February
Lachitatu, February 1
Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.—Yak. 4:8.
Kodi munadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa? Ngati ndi choncho ndiye kuti muli pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ubwenziwu ndi chinthu cha mtengo wapatali zedi. Koma ukhoza kusokonekera chifukwa choti tili m’dziko la Satana ndipo ndife ochimwa. Zimenezi zimakhudza mtumiki wa Mulungu wina aliyense. Choncho tiyenera kuyesetsa kuti ubwenzi wathu ndi Yehova uzikhala wolimba. Kodi mungatani kuti Yehova akhale mnzanu weniweni ndipo ubwenzi wanu ukhale wolimba kwambiri? Lemba la Yakobo 4:8, lomwe ndi lemba la tsiku lalero, limanena mmene mungachitire zimenezi. Lembali likusonyeza zinthu ziwiri zimene zimachitika. Tikamayesetsa kuyandikira Mulungu nayenso amachita chimodzimodzi. Kuchita zimenezi mobwerezabwereza kumalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Zotsatira zake n’zakuti Yehova amakhala mnzathu weniweni. Nafenso tingalankhule ngati Yesu amene anati: “Alipo ndithu amene anandituma . . . Ine ndikumudziwa.”—Yoh. 7:28, 29. w15 4/15 3:1, 2
Lachinayi, February 2
Pirirani masautso. Limbikirani kupemphera.—Aroma 12:12.
Taganizirani mmene zingakhalire ngati wachibale wanu atachotsedwa. Tonsefe timadziwa mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi anthu ochotsedwa. (1 Akor. 5:11; 2 Yoh. 10) Nthawi zina tingaone kuti n’zovuta kapenanso zosatheka kutsatira malangizo okhudza ochotsedwa. Koma tiyenera kukhulupirira kuti Yehova akhoza kutipatsa mphamvu kuti titsatire malangizo a m’Baibulo. Choncho ngati takumana ndi vutoli tiziona kuti tili ndi mpata wolimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Kodi pamenepa tikuphunzira kuti tisamakonde achibale athu? Ayi, nkhani si imeneyo. Mfundo ndi yakuti tiyenera kukonda Yehova kuposa aliyense. (Mat. 22:37, 38) Kukonda kwambiri Yehova kungathandizenso achibale athuwo, kaya panopa akutumikira Yehova kapena ayi. Koma ngati kuchotsedwa kwa m’bale wanu kukukupwetekani kwambiri muyenera kufotokozera Yehova nkhawa zanu zonse.—Afil. 4:6, 7. w15 4/15 4:14, 16
Lachisanu, February 3
Timakunyadirani ku mipingo ya Mulungu chifukwa cha kupirira kwanu ndi chikhulupiriro chanu.—2 Ates. 1:4.
Kusangalala ndi zinthu zabwino zimene ena achita kapena zimene ifeyo tachita si kulakwa. Sitichitanso manyazi chifukwa cha zinthu monga banja lathu, chikhalidwe chathu kapena dera limene tinakulira. (Mac. 21:39) Koma kunyada n’kumene kumasokoneza ubwenzi wathu ndi anthu komanso ndi Yehova. Munthu wonyada amakhala wodzikuza ndipo safuna kuuzidwa zochita kapena kulangizidwa. (Sal. 141:5) Munthu wotereyu amadziganizira kwambiri n’kumaona kuti ndi wapamwamba kuposa ena. Yehova amadana kwambiri ndi anthu oterewa. (Ezek. 33:28; Amosi 6:8) Koma Satana amasangalala akamaona anthu akunyada podziwa kuti akutengera khalidwe lake. Satana ayenera kuti anasangalala kwambiri poona anthu monga Nimurodi, Farao ndi Abisalomu akusonyeza mtima wonyada.—Gen. 10:8, 9; Eks. 5:1, 2; 2 Sam. 15:4-6. w15 5/15 2:5, 6
Loweruka, February 4
Mumatambasula dzanja lanu ndi kukhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.—Sal. 145:16.
Potsanzira Atate wake, Khristu ankathandiza anthu kupeza zinthu zimene ankafuna. (1 Akor. 1:24) Sankachita zimenezi pongofuna kusonyeza kuti ali ndi mphamvu. Koma ankafunitsitsa kuthandiza anthu. Taonani zimene zili pa Mateyu 14:14-21. Ophunzira a Yesu anamufunsa zimene angachite kuti apeze chakudya. Mwina iwowo anali ndi njala komanso ankadera nkhawa anthu ochokera kutali amene anayenda wapansi kuti atsatire Yesu. Anthuwo anali atatopa ndipo anali ndi njala. (Mat. 14:13) Kodi Yesu anachita chiyani? Anadyetsa amuna 5,000 komanso akazi ndi ana ambiri pongogwiritsa ntchito mitanda 5 ya mkate ndi nsomba ziwiri. Anthu onsewo “anadya n’kukhuta” ndipo chakudya chimene chinatsala chinadzaza madengu 12. Izi zikusonyeza kuti panali chakudya chambiri. Yesu anawapatsa chakudya chokwanira kuti asavutike ndi njala pa ulendo wawo wautali wobwerera kunyumba zawo.—Luka 9:10-17. w15 6/15 1:8, 9
Lamlungu, February 5
Ana a anthu amayamikira zoipa.—Sal. 12:8.
Chiwerewere n’chofala kwambiri moti munthu angaganize kuti n’zosatheka kukhala woyera. Koma Yehova akhoza kutithandiza kukhala anthu oyera. Popeza ndife anthu ochimwa, zinthu zachiwerewere zingatikope ngati mmene nyambo imakopera nsomba. Choncho tiyenera kusiya msanga ngati tayamba kuganizira zinthu zoipa. Kupanda kutero, maganizo amenewa angatichimwitse mpata ukangopezeka. Paja Baibulo limati: “Chilakolako chikatenga pakati, chimabala tchimo.” (Yak. 1:14, 15) Munthu akhoza kuchita tchimo lalikulu chifukwa choganizira kwambiri zinthu zoipa. Choncho tiyenera kusamala ndi zinthu zimene tayamba kuganizira kuti tipewe chiwerewere ndiponso mavuto amene angatsatire.—Agal. 5:16. w15 6/15 3:1-3
Lolemba, February 6
Chifuniro chanu chichitike . . . pansi pano.—Mat. 6:10.
Pafupifupi zaka 6,000 zapitazo, chifuniro cha Mulungu chinkachitika padzikoli. M’pake kuti Yehova anaona kuti “zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.” (Gen. 1:31) Koma kenako Satana anasiya kumvera Mulungu. Kuyambira nthawi imeneyo, anthu ochepa okha akhala akumvera Mulungu padzikoli. Koma masiku ano, pali a Mboni oposa 8 miliyoni amene amapemphera kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi komanso akuyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi pempheroli. Iwo amayesetsa kukhala ndi khalidwe labwino ndipo amagwira mwakhama ntchito yophunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu. Tipitiriza kupemphera kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padzikoli mpaka nthawi imene adani onse a Ufumu wa Mulungu adzachotsedwe. Pa nthawiyo, tidzaona chifuniro cha Mulungu chikuchitika kwambiri padzikoli ndipo anthu mabiliyoni ambiri adzaukitsidwa. (Yoh. 5:28, 29) Tidzasangalala kwambiri kulandira anzathu amene adzaukitsidwe. w15 6/15 4:15, 17
Lachiwiri, February 7
Ine ndidzalemekeza malo oikapo mapazi anga.—Yes. 60:13.
Ambirife timadziwa kuti paradaiso wauzimu amanena za mtendere ndiponso mgwirizano umene tili nawo ndi Mulungu ndiponso Akhristu anzathu. Komabe paradaiso wauzimu ndi wosiyana ndi kachisi wauzimu. Kachisi wauzimu akuimira zimene Mulungu wakonza kuti tizimulambira. Koma paradaiso wauzimu akuimira mtendere ndiponso mgwirizano umene anthu a Mulungu ali nawo ndipo umasonyeza kuti akutumikira m’kachisi wauzimu. (Mal. 3:18) N’zosangalatsa kuti kuyambira mu 1919, Yehova akulola anthu ochimwafe kugwira naye ntchito yokongoletsa ndiponso kukulitsa paradaiso wauzimu. Kodi inuyo mukugwira nawo ntchitoyi? Kodi mumafunitsitsa kugwirabe ntchito ndi Yehova polemekeza ‘malo oikapo mapazi ake’? w15 7/15 1:10, 11
Lachitatu, February 8
Ndidzadziyeretsa pamaso pawo, kudzera mwa iwe Gogi.—Ezek. 38:16.
Odzozedwa amene ali padzikoli akadzatsala pang’ono kupita kumwamba, Gogi adzaukira anthu a Mulungu. Pa nthawiyo, anthu a Mulunguwo adzaoneka kuti ndi osatetezeka. Koma adzatsatira malangizo amene Mulungu anapereka pa nthawi ya Mfumu Yehosafati akuti: “Ulendo uno simufunikira kumenya nkhondo. Khalani m’malo anu, imani chilili ndi kuona Yehova akukupulumutsani. Inu Ayuda ndi anthu a ku Yerusalemu, musaope kapena kuchita mantha.” (2 Mbiri 20:17) Koma kodi kumwamba kudzachitika chiyani pa nthawiyo? Kumbukirani kuti Gogi adzaukira anthu a Mulungu, odzozedwa amene atsala padzikoli atatsala pang’ono kutengedwa kupita kumwamba. Ndiyeno lemba la Chivumbulutso 17:14 limanena zimene zidzachitike odzozedwa onse ali kumwamba. Limati adani a anthu a Mulungu “adzamenyana ndi Mwanawankhosa, koma pakuti iye ndiye Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, Mwanawankhosayo adzawagonjetsa. Komanso oitanidwa aja, amene ali osankhidwa mwapadera ndi okhulupirika, nawonso adzagonjetsa naye limodzi.” Lembali likusonyeza kuti odzozedwa onse 144,000 limodzi ndi Yesu adzapulumutsa anthu a Mulungu. w15 7/15 2:16
Lachinayi, February 9
Chilichonse chili ndi nthawi yake.—Mlal. 3:1.
Tiyenera kuvala ndiponso kudzikongoletsa mwaulemu pofuna kusonyeza kuti timalemekeza Yehova amene watiitanira ku misonkhano. N’zoona kuti Yehova amafuna kuti anthu asamamangike pa Nyumba ya Ufumu. Koma tiyenera kupewa kutumizirana mauthenga pafoni, kudya, kumwa kapena kuchita chilichonse chimene chingasokoneze ena. Makolo ayenera kuphunzitsa ana awo kuti asamathamangethamange kapena kusewera pa Nyumba ya Ufumu. Kumbukiraninso kuti Yesu anakwiya ataona anthu akugulitsa zinthu m’kachisi ndipo anawathamangitsa. (Yoh. 2:13-17) Nazonso Nyumba za Ufumu si malo ochitirapo malonda koma ndi malo oti tiziphunzitsidwa ndiponso kulambira Yehova. Choncho sitiyenera kuchita zinthu zosemphana ndi cholinga cha Nyumba ya Ufumu.—Yerekezerani ndi Nehemiya 13:7, 8. w15 7/15 4:7, 8
Lachisanu, February 10
Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.—2 Tim. 3:1.
Baibulo limasonyeza kuti zinthu zidzaipiraipira “masiku otsiriza” ano. (2 Tim. 3:1, 13; Mat. 24:21; Chiv. 12:12) Choncho zinthu zipitirizabe kusokonekera m’dzikoli. Koma kodi zinthu zidzaipa kufika pati “chisautso chachikulu” chisanafike? (Chiv. 7:14) Ena angaganize kuti padzakhala nkhondo m’dziko lililonse, chakudya chidzasoweratu kulikonse ndipo m’banja lililonse mudzakhala matenda. Izi zitati zichitike, ngakhale anthu osakhulupirira Baibulo angadziwe kuti maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa. Koma Yesu ananena kuti anthu ambiri sadzadziwa ndipo ‘adzanyalanyaza’ chizindikiro moti azidzangochita zinthu za tsiku ndi tsiku ndipo akamadzazindikira mudzakhala m’mbuyo mwa alendo. (Mat. 24:37-39) Choncho Malemba akusonyeza kuti zinthu sizidzaipa mpaka kufika poti aliyense akhulupirire kuti tili m’masiku otsiriza.—Luka 17:20; 2 Pet. 3:3, 4. w15 8/15 2:6, 7
Loweruka, February 11
Kukoma mtima kwanu kosatha n’kwabwino kuposa moyo.—Sal. 63:3.
Kodi kukonzekera moyo wa m’dziko latsopano kukutanthauza kuti tizikhala moyo wosasangalala panopa? Ayi. Pajatu kutumikira Yehova n’kosangalatsa kwambiri kuposa china chilichonse. Sikuti timatumikira Yehova mokakamizika n’cholinga choti tingopulumuka basi. Tikutero chifukwa chakuti tinalengedwa kuti tizikonda kutumikira Mulungu. Choncho kutsogoleredwa ndi Yehova ndiponso kukhala naye pa ubwenzi n’kumene kumathandiza munthu kukhala wosangalala. (Sal. 63:1, 2) Tikamatumikira Yehova ndi mtima wonse tingapeze madalitso ambiri ngakhale panopa. Kunena zoona, enafe takhala tikulandira madalitso osiyanasiyana kwa nthawi yaitali ndipo taonadi kuti kutumikira Mulungu n’kwabwino kwambiri.—Sal. 1:1-3; Yes. 58:13, 14. w15 8/15 3:16
Lamlungu, February 12
Mwapulumutsidwa kudzera m’chikhulupiriro.—Aef. 2:8.
Chikhulupiriro chingatithandize kuchita zinthu zimene zingaoneke kuti n’zosatheka. (Mat. 21:21, 22) Mwachitsanzo, enafe tinasintha kwambiri makhalidwe athu moti anthu amene ankatidziwa kale amadabwa kwambiri. Yehova anatithandiza kusintha chifukwa chakuti tinasonyeza kuti timamukhulupirira. (Akol. 3:5-10) Chikhulupiriro chinatithandizanso kuti tidzipereke kwa Mulungu n’kukhala anzake. Sitikanatha kuchita zimenezi patokha. Chikhulupiriro n’chofunikabe masiku ano. Mwachitsanzo, chimatithandiza kupewa misampha ya Mdyerekezi yemwe ndi mdani wathu wamphamvu. (Aef. 6:16) Chimatithandizanso kuti tisamade nkhawa kwambiri tikakumana ndi mavuto. Yehova amanena kuti tikakhala ndi chikhulupiriro n’kumaika patsogolo Ufumu wake, iye adzatipatsa zinthu zofunika pa moyo. (Mat. 6:30-34) Tikakhalanso ndi chikhulupiriro tidzapeza moyo wosatha ndipo imeneyi ndi mphatso yamtengo wapatali yomwe sitingaipeze patokha.—Yoh. 3:16. w15 9/15 3:4, 5
Lolemba, February 13
Timasonyeza chikondi, chifukwa [Mulungu] ndi amene anayamba kutikonda.—1 Yoh. 4:19.
N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mulungu ndi amene “anayamba kutikonda”? Mtumwi Paulo ananena kuti: “Mulungu akuonetsa chikondi chake kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.” (Aroma 5:8) Khalidwe lalikulu kwambiri la Yehova ndi chikondi. M’pake kuti Yesu ananena kuti lamulo lalikulu ndi lakuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.” (Maliko 12:30) Yehova amasangalala kwambiri tikamamukonda ndi ‘mtima wathu wonse.’ Koma kukonda Yehova kumatanthauza zambiri osati mmene timamvera mumtima basi. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti tiyenera kukonda Mulungu ndi moyo wathu wonse, maganizo athu onse ndiponso mphamvu zathu zonse. Zimene mneneri Mika analemba zimatsimikizira mfundo imeneyi.—Mika 6:8. w15 9/15 5:1-3
Lachiwiri, February 14
Ndinkangomva za inu, koma tsopano diso langa lakuonani.—Yobu 42:5.
Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatilepheretse kuona dzanja la Mulungu likutithandiza? Nthawi zina, mavuto amene timakumana nawo angatisokoneze ndipo tingaiwale zabwino zimene Yehova watichitira kale. Mwachitsanzo, Eliya ataopsezedwa ndi Yezebeli, anachita mantha n’kuiwala zinthu zabwino zimene Mulungu anali atamuchitira. Baibulo limanena kuti iye “anayamba kupempha kuti afe.” (1 Maf. 19:1-4) Apa Eliya anafunika kudalira Yehova kuti amuthandize. (1 Maf. 19:14-18) Nayenso Yobu atakumana ndi mavuto anasiya kuona zinthu mmene Mulungu amazionera. Koma kenako anayesetsa kuti ayambenso kuona kuti Yehova akumuthandiza. (Yobu 42:3-6) Nanga ifeyo tingatani kuti tiziona Yehova akutithandiza tikakumana ndi mavuto? Tiyenera kuganizira mfundo za m’Baibulo n’kumaona kugwirizana kwake ndi zimene zikuchitika pa moyo wathu. Tikatero tidzatha kuzindikira kuti Mulungu akutithandiza. w15 10/15 1:15, 16
Lachitatu, February 15
Munthu iwe, ndani anandiika ine kukhala woweruza kapena wogawa chuma chanu?—Luka 12:14.
Yesu sankalola chilichonse kumusokoneza pa ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, atangoyamba ntchito yake anaphunzitsa anthu ambiri komanso kuchita zozizwitsa ku Kaperenao. Ndiyeno anthu a mumzindawo anamuuza kuti asachoke. Koma iye anayankha kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.” (Luka 4:42-44) Yesu ankayenda mitunda italiitali kukalalikira ndi kuphunzitsa uthenga wabwino kwa anthu ambiri ku Palesitina. Ngakhale kuti anali wangwiro, nthawi zina ankatopa ndipo ankafuna kupuma chifukwa chogwira kwambiri ntchito yolalikira. (Luka 8:23; Yoh. 4:6) Tsiku lina Yesu akuphunzitsa zimene ophunzira ake angachite akamatsutsidwa, munthu wina anamudula mawu n’kunena kuti: “Mphunzitsi, mundiuzireko m’bale wanga kuti andigawireko cholowa.” Koma Yesu sanalole kuti nkhani yawoyi imusokoneze.—Luka 12:13-15. w15 10/15 3:10, 11
Lachinayi, February 16
Mulungu ndiye chikondi.—1 Yoh. 4:8.
Chikondi ndi khalidwe lalikulu kwambiri la Mulungu. Iye amachita chilichonse chifukwa cha chikondi. N’zosangalatsa kwambiri kudziwa kuti Mulungu amene analenga zonse ndi wachikondi chachikulu chonchi. Yehova amakonda kwambiri anthu komanso zinthu zonse zimene analenga. Mfundo imeneyi imatitsimikizira kuti cholinga chake chokhudza anthufe chidzakwaniritsidwa m’njira yabwino kwambiri. Mwachitsanzo, Yehova ‘wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza m’chilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu, kudzera mwa Yesu Khristu amene iye wamuika.’ (Mac. 17:31) Zimenezi sizingalephereke ndipo anthu olungama adzalandira madalitso mpaka kalekale. w15 11/15 3:1, 2
Lachisanu, February 17
Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoma ngati mwawathira mchere.—Akol. 4:6.
Tikamalalikira, anthu ena amamvetsera koma ena amadana ndi uthenga wathu. Koma kaya anthu akumvetsera uthenga wathu kapena ayi, timatsatira malangizo a m’Baibulo. Tikamakambirana ndi anthu zimene timakhulupirira, timalankhula “ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri” chifukwa chakuti timawakonda. (1 Pet. 3:15) Ngakhale anthu akatilankhula mwachipongwe mu utumiki, timawasonyeza chikondi potsanzira zimene Yesu ankachita. Pamene “anali kunenedwa zachipongwe, sanabwezere zachipongwe. Pamene anali kuvutika, sanawopseze, koma anali kudzipereka kwa iye amene amaweruza molungama.” (1 Pet. 2:23) Nthawi zonse tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumatsatira malangizo akuti: “Osabwezera choipa pa choipa kapena chipongwe pa chipongwe, koma m’malomwake muzidalitsa.”—1 Pet. 3:8, 9. w15 11/15 4:17, 18
Loweruka, February 18
Aziwakumbutsa . . . kukonda ana awo.—Tito 2:4.
Yesu ankakonda kuuza ophunzira ake kuti amawakonda. (Yoh. 15: 9) Iye ankasonyezanso chikondi pocheza nawo kawirikawiri. (Maliko 6:31, 32; Yoh. 2:2; 21:12, 13) Nanunso muziuza ana anu kuti mumawakonda ndiponso mumawaona kuti ndi ofunika kwambiri. (Miy. 4:3) M’bale wina wa ku Australia dzina lake Samuel ananena kuti: “Ndili mwana, bambo anga ankandiwerengera Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo tsiku lililonse ndisanakagone ndiponso kuyankha zimene ndinkawafunsa. Kenako ankandikumbatira n’kundigoneka. Ndinadabwa nditamva kuti makolo awo sankawachitira zimenezi. Koma iwo ankayesetsa kundisonyeza chikondi. Zimenezi zinachititsa kuti tizikondana kwambiri ndipo ndinkamva kuti ndine wotetezeka komanso ndinkasangalala.” Ana anunso akhoza kumamva choncho mukamawauza kuti mumawakonda. Muziwasonyeza chikondi pocheza nawo, kudya nawo ndiponso kusewera nawo. w15 11/15 1:3, 4
Lamlungu, February 19
Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa chakudya pa nthawi yoyenera?—Mat. 24:45.
Gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” litangokhazikitsidwa mu 1919, linkalemba mabuku ndi zinthu zina m’Chingelezi, ndipo zambiri sizinkamasuliridwa m’zilankhulo zina. Koma panopa kapoloyu akuyesetsa kuphunzitsa anthu m’zilankhulo zambiri ndipo mabuku athu akupezeka m’zilankhulo zoposa 700. Komanso anthu a Mulungu ankafunika Baibulo lomasuliridwa molondola ndiponso losavuta kumva. Ndiyeno panakonzedwa komiti yoti imasulire Baibulo la Dziko Latsopano. Mbali yoyamba ya Baibuloli inatulutsidwa mu 1950, ndipo yomaliza inatulutsidwa mu 1960. Potulutsa mbali yoyamba ya Baibuloli pa msonkhano wa pa 2 August, 1950, M’bale Knorr ananena kuti ankafunitsitsa kuti Baibuloli lithandize anthu mamiliyoni ambiri kudziwa za Mulungu. w15 12/15 1:15, 17
Lolemba, February 20
Wosonkhanitsayo anafufuza mawu okoma ndipo analemba mawu olondola a choonadi.—Mlal. 12:10.
Kodi inuyo zimakuvutani kupeza “mawu okoma”? Ngati ndi choncho, muziwerenga Baibulo komanso mabuku athu kuti mudziwe mawu ena abwino omwe mungalankhule. Yesetsani kudziwa matanthauzo a mawu omwe ndi achilendo kwa inu. Chitsanzo cha Yesu chingakuthandizeninso kudziwa zimene mungachite kuti muzilankhula mawu olimbikitsa. Chifukwa cha zimene Yehova anamuphunzitsa, Yesu ankadziwa ‘mmene angayankhire munthu wotopa.’ (Yes. 50:4) Kuganizira kaye tisanalankhule kungatithandize kupeza mawu oyenera. (Yak. 1:19) Tizidzifunsa kuti: ‘Ndikalankhula mawu amenewa, kodi zimene munthuyu angamve ndi zimenedi ndikutanthauza? Kodi mawu amene ndikufuna kulankhulawa sangamukhumudwitse?’ w15 12/15 3:12
Lachiwiri, February 21
Chiwonongeko [cha Yerusalemu] chayandikira.—Luka 21:20.
Pamene Akhristu a ku Yudeya komanso a ku Yerusalemu anaona magulu a nkhondo atazungulira Yerusalemu, anayenera kutsatira malangizo a Yesu akuti athawe mwamsanga. (Luka 21:20-24) Pa zaka 28 kuchokera pamene Yesu ananena zimenezi, Akhristu achiyuda a ku Isiraeli anali atasonyeza kale kupirira chifukwa anali atazunzidwa komanso kukumana ndi mavuto ena. (Aheb. 10:32-34) Komabe Paulo ankadziwa kuti Akhristuwa anali atatsala pang’ono kukumana ndi mayesero ena aakulu kwambiri. (Mat. 24:20, 21; Aheb. 12:4) Ndiyeno ankafuna kuti iwo akhale okonzeka kukumana ndi vuto lililonse. Akhristuwo ankafunika kukhala opirira komanso kukhala ndi chikhulupiriro cholimba chimene chikanawathandiza kuti apulumuke. (Aheb. 10:36-39) Choncho mzimu wa Yehova unachititsa Paulo kuti awalembere kalata yowalimbikitsa. Kalatayi ndi buku la m’Baibulo la Aheberi. w16.01 1:1, 2
Lachitatu, February 22
Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda chonchi, ndiye kuti ifenso tiyenera kukondana.—1 Yoh. 4:11.
Ngati timayamikiradi chikondi cha Mulungu, tiyenera kukonda abale athu. (1 Yoh. 3:16) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timawakonda? Chitsanzo cha Yesu chingatithandize pa nkhaniyi. Ali padzikoli, ankaganizira kwambiri anthu ooneka ngati onyozeka. Ankathandiza anthu olumala, osaona, osamva ndiponso osalankhula. (Mat. 11:4, 5) Yesu ankasangalala kuphunzitsa anthu omwe atsogoleri a chipembedzo chachiyuda ankawaona ngati ‘otembereredwa.’ (Yoh. 7:49) Iye ankakonda kwambiri anthuwo ndipo ankayesetsa kuwathandiza. (Mat. 20:28) Ifenso tingachite bwino kuganizira kwambiri abale ndi alongo amumpingo wathu n’kuona ngati pali ena amene tingawathandize. Mwachitsanzo, mwina mumpingo wathu muli abale ndi alongo achikulire. Tikamaganizira mmene Mulungu amatikondera timafunitsitsa kusonyeza chikondi kwa abale athu. w16.01 2:12-14
Lachinayi, February 23
Ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za khola ili, zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa . . . ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.—Yoh. 10:16.
Kodi a nkhosa zina ayenera kudziwa mayina a odzozedwa onse a masiku ano? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti munthu amene wadzozedwa amakhala kuti wangosankhidwa koma sizinatsimikizike kuti adzalandiradi mphoto yake. Satana amadziwanso zimenezi ndipo n’chifukwa chake amagwiritsa ntchito “aneneri onyenga” kuti ‘asocheretse osankhidwawo.’ (Mat. 24:24) Akhristu odzozedwa sadziwa ngati adzalandiredi mphoto yawo, mpaka pamene Yehova wawadinda chidindo chomaliza posonyeza kuti ndi oyenera kulandira mphotoyo. Yehova amachita zimenezi wodzozedwa wokhulupirika asanamwalire. Koma kwa odzozedwa amene angakhalebe ndi moyo, Yehova adzawadinda chidindochi, “chisautso chachikulu” chitangotsala pang’ono kuyamba. (Chiv. 2:10; 7:3, 14) Choncho panopa n’zosatheka kudziwa anthu amene adzakhale m’gulu la 144,000. w16.01 4:2, 3
Lachisanu, February 24
[Mawu anga] adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.—Yes. 55:11.
Ntchito yolalikira imathandiza kuti cholinga cha Mulungu chokhudza anthu chidzakwaniritsidwe. Mulungu amafuna kuti anthu akhale ndi moyo wosatha padzikoli. Ngakhale kuti Adamu anachimwa, Yehova sanasinthe cholinga chakechi. Koma anakonza zoti anthu amasulidwe ku uchimo ndi imfa. Yesu anabwera padzikoli kudzapereka moyo wake kuti awombole anthu omvera. Komabe kuti munthu azimvera Mulungu, ayenera kudziwa zimene Mulunguyo amafuna. Choncho Yesu anaphunzitsa anthu zimene Mulungu amafuna ndipo anauza ophunzira ake kuti azichitanso zimenezi. Tikamalalikira, timakhala tikugwira ntchito ndi Mulungu pothandiza kuti anthu amasulidwe ku uchimo ndi imfa. Timasonyezanso kuti timawakonda komanso timakonda Yehova amene “chifuniro chake n’chakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.”—1 Tim. 2:4. w16.01 5:15, 16
Loweruka, February 25
[Ahazi] anawotcha ana ake pamoto.—2 Mbiri 28:1-3.
Zinthu zoipa zimene Hezekiya anaona bambo ake akuchita, zikanamukhumudwitsa kwambiri moti akanatha kukwiyira Yehova. Masiku ano, anthu ena amene anakumanapo ndi mavuto amaona kuti ali ndi zifukwa zomveka zoti ‘azikwiyira Yehova’ kapena gulu lake. (Miy. 19:3) Amachita zimenezi ngakhale kuti mavuto awo sakhala aakulu ngati a Hezekiya. Enanso amachita zinthu zoipa poganiza kuti sangachitire mwina chifukwa anakulira m’banja limene munkachitika zinthu zoipa. (Ezek. 18:2, 3) Koma kodi zimenezi ndi zoona? Chitsanzo cha Hezekiya chimasonyeza kuti zimenezi si zoona. Palibe chifukwa chomveka chotichititsa kukwiyira Yehova popeza iye si amene amachititsa zinthu zoipa zimene timakumana nazo. (Yobu 34:10) N’zoona kuti zochita za makolo, zikhoza kuchititsa kuti ana awo azichita zabwino kapena zoipa. (Miy. 22:6; Akol. 3:21) Koma izi sizikutanthauza kuti munthu amene anakulira m’banja limene munkachitika zinthu zoipa sangakhale wabwino. Tikutero chifukwa chakuti Yehova anatipatsa ufulu wosankha kuchita zabwino kapena zoipa.—Deut. 30:19. w16.02 2:8-10
Lamlungu, February 26
Pali olamulira ankhanza amene akufuna moyo wanga.—Sal. 54:3.
Abineri anathandiza Sauli kusaka Davide n’cholinga choti amuphe ngakhale kuti ankadziwa kuti Mulungu anali atasankha Davide kuti akhale mfumu ya Isiraeli. (1 Sam. 26:1-5) Sauli atamwalira, Abineri sanakhalenso kumbali ya Davide. Iye anakhala kumbali ya mwana wa Sauli dzina lake Isiboseti ndipo ankafuna kuti akhale mfumu. Kenako Abineri anagonanso ndi mdzakazi wa Mfumu Sauli ndipo n’kutheka kuti anachita zimenezi chifukwa chofuna kuti akhale mfumu. (2 Sam. 2:8-10; 3:6-11) Nayenso Abisalomu, yemwe anali mwana wa Davide, anali wosakhulupirika kwa Mulungu chifukwa sanali wodzichepetsa. Iye ankafuna kukhala mfumu choncho “anadzipangira galeta lokokedwa ndi mahatchi, ndipo amuna 50 anali kuthamanga patsogolo pake.” (2 Sam. 15:1) Anakopanso Aisiraeli ambiri kuti akhale kumbali yake. Mofanana ndi Abineri, Abisalomu ankafunanso kupha Davide, ngakhale kuti ankadziwa zoti Yehova anasankha Davideyo kuti akhale mfumu ya Isiraeli. (2 Sam. 15:13, 14; 17:1-4) Ngati munthu ndi wodzikuza ndipo akufunitsitsa kukhala ndi udindo, zimamuvuta kukhala wokhulupirika kwa Mulungu. Koma munthu amene amakonda kwambiri Yehova sangachite zinthu zoipa ngati zimene Abineri ndi Abisalomu anachita. w16.02 4:9-11
Lolemba, February 27
Chikhulupiriro pachokha, ngati chilibe ntchito zake, ndi chakufa.—Yak. 2:17.
Zimene mumachita zimasonyeza ngati chikhulupiriro chanu ndi cholimba kapena ayi. Achinyamata nanunso ‘muyenera kukhala ndi khalidwe loyera.’ (2 Pet. 3:11) Kuti musonyeze kuti muli ndi khalidwe loyera, nthawi zonse muyenera kupewa kuchita zoipa. Mwachitsanzo, taganizirani zimene mwachita pa miyezi 6 yapitayi. Ngati munayesedwa kuti muchite zoipa, kodi munaiganizira bwinobwino nkhaniyo n’kuzindikira zoyenera kuchita? (Aheb. 5:14) Kodi mukukumbukira nthawi ina pamene munakana mayesero kapena kutengera zochita za anzanu? Nanga kodi zimene mumachita kusukulu zimathandiza anthu kuti azilemekeza Yehova? Kodi mumakhala okhulupirika kwa Yehova kapena mumachita zofuna za anthu akusukulu n’cholinga choti asakunyozeni? (1 Pet. 4:3, 4) N’zoona kuti tonsefe timalakwitsa zinthu nthawi zina. Ngakhale anthu amene atumikira Mulungu kwa zaka zambiri, nthawi zina amachita mantha kulalikira kwa ena. Komabe munthu aliyense amene anadzipereka kwa Yehova ayenera kunyadira kuti ndi wa Mboni za Yehova ndipo ayenera kuyesetsa kukhala ndi khalidwe loyera. w16.03 2:10, 11
Lachiwiri, February 28
Njira ndi iyi. Yendani mmenemu anthu inu.—Yes. 30:21.
Kuyambira kale kwambiri, Yehova wakhala akupatsa anthu ake malangizo. Mwachitsanzo, m’munda wa Edeni anapereka malangizo omveka bwino omwe akanathandiza kuti anthu onse azikhala mosangalala komanso mpaka kalekale. (Gen. 2:15-17) Koma Adamu ndi Hava sanamvere malangizo a Mulungu. Hava anamvera zimene njoka inamuuza ndipo Adamu anamvera mkazi wake. Zotsatira zake n’zakuti onse anafa ndipo sadzakhalanso ndi moyo. Komanso kusamvera kwawoko kunachititsa kuti anthu onse azivutika ndiponso kufa. Masiku anonso Yehova amapereka malangizo othandiza kwa anthu ake. Amawauza zimene angachite kuti apewe zinthu zimene zingaike moyo wawo pa ngozi komanso zomwe angachite kuti adzapeze moyo wosatha. Yehova ali ngati m’busa amene amateteza ndiponso kuchenjeza nkhosa zake kuti zisalowere kolakwika. w16.03 4:2, 3