Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
N’chifukwa Chiyani Amayi Anga Akudwala Chomwechi?
Bambo ake a Al anamwalira ndi nthenda ya kansa.a Ataphunzitsidwa za malonjezo a m’Baibulo a chiukiriro, Al anatha kupirira imfa ya bambo akeyo. Koma pamene mayi akenso anaŵapeza ndi matenda a kansa, anayambanso kuda nkhaŵa. Al anachita mantha kwambiri poganizira kuti mwina kholo linalo n’kumwaliranso. ‘Chifukwa chiyani mayi anga akudwala?’ anali kudzifunsa mopwetekedwa mtima kwambiri.
MALINGA n’kunena kwa Dr. Leonard Felder, “Pali Aamereka oposa 60 miliyoni . . . omwe akusamalira okondedwa awo odwala kwambiri kapena olemala.” Felder anawonjezera kuti: “Tsiku lililonse pafupifupi mmodzi mwa antchito anayi alionse mu America amasenza udindo wowonjezera wopeza zosoŵa za kholo lodwala” kapena wokondedwa wina. Ngati muli m’mkhalidwe umenewo, dziŵani kuti siinu nokha ayi. Komabe, kuona yemwe mumam’konda akudwala n’zochititsa mantha ndi zopweteka. Kodi mungapirire motani?
N’chifukwa Chiyani Kholo Langa Likudwala?
Miyambo 15:13 imati: “Koma moyo umasweka ndi zoŵaŵa za m’mtima.” N’chachibadwa kusweka mtima pamene kholo lanu ladwala. Mwachitsanzo, mungadziimbe mlandu pamene kholo lanu lisakupeza bwino. Mwinamwake inu ndi kholo lanulo mwakhala musakugwirizana bwino. Mwinamwake munakanganapo kamodzi kapena kangapo. Tsono pamene kholo lanulo likudwala, mungaganize kuti mwina ndinu amene mwachititsa zimenezo. Komabe, ngakhale kuti kukangana m’banja kungachititse wina kupsinjika maganizo, sikaŵirikaŵiri kuti n’kuyambitsa matenda aakulu. Kusemphana malingaliro kapena mikangano yaing’ono kumakhalapo ngakhale m’mabanja okondana achikristu. Choncho simufunikira kudziimba mlandu, ngati kuti inu ndi amene mwayambitsa matenda a kholo lanulo.
Kwenikweni, mayi kapena bambo anuwo akudwala chifukwa cha kuchimwa kwa makolo athu oyamba aja, Adamu ndi Hava. (Aroma 5:12) Chifukwa cha tchimo loyamba limenelo, “cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zoŵaŵa pamodzi kufikira tsopano.”—Aroma 8:22.
Maganizo Opweteka
Ngakhale zili choncho, mungakhalebe wodandaula ndi wodera nkhaŵa. Mayi ake a Terri amadwala zithupsa, matenda osautsa zedi. Terri akuvomereza kuti: “Nthaŵi zonse pamene ndichoka panyumba, ndimada nkhaŵa, ndi kukayikira ngati mayi anga ali bwino. Kumakhala kovuta kwa ine kuzika malingaliro anga pa zomwe ndikuchitazo. Komabe, chifukwa chakuti sindifuna kuti azidandaula, ndimangozisungira mumtima.”
Miyambo 12:25 imati: “Nkhaŵa iŵeramitsa mtima wa munthu.” Kuchita tondovi n’kofala mwa achinyamata amene ali m’mkhalidwe umenewu. Terri ananena kuti amasweka mtima pamene aona kuti amayi ake sangathenso kugwira ngakhale ntchito zing’onozing’ono. Chimene chimawonjezera kupsinjika maganizo n’chakuti achinyamata—makamaka atsikana— kaŵirikaŵiri amakakamizika kutenganso maudindo ena. Malinga n’kunena kwa Polofesa Bruce Compas, “atsikana amasenzetsedwa mtolo ndi maudindo a m’banja, monga kugwira ntchito za panyumba ndi kulera achibale awo omwe adakali aang’ono, zimenezo n’zoti sangakhoze kuzikwanitsa ndipo zingasokoneze kukula kwawo ndi mikhalidwe yabwino.” Achinyamata ena amadzipatula, ndikumamvetsera nyimbo zowapangitsa kumangodzidandaulira ndi kudzimvera chisoni nthaŵi zonse.—Miyambo 18:1.
Mantha akuti mwina kholo langa limwalira n’ngofalanso. Terri ndi mwana yekhayo m’banjamo, ndipo mayi akewo alibenso mwamuna. Nthaŵi zonse Terri amakhala akulira pamene amayi ake apita kuchipatala, akumaopa kuti mwina sabwerako. Terri anati: “Tinalipo aŵiri tokha basi. Sindinkafuna kutaya mnzanga wapamtima.” Wachinyamata wina wotchedwa Martha anavomereza kuti: “Ine ndili ndi zaka 18, koma ndikuopa kutayikidwa makolo anga. Kusungulumwa kumeneku kungakhale kovulaza kwambiri.” Zomwe zimachitikira ena ngati kholo lawo likudwala n’zakuti samapeza tulo, amalota maloto oipa, ndipo samalakalaka chakudya.
Zomwe Mungachite
Ngakhale kuti zinthu zingaoneke kukhala zovuta tsopano, mungathe kupirira! Yambani kukambirana ndi makolo anuwo za mantha ndi nkhaŵa zomwe muli nazo. Kodi matenda akholo lanulo ndi aakulu motani? Kodi pali kuthekera konse kwakuti angachire? Kodi ndi makonzedwe otani okusamalirani ngati matenda a kholo lanulo atalephereka kuchizidwa? Kodi n’kotheka kuti mwina inunso n’kudzapezeka ndi vuto lofananalo m’tsogolo? Ngakhale kuti n’kovuta kwa makolo kukamba nkhani ngati zimenezo, koma ngati mutawafunsa modekha ndi mwaulemu, mosakayika adzachita mulimonse mmene angathere kukuthandizani ndi kukuchirikizani.
Fotokozaninso maganizo anu olimbikitsa. Al akukumbukira kuti analephera kuchita zimenezo pamene anazindikira kuti amayi ake awapeza ndi matenda a kansa. Iye anati: “Sindinaŵauze kuti ndinkaŵakonda zedi. Ndinkadziŵa kuti ankafuna kumva ndikunena zimenezo, koma monga wachinyamata ndinachita manyazi kuŵauza zimenezo. Mosakhalitsa anamwalira, ndipo panopo ndimadziimba mlandu chifukwa sindinathe kugwiritsa ntchito mwayi umene ndinali nawo panthaŵiyo. Ndimamva chisoni chifukwa anali munthu wofunika kwambiri m’moyo wanga.” Musazengereze kuuza makolo anu mmene m’maŵakondera.
Ngati n’kotheka, phunzirani zochuluka ponena za matenda a kholo lanulo. (Miyambo18:15) Mwinamwake dokotala wa banja lanulo angakuthandizeni pa nkhani imeneyi. Kudziŵa bwino lomwe kudzakuthandizani kukhala wachikondi, woleza mtima, ndi womvetsetsa zinthu. Ndipo zingathandize kuti mukonzekere kusintha kwina kulikonse kumene kungachitike pathupi la kholo lanu, monga zipsera, kusosoka tsitsi, kapena kumatopa kwambiri.
Kodi kholo lanulo lili m’chipatala? Ngati ndi choncho, pangani maulendo okaŵaona kukhala osangalatsa ndi olimbikitsa. Mulimonse mmene mungathere chititsani makambirano anu kukhala olimbikitsa. Afotokozereni za kusukulu ndi zochitika zachikristu. (Yerekezani ndi Miyambo 25:25.) Ngati mukukhala m’dziko limene achibale amafunikira kukapereka chakudya ndi thandizo lina kwa wodwala, chitani nawo zimenezo mosanyinyirika. Maonekedwe abwino akasangalatsa osati kholo lanu lokhalo, komanso akapereka chithunzi chabwino kwa ogwira ntchito m’chipatala ndi madokotala. Zimenezi zingathandize kuti kholo lanu lizilandira chithandizo chabwino. b
Kodi kholo lanulo likuchilira panyumba? Ndiyeno chitani chilichonse chimene mungakhoze kuti muthandize kusamala khololo. Dziperekeni mwa kumagwira ntchito za panyumba. Yesani kutsanzira Yehova mwa kupereka ‘modzala manja, ndi mosatonza.’ (Yakobo 1:5) Yesetsani kusonyeza kusadandaula, kukhala wolimbikitsa ndi wansangala.
N’zoona, kuti muli ndi zochita za kusukulu. Yesani kupatula nthaŵi padera kuti muchitenso zimenezo, chifukwa maphunziro anu n’ngofunika kwambiri. Ngati n’kotheka, patulani nthaŵi yopuma ndi yosangalala. (Mlaliki 4:6) Zimenezi zidzakupumulitsani ndi kukuthandizani kukhala wokhoza kuchirikiza kholo lanu. Potsirizira, pewani kudzipatula. Mupezerepo mwayi pa chithandizo chimene Akristu anzanu angapereke. (Agalatiya 6:2) Terri anati: “Mpingo unakhala banja langa. Akulu anali okonzeka nthaŵi zonse kulankhula nane ndi kundilimbikitsa. Sindidzaiŵala zimenezo.”
Kukhalabe Wolimba Mwauzimu
Chofunika koposa ndicho kukhalabe wolimba mwauzimu. Dzitangwanitseni ndi zinthu zauzimu, monga kuphunzira Baibulo, kupita ku misokhano ndi kulalikira kwa ena. (1 Akorinto 15:58) M’miyezi yachilimwe, Terri ankawonjezera ntchito yake yaulaliki monga mpainiya wothandiza. Akuwonjeza kuti: “Amayi anga nthaŵi zonse amandilimbikitsa kukonzekera ndi kupita ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Zimenezo zinaoneka kukhala zopindulitsa kwa tonsefe. Chifukwa chakuti samatha kukapezeka pa misonkhano yonse monga mmene amafunira, ndimakhala womvetsera kwambiri kuti ndikathe kuwauza zimene taphunzira nditabwerera kunyumba. Anadalira ine kuŵapatsa chakudya chauzimu pamene sakanatha kupitako.”
Nkhani ina mu The New York Times inafotokoza zinthu bwino pamene inakamba za wantchito yothandiza anthu yemwe wakhala “akuzizwa mobwerezabwereza ponena za momwe ana angakulire bwino ngakhale ali ndi nkhaŵa ya matenda a makolo awo.” Iye anati: “Amatulutsa maluso amene samazindikira kuti anali nawo. . . Ngati angathe kupirira vuto limeneli, angathenso kupirira zambiri.”
Inunso mungathe kupirira m’nyengo yovuta ngati imeneyi. Mwachitsanzo, amayi ake a Terri, ali wokhoza kudzisamalira okha. Mwinamwake, m’kupita kwanthaŵi, kholo lanulo lichiranso. Koma pakalipano, musaiŵale kuti mukuchirikizidwa ndi Mnzanu wakumwamba, Yehova. Iye ‘amamva pemphero’ ndipo adzamvetsera pamene mum’pempha chithandizo. (Salmo 65:2) Adzapereka kwa inu ndi kwa kholo lanu lowopa Mulungulo—“mphamvu yoposa yaumunthu” kuti muthe kupirira.—2 Akorinto 4:7, NW; Salmo 41:3.
[Mawu a M’munsi]
a Ena mwa mayinaŵa asinthidwa.
b Nkhani yakuti “Kuchezetsa Wodwala—Mmene Mungathandizire,” ya m’Galamukani! wa March 8, 1991 inalongosola zochuluka za mmene mungachitire.
[Mawu Otsindika patsamba 30]
“Nthaŵi zonse pamene ndichoka panyumba, ndimada nkhaŵa, ndi kukayikira ngati mayi anga ali bwino”
[Zithunzi patsamba 31]
Kuphunzira zoona zenizeni za matenda akholo lanu kungaku- thandizeni kupereka thandizo loyenera