Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es17 tsamba 47-57
  • May

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • May
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
  • Timitu
  • Lolemba, May 1
  • Lachiwiri, May 2
  • Lachitatu, May 3
  • Lachinayi, May 4
  • Lachisanu, May 5
  • Loweruka, May 6
  • Lamlungu, May 7
  • Lolemba, May 8
  • Lachiwiri, May 9
  • Lachitatu, May 10
  • Lachinayi, May 11
  • Lachisanu, May 12
  • Loweruka, May 13
  • Lamlungu, May 14
  • Lolemba, May 15
  • Lachiwiri, May 16
  • Lachitatu, May 17
  • Lachinayi, May 18
  • Lachisanu, May 19
  • Loweruka, May 20
  • Lamlungu, May 21
  • Lolemba, May 22
  • Lachiwiri, May 23
  • Lachitatu, May 24
  • Lachinayi, May 25
  • Lachisanu, May 26
  • Loweruka, May 27
  • Lamlungu, May 28
  • Lolemba, May 29
  • Lachiwiri, May 30
  • Lachitatu, May 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
es17 tsamba 47-57

May

Lolemba, May 1

Onse anayamba . . . kudabwa ndi mawu ogwira mtima otuluka pakamwa pake.​—Luka 4:22.

Tingatsanzire Yesu polankhula mokoma mtima ndiponso kuchita zinthu moganizira ena. Pa nthawi ina, anthu anayesetsa kupita kumene kunali Yesu, n’cholinga choti akamve mawu ake. Iye atawaona, anawamvera chifundo ndipo “anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Maliko 6:34) Ngakhale pamene anthu ankamunyoza, sanabwezere ndi mawu achipongwe. (1 Pet. 2:23) Nthawi zina zimakhala zovuta kulankhula mwaulemu kwa achibale kapena anzathu mu mpingo chifukwa choti tinawazolowera. Tingaganize kuti tikhoza kuwalankhula mawu alionse ndipo sangakhumudwe. Koma kodi Yesu ankaona kuti akhoza kulankhula mawu alionse kwa ophunzira ake chifukwa choti anali anzake? Ayi. Mwachitsanzo, atumwi ake atakangana pa nkhani yakuti wamkulu ndani, Yesu anawathandiza mokoma mtima pogwiritsa ntchito chitsanzo cha mwana wamng’ono. (Maliko 9:33-37) Nawonso akulu angachite bwino kutsanzira Yesu popereka malangizo “ndi mzimu wofatsa.”​—Agal. 6:1. w15 12/15 3:15, 16

Lachiwiri, May 2

Mupitirize kukonda abale.​—Aheb. 13:1.

N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kukonda abale? Chifukwa choyamba, ndi choti Mulungu amafuna kuti tizichita zimenezi. Sitinganene kuti timakonda Mulungu ngati sitikonda abale athu. (1 Yoh. 4:7, 20, 21) Chifukwa china n’chakuti timafunika kuthandizana, makamaka tikakumana ndi mavuto. Paulo ankadziwa kuti Akhristu ena achiheberi amene anawalembera kalata yake, adzayenera kuthawa n’kusiya nyumba komanso katundu wawo. Yesu ananena kuti nthawi imeneyo idzakhala yovuta kwambiri. (Maliko 13:14-18; Luka 21:21-23) Choncho Akhristuwo ankafunika kukondana kwambiri kuti adzathe kuthandizana pa nthawi yovutayo. (Aroma 12:9) Posachedwapa chisautso chachikulu chiyamba. (Maliko 13:19; Chiv. 7:1-3) Choncho kungosonkhana ndi abale athu sikokwanira. Mtumwi Paulo anauza Akhristu achiheberi kuti akasonkhana ayenera kulimbikitsana kuti azikondana.​—Aheb. 10:24, 25. w16.01 1:6-8

Lachitatu, May 3

Onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera.​—Mac. 2:4.

M’chaka cha 33 C.E., anthu ambiri anasonkhana ku Yerusalemu kuti achite mwambo wa Pentekosite. Ophunzira a Khristu pafupifupi 120 anali atasonkhana m’chipinda china cham’mwamba ndipo ‘ankapemphera.’ (Mac. 1:13-15) Zimene zinali zitatsala pang’ono kuchitika zinakwaniritsa ulosi wa Yoweli. (Yow. 2:28-32; Mac. 2:16-21) Pa tsikuli ophunzira a Khristuwo analandira mzimu woyera wa Mulungu. (Mac. 1:8) Kenako gulu la anthu linafika pamalopo ndipo ophunzirawo anayamba kuwauza zinthu zodabwitsa za Mulungu zimene anaona komanso kumva. Ndiyeno Petulo anawafotokozera kufunika kwa zimene zinachitikazo. Kenako anawauza kuti: “Lapani, ndipo aliyense wa inu abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Mukatero mudzalandira mphatso yaulere ya mzimu woyera.” Atanena zimenezi anthu pafupifupi 3,000 anabatizidwa n’kulandira mzimu woyera.​—Mac. 2:37, 38, 41. w16.01 3:1-3

Lachinayi, May 4

Aliyense wakudya mkatewu kapena kumwa za m’kapu ya Ambuye mosayenerera, adzakhala ndi mlandu wokhudza thupi ndi magazi a Ambuye.​—1 Akor. 11:27.

Kodi palembali Paulo ankatanthauza chiyani? Ankatanthauza kuti ngati wodzozedwa sakutumikira Mulungu mokhulupirika, ndiye kuti amadya zizindikiro “mosayenerera.” (Aheb. 6:4-6; 10:26-29) Lembali limathandizanso odzozedwa kukumbukira kuti ayenera kukhalabe okhulupirika kuti adzalandire mphoto yawo. Ayenera kuchita zimenezi mpaka ‘adzapeze mphoto ya chiitano cha Mulungu chopita kumwamba, chodzera mwa Khristu Yesu.’ (Afil. 3:13-16) Paulo anauza Akhristu odzozedwa kuti ‘aziyenda moyenera.’ Kodi angachite bwanji zimenezi? Iye anati: “Muziyenda modzichepetsa nthawi zonse, mofatsa, moleza mtima, ndiponso mololerana m’chikondi. Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa.” (Aef. 4:1-3) Mzimu wa Mulungu umathandiza munthu kuti akhale wodzichepetsa osati wonyada.​—Akol. 3:12. w16.01 4:5, 6

Lachisanu, May 5

Mulungu . . . anamuyesa Abulahamu.​—Gen. 22:1.

Pa nthawi ina, mwina Abulahamu ali ndi zaka 125 anali pa ulendo wodutsa m’njira ya m’mapiri. Pa ulendowu Abulahamu anali ndi mwana wake Isaki yemwe anali ndi zaka 25. Isaki ananyamula nkhuni ndipo Abulahamu ananyamula mpeni komanso zoyatsira moto. Ulendowu unali wovuta kwambiri kwa Abulahamu. Koma osati chifukwa choti anali wokalamba, popeza pa nthawiyi anali adakali ndi mphamvu. Unali wovuta chifukwa Yehova anali atamuuza kuti akapereke nsembe mwana wakeyo. (Gen. 22:1-8) Zimene Yehova anauza Abulahamu kuti achitezi, zikanasonyeza ngati Abulahamu analidi ndi chikhulupiriro cholimba kapena ayi. Si zoona kuti Abulahamu ankangomvera Mulungu m’chimbulimbuli. M’malomwake ankamvera chifukwa anali ndi chikhulupiriro cholimba. Ankadziwa kuti Atate wake wakumwamba sangamupemphe kuti achite zinthu zimene zingapangitse kuti avutike mpaka kalekale. Abulahamu ankadziwa kuti akamvera Yehova, Yehovayo adzamudalitsa komanso kudalitsa mwana wake. Koma kodi zinatheka bwanji kuti iye akhale ndi chikhulupiriro chimenechi? Ndi chifukwa cha zimene ankadziwa komanso zomwe anakumana nazo pa moyo wake. w16.02 1:3, 4

Loweruka, May 6

Ndinetu kapolo wa Yehova! Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.​—Luka 1:38.

Mariya anapatsidwa ntchito yoti adzabereke ndi kulera Mwana wa Mulungu. Nthawi zambiri timangoganizira za mwayi waukulu umene Mariya anapatsidwawu, koma sitiganizira nkhawa zimene mwina anali nazo atapatsidwa ntchitoyi. Mwachitsanzo, mngelo Gabirieli anamuuza kuti adzakhala ndi pakati ngakhale kuti sanagone ndi mwamuna aliyense. Gabirieli sananene kuti auza achibale ndiponso anzake a Mariya zimene zichititse kuti Mariyayo akhale ndi pakati. Choncho mwina Mariya ankadera nkhawa zimene anthu angaganize akamva kuti ndi woyembekezera. Ayeneranso kuti ankadera nkhawa kwambiri kuti amuuza bwanji Yosefe, yemwe anali naye pa chibwenzi. Kodi akanamufotokozera bwanji kuti akhulupirire zoti sanachite zosayenera? Komanso, kodi mukuganiza kuti Mariya ankamva bwanji akaganizira udindo waukulu womwe anali nawo wolera Mwana wa Mulungu? Sitingadziwe nkhawa zonse zimene Mariya anali nazo atamva nkhaniyi. Komabe chimene tikudziwa n’choti anayankha Gabirieli mawu amene ndi lemba lalerowa.​—Luka 1:26-37. w16.02 2:13, 14

Lamlungu, May 7

Husai Mwareki akubwera kudzakumana naye, atang’amba chovala chake ndiponso atadzithira dothi kumutu.​—2 Sam. 15:32.

Husai anali mnzake wokhulupirika wa Mfumu Davide. Pamene anthu ankafuna kuika Abisalomu kuti akhale mfumu, Husai anafunika kulimba mtima kuti akhalebe wokhulupirika kwa Davide komanso kwa Mulungu. Ankadziwa kuti Abisalomu walowa mu Yerusalemu limodzi ndi asilikali ake ndipo Davide wathawa mumzindawo. (2 Sam. 15:13; 16:15) Ndiye kodi Husai anatani? Kodi anasiya Davide n’kuyamba kutsatira Abisalomu? Ayi. Ngakhale kuti Davide anali wokalamba ndipo anthu ambiri ankafuna kumupha, Husai anakhalabe wokhulupirika kwa iye chifukwa anali mfumu yosankhidwa ndi Mulungu. Choncho anapita kukakumana ndi Davide kuphiri la Maolivi. (2 Sam. 15:30) Ndiyeno Davide anapempha Husai kubwerera ku Yerusalemu kuti akanamizire kukhala kumbali ya Abisalomu. Anapempha zimenezi chifukwa ankafuna kuti Abisalomu ayambe kumvera malangizo a Husai m’malo momvera Ahitofeli. Husai anamvera Davide ngakhale kuti izi zinaika moyo wake pa ngozi. Zimenezi zinasonyezanso kuti anali wokhulupirika kwa Yehova. Davide anapempha Yehova kuti athandize Husai ndipo anamuthandizadi. Tikutero chifukwa chakuti Abisalomu anayamba kumvera malangizo a Husai m’malo momvera Ahitofeli.​—2 Sam. 15:31; 17:14. w16.02 4:15, 16

Lolemba, May 8

Madalitso onsewa adzakutsata ndi kukupeza chifukwa ukumvera mawu a Yehova Mulungu wako.​—Deut. 28:2.

Malangizo amene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli ndi othandizanso kwa ife. Tikutero chifukwa chakuti ngakhale kuti sititsatira Chilamulo, mfundo zake zingatithandize pa moyo wathu komanso polambira Yehova. Yehova analola kuti Chilamulo chilembedwe m’Baibulo n’cholinga choti tiphunzirepo kanthu komanso mfundo zake zizititsogolera. Anafunanso kuti chizitithandiza kuzindikira kuti zimene Yesu anatiphunzitsa ndi zofunika kwambiri. Mwachitsanzo, Yesu ananena kuti: “Inu munamva kuti anati, ‘Usachite chigololo.’ Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.” Choncho, sikuti tiyenera kungopewa chigololo, koma tiyeneranso kupewa maganizo amene angatipangitse kuti tichite chigololocho.​—Mat. 5:27, 28. w16.03 4:6, 8

Lachiwiri, May 9

Utiikire mfumu yoti izitiweruza.​—1 Sam. 8:5.

Samueli sankafuna kuchita zimene anthu ananenazi moti Yehova anamuuza katatu kuti awamvere. (1 Sam. 8:7, 9, 22) Ngakhale zinali choncho, Samueli sankachitira nsanje munthu womulowa m’maloyo. Yehova atamuuza kuti adzoze Sauli, iye anachita zimenezi ndi mtima wonse osati monyinyirika. Masiku anonso, akulu ayenera kukhala ndi mtima wofuna kuphunzitsa anthu. (1 Pet. 5:2) Sayenera kuopa kuphunzitsa ena poganiza kuti awalanda udindo. Aphunzitsi abwino amaona kuti anthu amene akuwaphunzitsa ndi ‘antchito anzawo’ osati anthu amene akupikisana nawo. (2 Akor. 1:24) Iwo amadziwa kuti anthuwo ndi mphatso zamtengo wapatali mumpingo. (Aheb. 13:16) Kunena zoona aphunzitsi abwinowa amasangalala akaona anthu amene awaphunzitsa akuthandiza kwambiri mumpingo.​—Mac. 20:35. w15 4/15 1:16, 17

Lachitatu, May 10

Ndidzakuwongolera pa mlingo woyenera.​—Yer. 30:11.

Mfumu Azariya inapitiriza “kuchita zolungama pamaso pa Yehova.” Koma “Yehova anaichititsa khate mfumuyo moti inakhalabe yakhate mpaka tsiku limene inamwalira.” (2 Maf. 15:1-5) Baibulo silinena chifukwa chake Yehova anachita zimenezi. Kodi nkhaniyi iyenera kutidetsa nkhawa n’kumaona kuti Yehova analanga Azariya popanda chifukwa? Ngati timadziwa bwino mmene Yehova amachitira zinthu, sitingade nazo nkhawa. Mfumu Azariya ankatchedwanso Mfumu Uziya. (2 Maf. 15:7, 32) Ndiyeno pa 2 Mbiri 26:3-5, komanso vesi 16 mpaka 21, timawerenga kuti Uziya ankachita zolungama pamaso pa Yehova koma “atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza mpaka kufika pom’pweteketsa.” Iye sanali wansembe koma anasonyeza kukula mtima n’kuyamba kugwira ntchito ya ansembe. Ansembe 81 anamudzudzula koma iye anachita makani mpaka ‘anakwiyira kwambiri’ ansembewo. Izi zinachititsa kuti Yehova amulange pomuchititsa khate. w15 4/15 3:8, 9

Lachinayi, May 11

Chinjokacho chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.​—Chiv. 12:9.

Monga mmene taonera mulemba la leroli, Satana amatchulidwa ndi mayina akuti “Mdyerekezi,” “njoka yakale ija” ndiponso “chinjoka.” Dzina lakuti Mdyerekezi limatanthauza “Woneneza” ndipo limasonyeza kuti Satana wakhala akuneneza Yehova kuti ndi wabodza. Koma dzina lakuti “njoka yakale ija,” limatikumbutsa nthawi yomwe anagwiritsa ntchito njoka popusitsa Hava m’munda wa Edeni. Ndiyeno dzina lakuti “chinjoka,” likusonyeza kuti iye ali ngati chilombo choopsa chimene chikulimbana ndi zolinga za Yehova ndipo chimafuna kuwononga atumiki a Mulungu. Tikaganizira mayinawa, titha kuona kuti tiyenera kusamala kuti Satana asatilepheretse kutumikira Yehova. M’pake kuti Baibulo limatichenjeza kuti: “Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso. Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Pet. 5:8) N’zosakayikitsa kuti Satana amasangalala kwambiri akaona mtumiki wa Mulungu akuchita machimo akuluakulu. Ndipo zikatero amaona kuti wapambana n’kuyamba kunyoza Mulungu.​—Miy. 27:11. w15 5/15 1:3, 4, 10

Lachisanu, May 12

Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.​—1 Tim. 6:10.

Yehova amafuna kuti tizikhala ndi moyo wabwino kwambiri. Umboni wake ndi munda wokongola umene anapatsa Adamu ndi Hava. (Gen. 2:9) Koma Satana angasokoneze maganizo athu ndi “chinyengo champhamvu cha chuma.” (Mat. 13:22) Anthu ambiri amaganiza kuti chuma chambiri chingawachititse kukhala osangalala. Maganizo amenewa ndi bodza lenileni ndipo angasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Yesu anachenjeza otsatira ake kuti: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” (Mat. 6:24) Satana amafuna kuti tizichita khama kusakasaka chuma n’cholinga choti tisiye kutumikira Yehova. Choncho tisalole kuti chuma chisokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Kuti tigonjetse Satana tiyenera kupewa kukonda zinthu za m’dzikoli.​—1 Tim. 6:6-10. w15 5/15 2:12

Loweruka, May 13

Chiwalo chimodzi chikavutika, ziwalo zina zonse zimavutikira nacho limodzi.​—1 Akor. 12:26.

Kunena zoona, si zophweka kumvetsa mavuto a anthu ena chifukwa mavuto ena ndi oti sitinakumanepo nawo. Anthu ena akuvutika chifukwa chovulala, matenda kapena ukalamba. Enanso akuvutika maganizo chifukwa cha nkhawa kapena kuchitiridwa nkhanza. Ndiyenso pali ena amene ali m’banja ndi anthu osakhulupirira kapena akulera okha ana. Ndiye tingasonyeze bwanji chikondi cha Yehova kwa anthu amene akukumana ndi mavuto omwe sitinakumanepo nawo? Tiyenera kumawamvetsera mwachifundo akamafotokoza mavuto awo kuti tidziwe mmene akumvera mumtima mwawo n’kuona mmene tingawathandizire. Mwina tingawalimbikitse ndi mfundo za m’Baibulo kapena kuwathandiza m’njira ina. Tikamatero ndiye kuti tikutsanzira Yehova.​—Aroma 12:15; 1 Pet. 3:8. w15 5/15 4:6, 7

Lamlungu, May 14

Khristu ndiye mphamvu ya Mulungu.​—1 Akor. 1:24.

Mphamvu za Khristu zimachokera kwa Yehova. Choncho tingakhulupirire kuti Yehovayo akhoza kulamulira mosavuta mphamvu za m’chilengedwe. Mwachitsanzo, chigumula chisanachitike, Yehova anati: “Kwangotsala masiku 7 okha kuti ndigwetse chimvula padziko lapansi kwa masiku 40, usana ndi usiku.” (Gen. 7:4) Komanso lemba la Ekisodo 14:21 limati: “Yehova anachititsa mphepo yamphamvu yakum’mawa kuyamba kugawa nyanjayo.” Lemba la Yona 1:4 limanenanso kuti: “Yehova anabweretsa chimphepo champhamvu panyanjapo, ndipo panachita mkuntho wamphamvu. Chotero chombocho chinatsala pang’ono kusweka.” Timalimbikitsidwa kudziwa kuti Yehova amatha kulamulira mphamvu za m’chilengedwe. Choncho sitiyenera kudera nkhawa za m’tsogolo. Tangoganizirani, pa nthawiyo ‘chihema cha Mulungu chidzakhala pakati pa anthu’ ndipo mphamvu za m’chilengedwe sizidzaphanso anthu kapena kuwavulaza. (Chiv. 21:3, 4) Sitiyenera kukayikira kuti Khristu ali ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu ndipo adzatha kulamulira mphamvu za m’chilengedwe pa zaka zonse 1,000 za ulamuliro wake. w15 6/15 1:15, 16

Lolemba, May 15

Njira yako ikhale kutali ndi [mkazi wachiwerewere]. Usayandikire pakhomo la nyumba yake.​—Miy. 5:8.

Chaputala 7 cha buku la Miyambo chimasonyeza mavuto amene amakhalapo tikanyalanyaza malangizo ali pamwambawa. M’chaputalachi muli nkhani ya mnyamata wina amene anapita kukawongola miyendo pafupi ndi nyumba ya mkazi wachiwerewere. Mnyamatayo anachita chiwerewere ndi mkaziyo. Iye akanapewa kuyenda pafupi ndi mkaziyo, sakanakumana ndi mavuto amenewa. (Miy. 7:6-27) Kodi nafenso nthawi zina sitiganiza bwino? N’kutheka kuti timachita zinthu kapena kupezeka pamalo amene angatigwetsere m’mavuto. Mwachitsanzo, zinthu zokhudza chiwerewere zimakonda kuonetsedwa pa TV usiku. Ndiyeno ngati tili ndi chizolowezi chosakasaka matchanelo usikuwo, tikhoza kuona zosayenera. Nanga timachita bwanji tikakhala pa intaneti? Kodi timangotsatira malinki amene abwera kapena kupita pamalo ochezera alionse? Kupanda kusamala pa nkhaniyi, tikhoza kuonanso zolaula. Tikaona zinthu zosayenera ngati zimenezi tikhoza kuyamba kuzilakalaka mpaka kufika pochimwira Yehova. w15 6/15 3:8, 9

Lachiwiri, May 16

Mutikhululukire zolakwa zathu.​—Mat. 6:12.

Mawu a m’munsi a palemba laleroli, akusonyeza kuti mawu amene anamasuliridwa kuti “zolakwa” kwenikweni amatanthauza “ngongole.” (Luka 11:4) Mu 1951, Nsanja ya Olonda inafotokoza chifukwa chimene Yesu anagwiritsira ntchito mawuwo. Magaziniyo inati tikachimwira Yehova zimakhala ngati tili naye ngongole. Anthufe tiyenera kukonda ndiponso kumvera Yehova. Koma tikachimwa timalephera kupatsa Mulungu zinthu zimene amayenera kulandira. Timalephera kusonyeza kuti timamukonda. Ndiyeno Yehova ali ndi ufulu wothetsa ubwenzi wake ndi anthu amene achimwa chifukwa ali ndi ngongole yomwe malipiro ake ndi imfa. (1 Yoh. 5:3) Tsiku lililonse timalakwira Mulungu. Choncho timayamikira kwambiri kuti iye anapereka nsembe ya dipo ya Yesu kuti azitha kutikhululukira. Yesu anatifera zaka pafupifupi 2,000 zapitazo koma nsembeyo imatithandizabe panopa. Palibe munthu wina amene akanakwanitsa kupereka dipo limeneli.​—Sal. 49:7-9; 1 Pet. 1:18, 19. w15 6/15 5:9, 10

Lachitatu, May 17

Ine ndidzalemekeza malo oikapo mapazi anga.​—Yes. 60:13.

Mabuku athu ndi okongola kwambiri ndipo mumakhala nkhani zogwira mtima komanso zothandiza kwambiri. Muyenera kuti mumasangalala kugawira mabukuwa mu utumiki. Tikamagwiritsa ntchito webusaiti ya jw.org kuti tilalikire, timasonyeza mtima wa Yehova wofuna kuthandiza anthu kulikonse kuti apeze malangizo ofunika kwambiri. Timayamikiranso kuti zinthu zinasintha kuti tikhale ndi nthawi yochita Kulambira kwa Pabanja kapena kuphunzira Baibulo patokha. Mapulogalamu a misonkhano ikuluikulu asinthanso ndipo zinthu zosangalatsa pa misonkhanoyi zimawonjezereka chaka chilichonse. Timayamikiranso kuti masiku ano pali masukulu ambiri ophunzitsa Baibulo. Zonsezi zikusonyeza kuti Yehova ndi amene akuyendetsa zinthu. Iye akupitiriza kukongoletsa gulu lake ndiponso paradaiso wathu wauzimu. w15 7/15 1:16, 17

Lachinayi, May 18

Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.​—Luka 10:27.

Ngati zikukuvutani kudziwa zochita pa nkhani inayake, muyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi akanakhala Yesu akanachita chiyani?’ M’dziko limene Yesu ankakhala munali anthu ochokera m’madera osiyanasiyana monga Yudeya, Galileya ndi Samariya. Baibulo limasonyeza kuti anthu ochokera m’maderawa sankagwirizana. (Yoh. 4:9) Panalinso kusagwirizana pakati pa Afarisi ndi Asaduki, anthu wamba ndi okhometsa misonkho komanso anthu ophunzira ndi osaphunzira. (Mat. 9:11; Yoh. 7:49; Mac. 23:6-9) Chinanso n’chakuti pa nthawiyo Aisiraeli ankalamuliridwa ndi Aroma ndipo sankagwirizana nawo. N’zoona kuti Yesu ankauza anthu molimba mtima za Yehova ndipo ankadziwa kuti Aisiraeli anali anthu ake apadera. Koma sankaphunzitsa ophunzira ake kuti iwo anali abwino kuposa anthu ena. (Yoh. 4:22) M’malomwake, ankawaphunzitsa kuti azikonda anthu onse. w15 7/15 3:5

Lachisanu, May 19

Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa. Munthu . . . angandichite chiyani? Yehova ali kumbali yanga, . . . akundithandiza.​—Sal. 118:6, 7.

Anthufe tinalengedwa ndi mtima wofuna kukonda ena komanso kukondedwa. Koma nthawi zina tikhoza kukhumudwa chifukwa cha mavuto azachuma, matenda kapena mavuto ena pamene tikutumikira Mulungu. Mavuto amenewa angatichititse kumva ngati Yehova satikonda. Maganizowa akabwera tiyenera kukumbukira kuti iye amationa kuti ndife amtengo wapatali ndipo ‘wagwira dzanja lathu lamanja’ kuti atithandize. Tikakhalabe okhulupirika, iye sadzatiiwala. (Yes. 41:13; 49:15) Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Brigitte, analera yekha ana ake awiri mwamuna wake atamwalira. Iye anati: “Kulera ana m’dziko loipali n’kovuta kwambiri, makamaka ukamawalera wekha. Koma ndimayamikira kuti Yehova amandikonda kwambiri ndipo amandithandiza ndikakhala pa mavuto. Ndimamuthokonzanso kwambiri chifukwa salola kuti ndikumane ndi mavuto mpaka kufika pamene sindingathe kupirira.”​—1 Akor. 10:13. w15 8/15 1:1-3

Loweruka, May 20

Uziwayembekezerabe.​—Hab. 2:3.

Mneneri Habakuku anauzidwa kuti alosere zoti mzinda wa Yerusalemu udzawonongedwa. Pamene iye ankayamba ntchitoyi, n’kuti zoti mzindawu udzawonongedwa zitanenedwa kwa zaka zambiri ndipo zinthu zinali zitafika poipa. Baibulo limati ‘chilungamo chinapotozedwa chifukwa anthu oipa ankapondereza anthu olungama.’ Ndiyeno Habakuku anafunsa kuti: ‘Kodi ndidzalirira thandizo kufikira liti?’ Yehova anauza mneneri wokhulupirikayu kuti aziyembekezerabe ndipo anamutsimikizira kuti ulosiwo sudzachedwa kukwaniritsidwa. (Hab. 1:1-4) Kodi chikanachitika n’chiyani ngati Habakuku akanagwa ulesi n’kumati: ‘Aa zoti Yerusalemu adzawonongedwa tinayamba kuzimva kalekale. Mwina sizichitika posachedwa. Ndiye ine ndizidzivutitsa kulalikira ngati kuti mzindawo uwonongedwa pompanopompano? Ndingozisiya, olalikira adzapezeka.’ Habakuku akanakhala ndi maganizo amenewa ubwenzi wake ndi Yehova ukanasokonekera ndipo mwina akanafa pa nthawi imene Ababulo ankawononga Yerusalemu. w15 8/15 2:12, 13

Lamlungu, May 21

Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.​—1 Akor. 15:33.

Tiyenera kupewa kucheza ndi anthu oipa n’cholinga choti makhalidwe athu abwino asawonongeke. Apa tikutanthauza anthu omwe salambira Mulungu ndiponso anthu amene tili nawo mumpingo koma amachitanso zoipa. Si bwino kuchezanso ndi anthu amene amati ndi Akhristu koma amachita machimo akuluakulu ndipo salapa. (Aroma 16:17, 18) Vuto locheza ndi anthu osamvera malamulo a Mulungu ndi lakuti nafenso timayamba khalidwe lawo loipa n’cholinga choti tikakhala nawo tisamanyozeke. Mwachitsanzo, kuzolowerana ndi anthu achiwerewere kungachititse kuti nafenso tiyambe kuchita chiwerewere. Zimenezi zachitikirapo Akhristu ena ndipo anachotsedwa mumpingo chifukwa sanalape. (1 Akor. 5:11-13) Ngati Mkhristu wachita tchimo lalikulu koma osalapa amafanana ndi anthu amene Petulo anawatchula pa 2 Petulo 2:20-22. w15 8/15 4:4-6

Lolemba, May 22

Mupitiriza kukhala mabwenzi anga mukamachita zimene ndikukulamulani.​—Yoh. 15:14.

Yesu sankaona kuti munthu aliyense angathe kukhala mnzake wapamtima. Anasankha anthu amene ankatumikira Yehova ndi mtima wonse kuti akhale anzake. Kodi inunso mumasankha anthu amene amatumikira Yehova mokhulupirika kuti akhale anzanu apamtima? N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi n’kofunika? Chikondi cha abale ndi alongo chimatithandiza kuti tifike pokhala Akhristu olimba. Tiyerekeze kuti ndinu wachinyamata ndipo mukuganizira zimene mungachite pa moyo wanu. Kucheza ndi anthu amene akhala akutumikira Yehova mokhulupirika ndiponso mogwirizana ndi mpingo kungakuthandizeni kwambiri. Anthu oterewa ayenera kuti akumanapo ndi mavuto pa moyo wawo komanso potumikira Mulungu. Choncho akhoza kukuthandizani kusankha bwino zimene mungachite pa moyo wanu. Kucheza nawo kungakuthandizeni kuti muzisankha zinthu mwanzeru komanso kuti mukule mpaka kufika pokhala Akhristu olimba.​—Aheb. 5:14. w15 9/15 1:14, 15

Lachiwiri, May 23

Khalani olimba m’chikhulupiriro ndipo mulimbane naye [Mdyerekezi].​—1 Pet. 5:9.

Zimene Yesu ankalankhula ndiponso kuchita zinkalimbitsa chikhulupiriro cha ophunzira ake. (Maliko 11:20-24) Nafenso tizilimbitsa chikhulupiriro cha anthu ena chifukwa tikamatero timalimbitsanso chikhulupiriro chathu. (Miy. 11:25) Tikamaphunzitsa anthu tiziwauza umboni wakuti kuli Mulungu ndiponso kuti amatikonda. Tiziwathandiza kudziwa kuti Baibulo ndi Mawu ake. Tizithandizanso abale ndi alongo athu kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Mwachitsanzo, ngati taona kuti ena akudandaula za abale amene akutsogolera mumpingo, si bwino kufulumira kuwapewa. Koma tiziyesetsa kuwathandiza n’kulimbitsa chikhulupiriro chawo. (Yuda 22, 23) Kapena ngati muli kusukulu ndipo anthu akukambirana nkhani yosemphana ndi zimene mumakhulupirira, muzifotokoza molimba mtima zimene Baibulo limanena. Izi zikhoza kuthandiza anzanuwo kuchita chidwi ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Yehova amatithandizanso kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. (1 Pet. 5:10) Choncho tikamachita khama kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu tidzadalitsidwa kwambiri. w15 9/15 3:20, 21

Lachitatu, May 24

Zakumwamba zikulengeza ulemerero wa Mulungu. Ndipo m’mlengalenga mukufotokoza ntchito ya manja ake.​—Sal. 19:1.

Masiku ano, timadziwa zinthu zambiri zimene Yehova analenga komanso zimene akuchita pokwaniritsa cholinga chake. Anthu m’dzikoli amalimbikitsa maphunziro apamwamba. Koma pali umboni wosonyeza kuti nthawi zambiri maphunzirowo amachititsa anthu kusiya kukonda Mulungu ndiponso kumukhulupirira. N’zoona kuti Yehova amafuna kuti tidziwe zinthu koma amatiuzanso kuti tipeze nzeru ndi luso lomvetsa zinthu. Iye amafuna kuti tizigwiritsa ntchito zimene watiphunzitsa m’njira yoti zitithandize komanso zithandize anthu ena. (Miy. 4:5-7) Cholinga cha Mulungu n’chakuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Tikamachita khama kwambiri pouza anthu za Ufumu wa Mulungu komanso zolinga zake, timasonyeza kuti timakonda Yehova.​—Sal. 66:16, 17. w15 9/15 5:10, 11

Lachinayi, May 25

Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.​—Aroma 15:4.

Eliya anachita zinthu zosonyeza kuti ankadalira kwambiri Yehova. Mwachitsanzo, anauza Mfumu Ahabu kuti Yehova achititsa kuti kukhale chilala ndipo ananena molimba mtima kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, . . . sikugwa mame kapena mvula zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditalamula.” (1 Maf. 17:1) Eliya ankakhulupirira kuti Yehova aonetsetsa kuti iye ndi anthu ena ali ndi zofunika pa moyo wawo pa nthawi yachilalayo. (1 Maf. 17:4, 5, 13, 14) Pa nthawi ina, anakhulupiriranso kuti Yehova aukitsa mwana amene anamwalira. (1 Maf. 17:21) Anasonyezanso chikhulupiriro chifukwa sanakayikire kuti Yehova atumiza moto wopserezera nsembe yake imene anapereka paphiri la Karimeli. (1 Maf. 18:24, 37) Nthawi itafika kuti Yehova athetse chilalacho, Eliya anauza Ahabu kuti: “Pitani mukadye ndi kumwa, chifukwa kukumveka mkokomo wa chimvula.” (1 Maf. 18:41) Iye ananena mawuwa ngakhale kuti kunalibe chizindikiro chilichonse choti kugwa mvula. Nkhani ngati zimenezi zingatilimbikitse kudzifufuza kuti tione ngati chikhulupiriro chathu ndi cholimba. w15 10/15 2:4, 5

Lachisanu, May 26

Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama.​—1 Tim. 4:15.

Mulungu anatilenga m’njira yoti tizitha kulankhula. (Sal. 139:14; Chiv. 4:11) Ubongo wathu umachita zinthu zodabwitsa kwambiri. Anthufe timasiyananso ndi nyama chifukwa tinalengedwa “m’chifaniziro cha Mulungu” ndipo anatipatsa ufulu wosankha zochita. Choncho tingasankhe kugwiritsa ntchito mphatso ya kulankhula potamanda Yehova. (Gen. 1:27) Baibulo ndi mphatso inanso imene Yehova wapereka kwa anthu amene amafuna kumutamanda. Panopa, Baibulo lathunthu kapena mbali yake likupezeka m’zilankhulo zoposa 2,800. Munthu akamaphunzira Mawu a Mulungu amayamba kuganiza mofanana ndi mmene Yehova amaganizira. (Sal. 40:5; 92:5; 139:17) Munthu wotere amasinkhasinkha ‘nzeru zothandiza kuti adzapulumuke.’ (2 Tim. 3:14-17) Baibulo limanena kuti kusinkhasinkha kumatanthauza kuganizira kwambiri zinthu zinazake, zabwino kapena zoipa. (Sal. 77:12; Miy. 24:1, 2) Koma zinthu zabwino kwambiri zimene tingaziganizire ndi zokhudza Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu.​—Yoh. 17:3. w15 10/15 4:2-4

Loweruka, May 27

Ngati munthu sadziwa kuyang’anira banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalire bwanji?​—1 Tim. 3:5.

Zimene Yesu ankachita komanso kulankhula, zinkathandiza ophunzira ake kudziwa kuti ayenera kutumikira ena modzichepetsa. (Luka 22:27) Iye anaphunzitsa atumwi ake kuti ayenera kudzipereka potumikira Yehova komanso Akhristu anzawo. Nanunso mukhoza kuphunzitsa ana anu ngati mumachita zinthu modzipereka ndiponso modzichepetsa. Mlongo wina dzina lake Debbie ali ndi ana awiri ndipo ananena kuti: “Ana athu ali aang’ono, mwamuna wanga ankatanganidwa ndi kuthandiza anthu a mumpingo chifukwa choti ndi mkulu. Koma sindinkadandaula chifukwa ankayesetsanso kupeza nthawi yocheza ndiponso kusamalira banja lathu.” Mwamuna wa mlongoyu dzina lake Pranas, ananenanso kuti: “Ana athu ankafunitsitsa kuchita utumiki wosiyanasiyana pamisonkhano komanso kugwira nawo ntchito zosiyanasiyana m’gulu la Yehova. Zimenezi zinawathandiza kuti azisangalala ndiponso kudziwana ndi abale ndi alongo ambiri.” Panopa banja lonseli likuchita utumiki wa nthawi zonse. Makolo akamachita zinthu modzipereka ndiponso modzichepetsa, nthawi zambiri ana awo amachitanso zomwezo. w15 11/15 1:9

Lamlungu, May 28

Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga.​—Aroma 1:20.

Yehova wakhala akusonyeza chikondi chake m’njira zambiri. Mwachitsanzo, taganizirani za chilengedwe chokongolachi. Pali milalang’amba mabiliyoni ambiri ndipo uliwonse uli ndi mapulaneti komanso nyenyezi zambirimbiri. Imodzi mwa nyenyezi zimene zili mumlalang’amba wathu ndi dzuwa ndipo limathandiza kuti padzikoli pakhale zamoyo. Yehova ndi amene analenga zinthu zonsezi ndipo zimasonyeza kuti iye ndi wamphamvu, wanzeru komanso wachikondi. Yehova analenga dzikoli m’njira yoti pakhale zamoyo. Chilichonse padzikoli Mulungu anachipanga n’cholinga choti chizithandiza anthu ndiponso zinyama. Anakonzanso munda wokongola kuti anthu azikhalamo. Anthu amene anawalenga anali angwiro ndipo sakanafa. (Chiv. 4:11) Yehova ‘amaperekanso chakudya kwa zamoyo zonse ndipo kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.’​—Sal. 136:25. w15 11/15 3:7, 8

Lolemba, May 29

Ine ndili pamodzi ndi inu.​—Mat. 28:20.

M’zaka zapitazi, Mfumu yathu Yesu watipatsa zida zosiyanasiyana zoti tizigwiritsa ntchito. Zida zina tinazigwiritsa ntchito kwa zaka zochepa zokha pomwe zina zikutithandizabe mpaka pano. Komabe zida zonsezi zatithandiza kuti tizilalikira mwaluso komanso kuti anthu amve uthenga wathu mosavuta. Kuyambira mu 1933, abale ndi alongo ankagwiritsa ntchito timakadi tolalikirira. Timakaditi tinkakhala ndi uthenga wachidule wa m’Baibulo ndipo tinkathandiza abale ndi alongo m’njira zosiyanasiyana. Akhristu ena ankafunitsitsa kulalikira koma anali amanyazi ndipo ankadzikayikira. Koma ena anali olimba mtima moti akakumana ndi munthu, ankamuuza zonse zimene ankadziwa ndipo nthawi zina sankalankhula mwaulemu. Koma timakadi timeneti tinkathandiza kwambiri abale ndi alongo onsewa chifukwa tinkafotokoza uthenga wa m’Baibulo mwachidule ndiponso momveka bwino. w15 11/15 5:3-6

Lachiwiri, May 30

Onse . . . atamande dzina la Yehova.​—Sal. 148:13.

Malemba ambiri amasonyeza kuti dzina la Mulungu ndi lofunika kwambiri ndipo liyenera kulemekezedwa. (Eks. 3:15; Sal. 83:18; Yes. 42:8; 43:10; Yoh. 17:6, 26; Mac. 15:14) Yehova anachititsa kuti anthu amene anawagwiritsa ntchito polemba Baibulo alembe dzina lake kambirimbiri. (Ezek. 38:23) Choncho anthu akachotsa dzinali m’Baibulo, amasonyeza kuti salemekeza Yehova. Masiku ano pali umboni wosonyeza kuti dzina la Mulungu liyenera kupezeka m’Baibulo. Mu Baibulo la Dziko Latsopano lomwe linatuluka mu 1984, dzina la Mulungu linkapezekamo ka 7,210. Koma mu Baibulo lachingelezi lokonzedwanso lomwe linatuluka mu 2013, anawonjezera dzinali m’mavesi enanso 6, choncho limapezekamo ka 7,216. Mavesi ake ndi 1 Samueli 2:25; 6:3; 10:26; 23:14, 16 ndiponso Oweruza 19:18. Anawonjezera dzina la Mulungu pa Oweruza 19:18 chifukwa cha zimene akatswiri anapeza atafufuza m’zolemba zina zakale za Baibulo. Pamavesi enawo, anawonjezera dzinali chifukwa cha zimene anapeza m’mipukutu ya ku Nyanja Yakufa. w15 12/15 2:5, 6

Lachitatu, May 31

Mupitirize kukonda abale.​—Aheb. 13:1.

Tiyenera kuyamba panopa kukondana ndi abale athu. Zimenezi zidzatithandiza tikadzakumana ndi mayesero aakulu m’tsogolo. Ngakhale panopa abale athu ambiri amakumana ndi mavuto monga zivomezi, kusefukira kwa madzi ndiponso mphepo zamkuntho. Palinso ena amene akuvutika chifukwa chotsutsidwa komanso kuzunzidwa. (Mat. 24:6-9) Kuwonjezera pamenepo, timakumananso ndi mavuto azachuma chifukwa anthu ambiri m’dzikoli amachita zachinyengo. (Chiv. 6:5, 6) Akhristu anzathu akakumana ndi mavuto ngati amenewa, tiziona kuti ndi nthawi yosonyeza kuti timawakonda. Tiyenera kupitiriza kukonda abale athu ngakhale kuti masiku ano anthu ambiri alibe chikondi chenicheni.​—Mat. 24:12. w16.01 1:8, 9

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena