Mutu 12
Tanthauzo la Ubatizo Wanu
1, 2. (a) Kodi nchifukwa ninji ubatizo wa m’madzi uyenera kukhala wokondweretsa kwa aliyense wa ife? (b) Mwachidule, kodi mukanayankha bwanji mafunso ondandalikidwa pandime 2?
M’chaka cha 29 C.E., Yesu anamizidwa mu Mtsinje Yordano. Yehova iyemwiniyo anali kuwonerera ndipo anasonyeza chivomerezo. (Mat. 3:16, 17) Zaka zitatu ndi theka pambuyo pake, pambuyo pa chiukiriro chake, Yesu anapereka malangizo kwa ophunzira ake, akumati: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi. Chifukwa chake mukani ndi kupanga ophunzira mwa anthu amitundu yonse, mukumawabatiza.” (Mat. 28:18, 19, NW) Kodi mwabatizidwa mogwirizana ndi zimene Yesu pamenepa analangiza? Kapena kodi mukukonzekera kutero?
2 Uliwonse umene ungakhale mkhalidwewo kumvetsetsa bwino ubatizo kuli kofunika. Mafunso ofunikira kupendedwa amaphatikizapo awa: Kodi ubatizo wa Mkristu lerolino uli ndi tanthauzo lofanana ndi uja wa Yesu? Kodi chirichonse chimene Baibulo limanena za ubatizo chimagwira ntchito kwa inu? Kodi nchiyani chimene chimaphatikizidwa m’kukhala ndi moyo mogwirizana ndi chimene ubatizo wa m’madzi wa Mkristu umatanthauza?
Maubatizo Ochitidwa ndi Yohane
3. Kodi ubatizo wa Yohane unali wa ayani okha?
3 Pafupifupi miyezi isanu ndi umodzi Yesu asanabatizidwe, Yohane Mbatizi anapita m’chipululu cha Yudeya, nalalikira: “Tembenukani mitima; chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira.” (Mat. 3:1, 2) Anthu ochokera kuchigawo chonsecho anamva zimene Yohane ananena, naulula poyera machimo awo ndipo anabatizidwa ndi iye m’Yordano. Ubatizo umenewo unali wa Ayuda.—Mac. 13:23, 24; Luka 1:13-16.
4. (a) Kodi nchifukwa ninji Ayuda anafunikira kulapa mofulumira? (b) Kodi nchiyani chinafunika ngati anati adzapewe ‘kubatizidwa ndi moto’?
4 Ayuda amenewo anali ofunikira kulapa mofulumira. M’chaka cha 1513 B.C.E. pa Phiri la Sinai makolo awo anali atalowa m’pangano lamtundu ndi Yehova Mulungu. Koma sanakhale ndi moyo mogwirizana ndi mathayo awo pansi pa pangano limenelo ndipo chotero anatsutsidwa nalo monga ochimwa. Mkhalidwe wawo unali woipa kwambiri. “Tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova” lonenedweratu ndi Malaki linayandikira, ndipo mu 70 C.E. linadza pa Yerusalemu monga chiwonongeko chadzidzidzi. Yohane Mbatizi, pokhala ndi changu cha kulambira kowona chofanana ndi cha Eliya, anatumidwa chiwonongeko chimenecho chisanadze “kukakonzekeretsa anthu kaamba ka Yehova.” Iwo anafunikira kulapa machimo awo ochimwira pangano Lachilamulo ndi kukonzekeretsedwa mu mtima ndi maganizo kuvomereza Mwana wa Mulungu, amene Yehova anali kumtumiza kwa iwo. (Mal. 4:4-6; Luka 1:17, NW; Mac. 19:4) Monga momwe Yohane analongosolera, Mwana wa Mulungu akabatiza ndi mzimu woyera (ubatizo umene ophunzira okhulupirika analandira pa Pentekoste wa 33 C.E.) ndipo ndi moto (umene unadza pa osalapawo monga chiwonongeko mu 70 C.E.). (Luka 3:16) Kupewa mwachindunji kukomana ndi ‘ubatizo wa moto’ umenewo Ayuda a m’zaka za zana loyamba amenewo anafunikira kubatizidwa m’madzi kusonyeza kulapa kwawo, ndipo anafunikira kukhala ophunzira a Yesu Kristu pamene mwayi umenewu unatseguka.
5. (a) Pamene Yesu anadza kudzabatizidwa, kodi nchifukwa ninji Yohane anakaikira? (b) Kodi nchiyani chinasonyezedwa ndi ubatizo wa m’madzi wa Yesu? (c) Kodi Yesu anali wotsimikiza motani ponena za kukwaniritsa chifuniro cha Mulungu kwa iye?
5 Pakati pa awo amene anadza kwa Yohane kuzabatizidwa panali Yesu iyemwiniyo. Koma chifukwa ninji? Yohane anadziwa kuti Yesu analibe machimo akuwaulula, ndipo chotero anati: “Ndiyenera ine kubatizidwa ndi inu, ndipo inu mudza kwa ine kodi?” Koma ubatizo wa Yesu unali kusonyeza kanthu kena kosiyana. Chotero anayankha: “Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero.” (Mat. 3:13-15) Ubatizo wa Yesu sukanachitira chizindikiro kulapa uchimo; ndiponso iye sanafunikire kudzipatulira iyemwini kwa Mulungu, chifukwa chakuti anali chiwalo chamtundu wodzipatulira kale kwa Yehova. M’malo mwake, ubatizo wake, atapeza ukulu Wachiyuda pa zaka 30 zakubadwa, unasonyeza kudzionetsera kwa iyemwini kwa Atate wake wakumwamba kuchita chifuniro chake chowonjezereka. Chifuniro cha Mulungu kwa “munthu, Kristu Yesu,” chinaphatikizapo ntchito yogwirizana ndi Ufumu, ndiponso nsembe ya moyo wake waumunthu wangwiro monga dipo ndi monga maziko apangano latsopano. (Luka 8:1; 17:20, 21; Aheb. 10:5-10; Mat. 20:28; 26:28; 1 Tim. 2:5, 6) Yesu anasonyeza, motsimikizira kwambiri chimene ubatizo wake wam’madzi unasonyeza. Sanadzilole iyemwini kupambukitsidwira ku zinthu zina. Kufikira mapeto a moyo wake wapadziko lapansi anamamatira kukuchita chifuniro cha Mulungu.—Yoh 4:34.
Ubatizo mu Imfa
6. Kodi ndiubatizo wina wotani umene Yesu analowamo ndipo mkati mwa nyengo iti?
6 Mogwirizana ndi chimene ubatizo wa Yesu m’madzi unasonyeza, iye analowanso ubatizo wina. Anadziwa kuti gawo loikidwa pamaso pake ndi Mulungu likatsogolera kukupereka moyo wake waumunthu monga nsembe koma kuti akaukitsidwa mu mzimu patsiku lachitatu. Ananena za iyi kukhala ubatizo. “Ubatizo” umenewu unayamba mu 29 C.E. koma sunatsirizidwe kufikira atafadi ndi kuukitsidwa. Chotero pafupifupi zaka zitatu pambuyo pa kumizidwa kwake m’madzi akananena moyenerera kuti: “Ndiri ndi ubatizo ndikabatizidwe nawo; ndipo ndikanikizidwa ine kufikira ukatsirizidwa!”—Luka 12:50.
7. (a) Kodi ndaninso amene amabatizidwa mu imfa? (b) Kodi ndani amachita ubatizo umenewu?
7 Awo amene adzalamulira limodzi ndi Kristu mu Ufumu wakumwamba ayenera mofananamo kubatizidwa mu imfa. (Marko 10:37-40; Akol. 2:12) Pa imfa yawo amasiya moyo wawo waumunthu kwa muyaya, monga momwe anachitira Yesu. Ndipo pa chiukiriro chawo amagwirizana naye mu ulamuliro wakumwamba. Uwu ndiwo ubatizo wochitidwa, osati ndi munthu aliyense, koma ndi Mulungu kupyolera mwa Mwana wake wakumwamba.
8. Kodi ‘kubatizidwa mwa Kristu’ kwaonso kumatanthauzanji?
8 Awo obatizidwa mu imfa ya Yesu amanenedwanso kukhala “obatizidwa mwa Kristu Yesu.” Kupyolera mwa mzimu woyera wotsanuliridwa mwa Kristu amafikira kukhala ogwirizanitsidwa naye, mutu wawo, monga ziwalo zampingo wa odzozedwa ndi mzimu, “thupi” lake. Chifukwa chakuti mzimu umenewo umawakhozetsa kusonyeza umunthu wapamwamba wa Kristu, kunganenedwe za iwo kuti iwo onse afikira kukhala “mmodzi mwa Kristu Yesu.”—Aroma 6:3-5; 1 Akor. 12:13; Agal. 3:27, 28; Mac. 2:32, 33.
Ubatizo wa m’Madzi wa Ophunzira Achikristu
9. (a) Kodi ndiliti pamene ubatizo mwa mpagidwe wolamulidwa pa Mateyu 28:19 unachitika kwa nthawi yoyamba? (b) Mogwiritsira ntchito mafunso ndi malemba operekedwa limodzi ndi ndime ino, pendani chimene Yesu anatanthauza kuti oyembekezera ubatizo ayenera kuzindikira.
9 Ophunzira oyamba a Yesu anabatizidwa m’madzi ndi Yohane ndiyeno analozeredwa kwa Yesu monga ziwalo zoyembekezeredwa za mkwatibwi wake wauzimu. (Yoh. 3:25-30) Pansi pa chitsogozo cha Yesu iwo anachitanso ubatizo, umene unali ndi tanthauzo lofanana ndi Ubatizo wa Yohane. (Yoh. 4:1-3) Komabe, kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., anayamba kukwaniritsa lamulo lakubatiza “m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la mzimu woyera.” (Mat. 28:19) Mudzakupeza kukhala kopindulitsa kwambiri kupenda chimene umenewu umatanthauza, mounikiridwa ndi malemba olembedwa limodzi ndi mafunso otsatirawa:
Kubatizidwa “m’dzina la Atate,” kodi nchiyani chimene munthuyo ayenera kuzindikira ponena za Atate? (2 Maf. 19:15; Sal. 3:8; 73:28; Yes. 6:3; Aroma 15:6; Aheb. 12:9; Yak. 1:17)
Kodi ubatizo m’dzina “la Mwana” umafunikiritsa kuvomereza chiyani? (Mat. 16:16, 24; Afil. 2:9-11; Aheb. 5:9, 10)
Kodi nchiyani chimene munthu ayenera kukhulupirira kuti abatizidwe m’dzina “la mzimu woyera”? (Luka 11:13; Yoh. 14:16, 17; Mac. 1:8; 10:38; Agal. 5:22, 23; 2 Pet. 1:21)
10. (a) Kodi nchiyani chinasonyezedwa ndi ubatizo wa m’madzi Wachikristu lerolino? (b) Kodi ndimotani mmene wasiyanira ndi ubatizo wa Yesu iyemwiniyo? (c) Pamene anthu oyeneretsedwa Mwamalemba akubatizidwa, kodi iwo amafikira kukhala chiyani?
10 Oyambirira kubatizidwa mogwirizana ndi malangizo amenewo operekedwa ndi Yesu anali Ayuda (ndi otembenukira ku Chiyuda), amene monga mtundu anali kale odzipatulira kwa Mulungu ndipo anasonyezedwa chiyanjo chapadera ndi iye kufikira 36 C.E. Komabe, pamene mwayi wa kukhala wophunzira Wachikristu unaphatikizapo Asamariya ndi Akunja anthuwo asanabatizidwe anafunikira kupanga kudzipatulira kotheratu kwa Yehova kumtumikira monga ophunzira a Mwana wake. Kwa onse, kuphatikizapo Ayuda, iri lapitirizabe kukhala tanthauzo laubatizo wa mmadzi Wachikristu kufikira ku tsiku lathu. “Ubatizo umodzi” umenewu umagwira ntchito kwa onse amene amakhala Akristu owona. Chotero amafikira kukhala mboni Zachikristu za Yehova, aminisitala oikidwa a Mulungu.—Aef. 4:5; 2 Akor. 6:3, 4.
11. (a) Kodi ubatizo wa m’madzi Wachikristu umalingana nchiyani, ndipo motani? (b) Chotero kodi Mkristu amapulumutsidwa ku chiyani?
11 Ubatizo wotero uli wofunika kwambiri m’maso mwa Mulungu. Pambuyo pa kutchula kumangidwa kwa chingalawa kochitidwa ndi Nowa m’chimene iye ndi banja lake anasungidwiramo kupyola Chigumula, mtumwi Petro anasonyeza za uwu. Analemba: “Chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake lathupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu.” (1 Pet. 3:21) Chingalawa chinali umboni weniweni wakuti Nowa anali atadzipatulira kuchita chifuniro cha Mulungu ndi kuti panthawiyo anali atachita ntchito yogawiridwa ndi Mulungu mokhulupirika. Ichi chinatsogolera kukusungidwa kwake. Mwanjira yofananayo, awo odzipatulira kwa Yehova pamaziko a chikhulupiriro mwa Kristu woukitsidwayo, obatizidwa kusonyeza chimenecho ndi amene panthawiyo amapitirizabe kuchita chifuniro cha Mulungu kaamba ka atumiki ake m’tsiku lathu amapulumutsidwa kudziko loipa lamakonoli. (Agal. 1:3, 4) Iwo sakukhalanso paulendo wa kuchiwonongeko limodzi ndi mbali yotsala yadziko. Iwo apulumutsidwa ku chimenechi ndipo apatsidwa chikumbumtima chabwino ndi Mulungu.
Kukhala ndi Moyo Mogwirizana ndi Mathayo Athu
12. Kodi nchifukwa ninji kubatizidwa kwa munthu mwa iko kokha sikuli chitsimikiziro cha chipulumutso?
12 Kukakhala kulakwa kunena kuti kubatizidwa mwa iko kokha ndiko chitsimikiziro cha chipulumutso. Kumakhala ndi mtengo kokha ngati munthuyo wadzipatuliradi kwa Yehova kudzera mwa Yesu Kristu ndipo pambuyo pake achita chifuniro cha Mulungu, mokhulupirika kufikira mapeto.—Mat. 24:13.
13. (a) Kodi chifuniro cha Mulungu nchotani ponena za njira imene Akristu obatizidwa agwiritsirira ntchito miyoyo yawo? (b) Kodi kupanga ophunzira Achikristu kuyenera kukhala kofunika motani m’miyoyo yathu?
13 Chifuniro cha Mulungu kwa Yesu chinaphatikizapo mmene anagwiritsirira ntchito moyo wake monga munthu. Unali kudzaperekedwa mu imfa monga nsembe. Kwa ife matupi athu ayenera kuperekedwa kwa Mulungu, kukhala ndi moyo wodzimana. Ayenera kugwiritsiridwa ntchito kokha m’kuchitidwa kwa chifuniro cha Mulungu. (Aroma 12:1, 2) Ndithudi ife sitikakhala tikutero ngati, ngakhale mwakamodzi kamodzi, mwadala tinadzisungira mofanana ndi dziko lotizinga kapena ngati tisumika miyoyo yathu pazinthu zadyera pamene tikupereka utumiki wachiphamaso chabe kwa Mulungu. (1 Pet. 4:1-3; 1 Yoh. 2:15-17) Pamene Myuda wina anafunsa chimene anayenera kuchita kuti athe kupeza moyo wosatha, Yesu anamkumbutsa za kufunika kwa kukhala ndi moyo woyera mwa makhalidwe, ndiyeno anasonyeza kufunika kwa kupanga ophunzira Achikristu, kukhala wotsatira wa Yesu, chinthu chachikulu m’moyo. Sikunayenera kutenga malo achiwiri kukulondola zinthu zakuthupi.—Mat. 19:16-21.
14. (a) Kodi ndithayo lotani la Ufumu limene Akristu onse ali nalo? (b) Monga momwe zithunzi za patsamba 101 zikusonyezera, kodi nziti zimene ziri zina za njira zogwira mtima zochitira? (c) Ngati tiridi ndi mbali m’ntchito yotero mwa mtima wonse, kodi chimenecho chiri umboni wachiyani?
14 Kuyeneranso kukumbukiridwa kuti chifuniro cha Mulungu kwa Yesu chinaphatikizapo ntchito yofunika ya Ufumu. Yesu, iyemwiniyo anadzozedwera kukhala Mfumu. Koma akali padziko lapansi analinso mboni yachangu ya Ufumu. Tiri ndi ntchito ya kuchitira umboni yofananayo ya kuichita ndipo tiri ndi chifukwa chirichonse chokhalira ndi mbali mu iyo ndi mtima wonse. Mwakutero tikusonyeza chiyamikiro chathu cha ulamuliro wa Yehova ndi chikondi chathu pamunthu mnzathu. Ndiponso tikusonyeza kuti tiri ogwirizana ndi olambira anzathu padziko lonse lapansi, amenenso onse ali mboni za Ufumu, m’kuchirimika kulinga ku chonulirapo cha moyo wosatha m’gawo la Ufumu umenewo.
Makambitsirano Openda
● Kodi ndikufanana ndikusiyana kotani kumene kulipo pakati pa ubatizo wa Yesu ndi ubatizo wa m’madzi lerolino?
● Kodi ubatizo wa Yohane unali wa ayani? Kodi ndani amene amabatizidwa mu imfa? Kodi ndani amene “amabatizidwa mwa Kristu Yesu”?
● Kodi nchiyani chimene chikuphatikizidwa m’kukhala ndi moyo mogwirizana ndi mathayo aubatizo wa m’madzi Wachikristu?
[Bokosi/Zithunzi patsamba 101]
Kodi Mumalengezera Ufumu m’Njira Zotani?
Kunyumba ndi nyumba
Mwakubwereza kucheza ndi okondwerera
Pa maphunziro Abaibulo a panyumba
Pa makwalala
Kwa anzanu apasukulu
Kwa antchito anzanu