Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es17 tsamba 26-36
  • March

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • March
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
  • Timitu
  • Lachitatu, March 1
  • Lachinayi, March 2
  • Lachisanu, March 3
  • Loweruka, March 4
  • Lamlungu, March 5
  • Lolemba, March 6
  • Lachiwiri, March 7
  • Lachitatu, March 8
  • Lachinayi, March 9
  • Lachisanu, March 10
  • Loweruka, March 11
  • Lamlungu, March 12
  • Lolemba, March 13
  • Lachiwiri, March 14
  • Lachitatu, March 15
  • Lachinayi, March 16
  • Lachisanu, March 17
  • Loweruka, March 18
  • Lamlungu, March 19
  • Lolemba, March 20
  • Lachiwiri, March 21
  • Lachitatu, March 22
  • Lachinayi, March 23
  • Lachisanu, March 24
  • Loweruka, March 25
  • Lamlungu, March 26
  • Lolemba, March 27
  • Lachiwiri, March 28
  • Lachitatu, March 29
  • Lachinayi, March 30
  • Lachisanu, March 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
es17 tsamba 26-36

March

Lachitatu, March 1

Simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.​—Yak. 4:14.

Akulu amene amaganizira nkhosa amaphunzitsa anthu ena zinthu zimene iwo aphunzira kwa zaka zambiri. (Sal. 71:17, 18) Akulu amene amaphunzitsa ena amathandiza kwambiri mpingo. Iwo amathandiza kuti mpingo ukhale wotetezeka. Kodi tikutanthauza chiyani pamenepa? Anthu ena akaphunzitsidwa ndiye kuti padzakhala abale ambiri othandiza kuti mpingo ukhale wolimba ndiponso wogwirizana panopa komanso makamaka pa chisautso chachikulu. (Ezek. 38:10-12; Mika 5:5, 6) Choncho ngati ndinu mkulu, tikukupemphani kuti muyambe panopa kuphunzitsa anthu ena mumpingo. Tikudziwa kuti mumatopa chifukwa cha ntchito zina zofunika kwambiri mumpingo. Koma tikukupemphani kuti pa nthawi imene mumatanganidwayo, muzipatulapo ina kuti muphunzitse ena. (Mlal. 3:1) Mukatero mudzasonyeza kuti mukuona zam’tsogolo. w15 4/15 1:8-10

Lachinayi, March 2

Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwako, akuti: “Njira ndi iyi. Yendani mmenemu.”​—Yes. 30:21.

M’Baibulo muli uthenga umene Yehova walembera anthu onse. Koma kodi Baibulo limasonyeza zimene munthu aliyense payekha angachite kuti ayandikire Yehova? Inde. Tikutero chifukwa chakuti munthu akamaphunzira Baibulo n’kumatsatira zimene likunena zimakhala ngati Yehova akumulankhula. Izi zimathandiza kuti ubwenzi wa munthuyo ndi Yehova ulimbe. (Aheb. 4:12; Yak. 1:23-25) Tiyerekeze kuti munthu wawerenga mawu a Yesu akuti: “Lekani kudziunjikira chuma padziko lapansi.” Ngati munthuyo amatsatiradi mfundoyi n’kumaika patsogolo zinthu zokhudza Ufumu, amadziwa kuti akusangalatsa Yehova. Koma ngati akuona kuti ali ndi vuto pa nkhaniyi, amadziwa kuti Yehova wamuuza zinthu zimene ayenera kusintha n’cholinga choti akhale naye pa ubwenzi wolimba.​—Mat. 6:19, 20. w15 4/15 3:3-5

Lachisanu, March 3

Ambuye anaima pafupi ndi ine ndi kundipatsa mphamvu, kuti kudzera mwa ine, ntchito yolalikira ichitidwe mokwanira, ndi kuti mitundu yonse ya anthu imve uthengawo. Ndiponso ndinapulumutsidwa m’kamwa mwa mkango.​—2 Tim. 4:17.

Nafenso tikamayesetsa ngati Paulo kugwira mwakhama ntchito yolalikira, Yehova adzaonetsetsa kuti tikupeza zofunika pa moyo. (Mat. 6:33) Ndife “antchito anzake a Mulungu” ndipo iye “wationa kuti ndife oyenera kupatsidwa ntchito yolalikira uthenga wabwino.” (1 Akor. 3:9; 1 Ates. 2:4) Choncho tikamagwira ntchito yolalikira mwakhama, zidzakhala zosavuta kuyembekezera kuti Yehova atithandize. Choncho tiyeni tiyesetse panopa kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu. Tikakumana ndi vuto lililonse lodetsa nkhawa, tiziona kuti ndi mwayi wathu woti tiyandikire Yehova. Tiziyesetsa kuphunzira Mawu a Mulungu, kupemphera mosalekeza ndiponso kuchita nawo zinthu zonse zokhudza kulambira. Tikamatero, Yehova adzatithandiza pa vuto lililonse limene tingakumane nalo panopa ngakhale m’tsogolo. w15 4/15 4:17, 18

Loweruka, March 4

Kodi nkhondo zimene zikuchitika pakati panu zikuchokera kuti? Nanga kukangana pakati panu kukuchokera kuti?​—Yak. 4:1.

Kunyada kukhoza kusokoneza mtendere mumpingo. Munthu amene ali ndi mtima wodana ndi anthu ena komanso maganizo oti mtundu wake ndi wapamwamba kuposa wa ena, angalankhule kapena kuchita zinthu zimene zingapweteke kwambiri anzake. (Miy. 12:18) Aliyense ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndimadziona kuti ndine wapamwamba kuposa ena?’ Ngati yankho ndi loti inde, ndi bwino kukumbukira kuti “Yehova amanyansidwa ndi munthu aliyense wa mtima wonyada.” (Miy. 16:5) Kodi mumtima mwathu timamva bwanji tikaona anthu amene tikusiyana nawo mtundu, dziko kapena chikhalidwe? Kodi timaona kuti ndife apamwamba kuposa iwowo? Tisaiwale kuti “kuchokera mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu.” (Mac. 17:26) Malinga ndi lembali, anthufe ndi amtundu umodzi chifukwa ndife ana a Adamu. Ndi anthu opanda nzeru okha amene amaganiza kuti mtundu wina ndi wapamwamba kuposa unzake. Satana amasangalala akaona anthu akukhala ndi maganizo amenewa podziwa kuti akhoza kuchititsa kuti Akhristu asamakondane komanso asamagwirizane. (Yoh. 13:35) Choncho kuti tigonjetse Satana, tiyenera kupeweratu mtima wonyada.​—Miy. 16:18. w15 5/15 2:8, 9

Lamlungu, March 5

Muzitsanzira Mulungu.​—Aef. 5:1.

Timasangalala tikaganizira zimene Mulungu walonjeza. Mwachitsanzo, odzozedwa okhulupirika adzalandira moyo wosafa kumwamba ndipo a nkhosa zina adzalandira moyo wosatha padziko lapansi. (Yoh. 10:16; 17:3; 1 Akor. 15:53) Kaya tili ndi chiyembekezo chopita kumwamba kapena chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi, mavuto amene tikukumana nawowa adzatha. Yehova amadziwa bwino mavuto amene tikukumana nawo ngati mmene ankadziwira mavuto a Aisiraeli ku Iguputo. Paja Baibulo limati: “Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.” (Yes. 63:9) Patapita zaka mahandiredi angapo, adani a Aisiraeli sankafuna kuti Aisiraeliwo amangenso kachisi. Koma Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.” (Zek. 2:8) Yehova amachitira chifundo anthu ake ngati mmene mayi amachitira ndi mwana wake. (Yes. 49:15) Choncho Yehova amamvetsa zomwe tikukumana nazo ndipo tikhoza kumutsanzira.​—Sal. 103:13, 14. w15 5/15 4:2

Lolemba, March 6

Osaukawo muli nawo nthawi zonse.​—Mat. 26:11.

Kodi Yesu ankatanthauza kuti padzikoli padzakhala anthu osauka mpaka kalekale? Ayi. Koma ankatanthauza kuti vuto la umphawi silingathe m’dziko loipali. Masiku ano, anthu mamiliyoni ambiri amalephera kupeza zinthu zofunika pa moyo chifukwa cha ulamuliro wopanda chilungamo. Komabe timadziwa kuti posachedwapa anthu onse adzakhala ndi zinthu zonse zofunika. (Sal. 72:16) Zinthu zodabwitsa zimene Yesu ankachita zimasonyeza kuti ali ndi mphamvu ndiponso ndi wofunitsitsa kutithandiza. (Mat. 14:14-21) Ngakhale kuti ifeyo sitingachite zozizwitsa, tingathandize anthu kudziwa maulosi osonyeza zinthu zabwino zimene tikuyembekezera. Mboni za Yehovafe, tikudziwa zinthu zabwino zimene Mulungu watilonjeza. Choncho tili ndi udindo wothandiza anthu ena kudziwa zinthuzi. (Aroma 1:14, 15) Kuganizira zimenezi kungatilimbikitse kuti tizilalikira mwakhama za Ufumu wa Mulungu.​—Sal. 45:1; 49:3. w15 6/15 1:7, 10, 11

Lachiwiri, March 7

Yeretsani manja anu . . . ndipo yeretsani mitima yanu.​—Yak. 4:8.

Tikamaona kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu ndi wamtengo wapatali, timayesetsa kuchita ndiponso kuganizira zinthu zomusangalatsa nthawi zonse. Timayesetsa kuganizira zinthu zoyera kuti tikhalenso anthu oyera. (Sal. 24:3, 4; 51:6; Afil. 4:8) Yehova amamvetsa zoti ndife ochimwa komanso kuti zimativuta kupewa maganizo oipa. Koma sitifuna kumukhumudwitsa, choncho timayesetsa kupewa kuganizira zinthu zoipa. (Gen. 6:5, 6) Timachita zonse zimene tingathe kuti tiziganizira zinthu zabwino. Tingasonyeze kuti timadalira Yehova tikamamupempha kuti azitithandiza kupewa maganizo oipa. Tikamayandikira Mulungu popemphera iye amatiyandikiranso. Amatipatsa mzimu wake woyera kuti utithandize kukhalabe oyera n’kumapewa maganizo oipa. w15 6/15 3:4, 5

Lachitatu, March 8

Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.​—Mat. 6:11.

Yesu anatiphunzitsa kuti tizipempha chakudya “chathu” osati “changa.” Woyang’anira dera wina ku Africa dzina lake Victor anati: “Ndimathokoza kwambiri Yehova chifukwa ine ndi mkazi wanga sitidera nkhawa chakudya kapena ndalama ya lendi. Abale athu amatisamalira bwino tsiku ndi tsiku. Koma ndimapempha Yehova kuti azithandiza abalewa kupeza zinthu zofunika pa moyo.” Ngati tili ndi chakudya chokwanira, tiyenera kuganizira abale athu osauka kapena amene akhudzidwa ndi ngozi inayake. Tiziwapempherera ndiponso kuchita zinthu mogwirizana ndi mapemphero athuwo. Mwachitsanzo, tingawagawire zinthu zomwe tili nazo. Tingaperekenso ndalama zothandiza pa ntchito yapadziko lonse. Paja ndalamazi zimagwiritsidwanso ntchito pothandiza abale ovutika.​—1 Yoh. 3:17. w15 6/15 5:4-6

Lachinayi, March 9

Mulungu uyu ndi Mulungu wathu mpaka kalekale. Iye adzatitsogolera kufikira imfa yathu.​—Sal. 48:14.

Lemba la Yesaya 60:17 linaneneratu kuti mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova idzasintha kwambiri. Akhristu achinyamata ndiponso amene angolowa kumene m’gulu la Yehova amawerenga kapena kumva kwa ena za kusintha kumeneku. Koma pali abale ndi alongo ena amene akhala ndi mwayi woona okha kusinthaku. N’chifukwa chake amakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova akugwiritsa ntchito Yesu potsogolera gulu lake. Enafe timakhulupiriranso zimenezi chifukwa chakuti tili ndi umboni. Koma chikhulupiriro chathu chingalimbe kwambiri tikamamvetsera zimene abale ndi alongo amene aona kusintha kwa gululi angatifotokozere. Ndiyeno kaya takhala m’gulu la Yehova kwa nthawi yaitali bwanji, tiyenera kuuza anthu ena za gululi. N’zodabwitsa kuti tikukhala m’paradaiso wauzimu ngakhale kuti tili m’dziko loipa lomwe anthu ake sakondana. w15 7/15 1:12, 13

Lachisanu, March 10

Anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Haramagedo.​—Chiv. 16:16.

Nkhondo ya Aramagedo idzachititsa kuti dzina la Yehova lilemekezedwe. Pa nthawi imeneyi, anthu onse amene ali ngati mbuzi “adzachoka kupita ku chiwonongeko chotheratu.” (Mat. 25:31-33, 46) Zoipa zonse zidzachotsedwa padzikoli ndipo khamu lalikulu lidzapulumuka mbali yomaliza ya chisautso chachikulu. Ndiyeno popeza tadziwa zimene zidzachitike posachedwapa, kodi aliyense ayenera kuchita chiyani? Mtumwi Petulo analemba kuti: “Popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka, ganizirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala. Muyenera kukhala anthu akhalidwe loyera ndipo muzichita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu. Muzichita zimenezi poyembekezera ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova, . . . Chotero okondedwa, pakuti mukuyembekezera zinthu zimenezi, chitani chilichonse chotheka kuti iye adzakupezeni opanda banga, opanda chilema ndiponso muli mu mtendere.” (2 Pet. 3:11, 12, 14) Choncho tiyeni tiyesetse kukhalabe anthu oyera n’kumamvera Mfumu ya Mtendere. w15 7/15 2:17, 18

Loweruka, March 11

Yehova akapanda kumanga nyumba, omanga nyumbayo amagwira ntchito pachabe.​—Sal. 127:1.

Gulu la Yehova likuchita zambiri pothandiza kuti Nyumba za Ufumu zambirimbiri zimangidwe. Abale ndi alongo odzipereka ndi amene amagwira ntchito yopanga mapulani, kumanga ndiponso kukonza zowonongeka. Kuyambira pa November 1, 1999, Nyumba za Ufumu zoposa 28,000 zamangidwa padziko lonse. Apa tinganene kuti pa zaka 15, pafupifupi Nyumba za Ufumu 5 zinkamangidwa tsiku lililonse. Gululi limayesetsa kugwiritsa ntchito bwino ndalama zimene ena amapereka kuti Nyumba za Ufumu zimangidwe m’madera osiyanasiyana. Izi n’zogwirizana ndi mfundo ya m’Malemba yakuti zochuluka zimene ena ali nazo zithandizire pa zimene ena akusowa “kuti pakhale kufanana.” (2 Akor. 8:13-15) Zotsatira zake n’zakuti Nyumba za Ufumu zokongola zamangidwa m’mipingo imene payokha sikanakwanitsa. w15 7/15 4:9-11

Lamlungu, March 12

Uziwayembekezerabe.​—Hab. 2:3.

Chizindikiro chakuti Yesu akulamulira kumwamba chiyenera kuonekera mokwanira kuti anthu amene akumvera malangizo a Yesu oti tikhalabe maso, achizindikire. (Mat. 24:27, 42) Ndiyeno anthu amenewa akhala akuona kuti chizindikirochi chikukwaniritsidwa kuyambira mu 1914. Choncho zikuonekeratu kuti panopa tikukhala ‘m’mapeto a nthawi ino.’ Mapetowa ndi nthawi yochepa imene idzatha dziko loipali likadzawonongedwa. (Mat. 24:3) Ndiye ngati ndi choncho, kodi pali chifukwa choti Akhristu azikhalabe maso masiku ano? Inde, paja izi n’zimene Yesu ananena. Panopa tikuonanso bwinobwino chizindikiro chosonyeza kuti Khristu akulamulira. Sikuti tikungokhulupirira za m’maluwa ayi koma pali umboni wa m’Malemba wosonyeza kuti ino ndi nthawi yoyenera kukhala maso n’kumayembekezera mapeto a dziko loipali. w15 8/15 2:8, 9

Lolemba, March 13

[Mumakhutiritsa] zokhumba za chamoyo chilichonse.​—Sal. 145:16.

M’dziko latsopano tidzakhalanso ndi mwayi wochita zinthu zimene zimatisangalatsa. Tikutero chifukwa chakuti Yehova anatilenga ndi mtima wofuna kuchita zimenezo. (Mlal. 2:24) Iye adzaonetsetsa kuti akupereka zofuna za “chamoyo chilichonse.” N’zoona kuti kuchita zosangalatsa n’kothandiza, koma timasangalala nazo kwambiri ngati tayamba kaye kuchita zinthu zolimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Umu ndi mmene zidzakhalirenso m’dziko latsopano. Choncho si kulakwa kuchita zinthu zimene zimatisangalatsa, koma tiyenera kuona kuti kutumikira Yehova ndiponso madalitso amene amatipatsa ndiye zofunika kwambiri. (Mat. 6:33) M’dziko latsopano tidzasangalala kwambiri kuposa mmene tingaganizire. Choncho tiyeni tizisonyeza kuti tikufunadi kudzakhala ndi moyo weniweniwo ndipo tiyambe panopa kukonzekera. w15 8/15 3:17, 18

Lachiwiri, March 14

Muvale umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo umatsatira zofunika pa chilungamo chenicheni ndi pa kukhulupirika.​—Aef. 4:24.

Pamene Yesu anali padzikoli, ankakhala ndi anthu ochimwa. Nawonso makolo ake ndi achibale ake sanali angwiro. Ngakhale ophunzira ake enieniwo ankakangananso chifukwa chotengera maganizo odzikuza amene anthu ambiri anali nawo. Mwachitsanzo, usiku woti Yesu aphedwa mawa lake, “panabuka mkangano woopsa pakati pawo za amene anali kuoneka wamkulu kwambiri.” (Luka 22:24) Koma Yesu sankakayikira zoti ophunzirawo adzakhala Akhristu olimba n’kupanga mpingo wogwirizana. Usiku womwewo, Yesu anapempherera atumwi akewo ponena kuti: “Onsewa akhale amodzi, mmene inu Atate ndi ine tilili ogwirizana, kuti iwonso akhale ogwirizana ndi ife, . . . kuti iwo akhale amodzi mmene ifenso tilili amodzi.”​—Yoh. 17:21, 22. w15 9/15 1:10, 11

Lachitatu, March 15

Iye anamuuza kuti: “Bwera!” Nthawi yomweyo Petulo anatsika m’ngalawamo n’kuyenda pamadzi kupita kumene kunali Yesu.​—Mat. 14:29.

Petulo anayenda pang’ono koma kenako anayamba kuchita mantha chifukwa cha mphepo ndi mafunde. Mavuto amene timakumana nawo potumikira Yehova tingawayerekezerenso ndi mphepo kapena mafunde. Koma kaya mavutowo akule bwanji, Yehova akhoza kutithandiza kupirira. Kumbukirani kuti Petulo sanamire chifukwa chogwetsedwa ndi mphepo kapena mafunde. Tikutero chifukwa chakuti nkhaniyi imati: “Ataona mphepo yamkuntho, anachita mantha.” (Mat. 14:24-32) Chikhulupiriro cha Petulo chinayamba kuchepa atasiya kuyang’ana Yesu. Ifenso chikhulupiriro chathu chingachepe ngati titayamba kuganizira kwambiri mavuto athu. Tikhoza kuona kuti mavutowo ndi aakulu kwambiri n’kuyamba kukayikira zoti Yehova atithandiza. Popeza chikhulupiriro chathu chikhoza kuchepa, tiyenera kukhala osamala kwambiri. Paja Baibulo limanena kuti kuchepa kwa chikhulupiriro kuli ngati “tchimo limene limatikola mosavuta.” (Aheb. 12:1) Nkhani ya Petuloyi ikusonyeza kuti chikhulupiriro chathu chingachepe ngati titayamba kuganizira kwambiri zinthu zolakwika. w15 9/15 3:1, 6, 7

Lachinayi, March 16

Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, pakuti imatsika kuchokera kwa Atate wa zounikira zonse zakuthambo.​—Yak. 1:17.

Kodi mukalandira mphatso mumachita chiyani? Muyenera kuti mumayamikira komanso kuigwiritsa ntchito bwino. Nthawi zonse Yehova amatipatsa zinthu zofunika kuti tizikhala ndi moyo komanso kuti tizisangalala. Zimenezi zimatilimbikitsa kuti nafenso tizimukonda. Kwa zaka zambiri, Yehova ankasamalira ndiponso kudalitsa Aisiraeli. (Deut. 4:7, 8) Koma iwo ankayenera kumvera Chilamulo cha Mulungu kuti azidalitsidwabe. Mwachitsanzo, ankayenera kupereka kwa Yehova “zipatso zoyamba kucha zabwino koposa.” (Eks. 23:19) Akamachita zimenezi ankasonyeza kuti amayamikira kwambiri chikondi cha Yehova komanso madalitso ake.​—Deut. 8:7-11. w15 9/15 5:5, 6

Lachisanu, March 17

Odala ndi anthu oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu.​—Mat. 5:8.

Kodi tingatani kuti tiziona zimene Mulungu akuchita potithandiza? Mwina mukaganizira mmene munayambira kuphunzira Baibulo, mumaoneratu kuti Mulungu ndi amene anakuthandizani. Kapena nthawi ina muli pa misonkhano munamva nkhani inayake n’kunena kuti: “Zikungokhala ngati akukambira ineyotu.” N’kuthekanso kuti munaona mmene Mulungu anayankhira pemphero lanu. Mwinanso munaona mmene Yehova anakuthandizirani kuti muwonjezere utumiki wanu. Apo ayi, mwina munasiya ntchito kuti muzitumikira Yehova bwinobwino ndipo mwaona iye akukwaniritsa lonjezo lake lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheb. 13:5) Tonsefe tiyenera kuyesetsa kukhala oyera mtima kuti tizizindikira mmene Yehova akutithandizira. Koma kodi tingatani kuti tikhale “oyera mtima”? Tiyenera kukhala ndi maganizo oyera komanso kusiya makhalidwe oipa. (2 Akor. 4:2) Tikamayesetsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu komanso kukhala ndi makhalidwe abwino, timakhala m’gulu la anthu amene akuona Mulungu. w15 10/15 1:17, 19

Loweruka, March 18

Aliyense wonditumikira ine, Atate adzamulemekeza.​—Yoh. 12:26.

Anthu ena amene anabwera kudzachita nawo Pasika ku Yerusalemu anali Agiriki ndipo anachita chidwi ndi zimene Yesu anachita. Iwo anapempha Filipo kuti akonze zoti adzakumane ndi Yesu. Koma Yesu sanalole zimenezo podziwa kuti panali zinthu zofunika kwambiri zimene ankayenera kuchita. Iye sankafuna kusangalatsa anthu n’cholinga choti adzamuteteze pa nthawi imene adani a Mulungu azidzafuna kumupha. Choncho Yesu anakumbutsa ophunzira ake kuti watsala pang’ono kuphedwa ndipo anati: “Aliyense wokonda moyo wake akuuwononga, koma wodana ndi moyo wake m’dziko lino akuusungira moyo wosatha.” M’malo mopita kukakumana ndi Agirikiwo, iye analimbikitsa ophunzira ake kuti azimutsanzira ndipo ananena mawu omwe ali mulemba lalerowa. Filipo ayenera kuti anakauza Agirikiwo mawu olimbikitsawa. (Yoh. 12:20-25) N’zoona kuti Yesu sankafuna kusokonezedwa pa ntchito yolalikira koma ankapezanso nthawi yochita zinthu zina. w15 10/15 3:13, 14

Lamlungu, March 19

Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula ndi kuwalanga.​—Chiv. 3:19.

Ngakhale kuti ophunzira a Yesu ankakangana mobwerezabwereza kuti wamkulu ndani, Yesu sanasiye kuwathandiza. Pamene ankalephera kutsatira malangizo ake, iye ankasankha nthawi ndi malo abwino kuti awalangize mwachikondi ndiponso mofatsa. (Maliko 9:33-37) Nanunso muzisonyeza kuti mumakonda ana anu powalangiza. Nthawi zina mukhoza kungowafotokozera ubwino ndi kuipa kwa zinthu zina. Koma nthawi zina ana amalephera kutsatira zimene mwawauza. (Miy. 22:15) Zimenezi zikachitika muzitsanzira Yesu. Muzisankha nthawi ndi malo abwino kuti muwalangize mwachikondi ndiponso mofatsa. Mlongo wina wa ku South Africa dzina lake Elaine ananena kuti: “Makolo anga sankandilanga atapsa mtima ndipo nthawi zonse ankandiuza chifukwa chimene akuperekera chilangocho. Izi zinandithandiza kudziwa kuti amandikonda. Ndinkadziwanso bwino zimene ndiyenera kuchita komanso zimene sindiyenera kuchita.” w15 11/15 1:5, 6

Lolemba, March 20

Mulungu ndiye chikondi.​—1 Yoh. 4:16.

Kodi tsogolo lathu likanakhala bwanji zikanakhala kuti Mulungu satikonda? Ndiye kuti anthu akanapitiriza kulamulirana motsogoleredwa ndi Satana Mdyerekezi. Choncho zinthu sizikanayenda bwino chifukwa iye ndi wopanda chikondi ndiponso wokwiya kwambiri. (2 Akor. 4:4; 1 Yoh. 5:19; Chiv. 12:9, 12) Zimenezi zikusonyeza kuti tsogolo lathu likanakhala loipa kwambiri zikanakhala kuti Mulungu satikonda. Satana anatsutsa zoti Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse ndipo anasonyeza kuti iyeyo ndi amene angalamulire bwino. (Gen. 3:1-5) Popeza kuti Yehova ndi wanzeru, analola Satana kuti alamulire kwa nthawi yochepa n’cholinga choti zidziwike kuti zimene ananenazo ndi zabodza. Ndiyeno zimene zakhala zikuchitika m’dzikoli zasonyeza kuti Yehova yekha ndi amene angalamulire bwino osati anthu kapena Satana. w15 11/15 3:3, 4

Lachiwiri, March 21

Ayankheni ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.​—1 Pet. 3:15.

Kudzichepetsa kumatithandiza kumvera lamulo lofunika kwambiri limene Yesu anatipatsa. Iye ananena kuti: “Inu munamva kuti anati, ‘Uzikonda mnzako ndi kudana ndi mdani wako.’ Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani, kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba. Chifukwa iye amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mat. 5:43-45) Ngakhale adani athu atatichitira zinthu zoipa, tiyenera kuwakondabe. Nthawi zonse tiyenera kuchita zinthu zosonyeza kuti timakonda Yehova komanso anzathu. Mwachitsanzo, anthu ena amene amatitsutsa akakumana ndi mavuto, tiyenera kuwathandiza. w15 11/15 4:17, 19, 20

Lachitatu, March 22

Anamvetsa bwino mawu amene anawafotokozera.​—Neh. 8:12.

Anthu a Mulungu amagwiritsa ntchito chilankhulo pomutamanda komanso pouza ena zimene iye amafuna. M’zaka zaposachedwa, anthu a Mulungu akhala akumasulira Baibulo m’zilankhulo zosiyanasiyana n’cholinga choti anthu ambiri adziwe Mulungu. Mabaibulo alipo ambiri koma si onse omwe anamasuliridwa bwino. Choncho, m’zaka za m’ma 1940, Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano inakhazikitsa mfundo zitatu zomwe omasulira Baibulo ayenera kutsatira. Mfundozi zakhala zikutsatiridwa pomasulira Baibulo m’zilankhulo zoposa 130. Mfundo zake ndi: (1) Tizilemekeza dzina la Mulungu polibwezeretsa m’malo ake onse m’Mawu a Mulungu. (Mat. 6:9) (2) Tizimasulira potsatira mawu alionse omwe anali m’Baibulo loyambirira ngati zingatheke. Koma ngati kuchita zimenezi kungasokoneze tanthauzo lake, tizingomasulira zimene mawuwo akutanthauza. (3) Tizimasulira pogwiritsa ntchito mawu osavuta kumva.​—Neh. 8:8. w15 12/15 2:1, 2

Lachinayi, March 23

Ngati lipenga likulira mwa mamvekedwe osadziwika bwino, ndani angakonzekere nkhondo?​—1 Akor. 14:8.

Kale ku Isiraeli, ngati lipenga silikulira momveka bwino, linkasokoneza kwambiri asilikali. Ifenso tiyenera kulankhula zomveka bwino kuti tisasokoneze anthu. (1 Akor. 14:9) Komanso tiziyesetsa kulankhula mwaulemu ndiponso mowaganizira. Yesu ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosankha mawu oyenera. Taganizirani mawu amene anagwiritsa ntchito pa ulaliki wake umene umapezeka m’chaputala 5 mpaka 7 cha buku la Mateyu. Yesu sanalankhule mawu ambirimbiri, ovuta kapena ongofuna kugometsa anthu. Sanalankhulenso mawu omwe akanakhumudwitsa anthuwo. M’malomwake analankhula mawu osavuta kumva komanso ogwira mtima. Mwachitsanzo, anagwiritsa ntchito chitsanzo cha mmene Yehova amadyetsera mbalame pothandiza anthu kuti asamadere nkhawa za chakudya. Kenako anawafunsa kuti: “Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?” (Mat. 6:26) Mawu osavutawa anathandiza anthuwo kumvetsa mfundo yofunika kwambiri komanso anawalimbikitsa. w15 12/15 3:13, 14

Lachisanu, March 24

Mupitirize kukonda abale.​—Aheb. 13:1.

Kodi kukonda abale kumatanthauza chiyani? Mawu achigiriki amene Paulo anagwiritsa ntchito mulembali, (phi·la·del·phiʹa) amanena za kukonda munthu ndi mtima wonse ngati mmene timachitira ndi wachibale kapena mnzathu wapamtima. (Yoh. 11:36) Sikuti anthu a Mulungufe timangonena kuti timakondana. Chikondi chathu chimakhala chenicheni. (Mat. 23:8) Timatsatira malangizo akuti: “Pokonda abale, khalani ndi chikondi chenicheni pakati panu. Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) Timagwirizana kwambiri chifukwa chokhala ndi chikondi chimenechi komanso cha a·gaʹpe, chomwe munthu amakhala nacho chifukwa chotsatira mfundo zolungama za Mulungu. Akhristu amaona kuti Mkhristu aliyense ndi m’bale wawo, mosaganizira za mtundu wake. (Aroma 10:12) Yehova watiphunzitsa kuti tiyenera kukonda Akhristu anzathu ngati abale athu enieni.​—1 Ates. 4:9 w16.01 1:5, 6

Loweruka, March 25

Chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza.​—2 Akor. 5:14.

Chifukwa chokonda kwambiri Yesu, timalalikira mwakhama. (Mat. 28:19, 20; Luka 4:43) Pa nthawi ya Chikumbutso timakhala ndi mwayi wochita upainiya wothandiza wamaola 30 kapena 50. Kodi mungayambiretu kukonza zinthu kuti mudzachite nawo utumikiwu? M’bale wina wazaka 84 amene mkazi wake anamwalira, ankaganiza kuti sangathe kuchita upainiyawu chifukwa chakuti ndi wachikulire komanso amadwaladwala. Komabe apainiya ena amumpingo wawo anamuthandiza. Ankamutenga pa galimoto yawo akamapita mu utumiki komanso anasankha gawo loti m’baleyu akhoza kuyenda bwinobwino. Pamapeto pake, m’baleyo anakwanitsa kuchita nawo upainiya wamaola 30. Kodi inunso mukhoza kuthandiza winawake kuti achite nawo upainiya wothandiza pa nyengo ya Chikumbutso? N’zoona kuti si tonse amene tingakwanitse kuchita upainiya. Komabe tikhoza kuchita zonse zimene tingathe pa ntchito yolalikira. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tikutsanzira mtumwi Paulo amene ankayamikira kwambiri chikondi cha Khristu. w16.01 2:7, 11

Lamlungu, March 26

Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.​—Zek. 8:23.

Popeza panopa n’zosatheka kudziwa mayina a odzozedwa onse, kodi a nkhosa zina ‘angapite nawo limodzi’ bwanji? Ulosi wa Zekariya umanena kuti anthu 10 “adzagwira chovala cha munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’” Ngakhale kuti lembali latchula “Myuda,” limasonyeza kuti mawuwa sakuimira munthu mmodzi koma gulu la odzozedwa. A nkhosa zina akudziwa zimenezi ndipo amatumikira Yehova limodzi ndi gululi. Sikuti amafunika kudziwa munthu aliyense m’gululi n’kumamutsatira. Yesu ndiye Mtsogoleri wathu ndipo Baibulo limati tiyenera kutsatira iye yekha basi.​—Mat. 23:10. w16.01 4:4

Lolemba, March 27

Koma iwe Isiraeli, ndiwe mtumiki wanga, iwe Yakobo amene ndakusankha, mbewu ya bwenzi langa Abulahamu.​—Yes. 41:8.

Munthu aliyense amafuna kukondedwa pa moyo wake wonse. Ndipo sikuti timangofunikira chikondi chimene chimakhala pakati pa mwamuna ndi mkazi. Timafuna kukondana ndiponso kugwirizana ndi anthu osiyanasiyana. Koma anthufe timafunika kukondedwa ndi Yehova kuposa wina aliyense. Anthu ambiri amaona kuti n’zosatheka kukhala pa ubwenzi ndi Yehova popeza ndi Wamphamvuyonse, wosaoneka komanso amakhala kumwamba. Koma Akhristufe sitikhala ndi maganizo amenewa. Baibulo limasonyeza kuti anthu ena anali mabwenzi a Mulungu, ndipo mmodzi mwa anthuwa anali Abulahamu. (Yak. 2:23) Tingachite bwino kuganizira zimene anthuwa anachita kuti akhale mabwenzi a Mulungu. Tikutero chifukwa kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu n’kofunika kwambiri. Koma kodi zinatheka bwanji kuti Abulahamu akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova? Nkhani inagona pa chikhulupiriro. Ndipotu Baibulo limati Abulahamu anali ‘tate wa onse okhala ndi chikhulupiriro.’​—Aroma 4:11. w16.02 1:1, 2

Lachiwiri, March 28

Panalibenso mfumu ina yofanana naye.​—2 Maf. 18:5.

Ngakhale kuti Hezekiya anali mwana wa mfumu yoipa kwambiri, atakula anakhala mfumu yabwino. (2 Maf. 18:6) Hezekiya anakonza zinthu zoipa zimene bambo ake analakwitsa. Anayeretsa kachisi, kuchotsa mafano m’dziko lonse ndiponso kupempha Yehova kuti akhululukire anthu machimo awo. (2 Mbiri 29:1-11, 18-24; 31:1) Pamene Senakeribu mfumu ya Asuri anaopseza kuti aukira mzinda wa Yerusalemu, Hezekiya anachita zinthu molimba mtima ndipo anasonyeza kuti ankakhulupirira Yehova. Iye anadalira Yehova ndipo analimbikitsa anthu ake kuchita chimodzimodzi. (2 Mbiri 32:7, 8) Pa nthawi ina, Hezekiya anayamba mtima wodzikuza koma Yehova atamudzudzula, anadzichepetsa n’kusintha. (2 Mbiri 32:24-26) Iye ndi chitsanzo chabwino kwa tonsefe chifukwa sanalole kuti chitsanzo choipa cha bambo ake chimulepheretse kukhala munthu wabwino. M’malomwake anachita zinthu zimene zinamuthandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. w16.02 2:11

Lachitatu, March 29

Ngati munthu wapatuka n’kuyamba kulowera njira yolakwika mosazindikira, inu oyenerera mwauzimu, yesani kumuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.​—Agal. 6:1.

Inunso mungakhale wokhulupirika kwa Yehova ndiponso kwa anthu ena powachitira zinthu mokoma mtima. Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati mwadziwa kuti Mkhristu wina wachita tchimo lalikulu? Mwina mungafune kubisa tchimo lakelo pofuna kukhala wokhulupirika kwa munthuyo, makamaka ngati ndi wachibale kapena mnzanu wapamtima. Koma si bwino kuchita zimenezi chifukwa tiyenera kukhala okhulupirika kwa Yehova kuposa kwa wina aliyense. Choncho muyenera kumvera Yehova komanso kuchita zinthu mokoma mtima pofuna kuthandiza mnzanuyo. Mungamuuze kuti akafotokozere akulu za tchimo lakelo kuti amuthandize. Ngati papita nthawi ndipo munthuyo sanauze akulu, inuyo muyenera kuwauza. Mukachita zimenezi mungasonyeze kuti ndinu wokhulupirika kwa Yehova komanso wokoma mtima kwa mnzanuyo. Akulu adzayesetsa kumuthandiza ndi mzimu wofatsa kuti akhalenso pa ubwenzi ndi Yehova.​—Lev. 5:1. w16.02 4:14

Lachinayi, March 30

Ganizirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala. Muyenera kukhala anthu akhalidwe loyera ndipo muzichita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu.​—2 Pet. 3:11.

Kodi “ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu” ndi ziti? Izi ndi zinthu monga kusonkhana komanso kulalikira. Palinso zinthu zina zomwe anthu ambiri sangaone monga kupemphera komanso kuphunzira Baibulo panokha. Munthu amene anadzipereka kwa Yehova ndi mtima wonse saona zinthu zimenezi ngati zotopetsa. Koma amakhala ndi maganizo ofanana ndi a Mfumu Davide amene anati: “Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga, ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.” (Sal. 40:8) Muyenera kukumbukira kuti munthu aliyense adzayankha yekha kwa Mulungu. Choncho aliyense ayenera kusankha yekha kuti adzipereke kwa iye ndiponso kubatizidwa. Sayenera kudalira makolo ake kapenanso anthu ena potumikira Mulungu. Mukakhala ndi khalidwe loyera ndiponso mukamachita zinthu zosonyeza kuti ndinu wodzipereka kwa Yehova, mumasonyeza kuti mumamukonda ndiponso mumakonda mfundo zake. Komanso mumasonyeza kuti mukhoza kubatizidwa pasanapite nthawi yaitali. w16.03 2:10, 12, 15

Lachisanu, March 31

Chikhulupirirocho chisanafike, chilamulo chinali kutiyang’anira, . . . N’chifukwa chake Chilamulo chakhala mtsogoleri wotifikitsa kwa Khristu.​—Agal. 3:23, 24.

Chilamulo chinkateteza Aisiraeli kuti asatengere makhalidwe oipa komanso kulambira konyenga kwa anthu a mitundu ina. Aisiraeli akamamvera, Mulungu ankawadalitsa koma akasiya kumumvera ankakumana ndi mavuto aakulu. (Deut. 28:1, 2, 15) Koma palinso chifukwa china chimene Mulungu anaperekera malangizo atsopano kwa Aisiraeli kudzera m’Chilamulo. Chilamulo chinawathandiza kuti akonzekere kubwera kwa Mesiya ndipo kubwera kwa Mesiyako kunali kogwirizana kwambiri ndi cholinga cha Yehova. Komanso Chilamulochi chinkathandiza Aisiraeli kukumbukira kuti ndi ochimwa. Chinawathandizanso kudziwa kuti ankafunika nsembe ya dipo imene ingachotseretu machimo awo. (Agal. 3:19; Aheb. 10:1-10) Kuwonjezera pamenepa, Chilamulo chinathandizanso kuti mzere wobadwira Mesiya usasokonekere komanso kuti Aisiraeliwo adzathe kumuzindikira. Choncho Chilamulochi chinali ‘mtsogoleri wowafikitsa kwa Khristu.’ w16.03 4:6, 7

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena