Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
KODI munthu wina aliyense popanda kukayikira angatchedwe kuti munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako? Kodi mumayeza motani ukulu wamunthu? Mwanzeru zake zankhondo? nyonga zake zakuthupi? luso lake la maganizo?
Wolemba mbiri H. G. Wells anati ukulu wa munthu ungayezedwe ndi ‘chimene anasiya kuti chikule, ndi kuti kaya iye anayambitsa ena kuganiza ziganizo zatsopano mwamphamvu zimene zinalondola zochita zake.’ Ngakhale kuti sanadzinenere kukhala Mkristu, Wells akuvomereza kuti: “Mwa mapendedwe ameneŵa Yesu aposa onse.”
Alexander Wamkulu, Charlemagne (wotchedwa kuti “Wamkulu” ngakhale munthaŵi ya moyo wake) ndi Napoleon Bonaparte anali olamulira amphamvu. Mwa kukhalapo kwawo kochititsa mantha, anagwiritsira ntchito chisonkhezero chachikulu pa awo amene anawalamulira. Komabe, Napoleon akusimbidwa kukhala atanena kuti: “Yesu Kristu wasonkhezera ndi kulamulira anthu Ake popanda kukhalapo Kwake kwakuthupi kowoneka.”
Mwa ziphunzitso zake zamphamvu ndi njira imene anakhala ndi moyo mogwirizana nazo, Yesu mwamphamvu wasonkhezera mitima ya anthu kwapafupifupi zaka zikwi ziŵiri. Monga momwe wolemba wina ananenera molondola kuti: “Magulu ankhondo onse amene anaguba, ndi magulu ankhondo onse apamadzi amene anaumbidwa, ndi nyumba zonse zamalamulo zimene zinakhalako, mafumu onse amene analamulira, ataikidwa pamodzi sanasonkhezere miyoyo ya anthu mwamphamvu chotero padziko lino lapansi.”
Munthu wa Mumbiri
Komabe, mwachilendo, ena amanena kuti Yesu sanakhaleko—kuti iye, m’chenicheni, ali munthu wopekedwa wa anthu a m’zaka za zana loyamba. Poyankha zikayikiro zoterozo, wolemba mbiri wolemekezedwayo Will Durant akutsutsa kuti: “Kunena kuti anthu ena oŵerengeka chabe mumbadwo umodzi ayenera kukhala atapeka munthu wamphamvu ndi wosonkhezera kwambiri chotero, wolemekezeka ndi masomphenya osonkhezera kwambiri a ubale waumunthu, kukakhala chozizwitsa chosatheka konse choposa cholembedwa chirichonse m’Mauthenga Abwino.”
Dzifunseni kuti: Kodi munthu amene sanayambe wakhalako akanasonkhezera mbiri ya anthu mwapadera chotero? Bukhu lakuti The Historians’ History of the World linati: “Zotulukapo za mumbiri za zochita za [Yesu] zinali zofunika kwambiri, ngakhale palingaliro lenileni lakudziko, koposa zochita za munthu wina aliyense wa mumbiri. Nyengo yatsopano, yozindikiridwa ndi kutsungula kwakukulu kwa dziko, ikuyambira pakubadwa kwake.”
Inde, taganizani za iko. Lerolino ngakhale makalendala amazikidwa pachaka chimene Yesu analingaliridwa kukhala atabadwa. “Madeti a tsiku limenelo lisanakhale amalembedwa kuti B.C., kapena before Christ [Kristu asakhale],” imafotokoza motero The World Book Encyclopedia. “Madeti a pambuyo pa chakacho amalembedwa kuti A.D., kapena anno Domini (m’chaka cha Ambuye wathu).”
Komabe, osuliza, amasonyeza kuti zonse zimene tikudziŵa ponena za Yesu zimapezeka m’Baibulo. Palibe zolembedwa zina zapanthaŵi imodzimodziyo zonena za iye, iwo amatero. Ngakhale H. G. Wells analemba kuti: “Olemba mbiri amakedzana Achiroma ananyalanyaza Yesu kotheratu; sanasiye chizindikiro chirichonse pazolembera za mumbiri za munthaŵi yake.” Koma kodi zimenezi nzowona?
Ngakhale kuti umboni wonena za Yesu Kristu wopangidwa ndi olemba mbiri adziko oyambilira uli wochepa, umboni wotero ulipo. Cornelius Tacitus, wolemba mbiri Wachiroma wolemekezedwa wa m’zaka za zana loyamba, analemba kuti: “Dzinalo [Mkristu] latengedwa kwa Kristu, amene kazembeyo Pontiyo Pilato anapha muulamuliro wa Tiberiyo.” Seutonius ndi Pliny Wamng’ono, olemba ena Achiroma anthaŵiyo, nawonso anachitira umboni za Kristu. Ndiponso, Flavius Josephus, wolemba mbiri Wachiyuda wa m’zaka za zana loyamba, analemba za Yakobo, amene anamdziŵikitsa kukhala “mbale wa Yesu, amene anatchedwa Kristu.”
Motero The New Encyclopædia Britannica imati: “Zolembedwa zoima pazokha zimenezi zimatsimikizira kuti m’nthaŵi zakale ngakhale adani Achikristu sanakayikire kukhala wa mumbiri kwa Yesu, kumene kunachitiridwa mkangano kwanthaŵi yoyamba ndi pamaziko osakwanira kumapeto kwa zaka za zana la 18, mkati mwa zaka za zana la 19 ndi kuchiyambi kwa zaka za zana la 20.”
Komabe, chofunika, zonse zimene zikudziŵidwa ponena za Yesu zinalembedwa ndi otsatira ake a m’zaka za zana loyamba. Malipoti awo asungidwa m’Mauthenga Abwino—mabukhu a Baibulo olembedwa ndi Mateyu, Marko, Luka, ndi Yohane. Kodi zolembedwa zimenezi zimanenanji za kudziŵika kwa Yesu?
Kodi Iye, Analidi Yani?
Mabwenzi a Yesu a m’zaka za zana loyamba anasinkhasinkha za funso limenelo. Pamene anawona Yesu akutontholetsa nyanja ya mphepo ya namondwe mozizwitsa mwa kuidzudzula, iwo anazizwa: “Uyu ndani nanga?” Pambuyo pake, pachochitika china, Yesu anafunsa atumwi ake kuti: ‘Kodi mumati ine ndine yani?’—Marko 4:41; Mateyu 16:15, NW.
Ngati mukanafunsidwa funso limenelo, kodi mukanayankha motani? Kodi Yesu, kwenikweni, anali Mulungu? Lerolino ambiri amanena kuti iye anali. Komabe, mabwenzi ake sanakhulupilire kuti iye anali Mulungu. Yankho la mtumwi Petro kufunso la Yesu linali lakuti: “Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”—Mateyu 16:16.
Yesu sanadzinenere kukhala Mulungu, koma anavomereza kuti anali Mesiya wolonjezedwayo, kapena Kristu. Iye ananenanso kuti anali “Mwana wa Mulungu,” osati Mulungu. (Yohane 4:25, 26; 10:36) Komabe, Baibulo silimanena kuti Yesu anali munthu wofanana ndi wina aliyense. Iye anali munthu wapadera kwambiri chifukwa chakuti analengedwa ndi Mulungu zinthu zonse zisanakhaleko. (Akolose 1:15) Kwa zaka mabiliyoni osaŵerengeka, ngakhale thambo lowoneka lisanalengedwe, Yesu anakhala ndi moyo monga munthu wauzimu kumwamba ndi kusangalala ndi chiyanjano chapafupi ndi Atate wake, Yehova Mulungu, Mlengi Wamkulu.—Miyambo 8:22, 27-31.
Ndiyeno, pafupifupi zaka zikwi ziŵiri zapitazo, Mulungu anatengera moyo wa Mwana wake kumimba ya mkazi wina, ndipo Yesu anafikira kukhala mwana wa Mulungu waumunthu, wobadwa m’njira yozoloŵereka kupyolera mwa mkazi. (Agalatiya 4:4) Pamene Yesu analikukula m’mimba ndi pamene anali kusinkhuka monga kamnyamata, anali wodalira pa awo amene Mulungu anali atasankha kukhala makolo ake apadziko lapansi. Pambuyo pake Yesu anafikira paumunthu wachikulire, ndipo anapatsidwa chikumbukiro chonse chokwanira cha kuyanjana kwake ndi Mulungu kumwamba.—Yohane 8:23; 17:5.
Chimene Chinampangitsa Kukhala Wamkulu Woposa Onse
Chifukwa chakuti anatsanzira mosamalitsa Atate wake wakumwamba, Yesu anali munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako. Monga Mwana wokhulupirika, Yesu anatsanzira Atate wake ndendende kwakuti iye akanauza otsatira ake kuti: ‘Munthu amene wawona ine wawonanso Atate.’ (Yohane 14:9, 10, NW) Mumkhalidwe uliwonse pano padziko lapansi, anachita monga momwe akanachitira Atate wake, Mulungu Wamphamvuyonse. “Sindichita kanthu ka ine ndekha,” Yesu anafotokoza motero, “koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.” (Yohane 8:28) Chotero pamene tiphunzira za moyo wa Yesu Kristu, ife, m’chenicheni, timapeza chithunzithunzi chowonekera bwino cha chimene kwenikweni Mulungu ali.
Motero, ngakhale kuti mtumwi Yohane anavomereza kuti “kulibe munthu anawona Mulungu,” iye akanalemba kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (Yohane 1:18; 1 Yohane 4:8) Yohane akanachita zimenezi chifukwa chakuti anadziŵa za chikondi cha Mulungu kupyolera m’zimene anawona mwa Yesu, amene anali chisonyezero changwiro cha Atate wake. Yesu anali wachifundo, wokoma mtima, wodzichepetsa, ndi wofikirika. Anthu ofooka ndi otsenderezedwa analingalira kukhala akupeza bwino kukhala naye, chimodzimodzinso ndi anthu amitundu yonse—amuna, akazi, ana, achuma, ndi amphaŵi, oweruza, ngakhale ochita machimo aakulu. Ndioipa mitima okha amene sanamkonde.
Ndithudi, Yesu sanaphunzitse chabe otsatira ake kukondana, komanso iye anawasonyeza mmene akanachitira. “Monga ndakonda inu,” iye anatero, ‘inunso [muyenera] kukondana.’ (Yohane 13:34) Kudziŵa “chikondi cha Kristu,” anafotokoza motero mmodzi wa atumwi ake, ‘kuposa mazindikiridwe onse.’ (Aefeso 3:19) Inde, chikondi cha Kristu chosonyezedwacho chimapambana chidziŵitso cha m’mutu ndipo ‘chimasonkhezera’ ena kuchilabadira. (2 Akorinto 5:14) Motero, chitsanzo cha chikondi cha Yesu chopambanacho, mwapadera, ndicho chimene chinampanga kukhala munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako. Chikondi chake chakhudza mitima ya mamiliyoni ambiri mkati monse mwa zaka mazana ambiri ndipo chasonkhezera mitima yawo kaamba ka zabwino.
Komabe, ena angakane kuti: ‘Tawonani maupandu onse amene achitidwa m’dzina la Kristu—Nkhondo Zamtanda, Zizunzo Zankhalwe, ndi nkhondo zimene zachititsa mamiliyoni amene adzinenera kukhala Akristu kuphana wina ndi mnzake ndi anzawo otsutsana nawo.’ Koma chowonadi nchakuti, anthu ameneŵa amalephera kutsimikizira kudzinenera kwawo kukhala otsatira a Yesu. Ziphunzitso zake ndi njira ya moyo zimatsutsa ntchito zawo. Ngakhale m’Hinduyo, Mohandas Gandhi, anasonkhezereka kunena kuti: ‘Ndimakonda Kristu, koma ndimada Akristu chifukwa samakhala ndi moyo monga momwe Yesu anakhalira.’
Pindulani mwa Kuphunzira za Iye
Ndithudi palibe phunziro limene likanakhala lofunika kwambiri lerolino koposa lija la moyo ndi uminisitala za Yesu Kristu. ‘Yang’anani dwii . . . pa Yesu,’ anafulumiza motero mtumwi Paulo. ‘Ndithudi, lingalirani mosamalitsa munthu [ameneyo].’ Ndipo Mulungu mwiniyo analamula ponena za Mwana wake kuti: “Mverani iye.” Zimenezi ndizo zimene bukhuli Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako lidzakuthandizani kuchita.—Ahebri 12:2, 3; Mateyu 17:5.
Kuyesayesa kwapangidwa kusonyeza chochitika chirichonse m’moyo wa Yesu wapadziko lapansi umene walembedwa m’Mauthenga Abwino anayi, kuphatikizapo mawu amene ananena ndi mafanizo ndi zozizwitsa zake. Kufikira kumlingo wothekera, zonse zafotokozedwa mudongosolo la mmene zinachitikira. Pamapeto a mutu uliwonse pali mpambo wa malemba a Baibulo amene mutuwo wazikidwapo. Mukulimbikitsidwa kuŵerenga malemba ameneŵa ndi kuyankha mafunso openda amene agaŵiridwa.
Katswiri wina wa pa Yunivesite ya Chicago posachedwapa ananena kuti: “Zambiri zalembedwa ponena za Yesu m’zaka makumi aŵiri zapitazi koposa zikwi ziŵiri zapitazo.” Komabe pali kufunika kwakukulu kulingalira mwachindunji zolembedwa za Mauthenga Abwino, popeza kuti The Encyclopædia Britannica inati: “Kaŵirikaŵiri wophunzira wamakono wafikira kukhala wotanganitsidwa kwambiri ndi nthanthi zowombana poneza za Yesu ndi Mauthenga Abwino kwakuti wanyalanyaza kupenda magwero aakulu enieniwo.”
Pambuyo pa kulingalira kosamalitsa, kopanda tsankho kwa zolembedwa za Mauthenga Abwino, tiganiza kuti mudzavomereza kuti zochitika zopambana koposa m’mbiri ya anthu zinachitika muulamuliro wa Augusto Kaisara wa Roma, pamene Yesu wa ku Nazarete anawonekera padziko lapansi napereka moyo wake kaamba ka ife.