“Pitirizani Kutsata Ukulu Msinkhu”!
Tsopano popeza kuti mwaziphunzira zoonadi zina zamaziko za Baibulo, inu mufunikira kupitirizabe mu’kukula kwauzimu. Cotero inuyo mudzafuna kucita monga momwe mtumwi Paulo analangizira: “Mwa ici, polekana nao mau a ciyambidwe ca Kristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu.”—Ahebri 6:1.
Kukuthandizani inu kuti mutero, ife tikukulimbikitsani kuti muwerenge bukhu lopatsa cidziwitso ili:
“Zinthu Ziwiri Zosasinthika, M’mene Mulungu Sakhoza Kunama”
Cothandizira phunziro la Baibulo cofunika ici cidzakuthangatani inu kuufikira ukulu msinkhu, popeza kuti pakati pa zinthu zina, cimakupatsani inu: Cidziwitso copita patsogolo ndi kuwazindikira mokulira Mau a Mulungu a coonadi. Cithunzi cabwino kwambiri ca Baibulo lonse lathunthu. Mayankho ocokera ku Magwero apamwambamwamba a zothetsa nzeru zotayitsa mtima za masiku anozi. Liri ndi cikuto colimba ndi masamba 412. Liri ndi zithunzi zokongola. Tumizani 40c (Zambia 40n) tsopano kaamba ka kope lanu, simudzalipira ndarama zopositira.