukwa chakuti zinkakhala ngati ankangowononga nthaŵi yake, poti mwamuna wakeyo sankamzindikiranso ndipo sankanena ngakhale liwu limodzi. Mkaziyo anadzafotokoza pambuyo pa imfa ya mwamuna wakeyo, kuti, “Komabe ndinkafuna kukhala naye. Manesi anali otanganidwa kwambiri, choncho pamene mwamuna wanga anadziipitsira, ndinkamusambitsa ndi kumsintha zovala. Sindinali kudandaula nazo—sizinali kundivuta. Tsiku lina anavulala phazi pamene ndinali kumkankha m’chikuku. Ndinamfunsa kuti, ‘Kodi likupweteka?’ ndiye iye anayankha kuti, ‘Lisapweteke bwanji?’ Mpamene ndinazindikira kuti anali adakamvabe ululu ndi kukhoza kulankhula.”
Ngakhale m’mabanja amene anthu ake sanali kugwirizanamo matenda a AD asanayambe, odwazika matenda anakhozabe kulimba nazo.b Kungodziŵa chabe kuti zimene akuchita nzoyenera ndipo nzokondweretsa Mulungu kumawapangitsa kumva bwino. Baibulo limati, “Aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba” ndiponso limati, “Usapeputse amako atakalamba.” (Levitiko 19:32; Miyambo 23:22) Ndiponso Akristu amalamulidwa kuti: “Koma ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu. Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.”—1 Timoteo 5:4, 8.
Mothandizidwa ndi Mulungu, anthu ambiri osamala odwala akhala akuchita ntchito yoyamikirika posamala achibale odwala, kuphatikizapo odwala nthenda ya Alzheimer.
[Mawu a M’munsi]
a Anthu ena odwazika matenda anaona kuti nkothandiza kumuika wodwalayo chizindikiro, mwina chonga mphete kapena mkanda womwe angavale mkhosi.
b Kuti mumve zambiri ponena za kusamala wina ndi mmenenso ena angathandizire, onani nkhani zakuti “Kusamala Wina—Kukwanitsa Vutolo,” pamasamba 3-13 mu Galamukani! ya February 8, 1997.
[Bokosi patsamba 19]
Nthenda ya Alzheimer ndi Mankhwala Ake
NGAKHALE kuti pakali pano akuyesa mitundu ngati 200 ya mankhwala ochiritsa nthenda ya Alzheimer (AD), mankhwala enieni ochiritsa nthendayo sanapezekebe. Akuti mankhwala ena amamthandiza munthu kusaiŵala zinthu msanga pamene nthendayo yangoyamba kumene, kapena kwa odwala ena, amapangitsa kuti matendawo asakule mwamsanga. Komabe, nkoyenera kusamala, chifukwa mankhwala ameneŵa samagwira ntchito kwa odwala onse, ndipo ena angakhale ovulaza. Mankhwala ena amagwiritsidwa ntchito kuthetsa mavuto ena amene amatsagana ndi AD, monga kupsinjika maganizo, nkhaŵa, ndi kusoŵa tulo. Pokaonana ndi dokotala wa wodwalayo, a m’banja lililonse angaganizire za mapindu ndi kuipa kwa mankhwalawo asanasankhe chochita.
[Bokosi patsamba 19]
Mmene Alendo Odzaona Wodwala Angathandizire
CHIFUKWA chakuti anthu odwala nthenda ya Alzheimer (AD) ubongo wawo sumagwira bwino ntchito, amalephera kukamba zochitika tsiku ndi tsiku. Komabe, kukamba za zinthu zakale mwina kungasiyane. Zinthu zakale angamazikumbukirebe ndithu, makamaka nthendayo itangoyamba kumene. Anthu ambiri odwala AD amakonda kuganiza zimene ankachita kale. Choncho apempheni kuti akusimbireni nkhani zawo zomwe amakonda, ngakhale ngati munazimvapo kambirimbiri. Mukamatero ndiye kuti mukumthandiza wodwalayo kupezabe chimwemwe. Panthaŵi imodzimodziyo, mukhala mukumpumuza munthu wodwazika matenda nthaŵi yonseyo. Kunena zoona, mutadzipereka kwa nthaŵi yaitali ndithu kuti musamale wodwala, mwina kwa tsiku lonse, mungapatse munthu wodwazika matenda nthaŵi zonse mpata waukulu wopuma.
[Bokosi patsamba 20]
Zoyenera Kuchita Wodwalayo Akamadzikodzera
Chikalata cha Incontinence chinati, ngakhale kuti kudzikodzera “kungaoneke ngati chinthu chochotsa ulemu, pali zinthu zimene mungachite kaya kuti muchepetse vuto lenilenilo kapena kulipirira.” Kumbukirani kuti wodwalayo si kuti angakhale womangodzikodzera nthaŵi zonse; mwina anangosokonezeka maganizo kapena kuti anachedwa kufika kuchimbudzi. Ndiponso, wodwalayo mwina wangokhala ndi vuto lochiritsika limene ndilo likumpangitsa kudzikodzera kwa kanthaŵi, choncho, mungafune kuonana ndi dokotala.
Mulimonse mmene zingakhalire, kudzikodzera kuli vuto lokhoza kuchita nalo mosavuta ngati wodwalayo angamavale zovala zosavuta kuvala ndi kuvula, ngakhalenso zovala zongosokedwa mwapadera. Zingathandizenso ngati mungamayale zotetezera pabedi ndi pamipando. Peŵani kuyabwitsa khungu lake mwakusamgoneka wodwalayo papulasitiki. Ndiponso, msambitseni wodwalayo ndi madzi ofunda ndi asopo, ndiyeno mpukuteni bwino musanamveke zovala. Chotsani zinthu zimene zingamlepheretse wodwalayo kufika msanga kuchimbudzi. Zingathandizenso kusiya nyali ili chiyakire usiku kuchitira kuti aziona poponda. Popeza kuti panthaŵi ino wodwalayo angakhale wopanda mphamvu, mutakhomera chogwirirapo pakhoma mungamthandize kuti asamaope kuloŵa m’chimbudzi.
A bungwe la Alzheimer’s Disease Society of London amati: “Ngati mungayambenso kumuuza nthabwala zingampepule maganizo.” Kodi wodwazika matenda angakwanitse bwanji zimenezo? Wina wozoloŵera kwambiri kusamala odwala anayankha kuti: “Kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, ndi kumlemekeza wodwalayo kudzamthandiza kudzisungira ulemu wake nthaŵi zonse, popanda kuopa kuchita manyazi.”
[Bokosi patsamba 21]
Kodi Wodwalayo Asamutsidwe?
NZACHISONI kuti pamene matenda a Alzheimer (AD) akupita patsogolo zingapangitse kuti wodwalayo asamutsidwe panyumba pawo nkumakakhala kunyumba ya wachibale kapena kunyumba yosungiramo okalamba. Komabe, musanaganize zosamutsa wodwala pamalo amene anazoloŵera, muyenera kulingalira mfundo zina zofunika.
Wodwalayo atangosamuka angasokonezeke maganizo kwambiri. Dr. Gerry Bennett anapereka chitsanzo china cha wodwala yemwe ankachokachoka panyumba ndipo namasochera nthaŵi zina. Komabe, ankakhalabe yekha. Ndiyeno, achibale ake anaganiza kuti amsamutsire panyumba ina yapafupi ndi yawo kotero kuti azikhoza kumyang’anira bwino.
A Bennett anafotokoza kuti: “Zachisoni zinali zakuti mayiyo analephera kuzoloŵera malo ake atsopanowo. . . . Chokhumudwitsa chinali chakuti sanazoloŵerepo pamalopo, ndipo anangokhala tsopano wofuna kuchitiridwa chilichonse chifukwa sankakhoza kudzichitira zinthu pamalo atsopanowo. Khichini inali yachilendo, ndipo sankatha kukumbukira njira yatsopano yopita kuchimbudzi ndipo anayamba kumadzikodzera. Ngakhale kuti achibale akewo ankafuna kuti azimsamalira pafupi, koma wodwalayo anangovutika m’malo mwake ndipo potsirizira anangokamtula kwa osamala anthu opanda chithandizo.”—Alzheimer’s Disease and Other Confusional States.
Komabe, bwanji ngati kukuoneka kuti palibenso njira ina kusiyapo yakumsamutsa wodwalayo kuti akasamalidwe ndi boma? Chimenecho sichapafupidi kuchita. Kunena zoona, ena amati chimenecho “nchimodzi mwa zinthu zovutitsa maganizo kwambiri” kwa odwazika matenda, kaŵirikaŵiri chimawapangitsa kuganiza kuti alephera ndipo amtaya mbale wawo.
Nesi wina wozoloŵera kwambiri kusamala odwala AD, anatero kuti “nzachibadwa kuganiza choncho, koma zimenezo siziyenera kumpangitsa munthu kudziimba mlandu mopambanitsa.” Chifukwa? Iye anayankha kuti: “Chinthu chofunika kwambiri ndicho kusamala [wodwalayo] ndikuona kuti akukhala bwino.” Madokotala Oliver ndi Bock akuvomereza kuti: “Chinthu chovuta zedi kuchita nchomwecho chodziŵa kuti mwayesayesa izi ndi izi ndipo mwathedwa nzeru komanso matendawo akulephereka kuwasamala panyumba.” Komabe, atalingalira zinthu zonse malinga ndi mkhalidwe wawo, odwazika matenda ena angaganize kuti “kumpereka wodwalayo kuti akasamalidwe ndi boma . . . kungamthandize kwambiri wodwalayo.”—Buku lakuti Coping With Alzheimer’s: A Caregiver’s Emotional Survival Guide.
[Chithunzi patsamba 18]
Thandizani wodwalayo kuzindikira zimene zikuchitika kunja ndipo khalani pafupi naye