Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 12/12 tsamba 19-21
  • Caucasus Dera Lamapiri Komanso Zilankhulo Zosiyanasiyana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Caucasus Dera Lamapiri Komanso Zilankhulo Zosiyanasiyana
  • Galamukani!—2012
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu a Zinenero Zosiyanasiyana
  • Anthu “a Manenedwe Onse” Akumva Uthenga Wabwino
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzilalikira Anthu Oyankhula Chinenero China
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Kusonkhanitsa Anthu a Zinenero Zonse
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Kodi Zinenero Zathu Zinayambira pa “Nsanja ya Babele”?
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Galamukani!—2012
g 12/12 tsamba 19-21

Caucasus Dera Lamapiri Komanso Zilankhulo Zosiyanasiyana

TAYEREKEZANI kuti mwapita kudera linalake lalikulu kwambiri komanso lamapiri okhaokha. Mutafika, mukudabwa kuti kudera limenelo kuli anthu amitundu komanso zinenero zosiyanasiyana moti ngakhale anthu oyandikana midzi amalankhula zinenero zosiyana. Izi n’zimene akatswiri akale ofufuza za malo anapeza atafika kudera la Caucasus.

Derali lili pakati pa Nyanja Yakuda ndi ya Caspian ndipo zinthu monga zamalonda zimene zinkachitika m’derali zinachititsa kuti mukhale anthu a zikhalidwe zosiyanasiyana. Anthu a m’derali amadziwika kuti amalemekeza okalamba, amakonda kuvina komanso kuchereza alendo. Koma alendo okaona derali amachita chidwi kwambiri ndi kuchuluka kwa zinenero ndi zikhalidwe za anthu a kumeneko. Derali lili ndi zinenero zambiri kuposa madera ena a ku Europe.

Anthu a Zinenero Zosiyanasiyana

Cha m’ma 400  B.C.E., katswiri wina wa mbiri yakale wa ku Greece, dzina lake Herodotus ananena kuti: “Ku Caucasus kumapezeka anthu a mitundu yonse.” Komanso chaka cha 1 C.E. chitatsala pang’ono kufika, katswiri wina wa mbiri yakale wa ku Greece komweko, dzina lake Strabo, analemba nkhani zokhudza mafuko 70 a anthu a ku Caucasus. Fuko lililonse linali ndi chinenero chake komanso linkachita malonda m’tauni ya Dioscurias, dera lomwe masiku ano lili mu mzinda wa Sukhumi, mphepete mwa Nyanja Yakuda. Patadutsa zaka zambiri katswiri wina wa ku Roma, dzina lake Pliny Wamkulu, analemba kuti pochita malonda ku Dioscurias, Aroma ankafunika anthu 130 oti aziwamasulirira m’zinenero zosiyanasiyana.

Masiku ano ku Caucasus kuli mitundu ya anthu yoposa 50. Mtundu uliwonse uli ndi chikhalidwe chakechake. Ulinso ndi luso lakelake lopanga zinthu, lakamangidwe komanso lakavalidwe. M’derali muli zinenero pafupifupi 37 ndipo zinenero zina zimalankhulidwa ndi anthu ambiri pomwe zina ndi anthu a m’mudzi umodzi basi. Dera limene lili ndi zinenero zambiri ku Caucasus ndi dziko la Dagestan komwe kuli mitundu 30 ya anthu. Mpaka pano sizidziwika ngati pali kugwirizana pakati pa zinenero za anthu a ku Dagestan ndi za m’madera ena ku Caucasus.

Kodi mungakonde kudziwa zina mwa zinenero za m’dera la Caucasus? Pa Webusaiti ya Mboni za Yehova ya www.pr418.com, pali mabuku m’zinenero zoposa 400, ndipo zina mwa zinenerozi ndi zomwe zimalankhulidwa ku Caucasus.

CHIYUBEKI NDI CHINENERO CHOVUTA KUMVA

Zinenero za ku Caucasus zili ndi zilembo zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, Chiameniya chili ndi zilembo zosiyana ndi Chijojiya ndipo mawu a zinenero zina amawalemba pogwiritsa ntchito zilembo za m’Chilatini.

Zinenero zakumpoto chakumadzulo kwa Caucasus zili ndi makonsonanti ambiri ofanana ndi amene amapezekanso m’zinenero zambiri padziko lonse koma zili ndi mavawelo ochepa. Buku lina linanena kuti “anthu akudera limeneli akamalankhula, amamveka ngati akulankhulira kummero.” Munthu wina wolankhula Chiyubeki, yemwe anamwalira mu 1992, ankagwiritsa ntchito makonsonanti pafupifupi 80 koma ankagwiritsa ntchito mavawelo awiri okha.

Pali nthano ina yomwe imanena kuti mfumu ina ya ku Turkey inatumiza munthu wina ku Caucasus kuti akaphunzire Chiyubeki. Atabwerera, munthuyu ananena kuti walephera kuphunzira chinenerocho. Kuti mfumuyo imvetse, munthuyo anangotenga kathumba ka timiyala, n’kutikhuthulira pansi. Kenako anauza mfumuyo kuti: “Mwamva mmene timiyalati tikumvekera? Mmenemu ndi mmene mlendo amamvera anthu a ku Caucasus akamalankhula Chiyubeki.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena