Kodi Zovala Zimene Timavala Zilidi N’kanthu?
“SINDIKUDZIŴA kuti ndivale chiyani!” Kodi mumamva kaŵirikaŵiri munthu akukupemphani kum’thandiza pankhani yazovala? N’zoona, lerolino a masitolo ogulitsa zovala akufunitsitsa kukuthandizani—kapena kukusokonezani kwambiri—ndi zovala zawo zatsopano.
Masiku ano angakuuzeni kuti m’malo movala mwaulemu, muvale mosasamala, ndiye zimenezo zimapangitsanso kusankha zovala kukhala kovuta kwambiri. Ponena za kusintha kwa kavalidwe ka m’ma 90 muno, magazini ina yamafashoni inati: “N’zolimbikitsa kudziŵa kuti zovalazo si kokha kuti zimakupangitsani kumva kuti kuli bwino kuoneka ngati munthu wachikale, wosambuka, komanso zimakupangitsani kumva kuti n’zosangalatsa.”
Inde, zaka zaposachedwapa anthu osatsa malonda, anthu a m’mapologalamu a pa wailesi ya kanema, mabwenzi, ndiponso mtima wofuna kutchuka, zonsezo zapangitsa anthu makamaka achinyamata, kugula zovala zachilendo kwambiri. Ena a iwo amachita kuziba kuti aoneke ovala zabwino zamasitayelo.
Masitayelo ambiri otchuka a m’ma 90 muno, anachokera kwa anthu akale a maganizo osiyana ndi anzawo, monga gulu la anthu onyozera chikhalidwe chawo, a Kumadzulo, m’zaka za m’ma 60. Ukaona munthu wosunga ndevu, watsitsi lalitali losapesa, ndipo atavala zovala zanyankhalala, ndiye kuti ameneyo n’ngwosasamala mwambo wachikhalidwe cha anthu. Koma zovala zosonyeza kupanduka zinapangitsanso achinyamata ena kuyamba kutsanzira, mosonkhezeredwa ndi achinyamata anzawo.
Zovala zakhala chida chimene anthu ambiri amasonyezera umunthu wawo. Zovala, makamaka masikipa, akhala zikwangwani zotamanda mwakachetechete maseŵero ndi ngwazi zamaseŵero, zikwangwani zanthabwala, zosonyeza kuti munthu amanyansidwa ndi chakutichakuti, zosonyeza kuti munthuyo n’ngwolimba mtima, zosonyeza mawu a mwambo wachikhalidwe—kapena kupanda khalidwe—ndi zotsatsira malonda. Mwina zimawopsa kumene. Taganizani za mutu wina wankhani m’magazini yaposachedwapa ya Newsweek, wakuti: “Zovala Ndiyo Njira ya Achinyamata Yosonyezera Maganizo Awo Ankhanza.” Nkhaniyo inatchula mawu amene mnyamata wina wazaka 21 ananena za sikipa yake, kuti: “Ndimaivalira kuti ndiuze anthu mmene maganizo anga alili. Sindifuna munthu wina kundiuza zochita ndipo sindifuna munthu wina kundivutitsa iyayi.”
Zimene anthu amaonetsa pazifuŵa zawo ndi pamisana yawo zimasiyanasiyana malinga ndi munthuyo. Komabe zimangoonekeratu kuti aliyense amadzisonyeza kuti n’ngwagulu lakutilakuti kapena amasonyeza mzimu wa anthu ambiri opanduka, ndiponso maganizo akudzikonda, kuti n’ngwamphulupulu kapena n’ngwachiwawa. Katswiri wina wopanga masitayelo a zovala amaboola ziboo pazovala malinga ndi mmene makasitomala ake amuuzira. Iyeyo anati: “Makasitomalawo angasankhe ziboo zamfuti yaing’ono, zamfuti yaikulu, kapena ziboo zamfuti yachiwaya. Kwangokhala kuuza anthu maganizo ako kudzera m’zovala.”
Kodi Zovala Zimasonyezanji?
Jane de Teliga, woyang’anira dipatimenti yazovala zachionetsero, ku Powerhouse Museum, ku Sydney, Australia, anati: “Nthaŵi zonse zovala ndiyo njira yodzisonyezera wekha kuti uli wafuko lakutilakuti mwa anthu.” Anatinso: “Umasankha anthu afuko limene ukufuna kufanana nawo ndiyeno umavalanso ngati iwo omwewo.” Dr. Dianna Kenny, mphunzitsi wa psychology (sayansi yamaganizo) pa Yunivesite ya ku Sydney, anati, monga njira yozindikirira anthu, zovala n’zofunika monga mmene chilili chipembedzo, chuma, kulembedwa ntchito, kukhala ndi maganizo ofanana ndi anthu afuko lako, maphunziro, ndi adiresi yako. Malinga ndi kunena kwa magazini ya Jet, pali sukulu ina ku United States pomwe ana ochuluka ali azungu. “Tsopano atsikana Achizungu pasukulupo ankapota tsitsi, kuvala zovala zazikulu, ndi zamafashoni ena a ‘hip-hop.’ Ndiye atsikana achikuda oŵerengeka pasukulupo anayamba kuwada atsikana achizunguwo, akuti chifukwa mafashoni amenewo n’ngwoyenera anthu Akuda.”
Ngakhale pazochitika zina, monga pagulu la anthu oimba nyimbo, zimaoneka kuti nawonso amakonda kudzisonyeza kuti n’ngosiyana ndi anzawo. Magazini yotchedwa Maclean’s, inati: “Zovala zawo zimagwirizana ndi nyimbo zimene amakonda: okonda reggae amavala zovala zamitundu yoŵala ndi makapusi a ku Jamaica, pomwe okonda nyimbo zamtundu wa grunge rock, amakonda kuvala masokosi ochindikala ndiponso masikipa olukidwa mosasamala.” Ndiyeno, mosasamala kanthu kuti n’zamtundu wanji, zovala zanyankhalalazo, munthu akazivala amangooneka ngati wopanda kwawo ndiponso m’mphaŵi. Komabe, zovala zotchedwa za grunge, n’zokwera mtengo kwambiri ndithu.
Kodi Anthu Akulekeranji Kuvala Mwaulemu?
Wina wolemba za m’nyuzipepala, Woody Hochswender, anati: “Chilichonse changokhala chosiyana ndi zimene ungaganizire. Kale, zovala za amuna zomwe zinkasokedwa mwaulemu, pano zangokhala zosalemekezeka konse . . . Chovala chilichonse chimangokhala nyankhalala ngati kuti wochivalayo wabwereka.” Komabe, zovala zoterozo zimasonyeza kuti munthu wozivalayo n’ngwosadzisamala. Kapena zingasonyeze kuti munthuyo n’ngwosadzipatsa ulemu kapena wosadziŵa kupatsa ena ulemu.
M’magazini ina yotchedwa Perceptual and Motor Skills, munatuluka nkhani ina yonena za mmene ana a sukulu amaonera aphunzitsi kuti, “ngakhale kuti mphunzitsi wovala talauza la jeans tinkamuona ngati wotisangalatsa m’kalasi, zonena zake sitinkazisamala kwenikweni ndipo kaŵirikaŵiri tinkam’tchula ameneyoyo monga wosadziŵa kanthu kalikonse.” Magazini yomweyonso inati, “mphunzitsi wachikazi wovala talauza la jeans ankaoneka ngati woseketsa, wosavuta kulankhula naye, komabe wopanda nzeru kwenikweni, wosalemekezeka, wosaonekanso ngati mphunzitsi, ndiponso wosayanjika.”
Komanso, anthu ogwira ntchito m’makampani nawonso ali ndi njira yosonyezera maganizo awo mwa zovala zawo: kavalidwe kokopa chidwi cha anzawo pantchito. Zaka zaposachedwapa, akazi ambiri akhala akufuna kupeza mipando yapamwamba pantchito. Marie, woyang’anira kampani ina yofalitsa mabuku, anati: “Ine ndimavala moti munthu sangalephere kundicheukira.” Natinso, “ndimafuna kutchuka. Ndimafuna kudzisonyeza monga kanthu kena kochititsa chidwi.” Marie sabisa zoti iye amadziŵerengera kwambiri.
Zovala zamafashoni otchuka sizilephera kupezekanso ngakhale m’matchalitchi. Ena amene amakonda mafashoni amagwiritsa ntchito tchalitchi chawo kusonyezera anzawo zovala zawo zatsopano. Komabe, lerolino, mutati muyang’ane akuluakulu achipembedzo ataimirira kutsogolo m’tchalitchi, iwowo atavala mikanjo yawo yosesa pansi ija, koma amakhala akuyang’ana mpingo wovala matalauza a jeans ndi nsapato kapena zovala za pamaseŵera.
Kodi Anthu Amadzivutiranji Kudzisiyanitsa ndi Ena?
Akatswiri a zamaganizo amati, makamaka kwa achinyamata, zovala zawo ndiyo njira yodzisonyezera kuti n’ngosiyana ndi ena, moti zimawapangitsa kuzindikiridwa ndi anthu. Amati zovala zawozo ndiyo “njira imene achinyamata amadzisonyezera okha monga chinthu chopangitsa anzawo kuwasirira.” Zimakhala ngati akunena kuti: “Ndikuona kuti ukuganiza kwambiri za ine monganso ndimaganizira za ndekha.”—American Journal of Orthopsychiatry.
Kutamanda kwambiri anthu ndi kunyalanyaza Mulungu monga wosafunika nakonso kumachirikiza maganizo (omwe kaŵirikaŵiri amafalitsidwa ndi anthu amalonda) akuti iweyo, munthuwe, ndiwe wopambana m’chilengedwe chonse. Koma vuto n’lakuti ‘anthu ofunika kwambiriwo’ tsopano akukwana pafupifupi mabiliyoni asanu ndi imodzi. Anthu ambirimbiri a m’zipembedzo za Dziko Lachikristu nawonso amakonda chuma, amalimbikira kupeza “moyo wabwino tsopanolino.” (Yerekezerani ndi 2 Timoteo 3:1-5.) Komanso pali vuto lina lakuti chikondi chenicheni chikutha m’banja, ndiye n’chifukwa chake sizikudabwitsa kuti anthu ambiri, makamaka achinyamata, akumenyera nkhondo kudzisonyeza kuti n’ngodziimira paokha kuti adzizimva kuti n’ngosungika.
Komabe, anthu amene amadera nkhaŵa za mmene Mulungu amaonera kavalidwe kawo, salephera kudzifunsa kuti: Kodi ndingalolere mpaka pati kuvala nawo zovala zosinthasintha mafashoni? Kodi ndingadziŵe bwanji ngati zovala zanga zili zaulemu? Kodi zimapangitsa anthu kundikayikira kapena kuganiza kuti ndili ndi maganizo olakwika?
Kodi Ndavala Bwino?
Zovala zathu n’chinthu chodzisankhira. Tonsefe timakonda zinthu zosiyanasiyana, ndipo timapeza ndalama mosiyanasiyana. Ndipo miyambo imasiyana malo ndi malo, dziko ndi dziko, ndiponso madera ndi madera. Koma mulimonse mmene zingakhalire kwa inuyo, kumbukirani mfundo iyi: “Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chiri ndi mphindi yake.” (Mlaliki 3:1) Mwa mawu ena, valani moyenerana ndi pamalo amene muli. Komanso, ‘yendani modzichepetsa ndi Mulungu wanu.’—Mika 6:8.
Zimenezi sizikutanthauza kuvala mopambanitsa, koma ‘kuvala moyenera,’ ndi ‘mwamanyazi,’ [“mwaulemu,” NW]. (1 Timoteo 2:9, 10) Kaŵirikaŵiri, zimenezi zimangotanthauza kudziletsa, monganso magazini yotchedwa Working Woman inanenera kuti umenewo ndiwo mkhalidwe wabwino ndi wolemekezeka. Ingokhalani ndi kalamulo kanu kakuti zovala zanu zisamacheukitse ena. Magazini ya Working Woman inati: “Valani . . . mwanjira yoti anthu asangoona zovala zanu zokhazo, komanso aone ulemu wanu monga munthu.”
Magazini ya Perceptual and Motor Skills inati: “Mabuku ambiri onena za mmene zovala zimalankhulira popanda mawu pofotokoza maganizo a munthu, amasonyeza kuti zovala ndizo chizindikiro chimene munthu amadziŵira maganizo a ena.” Momwemonso, mkazi wina wazaka za m’ma 40, yemwe kale ankakonda kuchititsa ena kaso ndi zovala zake, anati: “Zinkandiputira mavuto aakulu kwambiri chifukwa anthu sankasiyanitsa kuti kaya ndili pantchito kapena ndaweruka. Nthaŵi zonse anthu omwe ndinkachita nawo bizinesi ankakonda kundipempha kuti tikadye kulesitilanti.” Akauntanti wina wachikazi, posimba mmene zimakhalira ngati ena avala zamasitayelo ena, anati: “Ndimaona mmene amuna amachitira ndi akazi omwe amavala mosadzilemekeza, kapena kuvala mofanana kwambiri ndi amuna. Amenewo amaonedwa ngati akazi ovuta, omwe angathe ngakhale kulimbana ndi amuna, moti pankhani zabizinesi, amuna sawasamala kwenikweni akazi oterowo.”
Mtsikana wina wotchedwa Jeffie anaona kuti anali kukayikitsa anthu pamene anameta tsitsi lake mwa sitayelo yachilendo. Anati: “Ndinkangoti ‘ndi sitayelo ina basi.’ Koma anthu ankangondifunsa kuti, ‘Kodi ndiwedi wa Mboni iweyo?’ ndiye zinkandinyazitsa.” Jeffie anafunikira kudzifunsa mafunso amphamvu. Kodi si chonchodi kuti si pakamwa pathu pokha komanso kapesedwe kanthu ndiponso zovala zathu ‘zimalankhula mwa kusefukira kwa mtima’? (Mateyu 12:34) Kodi zovala zanu zimavumbulanji—mtima wofuna kutamanditsa Mlengi kapena kudzitamanda nokha?
Dzivekeni Chovala “Choyenera”
Taganiziraninso za mmene inuyo mumamvera mukavala zovala zanu. Kuvala mopambanitsa kungakupangitseni kudzitukumula, zovala zanyankhalala zingakupangitseni kumva ngati wosanunkha kanthu, ndipo masikipa okhala ndi chithunzi cha kanema imene mumakonda kapena ngwazi ina yamaseŵero, angakusonkhezereni kuyamba kulambira ngwazi—mafano. N’zoonadi, zovala zanu zimalankhula ndi ena—zimawauza za inuyo.
Kodi zovala zanu zimati bwanji ngati mwavala kuti anthu akuyamikireni kapena ngati mwavalira kuchititsa anthu kaso? Kodi mukukulitsa mkhalidwe waumunthu womwe kwenikweni munayenera kukhala mukuyesetsa kuusiya? Makamaka kodi mukufuna kukopa chidwi cha yani? Uphungu wa pa Aroma 12:3 ungatithandize kusiya mtima wakudziŵerengera kwambiri, kunyada, ndi maganizo oipa. Pa lemba limenelo mtumwi Paulo akutilangiza kuti ‘tisadziyese koposa kumene tiyenera kudziyesa; koma tiganize modziletsa tokha.’ Kuganiza ‘modziletsa tokha’ kumatanthauza kukhala wanzeru.
Mfundo imeneyi n’njofunika makamaka kwa anthu amaudindo, anthu odaliridwa. Chitsanzo chawo chimapangitsa ena kuvalanso mwaulemu. Mmenedi ziyenera kukhala, ndiko kuti anthu omwe akukalimira maudindo autumiki mumpingo wachikristu, limodzi ndi akazi awo achikristu, nawonso ayenera kuvala ndi kupesa mwaulemu. Sitingafune kufanana ndi munthu wina amene Yesu anatchula m’fanizo lake laphwando laukwati, kuti: “Mfumuyo mmene inadza kuwaona akudyawo, anapenya momwemo munthu wosavala chovala chaukwati.” Itaona kuti munthuyo analibe chifukwa chabwino chovalira zovala zopanda ulemu ngati zakezo, “mfumu inati kwa atumiki, ‘mumange iye manja ndi miyendo, mum’ponye kumdima wakunja.’”—Mateyu 22:11-13.
Choncho, n’kofunika kuti makolo aziphunzitsa ana awo mwa mawu ndi mwachitsanzo kuti anawo azidziŵa kuvala mwaulemu. Zimenezi zingatanthauze kuti makolo afunikira kunena mawu motsimikiza polankhula ndi mwana wamwamuna kapena wamkazi. Koma zimalimbikitsatu kwambiri kungomva munthu akutiyamikira kuti ife limodzi ndi ana athu tili ndi khalidwe labwino ndi kutinso timavala mwaulemu!
Inde, atumiki a Yehova amasuka, salinso amtima wonyada, okonda zovala zandalama zambiri, salinso odzikonda. Amatsogozedwa ndi mapulinsipulo a Mulungu, osati a dziko. (1 Akorinto 2:12) Ngati mumayendera mapulinsipulo amenewa, kusankha zovala sikungakuvuteni. Ndiponso, monga mmene ilili pikishafuremu yabwino, zovala zanu zidzasonyeza bwino umunthu wanu, m’malo mokhumudwitsa nazo ena. Makamaka ngati mumayesetsa kukhala ngati Mulungu, m’pamenenso mudzakongola kwambiri mwauzimu kuposa mmene chovala chilichonse chingakukongoletsereni.