Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 10/8 tsamba 32
  • “Chikhumbo Changa Chachikulu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Chikhumbo Changa Chachikulu”
  • Galamukani!—1999
Galamukani!—1999
g99 10/8 tsamba 32

“Chikhumbo Changa Chachikulu”

KALASI la ophunzira ku Vranje, ku Yugoslavia, linauzidwa kulemba chimangirizo chokhala ndi mutu womwe uli pamwambapa. Nkhani yotsatirayi ndi chimangirizo cha Sergej, mnyamata wa zaka zisanu ndi zitatu zakubadwa, chimene potsiriza pake chinamatidwa pakhoma la sukuluyo kuti aliyense aŵerenge.

“Choyamba, ndinafuna kulemba kuti chikhumbo changa chachikulu ndicho kutsiriza maphunziro anga kukafika ku sekondale, ndi kukakhoza bwino kumeneko ndiponso kupita ku Belgrade kutchuthi. Koma pamene ndinali kunyumba ndinkaganiza zosiyana ndi zimenezi. Chikhumbo changa chachikulu n’chakuti dziko lonse lapansi likhale pamtendere, anthu onse azikhala mosangalala, ndiponso kuti azikondana ndi kuthandizana. Ndikufuna anthu onse akhale athanzi komanso kuti dziko likhale laukhondo kusiyana ndi mmene lilili pano.

“Masiku ano dziko laipa kwambiri chifukwa cha mankhwala oipa. Madzi ndi mpweya nazonso n’zoipa. Ana zikwizikwi akufa tsiku ndi tsiku chifukwa cha njala m’dzikoli, ndiponso ena ambiri akufa chifukwa cha matenda. Ndikufuna kuti zonse zimenezi zichoke, ndipo ndikufuna kuti ana onse azidziŵa kuti makolo awo amawakonda, kotero kuti azitha kupita kukagona ali osangalala ndi achimwemwe, akumadziŵa kuti maŵa lidzakhalanso tsiku losangalatsa. Zimenezi sizingatheke m’dziko lino koma m’tsogolo zidzatheka. Chimenechi ndicho chikhumbo changa chachikulu.”

Kodi chinam’limbitsa mtima Sergej kunena motsimikiza kuti zinthu zimenezi zidzachitikadi n’chiyani? Iye amakhulupirira malonjezo a Mulungu amene Baibulo limafotokoza. Bolosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? limafotokoza za malonjezo ameneŵa pamutu wakuti “Dziko Latsopano Lokongola Koposa la Mulungu.” Mutha kupeza bolosha lanulanu limeneli mwa kudzaza ndi kutumiza silipi lotsatirali ku adiresi yoyenera pamaadiresi osonyezedwa patsamba 5 la magazini ano.

□ Nditumizireni chidziŵitso chowonjezera cha mmene ndingapezere bolosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi?

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena