Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 11/8 tsamba 15
  • Analimbikitsidwa ndi Chikhulupiriro cha Iye

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Analimbikitsidwa ndi Chikhulupiriro cha Iye
  • Galamukani!—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Kusankhapo Pakati pa Atate Aŵiri
    Galamukani!—1998
  • Baibulo Limasintha Anthu
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Mavuto Anga Andithandiza Kulimbitsa Ubwenzi Wanga ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Kuyamikira Chichilikizo CHosalekeza cha Yehova
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 11/8 tsamba 15

Analimbikitsidwa ndi Chikhulupiriro cha Iye

Mtsikana wina wa zaka 17 analemba kalata ku ofesi ya Watch Tower Society ku Moldova, komwe kale kunkatchedwa Soviet Union, kuti athokoze chifukwa cha nkhani yomwe inatuluka mu Galamukani! wa June 8, 1998. Nkhaniyo inali ndi mutu wakuti “Kusankhapo Pakati pa Atate Aŵiri,” ndipo inasimba zomwe mnyamata wina wa ku Armenia anakumana nazo.

“Pamene ndinali kuŵerenga nkhaniyo,” anatero mtsikanayo, “misozi inatsika m’maso mwanga chifukwa chakuti zimenezo n’zimenenso ndakumana nazo ine.” Anapitiriza kuti: “Pamene ndinali ndi zaka 15 ndinayamba kuphunzira Baibulo, ndipo makolo anga sanatsutse poyamba. Koma pamene ndinayamba kupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova, iwo anandikaniza kotheratu. Kenako, mu 1997, pamene ndinayamba kugaŵana ndi ena zomwe ndinali kuphunzira, anandiuza amvekere: ‘Pita kwa abale ako a Mboni omwewo azikakudyetsa, azikakuveka, ndiponso akakupezere ntchito. Chimwana chanji chosamva!’ Makolo anga anafikira pondikankha, kumenyetsa mutu wanga kukhoma.

“Chinalidi chiyeso choŵaŵa kwa ine. Kaŵirikaŵiri ndinali ndi maganizo ofanana ndi omwe mnyamata wa ku Armenia uja analongosola kuti nthaŵi zina iye amakayikira ngati Yehova anali kukondwera naye. Ndinali kuganiza kuti, ‘Kodi ndine munthu wopanda pake? Kodi Yehova adzandikhululukira machimo anga am’mbuyomu? Kodi Yehova adzandikondabe?’

“Zinalidi zovuta zedi, makamaka pamene ndinkaganiza kuti Yehova sadzandikondanso. Kaŵirikaŵiri ndinkapempha Yehova m’pemphero, uku ndikukhetsa misozi, kuti andithandize, ndi kundilimbikitsa kuti ndisamusiye konse. Ndipo ndithudi, Yehova anamva ndiponso anayankha mapemphero anga. Anandipatsa chilimbikitso, chitsimikizo, ndiponso anandilimbitsa mtima. Makamaka anachita zimenezi kudzera mwa Mawu ake, mmene wamasalmo ananena mwachidaliro kuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.”—Salmo 27:10.

Pa September 27, 1997, ndinachita chizindikiro chosonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova pobatizidwa pa msonkhano wadera wa Mboni za Yehova ku Kagul. Ndikuona kuti Yehova Atate wathu wachikondi wakumwamba, amakwaniritsa malonjezo ake omwe ali pa Salmo 84:11 akuti: “Yehova Mulungu ndiye dzuŵa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.”

“Ndikuthokoza kwambiri mnyamata wa ku Armenia amene anagaŵana nafe nkhani yake yolimbitsa chikhulupiriro m’magazini a Galamukani! Ndikukhulupirira kuti makolo anga pamodzi ndi ake, m’kupita kwa nthaŵi adzachita chidwi ndi ziphunzitso za Baibulo.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena