Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 6/09 tsamba 30
  • Wodwala Ali Ndi Ufulu Wosankha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Wodwala Ali Ndi Ufulu Wosankha
  • Galamukani!—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mafunso Ophunzirira Brosha ya Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Kodi Kuthiridwa Mwazi Ndiko Mfungulo Yopulumukira?
    Galamukani!—1990
  • Yendani Monga Momwe Mwalangizidwa ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—2009
g 6/09 tsamba 30

Wodwala Ali Ndi Ufulu Wosankha

YOLEMBEDWA KU ITALY

◼ Mboni za Yehova zimakana kuikidwa magazi. Zimatero chifukwa malemba angapo m’Baibulo amaletsa magazi. Mwachitsanzo lemba la Genesis 9:4 limati: “Koma nyama, mmene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.” Akhristu a mu nthawi ya atumwi anauzidwanso kuti ‘apitirize kupewa magazi.’—Machitidwe 15:29; Levitiko 17:14.

Ana ena a ku sekondale ku Monterenzio, Italy, anauzidwa kuti alembe nkhani yonena za kufunika kopereka magazi. Mmodzi wa ana a sukuluwo anali Benedetta, yemwe ndi wa Mboni za Yehova. Iye analemba nkhani yotsatirayi:

“Pafupifupi aliyense amadziwa kuti a Mboni za Yehova amakana kuikidwa magazi chifukwa chakuti amatsatira mfundo za m’Baibulo. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti iwo salola kulandira thandizo lina lamankhwala. Ndipotu, a Mboni za Yehova amayesetsa kusamalira moyo wawo. Amayesetsa kupeza thandizo lamankhwala labwino kwambiri ngati iwo kapena ana awo adwala. Amayesetsanso kwambiri kugwirizana ndi madokotala, makamaka ngati madokotalawo sakuwakakamiza kuphwanya mfundo zimene iwo amatsatira.”

Benedetta analembanso kuti: “Wodwala aliyense ali ndi ufulu wosankha thandizo la mankhwala limene akukhulupirira kuti ndi labwino kwambiri. Ali ndi ufulu wolemekezedwa ndiponso wodziwa ubwino ndi kuipa kwa thandizo la mankhwala limene angalandire.”

Bungwe loona za magazi ku Monterenzio linapereka mphatso kwa ana amene anafotokoza bwino maganizo awo pankhaniyi. Magazini ya Monterenzio Vivace inati: “Benedetta Barbi anayamikiridwa kwambiri chifukwa cha nkhani yake yomwe inasiyana kwambiri ndi zimene anthu ambiri amaganiza. Ngakhale kuti iye analemba mfundo zosiyana kwambiri ndi za bungwe loona za magazi ku Monterenzio, m’nkhani yakeyi anafotokoza zimene amakhulupirira mwaulemu, popanda kunyoza ena.”

Ngakhale kuti zimene Mboni za Yehova zimakhulupirira zokhudza magazi n’zosiyana kwambiri ndi zimene anthu ambiri amakhulupirira, madokotala ambiri akuona kuti a Mboni amachita bwino kukana magazi. A Mboni za Yehova ndi amene athandiza kwambiri kuti madokotala atulukire njira zatsopano zothandiza kuti pochita opaleshoni, munthu asamataye magazi ambiri. Njira zimenezi zathandiza a Mboni za Yehova komanso anthu ena. Komabe chifukwa chachikulu chimene a Mboni za Yehova amakanira magazi n’chakuti amamvera zimene Baibulo limanena, monga tafotokozera kumayambiriro kwa nkhani ino.

Tsiku lina a Mboni za Yehova akadzafika panyumba panu mungadzachite bwino kuwafunsa kuti afotokoze mmene Mlengi amaonera magazi. Iwo adzasangalala kwambiri kukufotokozerani zimenezi ‘mwaulemu.’—1 Petulo 3:15.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 30]

NGATI MUKUFUNA KUDZIWA ZAMBIRI

Mboni za Yehova zinatulutsa DVD yakuti, Transfusion Alternatives, mothandizidwa ndi madokotala odziwika bwino. DVD imeneyi imafotokoza mfundo zokhudzana ndi zachipatala, malamulo komanso chikhalidwe. Mungapeze DVD imeneyi kwa Mboni za Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena