Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/02 tsamba 1
  • Kusonkhanitsa Anthu a Zinenero Zonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusonkhanitsa Anthu a Zinenero Zonse
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu “a Manenedwe Onse” Akumva Uthenga Wabwino
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzilalikira Anthu Oyankhula Chinenero China
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Ntchito Yamaphunziro Yofala Kwambiri
    Galamukani!—2001
  • Kukhazikitsa Gawo la Chinenero China
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
Onani Zambiri
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 7/02 tsamba 1

Kusonkhanitsa Anthu a Zinenero Zonse

1 Mawu a Mulungu akukwaniritsidwa! Anthu “a manenedwe onse a amitundu” akulandira kulambira koona. (Zek. 8:23) Kodi Mboni za Yehova zimawathandiza bwanji anthu a ‘mafuko ndi manenedwe’ onse kukhala oyera pamaso pa Yehova, ali ndi chiyembekezo choti adzapulumuka ‘chisautso chachikulu’?—Chiv. 7:9, 14.

2 Gulu la Mulungu Limathandiza: Bungwe Lolamulira lakonza zoti mabuku ofotokoza Baibulo azipezeka m’zinenero pafupifupi 380 kuti anthu padziko lonse amvetsetse kufunika kwa uthenga wabwino. Kukonza ndi kusindikiza mabuku m’zinenero zambiri chonchi sintchito yamaseŵera. Pamafunika kupanga magulu a anthu otembenuza amene ayeneretsedwa kugwira ntchitoyi ndiponso kuwathandiza mwa kuwapatsa zinthu zimene akufuna potembenuza mabuku m’zinenero zonsezi, komanso posindikiza ndi kutumiza mabukuwo. Koma, amene amagwira ntchito yofunika kwambiri ndi ofalitsa Ufumu, amene amakauza anthu uthenga wa m’Baibulo wopulumutsa moyo.

3 Kuvomera Kugwira Ntchito Yovuta: M’madera ambiri tsopano mukupezeka magulu aakulu a anthu olankhula chinenero china. Kuti anthu ameneŵa amve uthenga wabwino, atumiki a Mulungu omwe akuchulukirachulukirabe akuyesetsa kuphunzira chinenero china chofala m’dera lawolo. Anthu ena amene sanamvepo za Yehova kapena sadziŵa kanthu za Baibulo akulandira choonadi cha Mawu a Mulungu.—Aroma 15:21.

4 Kodi tingayesetse kwambiri kulalikira uthenga wabwino kwa anthu a chikhalidwe china amene akukhala m’gawo lathu? (Akol. 1:25) Choyamba, ofalitsa amaphunzira mawu a m’chinenero chimenecho ongokwanira ulaliki wosavuta, monga uwu: “Moni. Nawu uthenga wabwino kwa inu. [Ndiyeno amagaŵira thirakiti kapena bulosha la m’chinenero chimenecho.] Basi tapita.” Yehova akudalitsa kwambiri ulaliki wochepa umenewu.

5 Uthenga wa Ufumu umasangalatsa anthu a zikhalidwe ndi zinenero zonse. Tiyeni tigwiritse ntchito mpata uliwonse kuuza anthu ena uthengawu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena