‘Kodi Ntchito Yanu Imapindulitsa Bwanji Anthu?’
MTOLANKHANI wina wa ku India wotchedwa Chandrakant Patel, ndiye anafunsa funso limeneli, kufunsa wina wa palikulu ladziko lonse la Mboni za Yehova, ku Brooklyn, New York. Patel anali atafikako kuti akaone malowo, ndiye anachita chidwi kwabasi ndi zimene anaona kumeneko ndi zimenenso anamva, moti atabwerera kwawo anakalemba nkhani ina m’nyuzipepala yachigujarati.
Patel, posiyanitsa zikhulupiriro za Mboni za Yehova ndi za matchalitchi ena a ku India, analemba kuti Mboni za Yehova zimakhulupirira Mulungu wamphamvu yonse, Yehova, sizikhulupirira chiphunzitso cha Utatu chimene matchalitchi ambiri amaphunzitsa, ndipo Mboni sizigwiritsira ntchito mafano polambira. Analembanso kuti Mboni za Yehova zili ndi makhalidwe abwino kwambiri chifukwa zimatsatira ndithu njira zopambana zochitira zinthu monga mmene Baibulo limanenera, sachita chigololo, sataya mimba, sadana ndi anzawo kapena kuwapha. Anati Mboni ndi anthu okonda mtendere, n’ngoleza mtima, ndipo ndi anthu akhama, komanso n’ngopanda mantha, ndiponso n’ngachangu polengeza uthenga wa Baibulo kwa ena.
Kodi mtolankhani wa ku Indiayo anayankhidwa bwanji funso lake lakuti, ‘Kodi ntchito yanu imapindulitsa bwanji anthu?’ Analemba kuti: ‘Yankho linali lakuti kuphunzitsa anthu Baibulo kumapindulitsa pa zonse m’moyo wa munthu.’ Patel kwenikweni anafuna kudziŵa kanthu kena pankhani ya kusamalira thanzi ndi kupeza ntchito yolipidwa. Patel, pofotokoza zina mwa zimene anauzidwazo, anati: ‘Ngati munthu alabadira uphungu wa m’Malemba wakupeŵa zinthu zovulaza monga fodya ndi mankhwala osokoneza ubongo, namakhala ndi moyo waukhondo, ameneyo angapeŵe matenda osiyanasiyana. Ndipo anthu akhama, a moyo waukhondo, okhulupirika ndiwo amene amafulumira kupeza ntchito yolembedwa. Kuwonjezera apo, anthu akamathetsa mwachifundo ndi mwachikondi nkhani zawo zimene amalakwirana, onse amakhala pamtendere. Choncho, kuphunzitsa anthu zimene Baibulo limanena kumapindulitsa onse.’
Mtolankhani ameneyu atafika kulikulu la Mboni za Yehova anaonadi anthu akuchita zimene Baibulo limaphunzitsa. Nkhani imene analembayo inatamanda antchito odzifunira ogwira palikulu la ntchito yauzimuwo, kuti n’ngachimwemwe ndipo n’ngaukhondo. Inunso mungapindule ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Mboni za Yehova zingakuthandizeni mmene mungapindulire.
Ngati mungafune kudziŵa zambiri kapena kuti wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere, lemberani ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 2.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Newspaper background: Courtesy Naya Padkar, Gujarati Daily published from Anand, India