Yehova Atipatsa Mpulumutsi
29 Munthu woyamba amene Mulungu anapanga anali ngati mwana woyamba kubadwa kwa iye.
Mulungu anam’konda kwambiri ndipo akugwiritsira ntchito iyeyo kuwononga anthu oipa ndi kupulumutsa omvera.—Yohane 3:16, 36
30 Yehova anatumiza mwana wake kudzabadwa pa dziko lapansi. Iye anatchedwa Yesu. Dzina la mayi wake linali Mariya.—Luka 1:30-35
31 Pamene Yesu anakula anaphunzitsa zinthu zabwino kwambiri zochuluka. Iye anaphunzitsa kuti Yehova yekha ndiye Mulungu woona.—Marko 12:29, 30
Yesu anati tiyenera kulambira Yehova yekha.—Mateyu 4:10; Yohane 4:23, 24
Anaphunzitsanso za Ufumu wa Mulungu.—Luka 17:20, 21
32 Yesu anachiritsa odwala ndipo anachita zinthu zabwino zambiri. Iye sanachite zoipa.—Machitidwe 10:38; 1 Petro 2:21, 22
Koma kodi akanatipulumutsa motani ku uchimo ndi imfa?
33 Iye anayenera kupereka nsembe kwa Mulungu kuti apulumutse anthu abwino. Kale, Mulungu anauza anthu kupereka nsembe ya nyama kaamba ka machimo awo.—Ahebri 7:25, 27
34 Yesu sanapereke nsembe ya nyama. Iye anadzipereka iye mwini kukhala nsembe kwa ife.—Mateyu 20:28; Ahebri 10:12
Kodi mukudziŵa chifukwa chake?