Lingaliro la Baibulo
Kodi Kunyada N’kulakwa?
PALI mwambi wina umene umati kunyada ndi tchimo lalikulu kwambiri mwa machimo akuluakulu asanu ndi aŵiri. Komabe, anthu ambiri lerolino amakhulupirira kuti lingaliro limeneli n’lopandiratu ntchito. Kumayambiriro kwa zaka za zana la 21 lino, kunyada kukuonedwa ngati mkhalidwe wofunika, osati tchimo.
Komabe, Baibulo likamanena za kunyada, nthaŵi zambiri kumakhala ndi tanthauzo loipa. Buku la Baibulo la Miyambo lokha lili ndi mawu ambiri oletsa kunyada. Mwachitsanzo, Miyambo 8:13 imati: “Kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m’kamwa mokhota, ndizida.” Miyambo 16:5 imati: “Yense wonyada mtima anyansa Yehova.” Ndipo vesi 18 limachenjeza kuti: “Kunyada kutsogolera kuonongeka; Mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.”
Kunyada Koyenera
Kunyada kumene kumaletsedwa m’Baibulo kumatanthauza kudzitukumula mopambanitsa, kudziona kukhala wapamwamba chifukwa cha maluso kukongola, kulemera, maphunziro, malo antchito, ndi zina zotero. Kungawonekere ngati munthu ali ndi mkhalidwe wonyoza anthu ena, wodzitamandira, wachipongwe, ndi wodzikuza. Kudziganizira kwambiri kungam’chititse munthu kuti azikana kulandira uphungu wofunika; kukana kuvomereza zolakwa ndi kupepesa, kusintha maganizo mosaganizira za pangano, ndi kudzichotsera ulemu; kapena kufulumira kukwiya ndi zinthu zazing’ono zimene winawake wachita kapena wanena.
Onyada amafuna kuti nthaŵi zonse zinthu zizichitika mmene iwo akufunira apo ayi zisachitike n’komwe. Sikovuta kuona kuti khalidwe ngati limeneli nthaŵi zambiri limadzetsa mikangano yosiyanasiyana. Kudzikweza chifukwa cha fuko kapena mtundu kwapangitsa nkhondo zosaŵerengeka ndi kukhetsa mwazi. Malinga ndi kunena kwa Baibulo, kunyada ndilo vuto limene linapangitsa mwana wauzimu wa Mulungu kuti apanduke, ndipo anadzipanga yekha kukhala Satana Mdyerekezi. Ponena za ziyeneretso za akulu achikristu, Paulo analangiza kuti: “Asakhale wophunza [“wotembenuka kumene,” NW], kuti podzitukumula ungam’gwere mlandu wa Mdyerekezi.” (1 Timoteo 3:6; Yerekezerani ndi Ezekieli 28:13-17.) Ngati izi ndizo zotsatira zake za kunyada, sizodabwitsa kuti Mulungu amadana nako. Komabe, mungafunse kuti, ‘Kodi palibe nthaŵi imene kunyada kungakhale koyenera?’
Kodi Pali Kunyada Koyenera?
M’Malemba Achigiriki achikristu, verebu lakuti kau·khaʹo·mai, lotanthauza “kunyadira, kukondwera, kudzitamandira,” limagwiritsidwa ntchito ponse paŵiri m’lingaliro loipa ndi labwino. Mwachitsanzo, Paulo akuti, ndipo ‘tikondwere m’chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu.’ Komanso akulangiza kuti: “Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye.” (Aroma 5:2; 2 Akorinto 10:17) Izi zikutanthauza kunyadira Yehova monga Mulungu wathu, kumene kungatipangitse kukondwerera dzina ndi mbiri yake yabwino.
Mwachitsanzo: Kodi n’kulakwa kutchinjiriza dzina labwino pamene ena akulinenera zoipa? Ndithudi sikulakwa. Ngati anthu akunena zoipa za anthu am’banja mwanu kapena za ena amene mumawakonda ndi kuwalemekeza, kodi simungakwiye komanso kufuna kuti muwaikire kumbuyo? “Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri,” limatero Baibulo. (Miyambo 22:1) Nthaŵi ina yake, Mulungu Wamphamvuyonse anati kwa Farao wa ku Aigupto wonyadayo: “Chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi.” (Eksodo 9:16) Choncho Mulungu amakondwera ndi dzina lake komanso mbiri yake yabwino ndipo ali chire kutero. Ifenso tingakonde kutchinjiriza dzina lathu ndi mbiri yathu yabwino koma osati mosonkhezeredwa ndi kudzitamandira ndi kunyada.—Miyambo 16:18.
Ulemu n’gwofunika pa mayanjano alionse abwino. Mayanjano ndi mabizinesi athu samayenda bwino ngati sitimadalirana ndi anzathu. Mofananamo, ntchito kapena bizinesi yogwirira pamodzi ingasokonezeke ngati m’modzi achita zinthu zodzinyozetsa yekha kapena anzake. Pofuna kukwaniritsa zolinga zilizonse zimene zingakhalepo, payenera kukhala mbiri yabwino. Ichi n’chifukwa chimodzi chimene oyang’anira mu mpingo wachikristu ayenera kukhala ndi “mbiri yabwino” kwa akunja. (1 Timoteo 3:7, NW) Kukhumba kwawo mbiri yabwino sikumasonkhezeredwa, ndi kunyada podzitukumula, koma ndi cholinga chofuna kuimira Mulungu mwanjira yoyenera ndi yaulemu. Ndiponso, mtumiki angakhulupiridwe bwanji ngati ali ndi mbiri yoipa kwa akunja?
Bwanji nanga za kunyada chifukwa chakuti zinthu zimene tikuchita zikutiyendera bwino? Mwachitsanzo, lingalirani, chisangalalo chimene makolo angakhale nacho pamene mwana wawo wakhonza bwino kusukulu. Chinthu ngati chimenechi n’choyeneradi kuchinyadira. Polembera Akristu anzake a ku Atesalonika, Paulo ananena kuti iyenso anakondwera ndi zimene anachita: ‘Tiziyamika Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake; kotero kuti ife tokha tidzitamandira za inu m’Mipingo ya Mulungu, chifukwa cha chipiriro chanu, ndi chikhulupiriro chanu, m’mazunzo anu onse ndi zisautsozo muzimva.’ (2 Atesalonika 1:3, 4) Inde, n’chikhumbo chachibadwa kufuna kusangalala ndi zimene okondedwa achita. Choncho, kodi ndi chiyani chimene chimasiyanitsa kunyada kumene kuli koipa ndi kunyada kumene kuli kwabwino?
Si kulakwa kufuna kutchinjiriza mbiri yathu, kupambana, ndi kusangalala ndi chipambanocho. Komabe, kunyada, kudzikuza, ndi kudzitukumula ife eni kapena ena Mulungu amadana nako. Kungakhaledi komvetsa chisoni kuyamba ‘kudzitukumula’ kapena ‘kudziyesa koposa kumene uyenera kudziyesa.’ Akristu alibe chifukwa chokhalira onyada kapena odzitukumula kwa aliyense kapena pa chilichonse koma kokha mwa Yehova Mulungu ndi zinthu zimene wawachitira. (1 Akorinto 4:6, 7; Aroma 12:3) Mneneri Yeremiya akutipatsa pulinsipulo labwino loti titsatire lakuti: “Wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziŵa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m’dziko lapansi.”—Yeremiya 9:24.
[Chithunzi patsamba 26]
Pope Innocent X, chojambulidwa ndi Don Diego Rodríguez de Silva Velázquez
[Mawu a Chithunzi]
Scala/Art Resource, NY