Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • uw mutu 24 tsamba 184-191
  • Chifuno cha Yehova Chipeza Chipambano Chaulemerero

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifuno cha Yehova Chipeza Chipambano Chaulemerero
  • Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mkhalidwe Woyanjidwa wa Israyeli
  • Yehova Amagwirizanitsa Anthu Ake
  • Kusonkhanitsa “Zinthu za Padziko Lapansi”
  • Cholinga cha Yehova Chikwaniritsidwa ndi Ulemerero
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Aliyense Adzakhala Paufulu
    Nsanja ya Olonda—1999
  • “Mulungu Anatikonda Ife Kotero”
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Mulungu wa “Kalonga wa Mtendere” Akhala “Zinthu Zonse kwa Aliyense”
    Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
Onani Zambiri
Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
uw mutu 24 tsamba 184-191

Mutu 24

Chifuno cha Yehova Chipeza Chipambano Chaulemerero

1, 2. (a) Kodi nchiyani chimene chiri chifuno cha Yehova ponena za zolengedwa zake zanzeru? (b) Kodi ndani amene anaphatikizidwa m’banja logwirizana la Mulungu la olambira? (c) Ponena za ichi, kodi ndifunso laumwini lotani limene liyenera kupendedwa?

CHOLENGEDWA chonse chaluntha chogwirizanitsidwa m’kulambira kowona ndipo onse a iwo osangalala ndi Ufulu waulemerero wa ana a Mulungu—chimenecho ndicho chifuno chanzeru ndi chachikondi cha Yehova. Ndichonso chimene okonda chilungamo onse amakhumba mwaphamphu.

2 Yehova anayamba kukwaniritsa chifuno chachikulu ichi pamene anayamba ntchito zake zachilengedwe. Cholengedwa chake choyamba chinali Mwana wamwamuna, amene anatsimikizira kukhala “chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake.” (Aheb. 1:1-3) Ameneyu anali wapadera, pokhala wolengedwa ndi Mulungu mwiniyo. Kupyolera mwa iye ana ena anachititsidwa kukhalako—choyamba, angelo m’miyamba, ndiyeno munthu padziko lapansi. (Yobu 38:7; Luka 3:38) Ana onsewa anapanga banja limodzi lachilengedwe chonse. Kwa iwo onse Yehova anali Mulungu, munthu yekha woyenera kulambiridwa. Anali Wolamulira wa Chilengedwe chonse. Analinso Atate wawo wachikondi. Kodi iye alinso Atate wanu, ndipo kodi inu muli mmodzi wa ana ake? Ha ndi unansi wa mtengo wapatali chotani nanga mmene umenewo ungakhalire!

3. (a) Kodi nchifukwa ninji panalibe ndi mmodzi wa ife anali mwana wa Mulungu pa kubadwa? (b) Koma kodi ndimakonzedwe achikondi otani amene Yehova anapanga kaamba ka mbadwa za Adamu?

3 Komabe, tiyenera kuyang’anizana ndi chenicheni chakuti pamene makolo athu aumunthu oyamba anaweruziridwa ku imfa monga ochimwa adala, anachotsedwa mu Edene nakanidwa ndi Mulungu. Analeka kukhala mbali ya banja lachilengedwe chonse la Yehova. (Gen. 3:22-24; yerekezerani ndi Deuteronomo 32:4, 5.) Tonsefe, chifukwa ndife mbadwa za Adamu wochimwayo, tabadwa ndi zikhoterero zauchimo. Popeza tiri mbadwa za makolo ochotsedwa m’banja la Mulungu, sitingakhoze kudzinenera kukhala ana a Mulungu pamaziko okha a kubadwa monga anthu. Koma Yehova anadziwa kuti ena ochokera pakati pa mbadwa za Adamu akakonda chilungamo, ndipo mwachikondi Iye anapanga makonzedwe mwa amene amenewa akanapezera ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.—Aroma 8:20, 21.

Mkhalidwe Woyanjidwa wa Israyeli

4. (a) Kodi Aisrayeli anali “ana” a Mulungu pa maziko otani? (b) Kodi uku sikunatanthauze chiyani?

4 Zaka zokwanira 2,500 pambuyo pa kulengedwa kwa Adamu, Yehova kachiwirinso anapereka mwayi kwa anthu ena wa kukhala ndi unansi naye monga ana ake. Mogwirizana ndi pangano lake ndi Abrahamu, Yehova anasankha Israyeli kukhala anthu ake. Chotero, kwa Farao wa Igupto, analankhula za Israyeli monga “mwana wanga.” (Eks. 4:22, 23; Gen. 12:1, 2) Pambuyo pake anapatsa Israyeli Chilamulo chake pa Phiri la Sinai, napanga anthuwo kukhala mtundu nawagwiritsira ntchito mogwirizana ndi chifuno chake. Monga mtundu, anali kulankhulidwa monga “ana” a Mulungu chifukwa chakuti anali “chuma chapadera” cha Yehova. (Deut. 14:1, 2; Yes. 43:1) Ndiponso, chifukwa cha zochita zake zapadera ndi anthu ena mkati mwa mtunduwo, Yehova anasonya kwa anthuwo monga ana. (1 Mbiri 22:9, 10) Kaimidwe aka kanali kozikidwa pa unansi wa pangano ndi Mulungu. Komabe, iko sikanatanthauze, kuti anthuwo anasangalala ndi ufulu waulemerero umene Adamu anali nawo monga mwana wa Mulungu. Iwo anali chikhalirebe mu ukapolo ku uchimo ndi imfa.

5. Kodi ndimotani mmene Aisrayeli anatayira kaimidwe kawo kapadera ndi Mulungu?

5 Komabe, monga ana anali ndi kaimidwe koyanjidwa ndi Mulungu. Iwo analinso ndi thayo la kulemekeza Atate wawo ndi kugwira ntchito mogwirizana ndi chifuno chake. Yesu anagogomezera kufunika kwa kukwaniritsa kwawo thayo limenelo—osati kokha kudzinenera kuti Mulungu anali Atate wawo, koma ‘kudzitsimikizira’ kukhala ana ake. (Mat. 5:43-48; Mal. 1:6) Komabe, Ayuda monga mtundu analephera pamfundoyi. Chotero, mkati mwa chaka chotsirizira cha uminisitala wa padziko lapansi wa Yesu, pamene Ayuda amene anali kufunafuna kupha Yesu analengeza kuti, “tiri naye Atate mmodzi ndiye Mulungu,” Yesu anasonyeza mwamphamvu kuti zochita zawo ndi mzimu umene anasonyeza zinatsutsana ndi kudzinenera kumeneko. (Yoh 8:41, 44, 47) Mu 33 C.E. pangano la Chilamulo linathetsedwa ndi Mulungu, ndipo maziko a unansi wapadera umene Israyeli anasangalala nawo anatha. Komabe, Yehova sanaleke kukhala ndi awo amene anawavomereza monga ana pakati pa anthu.

Yehova Amagwirizanitsa Anthu Ake

6. Kodi ndi “makonzedwe” otani amene Paulo anawalongosola pa Aefeso 1:9, 10, ndipo cholinga chake nchiyani?

6 Kwa Akristu mu Efeso mtumwi Paulo analemba ponena za programu ya Yehova ya kugwirizanitsira anthu ake—kakonzedwe ka Mulungu mwa kamene osonyeza chikhulupiriro angakhalire ziwalo zokondedwa za banja Lake, kumati: “[Mulungu] anatizindikiritsa ife chinsinsi cha chifuniro chake, monga kunamkomera ndi monga anatitsimikiza mtima kale mwaiye, kuti pa makonzedwe [ulamuliro wabanja] amakwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Kristu, zakumwamba, ndi za padziko.” (Aef. 1:9, 10) “Makonzedwe” amenewa azikika pa Yesu Kristu. Kupyolera mwa iye, anthu amachititsidwa kukhala mu mkhalidwe wovomerezeka pamaso pa Mulungu—ena m’chiyembekezo cha kukhala kumwamba; ena, padziko lapansi—kutumikira mogwirizana ndi ana aungelo a Mulungu amene atsimikizira kukhala okhulupirika kwa Yehova.

7. Kodi nchiyani chimene chiri “zinthu zam’mwamba,” ndipo kodi kusonkhanitsidwa pamodzi kumatanthauzanji kwa izo?

7 Choyamba, kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., chisamaliro chinaperekedwa ku “zakumwamba,” ndiko kuti, awo amene akakhala olowa nyumba anzake Akristu mu Ufumu wakumwamba. Pamaziko a chikhulupiriro chawo mu mtengo wa nsembe ya Yesu, analengezedwa kukhala olungama ndi Mulungu. (Aroma 5:1, 2) Ndiyeno iwo “anabadwa mwatsopano,” kapena kubadwa monga ana a Mulungu okhala ndi chiyembekezo cha moyo wam’mwamba. (Yoh. 3:3; 1:12, 13) Ndi amenewa monga mtundu wauzimu Mulungu anapanga nawo pangano latsopano. M’nthawi yokwanira, onse Ayuda ndi Akunja omwe anayenera anaphatikizidwamo, ndipo amenewa akakwanira chionkhetso cha 144 000.—Agal. 3:26-29; Chiv. 14:1.

8. Kodi ndimotani mmene unansi wa olowa nyumba a Ufumu ndi Atate uliri poyerekezera ndi Ayuda okhala pansi pa Chilamulo cha Mose?

8 Ngakhale kuli kwakuti akali chikhalirebe opanda ungwiro m’thupi, otsalira a olowa nyumba a Ufumu wakumwamba otero amasangalala ndi unansi wamtengo wapatali ndi wapafupi ndi Atate. Ponena za izi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza mzimu wa Mwana wake alowe m’mitima yathu, wofuula Abba, Atate. Kotero kuti sulinso kapolo, koma mwana; koma ngati mwana, wolowa nyumbanso mwa Mulungu.” (Agal. 4:6, 7) Mawu Achiaramu amenewo akuti “Abba” amatanthauza “atate,” koma ali mu mpangidwe wa kanenedwe kolemekeza—ogwiritsiridwa ntchito ndi mwana wachichepere kwa atate wake. Chifukwa cha kupambana kwa nsembe ya Yesu ndi chisomo cha Mulungu mwini, Akristu odzozedwa ndi mzimu amenewa amasangalala ndi unansi ndi Mulungu umene uli woyandikana kwambiri koposa uliwonse umene unali wothekera kwa anthu opanda ungwiro pansi pa Chilamulo. Komabe, chimene chiripatsogolo pawo chiri ngakhale chabwinodi koposerapo.

9. Kodi kukwaniritsidwa kotheratu kwa kukhala kwawo ana ake kumatanthauzanji?

9 Ngati iwo atsimikizira kukhala okhulupirika kufikira imfa, iwo amalandira kukwaniritsidwa kotheratu kwa kukhala kwawo ana mwa chiukiriro ku moyo wosakhoza kufa kumwamba. Kumeneko adzakhala ndi mwayi wa kutumikira mogwirizana pamaso penipeni pa Yehova Mulungu. Chiwerengero chochepa kwambiri cha ana a Mulungu amenewa chikali chikhalirebe padziko lapansi.—Aroma 8:14, 23; 1 Yoh. 3:1, 2.

Kusonkhanitsa “Zinthu za Padziko Lapansi”

10. (a) Kodi nchiyani chimene chiri “zinthu za padziko lapansi,” ndipo ndi kuyambira liti pamene akhala akusonkhanitsidwa m’chigwirizano cha kulambira? (b) Kodi nchiyani chimene chiri unansi wawo ndi Yehova?

10 “Makonzedwe” ofananawo amene amatheketsa anthu kusonkhanitsidwira m’banja la Mulungu ndi lingaliro la moyo wakumwamba amaperekanso chisamaliro pa “zinthu za padziko lapansi.” Makamaka kuyambira 1935 C.E. anthu okhulupirira nsembe ya Kristu akhala akusonkhanitsidwa ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya padziko lapansi. Iwo amakuza dzina la Yehova ndi kukweza kulambiridwa kwake, phewa ndi phewa ndi otsalira a kagulu ka odzozedwa. (Zef. 3:9; Yes. 2:2, 3) Molemekeza kwambiri, amenewanso, amatcha Yehova “Atate,” akumamzindikira kukhala Magwero a moyo, ndipo amayesayesa mwaphamphu kusonyeza mikhalidwe yake monga momwe akuyembekezerera ana ake kuchita. Amasangalala ndi kaimidwe kovomerezeka pamaso pake pamaziko a chikhulupiriro chawo m’mwazi wokhetsedwa wa Yesu. (Mat. 6:9; Chiv. 7:9, 14) Koma iwo amadziwa kuti chisangalalo cha kukhala ovomerezedwa kotheratu ndi Mulungu monga ana ake chikali kutsogolo kwawo.

11. (a) Kodi nlonjezo lotani pa Aroma 8:19-21 limene likuperekedwa kwa anthu? (b) Kodi nchiyani chimene chiri “kuvumbulutsidwa kwa ana a Mulungu” kumene iwo akuyembekezera mwaphamphu?

11 Monga momwe kwasonyezedwera pa Aroma 8:19-21, iwo akuyembekezera mwaphamphu “kuvumbulutsidwa kwa ana a Mulungu,” chifukwa chakuti pamenepo nthawi idzafika yakuti a chilengedwe chaumunthu awa “amasulidwa ku ukapolo wachivundi.” “Kuvumbulutsidwa” kumeneko kudzachitika pamene anthu pano padziko lapansi awona umboni wakuti ana odzozedwa ndi mzimu a Mulungu amene apeza mphoto yawo yakumwamba akuchitapo kanthu monga anzawo a Mbuye wolemekezedwa, Yesu Kristu. Ichi chidzasonyezedwa m’kuwonongedwa kwa dongosolo lonse loipa lazinthu, lotsatiridwa ndi madalitso a Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu mu umene “ana a Mulungu” amenewa adzalamulira naye monga mafumu ndi ansembe.—Chiv. 2:26, 27; 20:6.

12. Pambuyo pa chisautso chachikulu, kodi ndi nyimbo iti yachitamando imene ana odzozedwa ndi mzimu opambanawo adzagwirizanamo, ndipo kodi ichi chimatanthauzanji?

12 Ha kudzakhala kosangalalatsa chotani nanga pamene chisautso chachikulu chipita ndipo ana a Mulungu amenewo amene adzakhala atagwirizanitsidwa ndi Kristu aphatikiza mawu awo m’chitamando kwa Mulungu, akumalengeza mokondwera kuti: “Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zowona, Mfumu inu ya nthawi zosatha. Ndani adzakhala wosawopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidawonetsedwa.” (Chiv. 15:3, 4) Inde, mtundu wonse wa anthu, wopangidwa ndi anthu ochokera m’mitundu yonse yakale, adzagwirizana m’kulambira Mulungu wowona. Ngakhale okhala m’manda a chikumbukiro adzaukitsidwa ndi kupatsidwa mpata wa kugwirizanitsa mawu awo m’chitamando kwa Yehova.

13. Kodi padzakhala kusangalala ndiufulu wodabwitsa wotani wa pa nthawi yomweyo kwa opulumuka chisautso chachikulu?

13 Satana Mdyerekezi sadzakhalanso “mulungu wa nthawi ya pansi pano.” Olambira Yehova a pano padziko lapansi sadzafunikiranso kulimbana ndi chisonkhezero chake choipa. (2 Akor. 4:4; Chiv. 20:1-3) Chipembedzo chonyenga sichidzaimiranso molakwa Mulungu wathu wachikondi ndi kukhala monga chisonkhezero chogawanitsa mkati mwa anthu. Atumiki a Mulungu wowona sadzavutikanso ndi chisalungamo ndi kulimidwa pamsana pamanja ndi anthu okhala m’malo a ntchito a boma. Ha ndiufulu wodabwitsa chotani nanga umene ichi chidzatanthauza kwa opyola chisautso chachikulu!

14. Kodi iwo adzamasulidwa mwanjira yotani ku uchimo ndi ziyambukiro zake zonse?

14 Monga “Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake ladziko lapansi,” Yesu Kristu adzagwiritsira ntchito mtengo wa nsembe yake kotero kuti afafanize kotheratu machimo akale a anthu. (Yoh. 1:29) Pamene Yesu analengeza za kukhululukidwa kwa machimo a munthu, padziko lapansi, iye anachiritsanso munthu wokhululukiridwayo monga umboni wa zimenezo. (Mat. 9:1-7) Mofananamo, kuchokera kumwamba iye mozizwitsa adzachiritsa akhungu, agonthi, osalankhula, opunduka mwakuthupi, opunduka mwamaganizo ndi awo okhala ndi mtundu wina uliwonse wa matenda. Pang’ono ndi pang’ono kupyolera mwa kudzichititsa kugwirizana mokhulupirika ndinjira zolungama za Mulungu, anthu onse ofunitsitsa ndi omvera adzachititsa “lamulo lauchimo” kufafanizidwa kotheratu mwa iwo kotero kuti zochita zawo zonse, maganizo awo ndi zikhumbo za mitima yawo zidzakhala zokondweretsa ponse pawiri kwa iwo eni ndi kwa Mulungu. (Aroma 7:21-23; yerekezerani ndi Yesaya 25:7, 8 ndi Chivumbulutso 21:3, 4.) Ulamuliro wa zaka chikwi usanathe, adzakhala atathandizidwa kufikira ungwiro wokwanira waumunthu. Adzakhala omasuka kotheratu ku uchimo ndi ziyambukiro zake zonse zovulaza. Iwo adzasonyeza bwino lomwe ‘chifanizo ndi chifanefane cha Mulungu’ pakati pa Paradaiso wadziko lapansi amene adzakuta mbulumbwa yonseyi.—Gen. 1:26.

15. Pamapeto a Zaka chikwi, kodi nchiyani chimene Kristu adzachita, ndipo ncholinga chotani?

15 Kristu akadzafikitsa mtundu wa anthu ku ungwiro, pamenepo adzabwezera kwa Atate ulamuliro umene unapatsidwa kwa iye kaamba ka ntchito iyi. Monga momwe kudanenedweratu pa 1 Akorinto 15:28: “Pamene zonsezo zagonjetsedwa kwa iye [Mwana], pomwepo Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa iye amene anam’gonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.”

16. Kodi anthu onse angwiro tsopano adzayang’anizana ndi chiyani ndipo chifukwa ninji?

16 Tsopano anthu angwiro adzapatsidwa mpata wa kusonyeza kuti chosankha chawo chosasinthika ndicho kutumikira Mulungu yekha wamoyo ndi wowona kunthawi zonse. Chifukwa chake, asanawalandire monga ana ake kupyolera mwa Yesu Kristu, Yehova adzachititsa anthu angwiro onsewo kuyang’anizana ndi chiyeso chotheratu ndi chotsiriza. Satana ndi ziwanda zake adzamasulidwa kuphompho kuja. Uku sikudzachititsa konse chivulazo chosatha pa awo okondadi Yehova. Koma ali onse amene mosakhulupirika adzilola kutsogoleredwa m’kusamvera Yehova adzawonongedwa kosatha limodzi ndi wopanduka woyambirirayo ndi ziwanda zake.—Chiv. 20:7-10.

17. M’kukwaniritsidwa kwa chifuno cha Yehova, kodi ndinkhalidwe wotani umene kachiwirinso udzakhala pakati pa chilengedwe chake chonse chaluntha?

17 Tsopano Yehova mwachikondi adzawalandira monga ana ake kupyolera mwa Kristu anthu angwiro onse amene apambana chiyeso chotsiriza ndi chotha makani chimenecho. Pamenepo adzakhala ndi phande lokwanira mu “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Potsirizira pake iwo adzakhala mbali ya banja logwirizana, lachilengedwe chonse la Mulungu, kwa amene onsewo Yehova adzakhala Mulungu yekha, Wolamulira Wachilengedwe chonse, ndi Atate wawo wachikondi kosatha. Pamenepa cholengedwa cha luntha chonse cha Yehova, m’mwamba ndi padziko lapansi, kachiwirinso chidzakhala chogwirizanitsidwa m’kulambiridwa kwa Mulungu mmodzi yekha wowona.

Makambitsirano Openda

● Chipanduko cha mu Edene chisanachitike, kodi ndiunansi wotani umene olambira onse a Yehova anali nawo kwa iye?

● Kodi ndithayo lotani limene liri pa awo amene ali ana a Mulungu?

● Kodi ndani lerolino amene ali ana a Mulungu? Kodi ndaninso adzakhala ana a Mulungu, ndipo kodi izi zikugwirizana motani ndi chifuno cha Yehova chonena za kulambira kogwirizana?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena