Chinthu Chamtengo Wapatali Kuposa Ndalama
YOSIMBIDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU CANADA
“[Iye] anapatsa mwana wake wamkazi mphatso yamtengo wapatali kuposa kuchuluka kwa ndalama zonse,” inatero ndemanga ya mkonzi wa nyuzipepala yotchedwa The Monitor ya ku Bridgetown, Nova Scotia. Kodi mphatsoyo inali chiyani? Inali “chitsanzo chapadera cha kuona mtima” kwake.
Anna ndi mwana wake wamkazi Tanya anaima panyumba ya munthu pamene panali selo ndipo anagula kachikwama kakang’ono koyera kuti Tanya aziikamo Baibulo lake. Atafika kunyumba, Tanya anatsegula zipi yam’kati mwa kachikwamako ndipo anadadwa kupeza kuti munali ndalama zokwana $1,000 zamapepala. Nthaŵi yomweyo mayi ake ndi iye anabwerera kupita kunyumba kuja kukapereka ndalama zonse kwa mzimayi yemwe anagulako kachikwamako. Zikuoneka kuti, kachikwamako sanali kukagwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri ndipo kanali ka malemu amayi ake a mzimayiyo, omwe anamwalira ndi matenda a ku ubongo, ndipo sanayang’anemo kaye asanakagulitse. M’mawu ake othokoza zedi, mzimayiyo anati: “Zimenezi zandiyambitsanso kukhulupirira anthu . . . N’zolimbikitsa kudziŵa kuti anthu oona mtima adakalipobe.”
Patsamba loyamba la nyuzipepala yakumaloko panali nkhani yomweyi ndipo nyuzipepalayi inagwira mawu a Anna akumati: “Ife monga Mboni za Yehova, limenelo ndilo khalidwe lathu. Tili ndi [chikumbumtima] chozikidwa m’Baibulo. Tikufunanso kuphunzitsa Tanya khalidwe labwino.” Kwa Tanya, kachikwama kake koyera katsopanoko kadzakhala chikumbutso chapadera cha phunziro la kuona mtima.