Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es17 tsamba 57-67
  • June

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • June
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
  • Timitu
  • Lachinayi, June 1
  • Lachisanu, June 2
  • Loweruka, June 3
  • Lamlungu, June 4
  • Lolemba, June 5
  • Lachiwiri, June 6
  • Lachitatu, June 7
  • Lachinayi, June 8
  • Lachisanu, June 9
  • Loweruka, June 10
  • Lamlungu, June 11
  • Lolemba, June 12
  • Lachiwiri, June 13
  • Lachitatu, June 14
  • Lachinayi, June 15
  • Lachisanu, June 16
  • Loweruka, June 17
  • Lamlungu, June 18
  • Lolemba, June 19
  • Lachiwiri, June 20
  • Lachitatu, June 21
  • Lachinayi, June 22
  • Lachisanu, June 23
  • Loweruka, June 24
  • Lamlungu, June 25
  • Lolemba, June 26
  • Lachiwiri, June 27
  • Lachitatu, June 28
  • Lachinayi, June 29
  • Lachisanu, June 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
es17 tsamba 57-67

June

Lachinayi, June 1

Lilime lofatsa likhoza kuthyola fupa.​—Miy. 25:15.

Ngakhale munthu wina atatilankhula zokhumudwitsa, ndi bwino kumuyankha mwaulemu. (Miy. 15:1) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina amene anali ndi mwana wachinyamata yemwe ankaoneka kuti akutumikira Yehova koma kumbali ankachita zinthu zoipa. Ndiyeno mlongo wina amene ankamvera chisoni mayi wa mnyamatayo anamuuza kuti: “Pepani kwambiri kuti mwalephera kuphunzitsa bwino mwana wanu.” Mayiyu ataganizira, anayankha kuti: “N’zoona kuti panopa zinthu sizikuyendadi bwino, koma ndikuyesetsabe kumuthandiza. Zonse zidzaoneka Aramagedo ikadzadutsa.” Mayiyu anayankhadi mwaulemu ndipo izi zinathandiza kuti alongowa apitirize kugwirizana. Komanso mwanayo anamva zimene mayi ake anayankha ndipo zinamulimbikitsa. Anazindikira kuti mayi ake sankamuona kuti ndi wokanika. Zimenezi zinamulimbikitsa kuti asiye kucheza ndi anthu oipa. Patapita nthawi, anabatizidwa ndipo kenako anayamba kutumikira pa Beteli. Kaya tikulankhula ndi abale a mu mpingo, achibale kapena anthu amene sitikuwadziwa, mawu athu azikhala ‘achisomo, okoma ngati tawathira mchere.’​—Akol. 4:6. w15 12/15 3:15, 17

Lachisanu, June 2

Malawi amoto ooneka ngati malilime . . . anakhala pa aliyense wa iwo limodzilimodzi.​—Mac. 2:3.

Ophunzira a Yesu amene analipo pamene zimenezi zinkachitika, sakanaiwala zimene zinachitikazo. Paja aliyense anali ndi mzimu woyera wooneka ngati lawi lamoto pamutu pake. Yehova anawathandizanso kuti athe kulankhula zilankhulo zina. Choncho iwo sanakayikire ngakhale pang’ono zoti adzozedwa ndi mzimu woyera. (Mac. 2:6-12) Koma kodi anthu onse amadzozedwa mofanana ndi mmene ophunzira 120 aja anadzozedwera? Ayi. Anthu ena amene anadzozedwa pa tsikulo, anadzozedwa pamene ankabatizidwa ndipo sanalandire mzimu woyera wooneka ngati malawi amoto. (Mac. 2:38) Asamariya anadzozedwa patapita nthawi kuchokera pamene anabatizidwa. (Mac. 8:14-17) Pomwe pa zifukwa zina, Koneliyo ndi anthu a m’banja lake anadzozedwa asanabatizidwe n’komwe.​—Mac. 10:44-48. w16.01 3:3, 5

Loweruka, June 3

Muzisunga umodzi wathu pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa.​—Aef. 4:3.

Akhristu odzozedwa saganiza kuti mzimu woyera umawathandiza kwambiri kuposa a nkhosa zina. Sanenanso kuti amadziwa zinthu zina zapadera kapena ndi abwino kuposa ena. Iwo salimbikitsanso anthu ena kuti ayambe kudya zizindikiro chifukwa amadziwa kuti Yehova ndi amene amasankha odzozedwa. Akhristu odzozedwa safuna kuti anthu aziwapatsa ulemu wapadera. (Aef. 1:18, 19; Afil. 2:2, 3) Mzimu wa Mulungu umawathandiza kudziwa kuti adzozedwa, koma sudziwitsa anthu onse za zimenezi. Choncho sadabwa ngati anthu ena zikuwavuta kukhulupirira kuti iwowo adzozedwa. Amadziwanso kuti Baibulo limalangiza Akhristu kuti asamangokhulupirira aliyense amene amati wapatsidwa udindo wapadera ndi Mulungu.​—Chiv. 2:2. w16.01 4:6, 7

Lamlungu, June 4

Madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri.​—Aroma 11:33.

Kangapo konse, Yehova anateteza Abulahamu ndi Sara mozizwitsa. (Gen. 12:10-20; 20:2-7, 10-12, 17, 18) Zimenezi zinalimbitsa kwambiri chikhulupiriro cha Abulahamu. Zimene tingaphunzire zokhudza Mulungu komanso zomwe tingakumane nazo pa moyo, zingatithandize kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Abulahamu ankangodziwa zinthu zochepa chabe zimene zili m’Baibulo, koma ifeyo tili ndi Baibulo lonse. (Dan. 12:4) M’Mawu a Mulungu muli zinthu zambiri zimene zingatithandize kuti timudziwe bwino Mulungu n’kuyamba kumulemekeza komanso kumukonda kwambiri. (Gen. 14:22) Zikatere timayamba kumumvera ndipo kenako timaona kuti zinthu zikutiyendera bwino. Timaonanso kuti amatidalitsa, kutipatsa mphamvu ndiponso malangizo ake amatiteteza. Timazindikira kuti tikamamutumikira ndi mtima wonse timakhala osangalala komanso ndi mtendere wamumtima. (Sal. 34:8; Miy. 10:22) Tikamaphunzirabe za Mulungu komanso kuona zimene akutichitira pa moyo wathu, timayamba kumukhulupirira kwambiri ndipo ubwenzi wathu ndi iye umalimba. w16.02 1:7, 8

Lolemba, June 5

Iye wathandiza mtumiki wake Isiraeli . . . , monga momwe anauzira makolo athu akale.​—Luka 1:54, 55.

Zimene Mariya analankhula palembali zimasonyeza kuti ankadziwa bwino Mawu a Mulungu. Zambiri zimene ananena zikufanana ndi zimene Hana, yemwe anali mayi ake a Samueli, ananena m’pemphero. (1 Sam. 2:1-10) Zikuoneka kuti m’mavesi amenewa, Mariya anatchula mawu a m’malemba pafupifupi 20. Izi zikusonyeza kuti Mariya ankakonda kwambiri kulankhula mfundo zimene anaphunzira kwa Mulungu ndipo anali naye pa ubwenzi wolimba. Nthawi zina nafenso Yehova angatipatse ntchito yooneka ngati yovuta. Zikatere tizitsatira chitsanzo cha Mariya. Tiyenera kulandira ntchitoyo modzichepetsa n’kukhulupirira kuti Yehova atithandiza kuti tiigwire bwino. Tingatsanzirenso Mariya tikamamvetsera zimene ena akunena zokhudza Yehova, tikamaganizira kwambiri zimene tamvazo ndiponso tikamauza ena mfundo za m’Baibulo zomwe taphunzira.​—Sal. 77:11, 12; Luka 8:18; Aroma 10:15. w16.02 2:17, 18

Lachiwiri, June 6

Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo?​—Luka 14:28.

Chaka chilichonse achinyamata ambiri amabatizidwa padziko lonse. (Mlal. 12:1) Komabe akulu ndiponso makolo achikhristu ayenera kuonetsetsa kuti achinyamatawa amasankha kubatizidwa chifukwa choti adziperekadi kwa Mulungu ndipo akudziwa zimene akuchita. Munthu akadzipereka kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa, amadalitsidwa kwambiri ndi Yehova koma amatsutsidwa ndi Satana. (Miy. 10:22; 1 Pet. 5:8) Choncho makolo ayenera kuphunzitsa ana awo kuti azidziwa bwino udindo umene Mkhristu amakhala nawo. Nawonso akulu ayenera kuthandiza achinyamata amene makolo awo si Mboni kuti adziwe udindowu n’cholinga choti akonzekere bwino. (Luka 14:27-30) Munthu amene akufuna kumanga nyumba, amafunika kukonzekera kuti adzaimalize bwino. N’chimodzimodzinso ndi kutumikira Yehova. Tiyenera kukonzekera bwino kuti tithe kumutumikira “mpaka pa mapeto.”​—Mat. 24:13. w16.03 1:1, 2

Lachitatu, June 7

Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.​—Mac. 10:34, 35.

Chilamulo chinaperekedwa kwa mtundu wa Aisiraeli wokha. Koma Isiraeli wauzimu anachokera m’mitundu komanso zikhalidwe zosiyanasiyana. Chilamulo cha Mose chinalembedwa pamiyala ndipo chinatsogolera Aisiraeli m’Dziko Lolonjezedwa. Koma Isiraeli wauzimu anapatsidwa “chilamulo cha Khristu” chomwe mfundo zake zinalembedwa m’mitima. (Agal. 6:2) Malangizo amene Mulungu anapatsa Akhristu kudzera mwa Mwana wake, anawathandiza kwambiri. Yesu asananene za pangano latsopano, anapereka malamulo awiri. Lamulo loyamba linali lokhudza ntchito yolalikira. Lachiwiri linali loti otsatira ake ayenera kumakondana. Malamulowa anali opita kwa Akhristu onse. Choncho akugwiranso ntchito kwa ifeyo, kaya tikuyembekezera kudzapita kumwamba kapena kudzakhala padzikoli. w16.03 4:10, 11

Lachinayi, June 8

Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.​—Aroma 12:10.

M’bale amene ndi mkulu ayenera kupeza mpata wocheza ndi m’bale amene akufuna kumuthandiza n’cholinga choti amasuke. Zimene mkuluyu angachite zingakhale zosiyana malinga ndi kumene akukhala komanso chikhalidwe chawo. Koma kaya zili bwanji kwanuko, mkulu amene amatanganidwa ayenera kupeza nthawi yocheza ndi anthu amene akufuna kuwaphunzitsa. Akatero zimakhala ngati akuwauza kuti: “Ndimaona kuti ndiwe munthu wofunika kwambiri.” Zimenezi zingathandize kwambiri anthu amene mukuwaphunzitsawo ndipo sadzaiwala. Mphunzitsi wabwino amakonda kuphunzitsa komanso amakonda anthu amene akuwaphunzitsawo. (Yerekezerani ndi Yohane 5:20.) Ophunzira amadziwa ngati mphunzitsi wawo amawakonda kapena ayi ndipo ngati aona kuti amawakonda amaphunzira mosavuta. Choncho ngati ndinu mkulu, chonde yesetsani kupeza mpata wocheza ndi anthu kuti muwaphunzitse bwino.​—Miy. 17:17; Yoh. 15:15. w15 4/15 1:19, 20

Lachisanu, June 9

Yehova anaichititsa khate mfumuyo moti inakhalabe yakhate mpaka tsiku limene inamwalira.​—2 Maf. 15:5.

Kodi mukanamva bwanji zikanakhala kuti m’Baibulo mulibe mfundo zina zotithandiza kumvetsa nkhani ya Mfumu Azariya, yemwe ankatchedwanso kuti Mfumu Uziya? (2 Maf. 15:7, 32; 2 Mbiri 26:3-5, 16-21) Kodi mukanayamba kukayikira zoti Mulungu amachita zinthu mwachilungamo? Kapena mukanayamba kuda nkhawa n’kumaona kuti Yehova ndi wopanda chilungamo komanso ngatidi ali woyenera kutiuza zomwe zili zabwino kapena zoipa? (Deut. 32:4) Kudziwa bwino Yehova kungatithandize kumukhulupirira kwambiri moti sitingade nkhawa ngati sanatiuze zifukwa zimene amachitira zinthu zina. Koma kuti munthu afike pomukhulupirira chonchi ayenera kuchita khama kwambiri pophunzira Mawu a Mulungu ndiponso kuwaganizira mozama. (Sal. 77:12, 13) Zikatero, ubwenzi wa munthuyo ndi Yehova umalimba kwambiri. w15 4/15 3:8, 10

Loweruka, June 10

Tamandani Yehova, inu angelo ake amphamvu, ochita zimene wanena, mwa kumvera malamulo ake.​—Sal. 103:20.

Baibulo limanena kuti angelo ndi “amphamvu.” Iwo ali ndi mphamvu komanso nzeru kuposa anthufe. Angelo okhulupirika amagwiritsa ntchito bwino mphamvu zawo. Mwachitsanzo, mngelo mmodzi yekha anawononga asilikali 185,000 a Asuri. N’zosatheka kuti munthu mmodzi achite zimenezi ndipo ngakhale litakhala gulu la asilikali likhoza kuvutika kupha asilikali onsewo. (2 Maf. 19:35) Pa nthawi ina, mngelo wina anamasula atumwi a Yesu m’ndende m’njira yodabwitsa. Mngeloyo anatsegula zitseko, kutulutsa atumwi kenako n’kutsekanso. Anachita zonsezi asilikali ali pomwepo. (Mac. 5:18-23) Koma Satana amagwiritsa ntchito mphamvu zake kuti achite zinthu zoipa. Iye ndi wamphamvu kwambiri ndipo wapotoza kale anthu ambirimbiri. Paja Baibulo limati iye ndi “wolamulira wa dzikoli.”​—Yoh. 12:31. w15 5/15 1:5, 6

Lamlungu, June 11

Chinyengo champhamvu cha uchimo chisaumitse mtima wa wina wa inu.​—Aheb. 3:13.

Kaya tili pa banja kapena ayi, tiyenera kupeweratu khalidwe lachiwerewere. N’zoona kuti kuchita zimenezi si kophweka. Mwina ngati muli pa sukulu, mumamva anzanu akunyadira zoti agonana ndi winawake kapena amatumizirana mauthenga a zachiwerewere. Mwina ena amatumizirananso zithunzi zolaula. Koma Baibulo limati: “Amene amachita dama amachimwira thupi lake.” (1 Akor. 6:18) Panopa pali anthu ambiri amene akudwala kapena amene amwalira chifukwa cha matenda opatsirana pogonana. Achinyamata ambiri amene amayamba kugonana amanena kuti amanong’oneza bondo. Mafilimu amasonyeza kuti chiwerewere n’chosangalatsa. Koma zoona zake n’zakuti pamakhala mavuto ambiri munthu akaphwanya malamulo a Mulungu pa nkhani imeneyi. Anthu amene amakhulupirira za m’mafilimuzi amapusitsidwa ndi “chinyengo champhamvu cha uchimo.” w15 5/15 2:14

Lolemba, June 12

Wam’mwambamwamba . . . ndi wachifundo kwa osayamika ndi kwa oipa.​—Luka 6:35.

Yesu ankatsanzira chifundo cha Yehova. Iye ankachita zimenezi chifukwa ankakomera anthu mtima ndipo ankaganizira mmene mawu ndi zochita zake zingawakhudzire. Mwachitsanzo, mayi wina yemwe ankadziwika kuti ndi wochimwa anabwera kwa Yesu n’kuyamba kulira ndipo misozi yake inanyowetsa mapazi a Yesu. Yesu anazindikira kuti mayiyo walapa ndipo zingamupweteke kwambiri ngati atamuthamangitsa. Choncho iye anayamikira mayiyo n’kumukhululukira. Mfarisi wina atasonyeza kuti sakugwirizana ndi zimenezi, Yesu anamuthandizanso mokoma mtima. (Luka 7:36-48) Kodi ifeyo tingatsanzire bwanji chifundo cha Yehova? Mtumwi Paulo anati: “Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu, koma ayenera kukhala wodekha [kapena kuti wosamala polankhula] kwa onse.” (2 Tim. 2:24) Munthu wodekha amasamala polankhula ndi anthu n’cholinga choti mawu ake asawapweteke. Tiyenera kuganizira mmene mnzathuyo akumvera mumtima mwake. Kenako tiyenera kuganizira mmene mawu athu angamukhudzire. Tikatero tidzatsanzira Yehova n’kumuyankha mnzathuyo mokoma mtima.​—Miy. 15:28. w15 5/15 4:8, 9

Lachiwiri, June 13

Usalephere kuchitira zabwino anthu amene akufunikira zabwinozo, pamene dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.​—Miy. 3:27.

Tingathandize abale athu pamene ali pa mavuto powapatsa zinthu zofunika kapena kuwalimbikitsa. (Miy. 17:17) Mwachitsanzo, tingawathandize ngati pachitika ngozi. Mlongo wina wamasiye, nyumba yake inawonongeka kwambiri ndi mphepo yamkuntho ndipo atathandizidwa anati: “Ndimathokoza kwambiri kuti ndili m’gulu la Yehova chifukwa abale ndi alongo andithandiza kupeza zinthu zofunika komanso kundilimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo.” Mlongo winanso wosakwatiwa anadandaula kwambiri nyumba yake itawonongeka ndi mvula yamkuntho. Iye atathandizidwa anati: “Ndikusowa chonena . . . Ndikungothokoza Yehova.” Timasangalala kuti tili m’gulu la abale amene amakondanadi ndi kuthandizana. Koma timasangalala kwambiri chifukwa Yehova ndi Yesu amatikonda ndi kutisamalira. w15 6/15 1:17

Lachitatu, June 14

[Uziona] akazi achikulire ngati amayi ako. Akazi achitsikana . . . ngati alongo ako, ndipo pochita zimenezi usakhale ndi maganizo alionse oipa.​—1 Tim. 5:2.

Baibulo limatithandiza kupewa kukhala ndi maganizo oipa ngati tili ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi mnzathu. Limasonyeza kuti si bwino kukopana. Ena amaganiza kuti palibe vuto ngati ayamba kukopana ndi maso kapena m’njira zina. Amaona kuti bola ngati sakukhudzana. Koma zoona zake n’zakuti khalidwe limeneli ndi loipa basi. Limachititsa kuti anthu aziganiza zoipa mwinanso n’kufika pochita chiwerewere. Ena zawavutapo m’mbuyomu chifukwa cha khalidweli ndipo zikhoza kukuchitikiraninso inuyo. Yosefe anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iye anakana pamene ankanyengereredwa ndi mkazi wa Potifara. Koma mkaziyo sanasiyire pomwepo. Tsiku lililonse ankamuuza kuti agone naye. (Gen. 39:7, 8, 10) Iye sanafune m’pang’ono pomwe kuti ayambe zinthu zimene zingamuchititse kuganizira zoipa mumtima mwake. w15 6/15 3:10, 11

Lachinayi, June 15

Mutikhululukire zolakwa zathu monga mmene ifenso takhululukira amene atilakwira.​—Mat. 6:12.

Yehova amafuna kuti tiziganizira anzathu ndipo tiziwathandiza kuti akhale naye pa ubwenzi wolimba. Tiyenera kuganiziranso ngakhale anthu amene atilakwira. Nthawi zambiri zinthu zimene anthu ena amatilakwira zimakhala zazing’ono ndipo tikawakhululukira timasonyeza kuti timawakonda. Timasonyezanso kuti timayamikira Yehova chifukwa chotikhululukira. (Akol. 3:13) Koma anthu ochimwafe nthawi zina timasungira ena zifukwa. (Lev. 19:18) Tikauza anthu ena zimene wina watilakwira, tingachititse kuti anthuwo azitiikira kumbuyo. Ndiyeno izi zingasokoneze mgwirizano mumpingo. Tikalola zimenezi kuchitika timasonyezanso kuti sitiyamikira kwenikweni chifundo cha Mulungu ndiponso dipo. Mulungu sangatikhululukire ngati ifeyo sitikhululukira anzathu. (Mat. 18:35) Yesu anafotokoza zimenezi pambuyo ponena pemphero lachitsanzo. (Mat. 6:14, 15) Komanso kuti Mulungu azitikhululukira tiyenera kuyesetsa kuti tisamachite machimo aakulu.​—1 Yoh. 3:4, 6. w15 6/15 5:9-11

Lachisanu, June 16

Mfumu imasangalala ndi wantchito wochita zinthu mozindikira.​—Miy. 14:35.

Yehova watilemekeza kwambiri potipatsa mwayi wokongoletsa nawo paradaiso wauzimu. Timachita zimenezi polalikira mwakhama ndiponso kuphunzitsa anthu. Tikaphunzitsa munthu mpaka kufika poti wadzipereka kwa Mulungu, timakhala kuti takulitsa paradaisoyu. (Yes. 26:15; 54:2) Timakongoletsanso paradaisoyo poyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino. Izi zimathandiza kuti anthu ena aziona kuti gulu la Yehova ndi lokongola. Nthawi zambiri anthu amayamba kukonda Yehova ndi Yesu chifukwa choona makhalidwe athu abwino ndiponso mtendere wathu osati chifukwa cha zimene timawaphunzitsa m’Baibulo. Yehova ndi Yesu ayenera kuti amasangalala kwambiri kuona mmene paradaiso wauzimu wakongolera masiku ano. Komatu zinthu zimene zikutisangalatsa masiku anozi n’zochepa tikaziyerekezera ndi zimene zidzachitike tikamadzasintha dzikoli kukhala paradaiso weniweni. w15 7/15 1:18-20

Loweruka, June 17

Mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.​—Gen. 3:5.

Munthu aliyense ayenera kusankha pakati pa ulamuliro wa Yehova ndi wa Satana. Kodi mumasonyeza kuti mwasankha ulamuliro wa Yehova pomumvera m’malo mochita zimene mukufuna? Kodi mumakhulupiriradi kuti Ufumu wake wokha ndi umene ungathetse mavuto a anthu? Kapena kodi mumaona kuti anthu akhoza kudzilamulira okha bwinobwino? Mayankho anu pa mafunsowa angakuthandizeni kudziwa zimene mungachite anthu akakufunsani maganizo pa nkhani za m’dzikoli. Anthu andale kapena amabungwe akhala akuyesetsa kuthetsa mikangano ya m’dzikoli. N’kutheka kuti iwo akufunitsitsa kuthandiza anthu. Koma Akhristu amadziwa kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene ungathetse mavuto n’kukhazikitsa chilungamo. Ngati Mkhristu aliyense atati alimbikitse anthu kutsatira njira imene akuona kuti ingathetse mavuto, mgwirizano ukhoza kusokonekera mu mpingo. Choncho tiyenera kusiya nkhaniyi m’manja mwa Yehova. w15 7/15 3:7, 8

Lamlungu, June 18

Ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zonse.​—Sal. 77:12.

Zinthu zimene Mulungu analenga zimasonyeza kuti ndi wachikondi. (Aroma 1:20) Iye analenga dziko ndiponso zinthu za padziko n’cholinga choti tizikhalabe ndi moyo bwinobwino. Mwachitsanzo, anatipatsa zinthu zosiyanasiyana zimene tingadye. Anatilenganso m’njira yoti tizimva kukoma kwa chakudyacho. (Mlal. 9:7) Yehova anatilenganso kuti tizigwira ntchito zosiyanasiyana zimene zingatithandize kukhala osangalala. (Mlal. 2:24) Cholinga chake chinali chakuti anthu adzaze dziko lapansi, aliyang’anire komanso ayang’anire zamoyo zonse zapadzikoli. (Gen. 1:26-28) Iye anasonyezanso chikondi kwambiri potilenga m’njira yoti tizitha kumutsanzira.​—Aef. 5:1. w15 8/15 1:4, 5

Lolemba, June 19

Samalani kuti mitima yanu isalemedwe . . . kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa ngati msampha.​—Luka 21:34, 35.

Zinthu zomwe zikuchitika padzikoli zikusonyeza kuti maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa ndipo mapeto afika posachedwapa. Lemba la Chivumbulutso 17:16 limanena kuti “nyanga 10” ndiponso “chilombo” zidzawononga Babulo Wamkulu kapena kuti zipembedzo zonyenga zonse. Koma tisamaganize kuti nthawi yoti zimenezi zichitike ili kutali. Paja Baibulo limanena kuti Mulungu ‘adzaika izi m’mitima yawo.’ Choncho zikhoza kuyambika mofulumira pa nthawi iliyonse. (Chiv. 17:17) Mapeto a dzikoli sali kutali, choncho ndi bwino kukumbukira chenjezo la Yesu limene lili mulemba laleroli. (Chiv. 16:15) Tiyeni tizitumikira Yehova mwakhama kwambiri podziwa kuti ‘amathandiza anthu amene akumuyembekezera.’​—Yes. 64:4. w15 8/15 2:17

Lachiwiri, June 20

Aliyense wochita chifuniro cha Mulungu, ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga ndi mayi anga.​—Maliko 3:35.

N’zoona kuti timafuna kukomera mtima anthu ngakhale amene satsatira malamulo a Mulungu koma tiyenera kupewa kugwirizana nawo kwambiri. Choncho n’kulakwa kuti m’bale kapena mlongo akhale pa chibwenzi ndi munthu amene sanadzipereke kwa Mulungu ndipo satsatira mfundo zake. Kukhala wokhulupirika kwa Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa kusangalatsa anthu amene samumvera. Tiyenera kugwirizana ndi anthu amene amachita zofuna za Mulungu. Kugwirizana ndi anthu oipa kumabweretsa mavuto aakulu. Umboni wake ndi zimene zinachitikira Aisiraeli. (Eks. 23:24, 25; Sal. 106:35-39) Chifukwa choti sanakhulupirike kwa Mulungu, pa nthawi ina Yesu anawauza kuti: “Tsopano tamverani! Mulungu wachoka n’kukusiyirani nyumba yanuyi.” (Mat. 23:38) Yehova anakana Aisiraeli n’kuyamba kudalitsa mpingo wachikhristu.​—Mac. 2:1-4. w15 8/15 4:7, 8

Lachitatu, June 21

Cholinga chokulamulira zimenezi n’chakuti tikhale ndi chikondi chochokera mumtima woyera [ndiponso] m’chikumbumtima chabwino.​—1 Tim. 1:5.

Polenga anthu, Yehova Mulungu anawapatsa ufulu wosankha zochita. Anawapatsanso chikumbumtima pofuna kuwathandiza kuti azisankha zinthu mwanzeru. Pamene tikuti chikumbumtima tikutanthauza mphamvu yachibadwa yotithandiza kuzindikira chabwino ndi choipa. Munthu akamagwiritsa ntchito bwino chikumbumtima chake, amachita zabwino n’kumapewa zoipa. Choncho chikumbumtima ndi umboni wakuti Yehova amatikonda ndiponso amafuna kuti anthu onse azichita zabwino mogwirizana. Munthu aliyense padzikoli ali ndi chikumbumtima. (Aroma 2:14, 15) N’chifukwa chake anthu ena amadana ndi zoipa n’kumachita zabwino ngakhale kuti sadziwa mfundo za m’Baibulo. Chikumbumtima chawo sichiwalola kuchita zinthu zimene n’zoipa kwambiri. Anthufe tikanakhala opanda chikumbumtima, dzikoli likanaipa kwambiri kuposa pamene lafikapa. Choncho timayamikira kwambiri kuti Mulungu anatipatsa chikumbumtima. w15 9/15 2:1, 2

Lachinayi, June 22

Taganizirani za chikondi chachikulu chimene Atate watisonyeza.​—1 Yoh. 3:1.

Mawu a mtumwi Yohane amenewa akutilimbikitsa kuti tiziganizira mmene Yehova amatikondera. Tikamachita zimenezi timayamba kumukonda kwambiri ndiponso kukhala naye pa ubwenzi wolimba. Anthu ena amaona kuti Mulungu sangawakonde. Mwina amaona kuti Mulungu amangopereka malamulo ndi kulanga anthu amene samvera malamulowo. Ena amaphunzitsidwa mabodza osonyeza kuti Mulungu ndi wankhanza ndipo n’zosatheka kumukonda. Pomwe anthu enanso amakhulupirira kuti Mulungu sangasiye kuwakonda ngakhale iwo atachita zinthu zoipa. Pamene munkaphunzira Baibulo munazindikira kuti khalidwe lalikulu la Mulungu ndi chikondi. Munaphunziranso kuti chifukwa cha chikondicho, Yehova anapereka Mwana wake kuti adzatiwombole.​—Yoh. 3:16; 1 Yoh. 4:8. w15 9/15 4:1, 2

Lachisanu, June 23

Chilango . . . chimakhala chowawa.​—Aheb. 12:11.

Apa sikuti mtumwi Paulo ankatanthauza kuti chilango si chabwino chifukwa anapitiriza kuti: “Komabe pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilangocho, chimabala chipatso chamtendere, chomwe ndi chilungamo.” Ngati timakonda Yehova tidzapewa kunyalanyaza malangizo ake kapena kunyansidwa nawo. Anthu ambiri masiku ano ndi odzikonda ndipo safuna kuuzidwa zochita kapena kupatsidwa malangizo. Ngakhale anthu amene amalandira malangizo, amachita zimenezi monyinyirika. Koma Akhristufe timalangizidwa kuti tipewe kutengera “nzeru za nthawi ino.” M’malomwake tiyenera kuzindikira ndiponso kuchita zimene Mulungu amafuna. (Aroma 12:2) Gulu la Yehova limatipatsa malangizo pa nkhani zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, limatipatsa malangizo okhudza zosangalatsa, anthu amene timacheza nawo komanso mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi anthu amene si amuna kapena akazi anzathu. Tikamatsatira malangizowa ndi mtima wonse timasonyeza kuti timakonda Yehova ndiponso timayamikira malangizo ake.​—Yoh. 14:31; Aroma 6:17. w15 9/15 5:13, 15

Loweruka, June 24

Limbitsani chikhulupiriro changa.​—Maliko 9:24.

Chikhulupiriro ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. (Agal. 5:22) Choncho munthu sangayambe kukhala ndi chikhulupiriro payekha. N’chifukwa chake Yesu anatiuza kuti tizipempha Yehova kuti atipatse mzimu wake woyera. Anatitsimikiziranso kuti Yehova “adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Munthu akakhala ndi chikhulupiriro amafunika kuchilimbitsa nthawi zonse. Chikhulupiriro tingachiyerekezere ndi moto. Munthu akayatsa moto amafunika kuusonkhezera kuti usazime. Kupanda kutero umayamba kuzirala mpaka kungotsala phulusa. N’chimodzimodzi ndi chikhulupiriro chathu. Kuphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse kumathandiza kuti chikhulupirirocho chisafooke. Choncho tiyenera kupitiriza kuphunzira Baibulo n’cholinga choti tizilikonda kwambiri komanso tizikonda Mulungu. Tikatero chikhulupiriro chathu chidzalimba kwambiri. w15 10/15 2:6, 7

Lamlungu, June 25

Ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zonse.​—Sal. 77:12.

Asayansi amanena kuti kuwerenga mokweza kumathandiza kuti tizikumbukira bwino zinthu. M’pake kuti Mulungu anauza Yoswa kuti azisinkhasinkha buku la Chilamulo. (Yos. 1:8) Kuwerenga Baibulo mokweza kumathandiza munthu kuchita khama kuti aziganizira zimene akuwerengazo komanso kuzikumbukira. Tikutero chifukwa chakuti ubongo wathu suchedwa kusokonezedwa ndi zinthu zina. Choncho tingachite bwino kuwerenga ndi kuganizira zimene tikuwerengazo pa nthawi imene sitinatope komanso pamalo opanda zinthu zosokoneza. Davide ananena kuti ankakonda kuganizira za Yehova usiku. (Sal. 63:6) Ngakhale kuti Yesu anali wangwiro, iye ankakonda kupita kumalo aphee kuti azikaganizira zinthu zofunika ndiponso kupemphera.​—Luka 6:12. w15 10/15 4:4, 6, 7

Lolemba, June 26

Anali kudziwa zimene zili m’mitima ya anthu.​—Yoh. 2:25.

Anthu ena amene ankamvetsera Yesu ku Galileya, ankaoneka kuti akufuna kukhala ophunzira ake. (Yoh. 6:22-24) Koma popeza Yesu ankadziwa zimene zinali m’mitima ya anthu, anazindikira kuti anthuwa ankangofuna chakudya chimene ankawapatsa osati zimene ankawaphunzitsa. Iye atazindikira zimenezi, anawalangiza moleza mtima n’kuwauza zimene ayenera kuchita. (Yoh. 6:25-27) Ngakhale kuti simungadziwe zimene zili mumtima wa mwana wanu, mukhoza kuzindikira ngati amakondadi kulalikira. Mwachitsanzo, ana ambiri amakonda kusewera ndi anzawo akakhala mu utumiki. Choncho mungadzifunse kuti: ‘Kodi tikakhala mu utumiki, mwana wangayu amakonda kulalikira kapena amangokonda kusewera ndi anzake?’ Mukazindikira kuti mwana wanu amakonda kusewera, muziyesetsa kuchita zinthu zomuthandiza kuti azisangalala ndi ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, mungamuuze zinthu zomwe angachite mu utumiki kuti azimva kuti akulalikira nawo. w15 11/15 1:10, 11

Lachiwiri, June 27

Zakalezo zapita.​—Chiv. 21:4.

Mulungu ndi wachikondi ndipo amafunira zabwino atumiki ake. Paja Baibulo limatiuzanso kuti: “Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” Kunena zoona, anthu amene amadalira Yehova ndiponso kumumvera ali ndi tsogolo labwino kwambiri. Baibulo limanena kuti: “Ona munthu wosalakwa ndipo yang’anitsitsa munthu wolungama, pakuti tsogolo la munthu ameneyu ndi lamtendere. Koma anthu onse ochimwa adzafafanizidwa.” (Sal. 37:37, 38) “Munthu wosalakwa” amene akunenedwa palembali amaphunzira za Yehova ndi Yesu ndipo amachita zimene Yehovayo amafuna. (Yoh. 17:3) Amakhulupiriranso mawu a pa 1 Yohane 2:17 akuti: “Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.” Choncho popeza mapeto ali pafupi kwambiri, tiyenera ‘kuyembekezera Yehova ndiponso kusunga njira zake.’​—Sal. 37:34. w15 11/15 3:11, 12

Lachitatu, June 28

Zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa.​—Mat. 9:37.

Atumiki a Yehova akhala akugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana polalikira uthenga wabwino. Izi zinali zothandiza kwambiri makamaka pa nthawi imene Akhristu anali ochepa. Mwachitsanzo, kale tinkagwiritsa ntchito manyuzipepala polalikira. Mlungu uliwonse M’bale Russell ankalemba nkhani n’kuzitumiza kuti zikasindikizidwe m’manyuzipepala a ku United States, ku Canada komanso ku Europe. Pofika chaka cha 1913, nkhani za M’bale Russell zinkasindikizidwa m’manyuzipepala okwana 2,000 ndipo anthu pafupifupi 15 miliyoni ankaziwerenga. M’bale Russell atamwalira, gulu lathu linayamba kulalikira pogwiritsa ntchito wailesi. Ndipo pa 16 April, 1922, M’bale Joseph F. Rutherford anakamba nkhani yake yoyamba pa wailesi ndipo anthu pafupifupi 50,000 anamvetsera nkhaniyi. Kenako pa 24 February, 1924, tinayamba kugwiritsa ntchito wailesi yathu yotchedwa WBBR. w15 11/15 5:10, 11

Lachinayi, June 29

Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.​—Eks. 3:14.

Yehova amagwiritsa ntchito anthu kapena chilichonse chimene analenga kuti akwaniritse zimene akufuna. Mwachitsanzo, Mulungu anachititsa kuti Nowa akhale mmisiri wokhoma chingalawa komanso kuti Bezaleli akhale katswiri wokonza zinthu. Anachititsanso kuti Gidiyoni akhale msilikali wodziwa nkhondo ndiponso kuti Paulo akhale mmishonale. Choncho dzina la Mulungu ndi lofunika kwambiri kwa anthu a Mulungu. N’chifukwa chake Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano inaonetsetsa kuti dzinali lipezeke m’Baibuloli. Masiku ano omasulira ambiri akuchotsa dzina la Mulungu m’Mabaibulo awo. M’malomwake, amaikamo dzina lakuti “Ambuye” kapena mayina ena amene amatchulira Mulungu kwawoko. Ichi ndi chifukwa chachikulu chimene chinachititsa kuti Bungwe Lolamulira liyesetse kuti anthu ambiri akhale ndi Baibulo limene dzina la Mulungu limapezekamo. (Mal. 3:16) Panopa Baibulo la Dziko Latsopano likupezeka m’zilankhulo zoposa 130. w15 12/15 2:7-9

Lachisanu, June 30

Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: “Ndikudwala.”​—Yes. 33:24.

Baibulo limasonyeza kuti Mulungu angathe kupangitsa kuti munthu adwale kapena kuchira. Mwachitsanzo m’nthawi ya Abulahamu, analanga Farao ndi matenda komanso pa nthawi ina anachititsa kuti Miriamu, mchemwali wake wa Mose, adwale khate. (Gen. 12:17; Num. 12:9, 10; 2 Sam. 24:15) Anachenjezanso Aisiraeli kuti akakhala osakhulupirika, adzawagwetsera “nthenda iliyonse ndi mliri.” (Deut. 28:58-61) Koma pa nthawi zina Yehova ankateteza anthu ake kuti asadwale. (Eks. 23:25; Deut. 7:15) Ankathanso kuwachiritsa. Mwachitsanzo, Yobu atadwala kwambiri mpaka kulakalaka atangofa, Mulungu anamuchiritsa. (Yobu 2:7; 3:11-13; 42:10, 16) Choncho n’zosakayikitsa kuti Mulungu ali ndi mphamvu zoti angachiritse munthu amene akudwala. N’chimodzimodzinso ndi Mwana wake, Yesu. Baibulo limati Yesu ankachiritsa anthu osaona, ofa ziwalo, odwala khate komanso odwala khunyu. (Mat. 4:23, 24; Yoh. 9:1-7) N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti zimene Yesu anachitazi zimasonyeza zimene adzachite padziko lonse m’tsogolo. w15 12/15 4:3, 4

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena