Mtedza Wotchedwa Tagua—Kodi Ungapulumutse Njovu?
YOSIMBIDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU ECUADOR
NDI zinthu ziŵiri zodalirana koma zosiyana kwambiri. Chimodzi chimalemera magalamu ochepa chabe; chinacho matani angapo. Chimodzi ndi chomera; chinacho ndi chinyama. Zimakhala m’makontinenti osiyana. Komatu, mtedza waung’onong’ono wa ku South America umenewu ungathe kupulumutsa njovu zazikuluzikulu za ku Africa kuti anthu asazisakaze. Kodi mtedza wa tagua ndi chiyani, ndipo kodi unakhala bwanji bwenzi la njovu?
Mtengo Wachilendo wa Kanjedza
Mtedza wa tagua ndi njere ya mtundu wina wa mtengo wa kanjedza umene kwenikweni umapezeka kumpoto kwa South America. Mitengo yokula pang’onopang’ono imeneyi imakhala ndi masamba okongola amene amamera kuchokera mtsinde mwenimweni mwa mtengowo. Kwa zaka zambiri thunthu lake silioneka. Kanjedza wa tagua amene thunthu lake lafika mamita aŵiri umakhala ndi zaka 35 mpaka 40. Phava lalikulu lokhala ngati muzu limatuluka m’tsinde mwenimweni mwa masamba. Phava lake, nthaŵi zambiri limalemera makilogalamu 10 ndipo limakhala ndi zipatso zolimba zothinana. Chipatso chilichonse chimakhala ndi njere zinayi kapena mpaka zisanu ndi zinayi, zimene kukula ndi kuoneka kwake zimakhala ngati dzira la nkhuku. Poyamba mkati mwa njerezo mumakhala madzi othetsa ludzu angati madzi a koko. Kenaka, madzi aja amalimba n’kukhala onyata otsekemera. Ndiyeno potsiriza, madzi onyata aja amalimba gwaa, n’kumaoneka mbee, ndipo amafanana ndendende ndi minyanga ya njovu.
Chifukwa Chimene Ulili Bwenzi la Njovu
Popeza umaloŵa mmalo mwa minyanga, mtedza wa tagua ungatchedwedi kuti bwenzi la njovu. Kupha njovu moswa lamulo chifukwa chofuna minyanga kwaopseza kwambiri miyoyo ya njovu za ku Africa. Komabe, mtedza wa tagua umaloŵa mmalo mwake bwino lomwe, chifukwa chakuti umaoneka ngati m’nyanga weniweni, ndi wolimba kwambiri, ungathe kusalazidwa ndipo umatha kupakidwa utoto mosavuta. Mtedza wa tagua ndi minyanga ya njovu n’zofanana kwambiri kotero kuti nthaŵi zambiri amalonda akamaupala amasiyako pang’ono khungwa lake kuti ogula akhulupirire kuti sakugulitsa minyanga ya njovu, imene ndi yoletsedwa padziko lonse.
Minyanga ya zomera sikuti yatulukiridwa posachedwa. M’mbuyomu cha m’ma 1750, munthu wina wa gulu la chipembedzo Juan de Santa Gertrudis wa ku South America anatchula mtedza wa tagua m’nkhani zake za m’mbiri, ndipo anauyerekezera ndi “miyala ya nsangalabwi” imene inali kugwiritsidwa ntchito posema ziboliboli. Chakumayambiriro kwa m’ma 1900, dziko la Ecuador, limene limalima tagua wambiri, linali kugulitsa matani zikwizikwi a mtedzawu ku mayiko a kunja chaka chilichonse, kuti makamaka azikapangira mabatani. Nkhondo Yachiŵiri Yapadziko Lonse itatha, kubwera kwa mabatani apulasitiki atsopano komanso otsika mtengo kunathetseratu malonda a tagua. Kusonyeza kuti malonda a minyanga ya zomera ayambiranso, posachedwapa, kwa miyezi 18, matani 1,650 a tagua ochokera ku Ecuador anagulitsidwa ku Germany, Italy, Japan, United States, ndi mayiko ena 18.a Kodi tagua amakonzedwa ndi kugwiritsidwa ntchito motani lero?
Mtedza wa Tagua Uli ndi Ntchito Zambiri
Njere zake amaziyanika pa dzuŵa kuti ziume, kwa mwezi umodzi kapena miyezi itatu malingana ndi uŵisi wake. Kenaka, amazifufuta ndi makina, n’kuzisankha malingana ndi kukula kwake, ndipo amaziphwanya m’tizidutswa timene amakapangira mabatani. Inde, mabatani a “minyanga” opangidwa kuchokera ku tagua amakongoletsa zovala zina zapamwamba kwambiri za padziko lino. Komabe, mtengo wa tagua sikuti amangopangira mabatani okha. Zinthu zina monga zovala zodzikometsera monga mikanda, nkhomo zoseŵerera maseŵera onga bawo otchedwa tchesi, zigawo zina za zida zoimbira nyimbo zochita kupeperera, mabatani a piyano, komanso zigwiriro za sumbulere zimapangidwa kuchokera ku tagua.
Koma ntchito za tagua si zokhazitu ayi! Ufa wopera bwino umene umatsalira popanga zinthu zina, amaugwiritsa ntchito pousakaniza m’zakudya za ziŵeto. Amaugwiritsanso ntchito monga nkhuni akamapanga makala amalasha. Masamba a kanjedza amafolelera denga kuti lisadonthe. Kuphatikizanso apo, kukolola, kukonza ndiponso kugulitsa tagua kumayiko akunja kumapereka mwayi wa ntchito kwa anthu ambiri.
Koposa zonse, minyanga ya zomera imeneyi ingathandize nawo kuteteza njovu za ku Africa. Choncho ngati mukufuna minyanga poti ndi yapamwamba, musaganize zokaifuna m’nkhalango za mu Africa. Koma ganizani za nkhalango za ku South America, kumene minyanga iliko yambiri kotero kuti imamera m’mitengo! Inde ganizani za mtedza wa tagua, bwenzi la njovu.
[Mawu a M’munsi]
a Kuyambira pa January 1, 1994, mpaka June 15, 1995.
[Zithunzi pamasamba 17, 18]
1. Mtengo wa kanjedza wa tagua
2. Maphava a zipatso za tagua
3. Mmene njere za tagua zimaonekera chipatso chake akachidula pakati
4. Njere ya tagua imauma n’kusanduka mtedza wolimba
5. Mabatani a tagua
6. Zokometsera zopangidwa kuchokera ku tagua zokhala ndi m’mphepete monyezimira
7. Tiziboliboli topangidwa kuchokera ku tagua