Akazi Anachita Mbali Yaikulu
MBALI yofunika imene akazi achikristu anagwira pomanga nthambi ya Mboni za Yehova ku Zimbabwe inagogomezeredwa m’pologalamu yopatulira, imene inachitika pa December 12, 1998. Mkati mwa zaka zinayi zantchito yomanga imeneyi, antchito odzifunira ochokera m’mayiko osiyanasiyana—kuphatikizapo ambiri ochokera m’Zimbabwe—anapereka nthaŵi yawo, mphamvu zawo, maluso awo, ndi katundu wawo kuti amange nyumba yokongola imene mukuiona pa chithunzipayi.
Kutsogoloko mukuona nyumba zogonamo zisanu ndi imodzi zaukulu wofanana. Nyumba yaikuluyo, imene ili nazo pafupi kwambiriyo, muli chipinda chodyera, khichini, ndi kochapila zovala. Nyumba zogonamozo zili ndi zipinda 61, ndipo chipinda chodyera n’chokwana anthu pafupifupi 200. Ali kutsogoloko, chakumanzereku, ndi maofesi. Ali pakatipo ndi malo olandirira alendo, ndipo ili chakumanjayo ndi nyumba yosungiramo katundu, imene munachitikira pologalamu yopatulira.
Nthambi yokongola imeneyi ku Zimbabwe, ku mwera kwa Africa, ndi imodzi chabe mwa ntchito zina zambiri zomanga zimene zatsirizidwa kuyambira pamene Mboni za Yehova zinayamba pologalamu yomanga yapadziko lonse mu November 1985. Galamukani! yachingelezi ya August 22, 1991, inafotokoza nkhani imeneyi pamutu wakuti “Chinthu China Chatsopano m’Kumanga kwa Padziko Lonse.”
Ponenapo za mbali ya akazi m’pologalamuyo, Galamukani! ameneyo anati: “Ambiri anaphunzitsidwa kumangirira pamodzi zitsulo pogwiritsa ntchito mawaya, kuika zinthu mwaluso ndi kumata matayilosi, komanso kusalaza zinthu ndi kupenta. Ena anali kusamalira zinthu zofunika panyumba. Mwakutero onse anathandiza mwanjira yabwino kugwira ntchito ya chimango padziko lonse.”
Posachedwapa ku Zimbabwe papologalamu yopatulira, George Evans ndi James Paulson, amene anali oyang’anira ntchito yomanga, anayerekezera mbali imene akazi anali nayo pomanga nthambi ya Zimbabwe ndi mbali imene akazi anali nayo pomanga chihema chakale cha Aisrayeli. “Anadza, aliyense wofulumidwa mtima,” limatero Baibulo ponena za Aisrayeli, ‘ndipo anadza amuna ndi akazi.’—Eksodo 35:21,22.
Mwakugwiritsa ntchito nkhani ya Baibulo imeneyi, Mbale Evans ndi Paulson anagogomezera kufunika kwa thandizo la akazi. Anagwira mawu a Baibulo akuti: “Akazi onse a mtima waluso anapota ndi manja awo, . . . akazi onse amene mitima yawo inawafulumiza ndi nzeru.” Ndithudi, akazi anali pakati pa anthu amene anadzipereka mofunitsitsa kugwira ntchito. “Amuna ndi akazi onse a ana a Israyeli amene mitima yawo inawafunitsa eni kubwera nazo za ku ntchito yonse imene Yehova anauza ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera nacho.”—Eksodo 35:25, 26, 29, NW.
Ponenapo za ntchito yomanga nthambi ku Zimbabwe, woyang’anira ntchito yomanga ananena kuti: ‘Akazi anagwira ntchito iliyonse imene amuna anagwira.’ Izi zinaphatikizapo kumangirira zitsulo ndi kuyendetsa zinthu zolemera. Mbale Paulson anati akazi ankatsuka magalimoto onyamula ndikusakaniza simenti ndi mchenga, komanso zinthu zina zolemera, kuti zikhale zopanda paliponse pakuda, zimene anati amuna sakonda kuchita.
Ndithudi, tikuthokoza akazi onse amene agwirako ntchito pamodzi ndi amuna yomanga maofesi anthambi ndi Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova padziko lonse!
[Chithunzi patsamba 18]
Nthambi ya Zimbabwe