Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es17 tsamba 37-46
  • April

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • April
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
  • Timitu
  • Loweruka, April 1
  • Lamlungu, April 2
  • Lolemba, April 3
  • Lachiwiri, April 4
  • Lachitatu, April 5
  • Lachinayi, April 6
  • Lachisanu, April 7
  • Loweruka, April 8
  • Lamlungu, April 9
  • Lolemba, April 10
  • Tsiku la Chikumbutso
    Dzuwa Litalowa
    Lachiwiri, April 11
  • Lachitatu, April 12
  • Lachinayi, April 13
  • Lachisanu, April 14
  • Loweruka, April 15
  • Lamlungu, April 16
  • Lolemba, April 17
  • Lachiwiri, April 18
  • Lachitatu, April 19
  • Lachinayi, April 20
  • Lachisanu, April 21
  • Loweruka, April 22
  • Lamlungu, April 23
  • Lolemba, April 24
  • Lachiwiri, April 25
  • Lachitatu, April 26
  • Lachinayi, April 27
  • Lachisanu, April 28
  • Loweruka, April 29
  • Lamlungu, April 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
es17 tsamba 37-46

April

Loweruka, April 1

Khalani maso. Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.​—1 Pet. 5:8.

Poyamba, Satana anali mngelo wabwino ndipo anali pa ubwenzi ndi Yehova. Koma kenako ankafuna kuti anthu azimulambira. Maganizo amenewa anamukulira mpaka anachimwa. (Yak. 1:14, 15) Satana “sanakhazikike m’choonadi.” Iye anayamba kudana ndi ulamuliro wa Yehova ndipo anakhala “tate wake wa bodza.” (Yoh. 8:44) Kuchokera pa nthawi imene Satana anachimwa, iye wakhala mdani wamkulu wa Yehova ndi anthu. Mayina omwe amadziwika nawo amasonyeza kuti iye ndi woipa kwambiri. Mwachitsanzo, dzina lakuti Satana limatanthauza “Wotsutsa” ndipo zimenezi zikusonyeza kuti iye amalimbana kwambiri ndi ulamuliro wa Yehova. Iye amafunitsitsa ulamulirowu utatha. w15 5/15 1:1, 2

Lamlungu, April 2

Ngati munthu akukonda Mulungu, ameneyo amadziwika kwa Mulungu.​—1 Akor. 8:3.

Sikuti munthu akamaphunzira Malemba amangoona zimene ayenera kusintha. Kuphunzirako kumathandizanso munthuyo kumvetsa makhalidwe abwino a Yehova n’kuyamba kumukonda kwambiri. Ndiyeno munthuyo akayamba kukonda kwambiri Yehova, Yehovayo amayambanso kumukonda kwambiri. Zikatere Yehova amakhala mnzake weniweni. Koma kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ulimbe, tiyenera kuwerenga Mawu ake ndi zolinga zoyenera. Lemba la Yohane 17:3 limati: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” Choncho tiyenera kuphunzira osati kuti tingodziwa zinthu koma kuti tidziwe bwino Yehova n’kumamukonda. (Eks. 33:13; Sal. 25:4) Munthu akayamba kukonda kwambiri Yehova sadandaula ngati sakumvetsa nkhani zina za m’Malemba. w15 4/15 3:6-8

Lolemba, April 3

[Timoteyo] adzakukumbutsani mmene ndimachitira zinthu potumikira Khristu Yesu, monga mmenenso ineyo ndikuphunzitsira kulikonse, mumpingo uliwonse.​—1 Akor. 4:17.

Chaposachedwapa, akulu ena amene amayesetsa kuphunzitsa abale kuti ayenerere maudindo mumpingo, anafunsidwa kuti afotokoze zimene amachita. Ngakhale kuti akuluwa amakhala m’madera osiyanasiyana, malangizo amene ananena ndi ofanana. Izi zikusonyeza kuti kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo n’kothandiza ‘kulikonse ndiponso mumpingo uliwonse.’ Mphunzitsi amafunika kukhala womasuka kuti athandize ophunzira. Zimenezi n’zofanana ndi zimene mlimi amachita. Iye asanafese mbewu amakonza kaye munda wake. Choncho mphunzitsi ayenera kukonzekeretsa ophunzira ake kuti aphunzire zinthu zatsopano. Angachite zimenezi potsatira zimene mneneri Samueli anachita pamene ankaphunzitsa Sauli kuti adzakhale mtsogoleri wa Aisiraeli.​—1 Sam. 9:15-27; 10:1. w15 4/15 1:11, 12

Lachiwiri, April 4

Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.​—1 Yoh. 5:19.

Dzikoli limalimbikitsa zinthu zambiri zosemphana ndi mfundo za m’Baibulo. Apa sitikutanthauza kuti zinthu zonse za m’dzikoli ndi zoipa. Koma tiyenera kukumbukira kuti Satana angakonde kuti titengeke ndi zinthu zimene timalakalaka n’kufika pochimwa kapena kusiya kutumikira Yehova. (1 Yoh. 2:15, 16) Baibulo limasonyeza kuti m’nthawi ya atumwi Akhristu ena anayamba kukonda zinthu za m’dzikoli. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analemba kuti: “Dema wandisiya chifukwa chokonda zinthu za m’nthawi ino.” (2 Tim. 4:10) Komabe Baibulo silitchula zinthu za m’dzikoli zimene Dema anayamba kuzikonda kuti asiye kuyenda ndi mtumwi Paulo. Mwina iye anayamba kukonda kwambiri chuma ndipo anasiya kutumikira Yehova. Ngati ndi choncho, ndiye kuti anataya mwayi wamtengo wapatali. Apatu sanaganize bwino chifukwa dzikoli silikanamupatsa zinthu zabwino kuposa madalitso amene Yehova akanamupatsa chifukwa choyenda ndi Paulo.​—Miy. 10:22. w15 5/15 2:10, 11

Lachitatu, April 5

Yehova ndi wachifundo ndi wachisomo.​—Sal. 103:8.

Yesu ankamvetsa mavuto a anthu ngakhale kuti mavuto a anthu ena anali oti iyeyo sanakumanepo nawo. Mwachitsanzo, anthu wamba ankaopa atsogoleri achipembedzo amene ankawanamiza komanso kuwapanikiza ndi malamulo ambirimbiri. (Mat. 23:4; Maliko 7:1-5; Yoh. 7:13) Yesu ankamvetsa mavuto a anthu wambawo ngakhale kuti iye sankaopa atsogoleriwo ndipo iwo sanamunamizepo. Yesu ataona chikhamu cha anthu, “anawamvera chisoni, chifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Yesu anatengera Atate wake ndipo ankakonda anthu komanso kuwachitira chifundo. Yesu akaona anthu ovutika ankawasonyeza chikondi powathandiza. Apa tingati ankatsanzira Atate wake. Pa nthawi ina, Yesu ndi ophunzira ake anapita kutali kwambiri kukalalikira. Ndiyeno anafuna kupeza malo oti apumule. Koma anthu ambirimbiri atafika, iye anawamvera chifundo n’kuyamba “kuwaphunzitsa zinthu zambiri.”​—Maliko 6:30, 31, 34. w15 5/15 4:3, 4

Lachinayi, April 6

Zinthu zimene zinali kundisangalatsa, zinali zokhudzana ndi ana a anthu.​—Miy.  8:31.

Mulungu anasonyeza nzeru zake zakuya pamene analenga Mwana wake woyamba. Pofotokoza za Mwanayo, Baibulo limamutchula kuti nzeru ndipo iye anali “mmisiri waluso” pamene ankagwira ntchito yolenga ndi Atate wake. Ayenera kuti anasangalala pamene Atate wake ankalenga kumwamba ndiponso ‘kukhazikitsa maziko a dziko lapansi.’ Koma ‘zinthu zimene zinali kumusangalatsa kwambiri zinali zokhudza ana a anthu.’ (Miy.  8:22-31) Zimenezi zikusonyeza kuti Yesu anayamba kukonda anthu kuyambira kale kwambiri ali kumwamba. Yesu anasonyeza kuti amakonda kwambiri Atate wake ndiponso anthu. Iye “anasiya zonse zimene anali nazo” ndipo anakhala wofanana ndi anthu n’cholinga choti apereke “moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Afil. 2:5-8; Mat. 20:28) Zimene anachitazi zimasonyeza kuti Yesu amakondadi kwambiri anthu. w15 6/15 2:1, 2

Lachisanu, April 7

Mulungu . . . anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzera mwa iye.​—1 Yoh. 4:9.

Kodi mumayamikira zimene Yehova wakuchitirani? Ngati ndi choncho ndiye kuti muyenera kudzipereka kwa iye komanso kubatizidwa. Komabe kumbukirani kuti munthu akadzipereka kwa Yehova amamulonjeza kuti azichita zimene Yehovayo amafuna zivute zitani. Ndiye kodi muyenera kuchita mantha ndi zimenezi? Ayi. Musaiwale kuti Yehova amakufunirani zabwino ndipo “amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” (Aheb. 11:6) Kudzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa kudzakuthandizani kukhala osangalala. Yehova ndi wosiyana kwambiri ndi Satana. Paja Satana sakufunirani zabwino ndipo sangakuthandizeni kukhala ndi tsogolo labwino. Sangachite zimenezi chifukwa nayenso alibiretu tsogolo. Choncho mukayamba kuchita zofuna zake nanunso simungakhale ndi tsogolo labwino. w16.03 2:16, 18, 19

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 9 kutacha) Luka 19:29-44

Loweruka, April 8

Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva. Inde, ndikudziwa kuti mumandimva nthawi zonse.​—Yoh. 11:41, 42.

Pemphero limatithandiza kuyandikira Yehova. Tikamapemphera tikhoza kutamanda Yehova, kumuthokoza ndiponso kumupempha kuti azititsogolera. (Sal. 32:8) Koma kuti Yehova akhale mnzanu weniweni, muyenera kutsimikizira kuti amamva mukamapemphera. Kuti timvetse zimenezi, tiyeni tiganizire za Yesu. Iye ali kumwamba ankaona Yehova akuyankha mapemphero a atumiki ake padziko lapansi. N’zosadabwitsa kuti Yesuyo ali padziko lapansi ankapemphera kwa Atate wake n’kumawauza za mumtima mwake. Tsiku lina anachezera usiku wonse akupemphera. Kodi iye akanachita izi zikanakhala kuti Yehova samvetsera munthu akamapemphera? (Luka 6:12; 22:40-46) Kodi iye akanalimbikitsa ophunzira ake kuti azipemphera? Yesu ankadziwa kuti pemphero limathandiza kuti anthu azilankhulana ndi Yehova. Nafenso tikhoza kukhala ndi chikhulupiriro chakuti Yehova ndi “wakumva pemphero.”​—Sal. 65:2. w15 4/15 3:11, 13

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 10 kutacha) Luka 19: 45-48; Mateyu 21:18, 19; 21:12, 13

Lamlungu, April 9

Abba, Atate, zinthu zonse n’zotheka kwa inu. Ndichotsereni kapu iyi. Komatu osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.​—Maliko 14:36.

Kodi ana anu amaphunzira chiyani akamva mapemphero anu? N’zoona kuti cholinga cha pemphero si kuphunzitsa ana. Koma mukamapemphera modzichepetsa, anawo amazindikira kuti ayenera kudalira Yehova. Mlongo wina wa ku Brazil dzina lake Ana anati: “Agogo akadwala, kapena pakakhala vuto lililonse, makolo anga ankapempha Yehova kuti awapatse mphamvu kuti apirire vutolo komanso azisankha zochita mwanzeru. Ngakhale pamene apanikizika kwambiri ankaonetsetsa kuti atulira Yehova nkhawa zawo. Izi zinandithandiza kuti nanenso ndizidalira Yehova.” Mukamapemphera limodzi ndi ana anu musamangowapempherera iwowo, koma muzipemphanso Yehova kuti akuthandizeni inuyo. Mwachitsanzo, mungapemphe Yehova kuti akuthandizeni kupempha abwana anu kuti mupite kumsonkhano kapena kuti mulimbe mtima n’kulalikira anthu amene mwayandikana nawo nyumba. Mukamadalira Yehova modzichepetsa, ana anu akhoza kuchitanso chimodzimodzi. w15 11/15 1:7, 8

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 11 kutacha) Luka 20:1-47

Lolemba, April 10

Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.​—Mat. 22:37.

Chinthu chimodzi chimene chingakuthandizeni kuti muzikonda Yehova ndi mtima wonse ndi kuganizira kwambiri dipo limene anapereka. (2 Akor. 5:14, 15; 1 Yoh.4:9, 19) Izi zingakuthandizeni kuti muzisonyeza kuti mumayamikira zimene Mulungu anachitazi. Tiyerekeze kuti mukumira m’madzi ndiye munthu wina wakupulumutsani. Kodi mungangopita kunyumba kukasintha zovala n’kuiwala zimene munthuyo wakuchitirani? Ayi. N’zodziwikiratu kuti mungathokoze munthuyo chifukwa wapulumutsa moyo wanu. N’chimodzimodzinso zimene Yehova ndi Yesu anatichitira. Dipo limene anapereka linatipulumutsa ku uchimo ndi imfa. Chifukwa cha chikondi chimene anatisonyezachi, tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. w16.03 2:16, 17

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 12 kutacha) Luka 22:1-6; Maliko 14:1, 2, 10, 11

Tsiku la Chikumbutso
Dzuwa Litalowa
Lachiwiri, April 11

Khristu anatifera.​—Aroma 5:8.

Yehova amakonda kwambiri Mwana wake Yesu ndipo anapwetekedwa mumtima ataona zinthu zopanda chilungamo zimene anthu anamuchitira. Koma zimene Yesu anachita zinasonyeza kuti munthu wangwiro akhoza kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova ngakhale atakumana ndi mavuto aakulu kwambiri. Yesu anasonyeza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndipo anakhalabe wokhulupirika mpaka imfa ngakhale kuti anakumana ndi mavuto aakulu. Tiyenera kuyamikira kwambiri chifukwa zimene Yesu anachitazi zinatithandizanso kuti tidzapeze moyo wosatha m’dziko latsopano. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu anatisonyeza ife chikondi chake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzera mwa iye. Chikondi chimenechi chikutanthauza kuti ife sitinakonde Mulungu, koma iye ndi amene anatikonda ndi kutumiza Mwana wake monga nsembe yophimba machimo athu.”​—1 Yoh. 4:9, 10. w15 11/15 3:13, 14

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisan 13 kutacha) Luka 22:7-13; Maliko 14:12-16 (Zochitika pa Nisani 14 dzuwa litalowa) Luka 22:14-65

Lachitatu, April 12

Imfa inafalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.​—Aroma 5:12.

Tonsefe tinatengera uchimo ndiponso imfa kwa Adamu. Choncho palibe amene anganene kuti nsembe ya Yesu ndi yosafunika kwa iye. Ngakhale munthu amene amatumikira Yehova mokhulupirika kwambiri amafunika nsembe ya Khristu imene Mulungu anatipatsa. Tonsefe tiyenera kukumbukira kuti Mulungu anatikomera mtima kwambiri potikhululukira machimo athu ndipo zili ngati anatikhululukira ngongole yaikulu. Kodi ifenso tingafune kuchita chiyani tikaganizira chikondi ndiponso chifundo cha Yehova? Ngati tikusungira zifukwa abale ndi alongo athu ena, tiyenera kutsanzira Yehova amene amakhala “wokonzeka kukhululuka.” (Sal. 86:5; Neh. 9:17) Ngati timayamikira kuti Yehova anatikhululukira ngongole yaikulu, timafunanso kukhululukira ena ndi mtima wonse. Yehova sangatikonde komanso kutikhululukira ngati sitikonda ndiponso kukhululukira anzathu. (Mat. 6:14, 15) N’zoona kuti kukhululukira ena sikungasinthe zimene anatilakwirazo, koma kungatithandize kuti tikhale ndi tsogolo labwino. w16.01 2:5, 15-17

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 14 kutacha) Luka 22:66-71

Lachinayi, April 13

Inu amene mwatsatira ine mudzakhalanso m’mipando yachifumu 12, kuweruza mafuko 12 a Isiraeli.​—Mat. 19:28.

Yesu ananena mawu a mulemba lalerowa pofuna kuthandiza Petulo ndi ophunzira ena kuti aziganizira za m’tsogolo. Mawuwa ayenera kuti anathandiza Petulo ndi anzakewo kuona m’maganizo mwawo akulamulira dziko n’kumathandiza anthu omvera kupeza madalitso osaneneka. Anthu a Yehova amasangalala kwambiri akamaganizira zimene zidzachitike pamene Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake. Zinthu zimene Abele ankadziwa zokhudza cholinga cha Mulungu zinamuthandiza kuona kuti ali ndi tsogolo labwino ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Nayenso Abulahamu anali ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa choti ankaona m’maganizo mwake malonjezo onse a Yehova okhudza mbewu yake atakwaniritsidwa. (Gen. 3:15) Mose “anayang’anitsitsa pamphoto imene adzalandire” ndipo izi zinamuthandiza kukonda kwambiri Yehova komanso kumukhulupirira kwambiri. (Aheb. 11:26) Ifenso tikamaona m’maganizo mwathu zimene Mulungu watilonjeza tidzayamba kumukonda kwambiri ndiponso kumukhulupirira ndi mtima wonse. w15 5/15 3:17, 18

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 15 kutacha) Mateyu 27:62-66

Lachisanu, April 14

Khristu . . . anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.​—1 Pet. 2:21.

Mkhristu amene akufuna kufanana ndi Yesu amayesetsanso kudziwa bwino Baibulo. Iye amaliphunzira mozama podziwa kuti “chakudya chotafuna ndi cha anthu okhwima mwauzimu.” (Aheb. 5:14) Mkhristu wolimba amafunitsitsa kuti ‘adziwe molondola Mwana wa Mulungu.’ (Aef. 4:13) Kodi inuyo mumawerenga Baibulo tsiku lililonse? Kodi mumaphunzira Baibulo panokha ndiponso kuchita Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse? Mukamaphunzira Baibulo, muzifufuza mfundo zimene zingakuthandizeni kumvetsa bwino mmene Yehova amaonera zinthu. Kenako muziyesetsa kugwiritsa ntchito mfundozo posankha zochita n’cholinga choti mulimbitse ubwenzi wanu ndi Yehova. Komanso muzilola kuti mzimu woyera uzikutsogolerani. Izi zidzakuthandizani kuti mukhale Mkhristu wolimba. w15 9/15 1:5, 9, 10

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 16 kutacha) Luka 24:1-12

Loweruka, April 15

Khristu ndiye mphamvu ya Mulungu.​—1 Akor. 1:24.

Yesu amadziwa bwinobwino zinthu zonse zokhudza dziko lapansi. Iye amadziwa zimene angachite kuti alamulire bwinobwino zinthu za m’chilengedwe. Yesu ali padziko lapansi, anasonyezadi kuti ali ndi “mphamvu ya Mulungu” chifukwa ankalamulira mphamvu za m’chilengedwe. Taganizirani zimene zinachitika pa nthawi ina. Khristu anali atatoperatu chifukwa chogwira ntchito yolalikira. Mafunde ankamenya kwambiri ngalawa yawo ndipo madzi ankalowa mkati. Koma ngakhale kuti chimphepocho chinkasokosera komanso ngalawayo inkagwedezeka, Yesu ankagonabe chifukwa chotopa kwambiri. Ophunzira ake anachita mantha kwambiri ndipo anamudzutsa pofuula kuti: “Tikufa!” (Mat. 8:25) Yesu anadzuka n’kulamula mphepo ndi nyanja kuti: “Leka! Khala bata!” Nthawi yomweyo, chimphepocho chinasiya. (Maliko 4:39) Ndiyeno “panachita bata lalikulu.” Iye anasonyezadi kuti ali ndi mphamvu zambiri. w15 6/15 1:12-14

Lamlungu, April 16

Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.​—Mat. 6:11.

Pamene Yesu ananena za kupempha chakudya chalero, ankatanthauzanso kuti tisamadere nkhawa za m’tsogolo. Iye anasonyeza kuti Mulungu amaveka maluwa akutchire ndipo anati: “Kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo, achikhulupiriro chochepa inu? Pomaliza, Yesu anabwereza malangizo ofunika kwambiri akuti: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira.” (Mat. 6:30-34) Zimenezi zikusonyeza kuti m’malo mofunafuna chuma, tizikhutira ndi zinthu zofunika za tsiku lililonse. Apa tikunena zinthu monga nyumba, ntchito yotithandiza kusamalira banja lathu ndiponso nzeru zotithandiza kusankha bwino zochita ngati tadwala. Koma tiyenera kupemphereranso zinthu zokhudza kutumikira Yehova, chifukwa ndi zofunika kwambiri. Yesu ananena kuti, “munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mat. 4:4) Choncho tiyenera kumapemphera kuti Yehova apitirize kutipatsa chakudya pa nthawi yake. w15 6/15 5:4, 7, 8

Lolemba, April 17

Musatilowetse m’mayesero.​—Mat. 6:13.

Kodi timapemphera kwa Yehova nthawi zonse kuti atithandize kukhalabe okhulupirika tikakumana ndi mayesero? Mwina tisanaphunzire za Yehova tinkakonda kuchita zinthu zimene iye amadana nazo ndipo n’kutheka kuti zimabwerabe m’maganizo mwathu. Ngakhale zili choncho, Yehova angatithandize kukhalabe oyera. Davide ankadziwa bwino zimenezi. Iye atachita chigololo ndi Bati-seba, anapempha Yehova kuti: “Lengani mtima wolungama mkati mwanga, ndipo ikani maganizo atsopano ndi okhazikika mwa ine.” (Sal. 51:10, 12) N’zoona kuti tingalakelake zinthu zoipa ndipo zingativute kusiya maganizo oipawo. Koma Yehova akhoza kutitsogolerabe kuti tizimvera malamulo ake. Iye akhoza kutithandiza kuti tisamalamuliridwe ndi maganizo oipa.​—Sal. 119:133. w15 6/15 3:5, 6

Lachiwiri, April 18

Pakakhala aphungu ochuluka anthu amapulumuka.​—Miy. 24:6.

Akhristu ena achikulire angakumbukire pamene mpingo uliwonse unkatsogoleredwa ndi mtumiki wa mpingo, nthambi inkatsogoleredwa ndi mtumiki wa nthambi ndipo kulikulu kunkakhala munthu mmodzi wotsogolera zinthu. N’zoona kuti abalewo ankakhala ndi owathandiza, koma munthu mmodzi ndi amene ankasankha zochita. Ndiyeno m’ma 1970 izi zinasintha n’cholinga choti udindo wosankha zochita ukhale wa gulu la abale osati munthu mmodzi. Abale anasankha kusintha zinthuzi atamvetsa zimene Malemba amanena pa nkhani yotsogolera mpingo. M’malo moyendera nzeru za munthu mmodzi, abale osiyanasiyana amathandiza kutsogolera m’gulu la Yehova.​—Aef. 4:8. w15 7/15 1:14, 15

Lachitatu, April 19

Sali mbali ya dziko.​—Yoh. 17:16.

Akhristu ayenera kukhala okhulupirika kwa Mulungu nthawi zonse ndipo sayenera kulowerera ndale. Tikutero chifukwa chakuti munthu amene wadzipereka kwa Yehova amalonjeza kuti azimukonda ndiponso kumumvera nthawi zonse. (1 Yoh. 5:3) Timafunika kumvera malangizo a Yehova mosatengera kumene timakhala, mtundu wathu kapena chikhalidwe chathu. Tiyenera kukonda Yehova ndiponso Ufumu wake kuposa munthu aliyense kapena chinthu chilichonse. (Mat. 6:33) Kuti zimenezi zitheke, Akhristu ayenera kupewa kulowerera m’mikangano yonse ya m’dzikoli. (Yes. 2:4; Yoh. 17:11, 15, 16) Koma anthu omwe si atumiki a Yehova amakonda kwambiri dziko lawo, mtundu wawo, chikhalidwe chawo ngakhalenso timu yamasewera ya dziko lawo. Zimenezi zimachititsa kuti anthu azipikisana, kudana kapena kuphana kumene. Izi zikachitika n’zosavuta kuti nafenso tiyambe kulowerera m’mikangano ya m’dzikoli. w15 7/15 3:1, 2

Lachinayi, April 20

Zinthu zonse zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.​—1 Akor. 14:40.

Nyumba ya Ufumu ikamangidwa, tiyenera kuisamalira kuti izilemekeza Mulungu wadongosolo amene timamulambira. (1 Akor. 14:33) Yehova amafuna kuti anthu ake azikhala oyera. Choncho tiyenera kukhala anthu aukhondo, amaganizo oyera, amakhalidwe abwino ndiponso osadetsedwa ndi kulambira konyenga. (Chiv. 19:8) Tikamayeretsa Nyumba ya Ufumu, sitichita manyazi kuitanira anthu ku misonkhano yathu. Anthuwo akabwera, amaonadi kuti timalambira Mulungu woyera amene adzakonze zinthu padzikoli kuti likhalenso loyera. (Yes. 6:1-3; Chiv. 11:18) Choncho kaya zinthu zili bwanji kwathuko, Nyumba za Ufumu ziyenera kukhala zaukhondo kwambiri chifukwa ndi malo olambirira Yehova.​—Deut. 23:14. w15 7/15 4:13-15

Lachisanu, April 21

Khalani maso.​—Maliko 13:35.

Akhristu atazindikira kuti Yesu wayamba kulamulira mu 1914, anayamba kukonzekera podziwa kuti mapeto akhoza kufika nthawi iliyonse. Iwo anayamba kulalikira mwakhama kwambiri. Kumbukirani kuti Yesu anati akhoza kubwera “atambala akulira kapena m’mawa.” Ndiyeno kodi anati Akhristu ayenera kuchita chiyani? Iye anati: “Khalani maso.” Choncho kaya tadikira kwa nthawi yaitali bwanji, sitiyenera kuganiza kuti mapeto akuchedwa kwambiri kapena alephereka. M’dziko latsopano tizidzakumbukira kuti maulosi onse onena za mapeto a dziko loipali anakwaniritsidwa. Kuganizira zimenezi kudzatithandiza kukhulupirira kwambiri Yehova ndiponso malonjezo ake. (Yos. 23:14) Tidzayamikira kwambiri kuti Mulungu anasankha nthawi yabwino yowonongera dziko loipa ndiponso anatilimbikitsa kukhalabe maso pamene mapetowo ankayandikira.​—Mac. 1:7; 1 Pet. 4:7. w15 8/15 2:10, 11, 14

Loweruka, April 22

Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.​—2 Tim. 3:12.

Anthu ambiri m’dzikoli amasangalala ndi zinthu zimene Baibulo limaletsa. Mwachitsanzo, amakonda zosangalatsa zokhudza chiwawa, chiwerewere ndiponso matsenga. Zinthu zoipazi zimapezeka pa intaneti, pa TV, m’mafilimu, m’mabuku ndiponso m’magazini. Masiku ano, makhalidwe omwe kale ankaoneka kuti ndi oipa akuvomerezedwa m’mayiko ena. Koma Yehova sanasinthe, ndipo amadanabe ndi makhalidwewa. (Aroma 1:28-32) Akhristu oyambirira ankakana kuchita zosangalatsa zosayenera ndipo khalidwe lawo labwino linkachititsa kuti azizunzidwa. M’pake kuti mtumwi Petulo anati: “Chifukwa chakuti simukupitiriza kuthamanga nawo limodzi m’chithaphwi cha makhalidwe oipa, anthu a m’dzikoli sakumvetsa, choncho amakunyozani.”​—1 Pet. 4:4. w15 8/15 4:2, 3

Lamlungu, April 23

Thupi lonselo limakula podzimanga lokha mwachikondi . . . malinga ndi ntchito yoyenerera ya chiwalo chilichonse.​—Aef. 4:16.

Mkhristu wolimba amathandiza kuti mpingo ukhale wogwirizana. (Aef. 4:1-6, 15) Tonsefe timafuna kuti tizichita zinthu mogwirizana mumpingo. Koma kuti zimenezi zitheke, Mawu a Yehova amasonyeza kuti tiyenera kukhala odzichepetsa. Mkhristu wolimba amadzichepetsa n’kumayesetsa kukhala mwamtendere ndi Akhristu anzake ngakhale pamene iwo alakwitsa zinazake. Kodi inuyo mumatani ngati munthu wina mumpingo wakukhumudwitsani kapena walakwitsa zinthu zina? Kodi mumayamba kumupewa ndiponso kusiya kumulankhula? Kapena kodi mumayesetsa kukonza ubwenzi wanu ndi munthuyo? Mkhristu wolimba amayesetsa kuthetsa vutolo osati kulikulitsa. Kodi inuyo mumayesetsa kuthandiza kuti mpingo ukhale wogwirizana? w15 9/15 1:12, 13

Lolemba, April 24

Mawu anu ndiwo choonadi.​—Yoh. 17:17.

Yesu ankakhulupirira kwambiri kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu ndiponso kuti malangizo ake ndi othandiza. Ifenso tiyenera kuwerenga Baibulo tsiku lililonse, kuliphunzira ndiponso kusinkhasinkha zimene taphunzirazo. Tiyeneranso kufufuza mozama m’Baibulo kuti tipeze mayankho a mafunso amene tingakhale nawo. Mwachitsanzo, tikhoza kuphunzira mwatsatanetsatane umboni wa m’Baibulo wakuti tikukhala m’masiku otsiriza. Kuchita zimenezi kungatithandize kukhulupirira kwambiri kuti mapeto ayandikira. Tikhozanso kuphunzira maulosi amene akwaniritsidwa kale n’cholinga choti tizikhulupirira kwambiri malonjezo amene adzakwaniritsidwe m’tsogolo. Kuwerenga za anthu amene anasintha moyo wawo ataphunzira za Yehova, kungatithandizenso kukhulupirira zoti mfundo za m’Baibulo n’zothandiza kwambiri. (1 Ates. 2:13) Tingatsanzire Yesu tikamaganizira zinthu zabwino zimene Yehova watilonjeza. (Aheb. 12:2) Aliyense ayenera kuona kuti zinthu zimene tikuyembekezera n’zimene Mulungu wamulonjeza iyeyo payekha osati gulu la anthu. w15 9/15 3:16, 17

Lachiwiri, April 25

Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali.​—Miy. 3:9.

Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Mulungu? Tikhoza kupereka chuma chathu kuti chithandize pa ntchito yolalikira m’dziko lathu kapena padziko lonse. Kaya timapereka zambiri kapena zochepa, timasonyezabe kuti timakonda Yehova. (2 Akor. 8:12) Koma tingasonyeze kuti timakonda Yehova m’njira zinanso. Kumbukirani kuti Yesu ananena kuti tisamade nkhawa za chakudya kapena zovala koma tiziika patsogolo Ufumu. Paja Atate wathu wakumwamba analonjeza kuti azitipatsa zinthu zofunika pa moyo. (Mat. 6:31-33) Tikamakhulupirira kwambiri lonjezo limeneli timasonyeza kuti timakonda kwambiri Yehova. Tikutero chifukwa chakuti munthu sangakonde mnzake amene samukhulupirira. (Sal. 143:8) Choncho tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zolinga ndiponso zochita zanga zimasonyeza kuti ndimakondadi Yehova? Kodi zimene ndimachita tsiku lililonse zimasonyeza kuti ndimakhulupirira zoti Yehova adzandisamalira?’ w15 9/15 5:7, 8

Lachitatu, April 26

Popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu.​—Aheb. 11:6.

Mwina munayamba mwadzifunsapo kuti, ‘Kodi Yehova amaona kuti ineyo ndi woyenera kupulumuka chisautso chachikulu n’kulowa m’dziko latsopano?’ Chinthu chofunika kwambiri ndi kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Mtumwi Petulo ananena kuti anthu amene chikhulupiriro chawo chayesedwa adzadalitsidwa pa nthawi imene ‘zochita za Yesu Khristu zidzaululika.’ (1 Pet. 1:7) Popeza chisautso chachikulu chikuyandikira, tiyenera kuyesetsa kuti tikhale m’gulu la “anthu okhala ndi chikhulupiriro chosunga moyo.” (Aheb. 10:39) Izi zingatichititse kupemphera ngati munthu wina amene anati: “Limbitsani chikhulupiriro changa.” (Maliko 9:24) Apo ayi, tikhoza kunena mawu a atumwi a Yesu akuti: “Tiwonjezereni chikhulupiriro.”​—Luka 17:5. w15 10/15 2:1, 2

Lachinayi, April 27

Tiyeninso tivule cholemera chilichonse.​—Aheb. 12:1.

Paulo ankaika maganizo ake pa “zinthu zofunika kwambiri.” Ankalalikira mwakhama m’madera monga ku Siriya, Asia Minor, Makedoniya komanso ku Yudeya. Iye analemba kuti: “Ndikuiwala zinthu zakumbuyo ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo. Ndikuyesetsa kuchita zimenezi mpaka nditapeza mphoto.” (Afil. 1:10; 3:8, 13, 14) Paulo anali wosakwatira ndipo zimenezi zinamuthandiza kuti azitumikira “Ambuye nthawi zonse popanda chododometsa.” (1 Akor. 7:32-35) Akhristu ena amasankhanso kuti asakhale pa banja n’cholinga choti akhale ndi nthawi yambiri yotumikira Yehova. (Mat. 19:11, 12) Atumiki a Yehova amene ali pa banja amakhala ndi maudindo ambiri osamalira banjalo. Komabe kaya tili pa banja kapena ayi, tonsefe tikhoza ‘kuvula cholemera chilichonse’ chimene chingatisokoneze potumikira Yehova. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kupewa zinthu zimene zingatiwonongere nthawi n’cholinga choti tizichita zambiri mu utumiki. w15 10/15 3:15, 16

Lachisanu, April 28

Anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe.​—2 Tim. 3:13.

Zimene zakhala zikuchitika padzikoli zikutsimikizira mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Ine ndikudziwa bwino, inu Yehova, kuti munthu wochokera kufumbi alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” (Yer. 10:23) Yehova sanalenge anthu kuti azidzilamulira okha. Zimene Mulungu walola kuti zichitikezi zatsimikizira kuti ulamuliro wake wokha ndi umene ungathandize anthu. Posachedwapa Mulungu adzachotsa oipa onse. Pambuyo pa zimenezi, Yehova sadzalekereranso munthu aliyense amene angadzatsutse ulamuliro wake. Izi zidzakhala choncho chifukwa panopo tili ndi umboni wokwanira wosonyeza kuti anthu otsutsa sangalamulire bwino ndipo ayenera kuwonongedwa mwamsanga. w15 11/15 3:5, 6

Loweruka, April 29

Mulungu wamtendere . . . akukonzekeretseni ndi chilichonse chabwino kuti muchite chifuniro chake.​—Aheb. 13:20, 21.

Yesu ali padziko lapansi, ankakonda kulalikira za Ufumu wa Mulungu. Baibulo limasonyeza kuti iye anatchula za Ufumu wa Mulungu maulendo oposa 100. Zimenezi zikusonyeza kuti ankaona kuti Ufumuwo ndi wofunika kwambiri. (Mat. 12:34) Tsiku lina Yesu ataukitsidwa, anakumana ndi anthu oposa 500. (1 Akor. 15:6) N’kutheka kuti pa nthawiyi m’pamene anapereka lamulo lakuti otsatira ake azikalalikira “anthu a mitundu yonse.” Koma ntchito imene anawauza kuti agwireyi sinali yophweka. Iye ananeneratu kuti ntchito yolalikirayi idzachitika mpaka “m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” Choncho tikamagwira nawo ntchito imeneyi timathandiza kuti ulosiwu ukwaniritsidwe. (Mat. 28:19, 20) Ndipotu Yehova amatipatsa “chilichonse chabwino” kuti tizigwira bwino ntchito imeneyi. w15 11/15 5:1-3

Lamlungu, April 30

Limeneli ndilo dzina langa mpaka kalekale.​—Eks. 3:15.

M’mipukutu imene inapezeka pafupi ndi Nyanja Yakufa komanso m’zolemba zina zakale zachiheberi, mumapezeka kambirimbiri zilembo 4 zoimira dzina la Mulungu. Dzina la Mulungu limapezekanso m’Mabaibulo ena achigiriki (a Septuagint) omwe anapezeka pakati pa zaka pafupifupi 200 Yesu asanabadwe ndi zaka pafupipafupi 100 iye atabadwa. Ngakhale kuti pali umboni wokwanira woti dzina la Mulungu liyenera kupezeka m’Baibulo, pali Mabaibulo ambiri amene dzinali linachotsedwamo. Mu 1952, M’Baibulo la Revised Standard Version anachotsamo dzina la Mulungu ngakhale kuti pamene linkatuluka koyamba mu 1901, dzinali linkapezekamo. Mawu ake oyamba amafotokoza chifukwa chimene anachotsera dzinali. Amati: “Kugwiritsa ntchito dzina lenileni la Mulungu . . . n’kosayenera pa chikhulupiriro cha Akhristu.” Izi zitachitika, omasulira ena anachotsanso dzina la Mulungu m’Mabaibulo awo. w15 12/15 2:3-5

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena