Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 12/12 tsamba 16-18
  • Kodi Mwamuna Weniweni Amakhala Wotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mwamuna Weniweni Amakhala Wotani?
  • Galamukani!—2012
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Lolani Kupita Patsogolo Kwanu Kuwonekera’
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Bambo Angatani Kuti Azigwirizana Kwambiri Ndi Mwana Wake Wamwamuna?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Ndimangocheza Naye, Kapena Ndimamufuna? Gawo 2
    Galamukani!—2012
  • Kodi Munthu Ameneyu Ndi Woyenera Kuti Ndimange Naye Banja?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
Onani Zambiri
Galamukani!—2012
g 12/12 tsamba 16-18

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Mwamuna Weniweni Amakhala Wotani?

“Bambo anga anamwalira ndili ndi zaka zitatu moti nthawi zina ndimasirira anyamata amene ali ndi bambo awo. Amaoneka kuti amachita zinthu mosadzikayikira kusiyana ndi mmene ndimachitira.”—Anatero Alex.a

“Sindicheza kwambiri ndi bambo anga moti ndimachita kuphunzira ndekha zinthu zimene mwamuna ayenera kuchita.”—Anatero Jonathan.

KODI inuyo munayamba mwamvapo ngati mmene anyamata awiri omwe atchulidwa pamwambawa amamvera? Kodi mumakayikira zoti mungakwanitse kuchita zimene mwamuna weniweni amayenera kuchita? Ngati zili choncho, musadandaule.

Tiyeni tione zimene mungachite kuti muthane ndi mavuto awiri amene anyamata ambiri amakumana nawo.

VUTO LOYAMBA: Kukhala ndi maganizo olakwika pa nkhani ya mwamuna weniweni

Zimene ena amanena:

  • Mwamuna salira.

  • Mwamuna weniweni sauzidwa zochita.

  • Mwamuna weniweni sachita zinthu ngati mkazi.

Zoona zake: Sizoona kuti mwamuna amakhala ndi nzeru kuposa mkazi, koma zoona zake n’zakuti mwamuna weniweni sachita zinthu mwachibwana. Munthu amakhala mwamuna weniweni akayamba kuchita zinthu ngati munthu wamkulu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene ndinali kamwana, ndinali kulankhula ngati kamwana, kuganiza ngati kamwana, ndiponso kuona zinthu ngati kamwana. Koma tsopano pamene ndakula, ndasiya zachibwana.” (1 Akorinto 13:11) Mawu amenewa akusonyeza kuti munthu akasiya kuganiza, kulankhula komanso kuchita zinthu ngati mwana ndiye kuti ndi mwamuna weniweni.b

Yesani izi: Lembani papepala mayankho a mafunso awa:

  1. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zikusonyeza kuti ndasiya “zachibwana”?

  2. Kodi ndi zinthu ziti zomwe ndikufunikabe kusintha?

Mavesi amene mungawerenge: Luka 7:36-50. Pamene mukuwerenga mavesiwa yesani kuona zimene Yesu anachita zosonyeza kuti anali mwamuna weniweni (1) poyesetsa kuchita zinthu mwachilungamo komanso (2) kulemekeza ena kuphatikizapo azimayi.

“Ndili ndi mnzanga, dzina lake Ken, ndipo ndimamusirira chifukwa ndi wamphamvu, wolimba mtima, wokonda kutsatira mfundo za m’Baibulo komanso ndi wachifundo. Zimene amachita zandithandiza kuona kuti mwamuna weniweni saona kuti anthu ena ndi otsika.”—Anatero Jonathan.

VUTO LACHIWIRI: Kukula popanda kuthandizidwa ndi bambo

Zimene ena amanena:

  • Ngati mnyamata alibe bambo ake sangadziwe zimene mwamuna weniweni ayenera kuchita.

  • Ngati mnyamata ali ndi bambo omwe sasonyeza chitsanzo chabwino, akakula amachita zimene bambo ake ankachita.

Zoona zake: Ngakhale kuti munakula opanda bambo kapena bambo anu sankasonyeza chitsanzo chabwino, sizikutanthauza kuti mulibe tsogolo labwino. Pali zimene mungachite kuti zinthu zikuyendereni bwino. (2 Akorinto 10:4) Mukhoza kutsatira malangizo amene Mfumu Davide anapereka kwa mwana wake Solomo kuti: “Uchite zinthu mwamphamvu ndipo ukhale wolimba mtima.”—1 Mafumu 2:2.

N’zoona kuti ndi zovuta kukula popanda bambo kapena kukhala ndi bambo amene sasamala ana. Alex amene tamutchula koyambirira uja ananena kuti: “Zimakhala zovuta kwambiri ukakhala kuti suwadziwa bambo ako bwinobwino. Panopa ndili ndi zaka 25, koma ndimaona kuti zimene ndikuphunzira panopa ndimayenera kuziphunzira kalekale.” Kodi mungatani ngati muli ndi mavuto ngati a Alex?

Yesani izi: Pezani munthu amene mukuona kuti ndi chitsanzo chabwino pa zimene mwamuna ayenera kuchita.c Mufunseni kuti ndi makhalidwe ati amene akuona kuti mwamuna weniweni ayenera kukhala nawo. Kenako akuuzeni zimene inuyo mungachite kuti mukhale ndi makhalidwewo.​—Miyambo 1:5.

Mavesi amene mungawerenge: Miyambo chaputala 1 mpaka 9. Pamene mukuwerenga machaputalawa, yesani kupeza malangizo omwe angathandize mnyamata kuti akhale wanzeru komanso kuti azikonda kutsatira mfundo za m’Baibulo.

“Ndikusangalala kuti panopa ndili ndi makhalidwe amene mwamuna weniweni amafunika kukhala nawo. N’zoona kuti zikanakhala bwino kwambiri ndikanakula ndi bambo anga koma sindiganizira kwambiri zam’mbuyo ndipo ndimaona kuti ndili ndi tsogolo labwino.”—Anatero Jonathan.

Kuyambira ndi Galamukani! ya January 2013, nkhani zakuti Zimene Achinyamata Amafunsa zizipezeka pa Webusaiti

a Tasintha mayina ena m’nkhani ino.

b Onani bokosi lakuti “Kusiyana Kwa Mwamuna Weniweni Ndi Munthu Wachibwana.”

c Mungapemphe akulu mumpingo wachikhristu kuti akuthandizeni.

Ian—Mwamuna weniweni sachita zinthu modzionetsera. Koma amalimbikira ntchito, amachita zinthu mozindikira komanso amakhala wodalirika.

KUSIYANA KWA MUNTHU WACHIBWANA NDI MWAMUNA WENIWENI

Nthawi zambiri munthu wachibwana . . .

  • amakhala wamwano.

  • amakhala wodzikonda.

  • amangokonda zosangalatsa.

  • amachita zinthu asanaganize kaye.

Mwamuna weniweni amayesetsa . . .

  • kulemekeza ena.​—Aroma 12:10.

  • kuchita zinthu modzipereka.​—1 Akorinto 10:24.

  • kukwaniritsa udindo wake.​—Agalatia 6:5.

  • kuganiza kaye asanachite zinthu​—Miyambo 16:32.

FUNSANI MAKOLO ANU

Kodi inuyo mumaganiza kuti mwamuna weniweni ndi wotani? Kodi mukuona kuti ineyo ndimachitabe zachibwana?

MAWU KWA MAKOLO

AZIBAMBO—

Inuyo muli ndi udindo waukulu wothandiza mwana wanu kuti azichita zinthu ngati mwamuna weniweni. Ngati mumasonyeza ulemu mkazi wanu, ndiye kuti mukuphunzitsa mwana wanu kulemekeza akazi. Ngati mumalimbikira ntchito kuti musamalire banja lanu, mwina kugwira ntchito zooneka ngati zonyozeka kapena zotopetsa, ndiye kuti mukuphunzitsa mwana wanu kuti azilimbikira ntchito komanso adzathe kudzisamalira.—1 Timoteyo 5:8.

N’kutheka kuti muli wachinyamata simunkagwirizana kwambiri ndi bambo anu, mwina chifukwa chakuti bambo anuwonso sankagwirizana kwambiri ndi bambo awo. Koma dziwani kuti inuyo mukhoza kupewa kutengera khalidwe limeneli. Mungachite bwino kumapeza nthawi yocheza ndi mwana wanu.d Ngati inuyo mutamusonyeza chitsanzo chabwino, akhoza kudzakhala mwamuna weniweni amene inuyo muzidzamunyadira.—Miyambo 23:24.

AZIMAYI—

Kodi mungathandize bwanji mwana wanu wamwamuna kuti azichita zinthu ngati mwamuna weniweni? Muzipewa kumuyerekeza ndi bambo ake. Mwachitsanzo, mwana akalakwitsa zinazake zomwenso bambo ake amalakwitsa musamanene kuti: “Tamuoneni! Umangochita zosalongosoka ngati bambo ako.” N’zoona kuti muli ndi udindo wodzudzula mwana wanu ngati walakwitsa. Koma ngati nthawi zonse mumalankhula kapena kuchita zinthu zosonyeza kuti zimene bambo ake amachita ndi zolakwika, mosadziwa mungakhale mukulepheretsa mwana wanu kuchita zinthu ngati mwamuna weniweni.

Muzithandiza mwamuna wanu kuti aziyesetsa kucheza ndi mwana wanu wamwamuna. Muziwalimbikitsa kuti azipeza nthawi yochezera limodzi ndipo muziuza mwana wanu makhalidwe komanso zinthu zabwino zimene bambo ake amachita. Ngati mwamuna wanu amayesetsa kusamalira banja, kucheza ndi ana komanso kulemekeza ena, muuzeni mwana wanu kuti mumayamikira makhalidwe amenewo. Zimenezi zingathandize mwana wanuyo kudziwa makhalidwe amene mwamuna weniweni amayenera kukhala nawo.

d Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti, “Kodi Bambo Angatani Kuti Azigwirizana Kwambiri Ndi Mwana Wake Wamwamuna?” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2011, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena