Mmene Tikupulumutsidwira ku Uchimo ndi Imfa
35 Kodi mukukumbukira kuti Adamu, mwamuna woyambirira, anachimwa? Iye anataya moyo ndi paradaiso, ndipo tonsefe timafanso, chifukwa chakuti ndife ana ake.—Aroma 5:12; 3:23
36 Tikatha kupezanso moyo wangwiro umenewu, ngati munthu wina wangwiro anapereka moyo wake kaamba ka ife, kapena anatiombola ku imfa.—1 Akorinto 15:45; Aroma 5:19, 21
37 Yesu anali mwana wa Mulungu. Iye anali munthu wangwiro. Iye sanachimwe.—Ahebri 5:9; 7:26
38 Iye anadzilola kuphedwa ndi anthu amene sanakonde Mulungu.—Machitidwe 2:23
Kumeneku kunali kudzipereka yekha nsembe kaamba ka ife.—1 Timoteo 2:6
39 Yesu anaikidwa m’phanga losemedwa kapena manda. Iye anali wakufa kwa masiku atatu. Kenako Mulungu anam’dzutsa.—Machitidwe 2:24
40 Iye anabwerera kumwamba. Iye tsopano angathe kupempha Mulungu kuthandiza awo amene amamvera Mulungu.—Ahebri 9:24; 1 Yohane 2:1, 2