Ntchito ya Makolo
Kunena zoona, kulera ana kuti akule ndi kukhala abwino m’chitaganya chamakono ndi ntchito yovuta.
U.S. NATIONAL Institute of Mental Health inafalitsa zimene inapeza pa kufufuza makolo amene analingaliridwa kukhala achipambano—amene ana awo, azaka zoposa pa 21, “onse anali achikulire othandiza kwambiri amene mwachionekere anali kusintha popanda vuto malinga ndi chitaganya chathu.” Makolo ameneŵa anafunsidwa: ‘Malinga ndi zimene inu mwapeza, kodi ndi uphungu wabwino wotani umene mungapatse makolo ena?’ Otsatirawa ndiwo mayankho amene ambiri anawapereka: ‘Akondeni kwambiri,’ ‘alangeni mwa njira yothandiza,’ ‘chezani nawo,’ ‘phunzitsani ana anu kudziŵa chabwino ndi choipa,’ ‘kulitsani kulemekezana,’ ‘amvetsereni mosamalitsa,’ ‘alangizeni m’malo mowadzudzula,’ ndipo ‘khalani oona mtima.’
Komabe, makolo sali okha pantchito yokulitsa ana kukhala achikulire oyenera. Aphunzitsi nawonso amathandiza kwambiri pa zimenezi. Phungu wa sukulu wina wachidziŵitso anati: “Cholinga chachikulu cha maphunziro a kusukulu ndicho kuchirikiza makolo kukulitsa ana kukhala achikulire osamala anzeru zokwana, okhwima kuthupi, ndi malingaliro.”
Chotero makolo ndi aphunzitsi ali ndi chonulirapo chimodzi—kukulitsa achichepere amene pambuyo pake adzakhala achikulire okhwima ndi abwino amene amakondwa nawo moyo ndi okhoza kupeza malo owayenera m’chitaganya chimene akukhalamo.
Antchito Anzanu, Osati Opikisana Nawo
Komabe, mavuto amabuka pamene makolo sagwirizana ndi aphunzitsi. Mwachitsanzo, makolo ena samasamala za maphunziro a ana awo; ena amayesa kupikisana ndi aphunzitsi. Pofotokoza mkhalidwe umenewu, magazini Achifrenchi anati: “Mphunzitsi salinso mtsogoleri yekha wa maphunziro a ana. Makolo, amene amalakalaka kuti ana awo apambane, amafufuza mabuku akusukulu, amaweruza ndi kusuliza njira zophunzitsira, ndipo amakwiya msanga chifukwa cha kulephera koyamba kwa mwana wawo.” Machitidwe amenewo angaluluze ukumu wa aphunzitsi.
Mboni za Yehova zimaganiza kuti ana awo amathandizidwa kwambiri pamene makolo agwirizana ndi aphunzitsi, akumafuna kuthandiza m’maphunziro a ana awo mwa njira yogwira ntchito. Iwo amakhulupirira kuti kugwirizana kotero nkofunika kwambiri chifukwa chakuti ntchito yanu ya uphunzitsi yakhala yovuta kwambiri.
Mavuto a Kusukulu Lerolino
Popeza kuti sukulu zimasonyeza mzimu wa chitaganya chimene zilimo, nazonso zimakhudzidwa ndi mavuto a chitaganya chonse. Mavuto a kakhalidwe ka anthu akula mofulumira m’zaka zapitazi. Pofotokoza mikhalidwe ya pasukulu ina ku United States, The New York Times inati: “Ana a sukulu amagona m’kalasi, amawopsezana m’malikole olembedwa mawu otukwana, amanyoza ana a sukulu amene akuchita bwino. . . . Pafupifupi ana a sukulu onse akuchita ndi mavuto onga kusamalira makanda, makolo opanikizika ndi kuthaŵa timagulu ta chiwawa. Patsiku lililonse, pafupifupi chimodzi mwa zigawo zisanu samapezekako kusukulu.”
Limene likuwopsa kwambiri ndi vuto lomakula padziko lonse la chiwawa cha pasukulu. M’malo mwa ndewu za apa ndi apo za kukankhana ndi kumenyana, tsopano pali kuwomberana mfuti ndi kubayana mipeni kwa masiku onse. Zida zafalikira kwambiri, kuukirana kwakhala kowopsa kwambiri, ana akumachita chiwawa mwamsanga pamene akali aang’ono kwambiri.
Ndithudi, si dziko lililonse limene lili ndi mikhalidwe yoipa imeneyo. Komabe, aphunzitsi ambiri padziko lonse amakumana ndi mkhalidwe wotchulidwa m’magazini Achifrenchi a mlungu ndi mlungu otchedwa Le Point: “Mphunzitsi samalemekezedwanso; alibenso mphamvu.”
Kusalemekeza ulamuliro koteroko kukhozadi kuyambukira ana moipa kwambiri. Chotero Mboni za Yehova zimayesa kuphunzitsa ana awo kumvera ndi kulemekeza ulamuliro, mikhalidwe imene kambiri ikusoŵeka kusukulu lerolino.