Moyo Wabwino Kwambiri Ngakhale Alibe Chiŵalo China
PAMENE Tom Whittaker anafika kunsonga ya Phiri la Everest, nyuzipepala ina inati: “Wokwera mapiri uja wafikanso kunsonga.” Mmbuyomu, ambiri anafikapo kunsonga ya phiri lalitali limeneli, koma Tom Whittaker anali munthu woyamba wopanda chiŵalo china, kufika kunsongayo! Whittaker anaduka phazi pangozi ya pamsewu. Komabe, ataikidwa phazi lopanga, Whittaker anapitirizabe kukwera mapiri. Ziŵalo zopanga zikuthandiza anthu ena ambirimbiri oduka ziŵalo kukhalabe bwino monga munthu wina aliyense. Tingoti masiku ano si chachilendo kuona anthu oduka chiŵalo akuthamanga, akuseŵera mpira, kapena akupalasa njinga.
Kale, miyendo ndi manja opanga, ankakhala amatabwa, olumikizidwa ndi chitsulo. Koma anayamba kukonza miyendo ndi manja abwino nkhondo zitayamba kupundula anthu ambirimbiri. N’chifukwa chake n’zosadabwitsa kuti amene anayamba kupanga ziŵalo zoikira anthu anali dokotala wina wa asilikali wa ku France, yemwe anakhalako m’zaka za zana la 16, wotchedwa Ambroise Paré. Lero, ziŵalo zochita kuikira zamakono zimagwiritsira ntchito mphamvu ya hydraulic, mfundo zam’maondo zopangidwa mwaluso lapamwamba, mapazi opindika mosavuta opangidwa ndi carbon, silicone, pulasitiki, ndi zipangizo zina za luso lapamwamba kwambiri zimene zimatheketsa anthu kuyenda mwachibadwa ndi mosavutikira ngakhale pang’ono—chinthu chimene sichinaganizidwepo ndi kalelonse. Sayansi yatsogola kwambiri moti anthu akugwiritsira ntchito mikono ndi manja mofanana kwambiri ndi ziŵalo zachibadwa. Nazo ziŵalo zopanga zasintha kaonekedwe. Ziŵalo zimene akupanga makono zili ndi zala za kumanja ndi za kumapazi, ndipo zina zimaoneka ngati kuti zili ndi mitsempha. Munthu wina wamkazi, wotsatsa malonda a zovala mwa kuzivala, anadulidwa mwendo chifukwa cha kansa, koma anaikidwa mwendo wopanga umene unkangooneka ngati weniweni moti sanaleke ntchito yake.
Kuona Bwino Vuto Lanu N’kofunika
Komabe, katswiri wina wa zamaganizo, Ellen Winchell, anachenjeza kuti: “Ngati wakumana ndi tsoka longa la kudulidwa chiŵalo, ndiye kuti vutolo likhudza moyo wako wonse—thupi, maganizo, ndi mkhalidwe wako wauzimu.” Taganizani za William, amene anadulidwa mwendo chifukwa choti magazi anasiya kuyenda m’mitsempha yake pamene anavulala. Iyeyo anati: “Njira ina yabwino kwambiri yopiririra vuto lililonse m’moyo ndiyo kuona vutolo bwino. Sindifuna kuona kupunduka kwanga monga chondilepheretsa kuchita zinthu. Koma chichitireni ngoziyo, m’malo modzimvera chisoni ndikalephera penapake, ndimangodziona kuti ndingachitebe zinthu monga wina aliyense.” Ellen Winchell, yemwenso anadulidwa mwendo, anavomereza kuti, anthu amene salola kumadzimvera chisoni, amazoloŵera msanga kukhala opanda chiŵalo china kuposa anthu amene amadandauladandaula. Monga mmene Baibulo limanenera, “Mzimu wosekerera uchiritsa bwino.”—Miyambo 17:22.
Atolankhani a Galamukani! analankhula ndi Akristu angapo amene azoloŵera mosavuta kukhala opanda chiŵalo chinachake. Ambiri mwa iwo ananena kuti anthu odulidwa chiŵalo sayenera kumadziona ngati osiyana ndi anzawo kapena sayenera kupeŵa kulankhula za kupunduka kwawo. Dell anati: “Bwenzi zikumandinyansa kwambiri ngati anthu angamaganize kuti imeneyi ndi nkhani yosayenera kutchulidwa. Kwa ineyo, zimenezo n’zosoŵetsa mtendere aliyense.” Akatswiri ena amanena kuti ngati mulibe dzanja lamanja, ndiye mnzanu wakuitanani kuti mudzapatse moni munthu wina, yambani inuyo kum’patsa moni ndi dzanja lanu lamanzere. Ngati munthu aliyense atakufunsani za chiŵalo chanu chopangacho, m’fotokozereni. Kusachita manyazi kumam’pangitsa munthu winayonso kumasuka. Nthaŵi zambiri, mumangoona kuti mwayamba kukamba nkhani zina.
Pali “mphindi yakuseka.” (Mlaliki 3:4b) Mayi wina amene anaduka dzanja anati: ‘Chimwemwe chanu cha masiku onse chisakuthereni! Tiyenera kumakumbukira nthaŵi zonse kuti nthaŵi zambiri mmene timadzionera tokha ndi mmenenso anthu onse amationera.’
“Mphindi Yakugwetsa Misozi”
Dell, ataduka mwendo wamanzere, poyamba anati, “Basi, zonse zathera pano. Moyo wanga watha.” Florindo ndi Floriano, anadulidwa ziŵalo ndi bomba lokwiriridwa pansi ku Angola. Florindo ananena kuti analira masiku atatu, usana ndi usiku. Floriano nayenso zinam’tengera nthaŵi kuiŵala chisoni chake. Iye analemba kuti: “Ndinali ndi zaka 25 basi. Ine munthu woti ndinkatha kuchita chilichonse, koma tsiku limodzi lokha kulephera ngakhale kuimirira. Ndinavutika maganizo kwambiri ndipo ndinakhumudwa kwambiri.”
Pali “mphindi yakugwetsa misozi.” (Mlaliki 3:4a) Ndikwachibadwa kumva chisoni pameme wataya chinthu china chofunika. (Yerekezerani ndi Oweruza 11:37; Mlaliki 7:1-3.) Ellen Winchell analemba kuti: “Kuti chisoni chako chithe uyenera kupirira nacho.” Kulankhula za chisoni chako ndi munthu womvetsera mwachifundo n’kothandizanso. (Miyambo 12:25) Komabe chisonicho sichikhala mpaka kalekale. Pambuyo pa ngozi imene inawapangitsa kudulidwa chiŵalo, anthu ena amasinthasintha, pena akhale aukali, pena akhale achifundo, pena amakhala ndi nkhaŵa, ndipo pena amadzipatula. Komabe, nthaŵi zambiri zonsezi zimadzatha. Ngati sizitha, ndiye kuti munthuyo akudwala m’maganizo—tsopano pamenepo mpofuna kupita kwa dokotala weniweni. A m’banja la munthuyo limodzi ndi mabwenzi ake ayenera kuonetsetsa ngati pali zizindikiro zosonyeza kuti mnzawoyo akufunadi chithandizo.a
W. Mitchell, amene anafa miyendo yonse iŵiri analemba kuti: “Aliyense amafuna kukhala ndi anthu amene amaganizira anzawo. Munthu angapirire pafupifupi chilichonse ngati ali ndi mabwenzi ndi a m’banja ogwirizana, pomwe ngati akulimbana ndi mavuto a m’moyo ali yekhayekha, ngakhale kavuto kakang’ononong’ono kangam’fooketse. Ndipo ubwenzi sungoyambika wokha, koma muyenera kuuyamba ndi kuukulitsa, mukapanda kutero, umatha.”—Yerekezerani ndi Miyambo 18:24.
Kukhala ndi Moyo Wabwino Popanda Chiŵalo China
Anthu ambiri opanda ziŵalo zina akukhalabe moyo wabwino ngakhale ali opunduka. Mwachitsanzo, Russell anabadwa ali ndi nchafu yokha ya mwendo wake wakumanzere. Pano ali ndi zaka 78, koma adakachitabe maseŵera olimbitsa thupi ndipo akukhala monga mwanthaŵi zonse, ngakhale kuti tsopano akuyenda ndi ndodo. Russell n’ngwachimwemwe mwachibadwa, ndipo amavomereza kuti dzina lake limene anthu anangom’patsa n’lakuti Chimwemwe.
Douglas, amene anaduka mwendo pa Nkhondo Yadziko II, amayenda ndi chiŵalo chamakono chochita kupanga. Iyeyo ndi mmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo wakhala akuchita upainiya wokhazikika, kulalikira uthenga nthaŵi zonse, kwa zaka zisanu ndi chimodzi. Kodi mukum’kumbukira Dell, uja amene anaganiza kuti moyo wake unali utatha pamene anaduka mwendo? Nayenso amakhala bwinobwino, pano ndi mpainiya, ndipo amadzisamala yekha.
Komabe, kodi anthu amene anaduka ziŵalo okhala m’mayiko ankhondo amakhala bwanji? A bungwe la World Health Organization anati: “Kunena zoona, lero, anthu opunduka oŵerengeka chabe ndiwo amathandizidwa.” Ambiri amadalira mitengo ndi ndodo za opunduka kuti ayende. Komabe, nthaŵi zina pamakhala chithandizo. Florindo ndi Floriano, amene anavulazidwa ndi bomba lokwiriridwa pansi ku Angola, anathandizidwa ndi bungwe la International Red Cross limodzi ndi boma la Switzerland. Floriano ndi mtumiki wotumikira wa mumpingo wa kwawo wa Mboni za Yehova, ndipo Florindo ndi mkulu ndiponso mlaliki wa nthaŵi zonse.
Bungwe lina losamala anthu opunduka linafotokoza bwino—ponena kuti: “Anthu okha amene angatchedwe opunduka ndiwo aja amene ataya chiyembekezo!” N’zosangalatsa kuti Baibulo likuthandiza kwambiri pakupatsa anthu opunduka chiyembekezo. Dell anati, “Pamene ndinali kuchira ndinkaphunzira choonadi cha m’Baibulo ndipo ndinathandizika kwambiri.” Russell naye ananena zonga zomwezo, kuti: “Chiyembekezo changa chopezeka m’Baibulo chimandithandiza nthaŵi zonse kupirira mavuto.” Kodi Baibulo limapereka chiyembekezo chotani kwa opunduka?
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Mmene Mungathandizire Ochita Tondovi Kupezanso Chimwemwe,” mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 1990.
[Bokosi patsamba 8]
Ululu Wosaoneka
Kuganizira za chiŵalo chimene palibe, ndiko kuti munthu amamva ngati kuti chiŵalo chimene chinadulidwacho chidakalipobe. Aliyense wodulidwa chiŵalo amamva choncho pambuyo pochitidwa opaleshoni, ndipo zimakhala ngati zenizeni kotero kuti kabuku kena kolembedwera anthu odulidwa ziŵalo kanati: “Muzisamala kwambiri pochoka pa bedi kapena ponyamuka pa mpando musanavale ziŵalo zanu zopanga, chifukwa mudzamva ngati kuti muli nayo miyendo yanu yonse. Nthaŵi zonse muziyang’ana pansi kuti mukumbukire kuti phazi lina mulibe.” Wina amene anaduka miyendo yonse anafuna kuti anyamuke akapatse moni dokotala wake, koma anagwa pansi!
Vuto lina ndi kumva ululu pamene panali chiŵalo chodulidwacho. Umenewu ndi ululu weniweni womwe umamveka pa chiŵalo chimene chinadulidwacho. Ukulu wa ululuwo, ndi kapwetekedwe kake ndi utali wa nthaŵi imene ululuwo umamveka, zimasiyana kwa munthu aliyense. Koma ubwino wake n’ngwakuti kuganizira za chiŵalocho ndi kumva ululu pamene panali chiŵalo chimene chinadulidwacho zonse zimadzatha.
[Chithunzi patsamba 6]
Ziŵalo zopanga zamakono zimathandiza anthu ambiri opunduka kukhala ndi moyo wabwino kwambiri
[Mawu a Chithunzi]
Photo courtesy of RGP Prosthetics
[Chithunzi patsamba 7]
Kulira n’kwachibadwa ngati munthu wataya chinthu china chofunika
[Chithunzi patsamba 8]
Anthu ambiri opunduka ali ndi moyo wabwino kwambiri