Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es17 tsamba 67-77
  • July

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • July
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
  • Timitu
  • Loweruka, July 1
  • Lamlungu, July 2
  • Lolemba, July 3
  • Lachiwiri, July 4
  • Lachitatu, July 5
  • Lachinayi, July 6
  • Lachisanu, July 7
  • Loweruka, July 8
  • Lamlungu, July 9
  • Lolemba, July 10
  • Lachiwiri, July 11
  • Lachitatu, July 12
  • Lachinayi, July 13
  • Lachisanu, July 14
  • Loweruka, July 15
  • Lamlungu, July 16
  • Lolemba, July 17
  • Lachiwiri, July 18
  • Lachitatu, July 19
  • Lachinayi, July 20
  • Lachisanu, July 21
  • Loweruka, July 22
  • Lamlungu, July 23
  • Lolemba, July 24
  • Lachiwiri, July 25
  • Lachitatu, July 26
  • Lachinayi, July 27
  • Lachisanu, July 28
  • Loweruka, July 29
  • Lamlungu, July 30
  • Lolemba, July 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
es17 tsamba 67-77

July

Loweruka, July 1

Musaiwale kuchereza alendo.​—Aheb. 13:2.

Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “kuchereza alendo,” amatanthauza “kukomera mtima anthu osawadziwa.” Mawu amenewa akutikumbutsa zimene Abulahamu ndi Loti anachita. Pa nthawi ina, analandira bwino anthu amene sankawadziwa. Koma kenako anazindikira kuti anthuwo anali angelo. (Gen. 18:2-5; 19:1-3) Kodi nafenso timasonyeza chikondi poitanira anthu kunyumba kwathu kuti tidzadye nawo kapena kucheza nawo? Tisaganize kuti tiyenera kukonza chakudya chambiri kapena chapamwamba. Komanso sitiyenera kuitana anthu okhawo amene angadzatiitanenso kapena kutichitira zinazake. (Luka 10:42; 14:12-14) Tisaiwale kuti cholinga chathu ndi kulimbikitsana osati kuwasonyeza kuti tili ndi zinthu zambiri. N’kutheka kuti sitikudziwa bwino woyang’anira dera wathu komanso mkazi wake. Ndiye kodi sizingakhale bwino kuwaitanira kunyumba kwathu? (3 Yoh. 5-8) N’zoona kuti tonse timatanganidwa ndiponso timakumana ndi mavuto. Komabe tiyenera kukumbukira kuti “kuchereza alendo” n’kofunika kwambiri. w16.01 1:11, 12

Lamlungu, July 2

Munaikidwa chidindo cha mzimu woyera wolonjezedwawo, umene ndi chikole cha cholowa chathu cham’tsogolo.​—Aef. 1:13, 14.

Yehova amapatsa odzozedwa mzimu woyera ngati chizindikiro kapena chidindo chowatsimikizira kuti asankhidwa kudzapita kumwamba ndipo zimakhala ngati alandira chikole. (2 Akor. 1:21, 22; 5:5) N’zoona kuti munthuyo amadziwa kuti wasankhidwa kuti adzapita kumwamba. Koma adzapitadi pokhapokha akakhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Petulo anati: “Pa chifukwa chimenechi abale, chitani chilichonse chotheka kuti mukhalebe okhulupirika, n’cholinga choti mupitirizebe kukhala pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana ndi kuwasankha, pakuti mukapitiriza kuchita zinthu zimenezi simudzalephera ngakhale pang’ono. Ndipo mukatero, adzakutsegulirani khomo kuti mulowe mwaulemerero mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.” (2 Pet. 1:10, 11) Choncho wodzozedwa aliyense ayenera kuyesetsa kukhalabe wokhulupirika chifukwa kupanda kutero, sadzalandira mphoto yake.​—Aheb. 3:1; Chiv. 2:10. w16.01 3:6, 7

Lolemba, July 3

Aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, koma aliyense wodzichepetsa adzakwezedwa.​—Mat. 23:12.

Sitiyenera kupereka ulemu wapadera kwa anthu ena, ngakhale kwa abale odzozedwa a Khristu. Baibulo limatiuza kuti tiyenera kutsanzira chikhulupiriro cha anthu amene akutitsogolera, koma silinena kuti tiyenera kulemekeza munthu wina ngati kuti ndi mtsogoleri wathu. (Aheb. 13:7) N’zoona kuti Baibulo limanena kuti anthu ena ayenera kupatsidwa “ulemu waukulu.” Komabe anthuwo ayenera kupatsidwa ulemu osati chifukwa choti ndi odzozedwa koma chifukwa ‘amatsogolera bwino’ komanso “amachita khama kulankhula ndi kuphunzitsa.” (1 Tim. 5:17) Choncho odzozedwa akhoza kuchita manyazi abale ndi alongo akamawalemekeza kwambiri kuposa anthu ena. Komanso odzozedwa akamapatsidwa ulemu wapadera, mwina zingawavute kuti akhalebe odzichepetsa. (Aroma 12:3) Palibe Mkhristu amene angafune kuchita zinthu zimene zingapangitse kuti m’bale wina wa Yesu akhale wosakhulupirika.​—Luka 17:2. w16.01 4:9

Lachiwiri, July 4

Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse.​—Miy. 17:17.

Kukhala ndi mnzanu wapamtima ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri. Komabe ubwenzi suli ngati chinthu chimene ungagule, kuchigwiritsa ntchito kamodzi, kenako n’kuchisiya penapake mpaka kuchita fumbi. M’malomwake ubwenzi uli ngati mbewu imene imafunika kuithirira ndi kuisamalira kuti izikula bwino. Abulahamu ankachita zinthu zomwe zinkathandiza kuti ubwenzi wake ndi Yehova upitirire. Kodi ankachita chiyani? Abulahamu sankaona kuti zinthu zabwino zimene anali atachita kale zinali zokwanira kuti ubwenzi wake ndi Yehova upitirire. Pamene iye ndi banja lake ankapita ku Kanani, ankadalirabe Yehova kuti azimutsogolera ngakhale pa nkhani zing’onozing’ono. Kutatsala chaka chimodzi kuti Isaki abadwe ndipo Abulahamu ali ndi zaka 99, Yehova anamuuza kuti amuna onse a m’banja lake adulidwe. Kodi ananyinyirika n’kuyamba kupeza njira zoti asachite zimene Yehova anamuuzazi? Ayi, koma anakhulupirira Mulungu ndipo anamvera “tsiku lomwelo.”​—Gen. 17:10-14, 23. w16.02 1:9, 10

Lachitatu, July 5

Mnyamata amadziwika ndi ntchito zake, ngati zochita zake zili zoyera ndiponso zowongoka.​—Miy. 20:11.

Achinyamata ena aang’ono amatha kudziwa zoyenera kuchita komanso amamvetsa bwino zimene kudzipereka kwa Mulungu kumatanthauza. Choncho achinyamata oterewa amasonyeza kuti ndi wolimba mwauzimu ndipo akhoza kudzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa. (Miy. 20:7) Kodi inuyo mungasonyeze bwanji kuti ndinu wolimba moti mukhoza kubatizidwa? Izi sizidalira msinkhu kapena zaka zanu zobadwa. Baibulo limasonyeza kuti anthu olimba, kapena kuti “okhwima mwauzimu,” ndi ‘amene aphunzitsa mphamvu zawo za kuzindikira kuti azitha kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.’ (Aheb. 5:14) Choncho munthu wolimba amazindikira zimene Yehova amafuna ndipo amatsimikiza mtima kuti azichita zimenezo. Satengeka ndi zinthu zoipa ndipo sachita kuuzidwa kuti azichita zoyenera. Ndiyetu wachinyamata amene akufuna kubatizidwa ayenera kukhala kuti amatsatira mfundo za m’Baibulo, ngakhale pamene makolo ake kapena anthu ena aakulu palibe.​—Afil. 2:12. w16.03 1:4, 5

Lachinayi, July 6

Usachite mantha, chifukwa dzanja la Sauli bambo anga silikupeza, moti iwe ukhaladi mfumu ya Isiraeli, ndipo ine ndidzakhala wachiwiri kwa iwe.​—1 Sam. 23:17.

Yonatani ayenera kuti anadabwa kwambiri pamene Davide anapha Goliati. Kenako Davide anapita kwa Mfumu Sauli “ali ndi mutu wa [Goliati] m’manja mwake.” (1 Sam. 17:57) Mosakayikira, Yonatani anachita chidwi ndi Davide chifukwa anali mnyamata wolimba mtima kwambiri ndipo zinali zoonekeratu kuti Mulungu ankamuthandiza. Kenako anthu awiriwa anayamba kugwirizana kwambiri moti “anachita pangano, chifukwa Yonatani anali kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondera.” (1 Sam. 18:1-3) Ndiyeno Yonatani anakhala wokhulupirika kwa Davide moyo wake wonse. Yonatani anapitiriza kukonda Davide ngakhale kuti Mulungu anamusankha kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli. Pamene Sauli ankafuna kupha Davide, Yonatani ankadera nkhawa kwambiri mnzakeyu. Choncho anapita kukamuona m’chipululu kumene ankabisala pafupi ndi Horesi. Iye anamulimbikitsa kuti azidalira Yehova ndipo anamuuza mawu a mulemba lalerowa.​—1 Sam. 23:16. w16.02 3:1, 2

Lachisanu, July 7

Ine ndinali pambali pake [pa Yehova] monga mmisiri waluso. Tsiku ndi tsiku, iye anali kusangalala kwambiri ndi ine.​—Miy. 8:30.

Yehova ndi Yesu anayamba kugwirizana kalekale zinthu zina zonse zisanalengedwe. Chifukwa cha zimenezi, anakwanitsa kulenga zamoyo zonse zomwe timaonazi. Nawonso atumiki a Yehova akale ankachita zinthu mogwirizana. Mwachitsanzo, Nowa ndi banja lake anamanga chingalawa. Patapita nthawi, Aisiraeli anagwira ntchito yomanga chihema. Akamasamuka, ankachiphwasula n’kukachimanga pamalo ena. Komanso Aisiraeli ankaimba nyimbo zotamanda Mulungu pakachisi. Anthu a Mulunguwa anatha kuchita zonsezi chifukwa chakuti anali ogwirizana. (Gen. 6:14-16, 22; Num. 4:4-32; 1 Mbiri 25:1-8) Nawonso Akhristu oyambirira ankagwirizana. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti ngakhale kuti Akhristu odzozedwawa anali ndi luso komanso ntchito zosiyanasiyana, ankachita zinthu mogwirizana. Iwo ankatsatira Yesu Khristu, yemwe ndi Mtsogoleri wawo. Paulo anati Akhristuwa anali ngati thupi limene limakhala ndi ziwalo zosiyanasiyana koma zonse zimagwira ntchito limodzi.​—1 Akor. 12:4-6, 12. w16.03 3:1, 2

Loweruka, July 8

Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse.​—Mat. 28:19.

Taganizirani za lamulo lokhudza kulalikira uthenga wabwino limene Yesu anapatsa otsatira ake. Kale, anthu a mitundu ina ankafunika kupita ku Isiraeli kuti akalambire Yehova. (1 Maf. 8:41-43) Pa nthawiyi n’kuti Yesu asanapereke lamulo la m’lemba lathu laleroli. Koma tsopano iwo ankafunika kuti ‘apite’ kukalalikira kwa anthu onse. Ndiyeno zimene zinachitika pamwambo wa Pentekosite mu 33 C.E. zinasonyeza kuti Yehova akufuna kuti uthenga wabwino ulalikidwe padziko lonse lapansi. Pa nthawiyi, mzimu woyera unathandiza ophunzira 120 kuti alankhule m’zilankhulo zosiyanasiyana kwa Ayuda komanso kwa anthu amene analowa Chiyuda. (Mac. 2:4-11) Patapita nthawi, ophunzirawo ankafunikanso kuti azilalikira kwa Asamariya. Komanso m’chaka cha 36 C.E., tingati gawo linakula chifukwa ankayenera kulalikiranso kwa anthu a mitundu ina, osadulidwa. Apa ndiye kuti Akhristu anayenera kulalikira padziko lonse. w16.03 4:12

Lamlungu, July 9

Zinthu zimene unazimva kwa ine . . . , uziphunzitse kwa anthu okhulupirika.​—2 Tim. 2:2.

Atumiki a Mulungu amadziwa kuti kuphunzitsa ena n’kothandiza kwambiri. Mwachitsanzo, Abulamu anakwanitsa kupulumutsa m’bale wake Loti chifukwa choti anali ndi “anyamata ake odziwa kumenya nkhondo” kapena kuti ophunzitsidwa bwino. (Gen. 14:14-16) M’nthawi ya Mfumu Davide, anthu omwe ankaimba m’nyumba ya Mulungu anali “ophunzitsidwa kuimbira Yehova” ndipo izi zinkalemekeza Yehova. (1 Mbiri 25:7) Masiku ano tikumenya nkhondo yolimbana ndi Satana ndi otsatira ake. (Aef. 6:11-13) Komanso tikuyesetsa kuchita zimene tingathe kuti tizitamanda Yehova. (Aheb. 13:15, 16) Choncho nafenso tiyenera kuphunzitsidwa kuti zinthu zizitiyendera bwino. Kuti zimenezi zitheke, Yehova waika akulu m’mipingo kuti aziphunzitsa ena. Akulu asanayambe kuphunzitsa munthu zinthu zatsopano, ayenera kumulimbikitsa ndi mfundo za m’Mawu a Mulungu. Izi zimathandiza kuti aphunzire bwino zinthu zatsopanozo.​—1 Tim. 4:6. w15 4/15 2:1, 2

Lolemba, July 10

[Yesu] adzawononga Mdyerekezi, amene ali ndi njira yobweretsera imfa.​—Aheb. 2:14.

Lembali silikutanthauza kuti Mdyerekezi ndi amene amapha munthu aliyense. Koma mtima wake wofuna kupha anthu wafala kwambiri m’dzikoli. Komanso kungoyambira pamene Hava anakhulupirira bodza la Satana ndipo Adamu sanamvere Mulungu, uchimo ndi imfa zafalikira kwa anthu onse. (Aroma 5:12) Choncho tinganenedi kuti Satana “ali ndi njira yobweretsera imfa.” M’pake kuti Yesu ananena kuti Satana ndi “wopha anthu.” (Yoh. 8:44) Apatu mutha kuona kuti Satana ndi mdani wamphamvu kwambiri. Tikamatsutsa Satana timakhala pa udani ndi Satanayo komanso aliyense amene ali kumbali yake potsutsa ulamuliro wa Yehova. Kumbali yakeyo kulinso ziwanda. (Chiv. 12:3, 4) Ziwandazi ndi zamphamvunso ndipo zakhala zikuzunza anthu kwa nthawi yaitali. (Mat. 8:28-32; Maliko 5:1-5) Popeza ziwanda komanso wolamulira ziwandazo amadana nafe, tiyenera kusamala kwambiri. (Mat. 9:34) Popanda thandizo la Yehova sitingalimbane ndi Satana. w15 5/15 1:6, 7

Lachiwiri, July 11

Adama, opembedza mafano, achigololo, amuna amene amagonedwa ndi amuna anzawo, amuna ogona amuna anzawo, akuba, aumbombo, zidakwa, olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.​—1 Akor. 6:9, 10.

Kodi mungatani ngati mukuyesedwa kuti muchite chiwerewere? Choyamba, muyenera kuvomereza kuti panokha simungalimbe. (Aroma 7:22, 23) Ndiyeno muyenera kupempha Yehova kuti akupatseni mphamvu. (Afil. 4:6, 7, 13) Muyeneranso kupewa zinthu zimene zingakugwetsereni mumsampha wa chiwerewere. (Miy. 22:3) Ndiyeno mayeserowo akafika muyenera kukanitsitsa nthawi yomweyo. (Gen. 39:12) Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yopewa mayesero. Iye sanapusitsidwe ndi zimene Satana anamulonjeza ndipo sanataye nthawi n’kumaganizaganiza kuti, ‘Kodi ndichite, ndisachite?’ M’malomwake ankayankha nthawi yomweyo kuti: “Malemba amati.” (Mat. 4:4-10) Yesu ankadziwa bwino Mawu a Mulungu ndipo izi zinamuthandiza kuti pamene ankayesedwa asachedwechedwe kukana ndipo ankatchula malemba oyenerera. Choncho kuti tigonjetse Satana, tiyenera kupewa chilichonse chimene chingatigwetsere mumsampha wa chiwerewere. w15 5/15 2:15, 16

Lachitatu, July 12

Muzitsanzira Mulungu.​—Aef. 5:1.

Popeza timatha kumvetsa zinthu zomwe sitinakumanepo nazo, tikhoza kutsanzira nzeru za Yehova n’kuoneratu zotsatira za zochita zathu. Yehova akasankha kugwiritsira ntchito khalidweli, amatha kudziwa bwinobwino zotsatira za zinthu zinazake. Ife tilibe nzeru ngati za Yehova, koma tikhoza kuoneratu zotsatira za zochita zathu. Nafenso tingatsanzire Yehova poganizira kapena kuona m’maganizo mwathu zotsatira za zochita zathu. Mwachitsanzo, ngati tili pa chibwenzi tiyenera kukumbukira kuti n’zosavuta kuti tichite chiwerewere. Sitiyenera kuganizira kapena kuchita chilichonse chimene chingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. M’malomwake tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Paja limati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.”​—Miy. 22:3. w15 5/15 4:10, 11

Lachinayi, July 13

Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.​—Mat. 5:28.

Nkhani ya Mfumu Davide imasonyeza mavuto amene amakhalapo ngati tayang’anitsitsa zosayenera. Iye ali padenga la nyumba “anaona mkazi akusamba.” (2 Sam. 11:2) Ndiyeno ankangomuyang’anitsitsa osasiya. Izi zinachititsa kuti ayambe kulakalaka mkazi wamwiniyo ndipo kenako anagona naye. Kuti tisayambe kulakalaka zoipa, tiyenera kutsanzira Yobu. Paja iye ‘anachita pangano ndi maso ake.’ (Yobu 31:1, 7, 9) Tiyenera kutsimikiza mumtima mwathu kuti tisamayang’anitsitse anthu mpaka kufika powalakalaka. Mfundo imeneyi tiyenera kuitsatiranso ngati taona zithunzi zoipa pa TV, pa intaneti, m’mabuku, kapena m’zikwangwani. Mwina mukaganizira mfundo zimenezi mukuona kuti pali zina zimene muyenera kusintha. Ngati ndi choncho, chonde musinthiretu panopa. Yesetsani kutsatira malangizo a m’Mawu a Mulungu amene angakuthandizeni kukhalabe oyera.​—Yak. 1:21-25. w15 6/15 3:12-14

Lachisanu, July 14

Musatilowetse m’mayesero.​—Mat. 6:13.

Tikaganizira zimene zinachitikira Yesu atangobatizidwa, tikhoza kuona ubwino wopempha Mulungu kuti ‘asatilowetse m’mayesero.’ Paja Yesu atangobatizidwa, mzimu unamutsogolera kuchipululu “kuti akayesedwe ndi Mdyerekezi.” (Mat. 4:1) Ndiyeno funso n’kumati, N’chifukwa chiyani Mulungu analola kuti zimenezi zichitike? Choyamba, tiyenera kukumbukira kuti Adamu ndi Hava anakana ulamuliro wa Mulungu ndipo Satana anayambitsa nkhani yaikulu. Panali mafunso amene anafunika nthawi yaitali kuti ayankhidwe. Mwachitsanzo, kodi Mulungu analenga bwino anthu kapena ayi? Kodi munthu wangwiro akhoza kukhala wokhulupirika kwa Mulungu ngakhale atayesedwa kwambiri ndi “woipayo”? Kodi zimene Satana ananena zoti anthu akhoza kudzilamulira okha bwinobwino zinali zoona? (Gen. 3:4, 5) Ndiyeno kukhulupirika kwa Yesu kunasonyeza kuti Mdyerekezi ndi wabodza. M’tsogolomu mafunso onsewa akadzayankhidwa bwinobwino, anthu onse ndiponso angelo adzadziwa kuti Yehova ndi amene amalamulira bwino kwambiri. w15 6/15 5:12

Loweruka, July 15

Kudzakhala chisautso chachikulu.​—Mat. 24:21.

Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti chisautso chachikulu chidzayamba ndi kuwonongedwa kwa “Babulo Wamkulu.” (Chiv. 17:5-7) Baibulo limagwiritsa ntchito mawu oti hule ponena za zipembedzo zonse zonyenga. Izi n’zomveka chifukwa chakuti atsogoleri a zipembedzo akhala pa ubwenzi ndi atsogoleri andale. Iwo sanakhulupirike kwa Yesu ndiponso Ufumu wake. M’malomwake, akhala akugwirizana ndi olamulira a dzikoli ndipo achita zinthu zosemphana ndi mfundo za m’Baibulo pofuna kuwasangalatsa. Iwo amasiyana kwambiri ndi odzozedwa a Mulungu omwe ali ngati anamwali oyera. (2 Akor. 11:2; Yak. 1:27; Chiv. 14:4) Koma kodi amene adzawononge “Babulo Wamkulu” ndi ndani? Yehova adzaika “maganizo ake” m’mitima ya “nyanga 10” za ‘chilombo chofiira.’ ‘Chilombo chofiira’ chikuimira bungwe la United Nations ndipo “nyanga 10” zikuimira maboma onse amene amathandiza bungweli.”​—Chiv. 17:3, 16-18. w15 7/15 2:3, 4

Lamlungu, July 16

Ena mwa inu amanena kuti: “Ine ndine wa Paulo,” ena amati, “Ine ndine wa Apolo,” enanso amati “Ine ndine wa Kefa,” pamene ena amati, “Ine ndine wa Khristu.”​—1 Akor. 1:12.

Kodi Akhristu oyambirira anachita zotani pamene ena mumpingo anayamba kugawikana? Paulo anauza Akhristuwo kuti: “Ndikukudandaulirani abale . . . kuti nonse muzilankhula mogwirizana ndi kuti pasakhale magawano pakati panu, koma kuti mukhale ogwirizana pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.” (1 Akor. 1:10, 11, 13) Masiku anonso sitiyenera kulola kuti nkhani zina zitilekanitse. (Aroma 16:17, 18) Paulo analimbikitsa Akhristu odzozedwawa kuti azikumbukira kuti iwo ndi nzika zakumwamba osati zapadzikoli. (Afil. 3:17-20) Iwo ankafunika kuchita zinthu ngati akazembe oimira Khristu. Paja akazembe salowerera m’nkhani za m’dziko limene akugwira ntchito chifukwa si dziko lawo. (2 Akor. 5:20) Nawonso Akhristu amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi ndi nzika za Ufumu wa Mulungu. Choncho iwo sayenera kulowerera m’mikangano ya m’dzikoli. w15 7/15 3:9, 10

Lolemba, July 17

Anawamvera chifundo. Anali kukhululukira machimo awo ndipo sanali kuwawononga. Nthawi zambiri anali kubweza mkwiyo wake, ndipo sanali kuwasonyeza ukali wake wonse.​—Sal. 78:38.

Kuganizira mawu a mulemba lalerowa kungatithandize kuona kuti Yehova amatikonda. Choncho musakayikire kuti Yehova amakukondani kwambiri. (1 Pet. 5:6, 7) Kuti makolo ndi ana azikhulupirirana ndiponso kukondana, ayenera kulankhulana momasuka komanso mwachikondi. N’chimodzimodzi ndi Atate wathu wakumwamba. Ngakhale kuti sitiona Mulungu ndiponso kumva mawu ake, iye amagwiritsa ntchito Baibulo kuti azilankhula nafe. Choncho tiziona kuti Baibulo ndi lamtengo wapatali ndipo tiziliwerenga. (Yes. 30:20, 21) Yehova amafunitsitsa kutitsogolera ndiponso kutiteteza. Iye amafunanso kuti timudziwe komanso tizimukhulupirira.​—Sal. 19:7-11; Miy. 1:33. w15 8/15 1:6, 7

Lachiwiri, July 18

Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.​—Yak. 4:8.

Pamene tikuyembekezera Paradaiso m’tsogolomu, tiyenera kukumbukira kuti zinthu zofunika kwambiri zimene zidzachitike m’Paradaisomo ndi zokhudza Yehova. Tidzasangalala podziwa kuti dzina lake layeretsedwa ndiponso wasonyeza kuti ndi woyeneradi kulamulira. (Mat. 6:9, 10) Tidzakhalanso ndi mwayi woona cholinga chake chokhudza anthu padzikoli chikukwaniritsidwa. Pa nthawiyi zidzakhala zosavuta kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova chifukwa uchimo udzayamba kuchepa mpaka kutheratu. (Sal. 73:28) N’zotheka kudzapeza madalitso amenewa. Paja Yesu ananena kuti ‘zinthu zonse n’zotheka ndi Mulungu.’ (Mat. 19:25, 26) Koma kuti tidzakhaledi m’dzikolo, tiyenera kuyamba panopa kuchita zinthu zomwe zingatithandize kuti ‘tigwire mwamphamvu moyo weniweniwo.’ (1 Tim. 6:19) Zochita zathu zizisonyeza kuti tikudziwa zoti dziko loipali litha posachedwapa, ndipo tiyambe panopa kuchita zinthu ngati tili kale m’dziko latsopano. w15 8/15 3:2, 3

Lachitatu, July 19

Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.​—Yoh 17:3.

Zinthu zambiri m’dzikoli zimene anthu angawerenge kapena kuonera ndi zoipa. Siziwathandiza kukhulupirira Yehova ndiponso malonjezo ake. Koma zimawalimbikitsa kukhala ndi maganizo ndiponso zolinga zogwirizana ndi dziko loipali. Choncho tiyenera kusamala kwambiri kuti tisamawerenge kapena kuonera zinthu zolimbikitsa “zilakolako za dziko.” (Tito 2:12) Mosiyana ndi dzikoli, gulu la Yehova limatulutsa mabuku ndiponso mavidiyo amene angathandize anthu kuti adzapeze moyo wosatha. Tilitu ndi mwayi waukulu wophunzira za Yehova pogwiritsa ntchito magazini, mabuku, mavidiyo ndiponso zinthu za pa webusaiti yathu. Gulu la Yehova limakonzanso misonkhano m’mipingo yoposa 110,000 padziko lonse. Pa misonkhano yampingo ndiponso ikuluikulu timaphunzira mfundo za m’Baibulo zomwe zimatithandiza kukhulupirira kwambiri Yehova ndiponso malonjezo ake.​—Aheb. 10:24, 25. w15 8/15 4:9, 11

Lachinayi, July 20

Chikumbumtima chawo chimachitira umboni pamodzi ndi iwowo.​—Aroma 2:15.

Atumiki a Yehova amafunitsitsa kuphunzitsa chikumbumtima chawo pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. Amadziwa kuti kuchita zimenezi kungathandize kuti azisiyanitsa zabwino ndi zoipa komanso azigwirizana mumpingo. Koma kuti tiphunzitse chikumbumtima chathu pamafunika zambiri osati kungodziwa zimene Baibulo limanena. Tiyenera kukonda mfundo za m’Baibulo ndiponso kukhulupirira kuti n’zothandiza. Paja Paulo analemba kuti: “Cholinga chokulamulira zimenezi n’chakuti tikhale ndi chikondi chochokera mumtima woyera, m’chikumbumtima chabwino, ndiponso m’chikhulupiriro chopanda chinyengo.” (1 Tim. 1:5) Munthu akaphunzitsa chikumbumtima chake n’kumachitsatira, amayamba kukonda kwambiri Yehova ndipo chikhulupiriro chake chimalimba. Amasonyezanso kuti ali ndi mtima wabwino ndipo akufunitsitsa kusangalatsa Yehova. w15 9/15 2:2, 3

Lachisanu, July 21

Taganizirani za chikondi chachikulu chimene Atate watisonyeza.​—1 Yoh. 3:1.

Yehova ndi amene anatilenga. (Sal. 100:3-5) N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti Adamu anali “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Nayenso Yesu anaphunzitsa kuti tizitchula Mulungu kuti “Atate wathu wakumwamba.” (Mat. 6:9) Popeza Yehova ndi amene anatilenga, ifeyo tili ngati ana ake. Choncho Yehova amatikonda ngati mmene bambo wabwino amakondera ana ake. Koma ngakhale bambo wabwino atayesetsa kwambiri kusonyeza chikondi, sangafanane ndi Yehova. Ndipo pali abambo ena amene amazunza ana awo moti anawo saiwala nkhanza zimene anachitiridwa. Izitu n’zopweteka komanso zomvetsa chisoni. Koma Yehova sachita zimenezi. (Sal. 27:10) Iye amatikonda komanso kutisamalira bwino. Kudziwa zimenezi kungatithandizenso kuti tizimukumukonda kwambiri.​—Yak. 4:8. w15 9/15 4:3, 4

Loweruka, July 22

Mulungu amachita zinthu m’njira imene imamusangalatsa. Iye amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.​—Afil. 2:13.

Ngati timakonda Mulungu ndiponso kumudalira, timaganizira zimene iye amafuna tisanasankhe zochita. Pa nthawi ya mneneri Samueli, Aisiraeli anagonjetsedwa ndi Afilisiti ndipo ankafunikira kwambiri thandizo la Yehova. Zitatero, Aisiraeliwo anati: “Tiyeni tikatenge likasa la pangano la Yehova ku Silo, kuti likhale pakati pathu ndi kutipulumutsa m’manja mwa adani athu.” Koma atachita zimenezi “panaphedwa amuna oyenda pansi a Isiraeli okwanira 30,000. Ngakhalenso likasa la Mulungu linalandidwa.” (1 Sam. 4:2-4, 10, 11) Mwina tingaganize kuti Aisiraeliwo ankadalira Yehova chifukwa chakuti anatenga Likasa pokamenyana ndi Afilisiti. Koma sanapemphe Yehova kuti awathandize. M’malomwake anatsatira nzeru zawo ndipo anakumana ndi zoopsa kwambiri.​—Miy. 14:12. w15 9/15 5:16, 17

Lamlungu, July 23

Tiwonjezereni chikhulupiriro.​—Luka 17:5.

Pali zimene tingachite kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu. Tikaphunzira n’kufika pobatizidwa tiyenera kupitiriza kuphunzira Baibulo mozama. (Aheb. 6:1, 2) Mwachitsanzo, tingaphunzire maulosi amene anakwaniritsidwa kale. Pophunzira Baibulo tiyeneranso kudziyesa n’kuona ngati zochita zathu zikugwirizana ndi zimene Mulungu amayembekezera kwa anthu amene ali ndi chikhulupiriro champhamvu. (Yak. 1:25; 2:24, 26) Mtumwi Paulo ananena kuti Akhristu akhoza kulimbikitsana ndiponso kuthandizana kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. (Aroma 1:12) Kucheza ndi Akhristu anzathu, makamaka amene ‘chikhulupiriro chawo chayesedwa,’ kungathandize kuti chikhulupiriro chathunso chilimbe kwambiri. (Yak. 1:3) Munthu akamagwirizana ndi anthu oipa chikhulupiriro chake chimafooka, koma akamagwirizana ndi anthu abwino chimalimba kwambiri. (1 Akor. 15:33) N’chifukwa chake Baibulo limatiuza kuti “tisaleke kusonkhana pamodzi” komanso kulimbikitsana.​—Aheb 10:24, 25. w15 10/15 2:2, 8, 9

Lolemba, July 24

Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Dzipereke pa zinthu zimenezi.​—1 Tim. 4:15.

Tikamakonzekera kukaphunzitsa ena, ndi bwino kuganizira mafunso komanso zitsanzo zimene zingathandize wophunzirayo. Zimenezi zingatithandize kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuti tiziphunzitsa Mawu a Mulungu mwaluso. Kuganizira zinthu zolimbikitsa tisanapite mu utumiki n’kothandizanso. (Ezara 7:10) Ngati tingawerenge nkhani inayake ya m’buku la Machitidwe tikhoza kulalikira mwakhama. Tingachitenso bwino kuganizira mavesi komanso mabuku amene tikufuna kukawagwiritsa ntchito mu utumiki. (2 Tim. 1:6) Tiziganiziranso nkhani zimene zingachititse chidwi anthu a m’gawo lathu. Tikamachita zimenezi tidzatha kuphunzitsa Mawu a Mulungu mogwira mtima.​—1 Akor. 2:4. w15 10/15 4:9

Lachiwiri, July 25

Ngati diso lako lakumanja limakuchimwitsa, ulikolowole ndi kulitaya.​—Mat. 5:29.

Makolo, mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi n’chiyani chingachititse kuti mwana wanga akopeke ndi zinthu zolaula? Kodi amadziwa bwinobwino kuopsa kwa zolaula? Kodi timamasukirana moti angandifotokozere ngati atayesedwa kuti aonere zoipazi? Mungachite bwino kuyamba kumuthandiza adakali wamng’ono. Mwina mungamuuze kuti: “Tsiku lina ukadzakhala ndi kamtima kofuna kuonera zinthu zinazake zoipa, udzandiuze. Usadzachite manyazi chifukwa ndidzakuthandiza.” Inunso muyenera kukhala ozindikira posankha zosangalatsa. Bambo wina dzina lake Pranas anati: “Ana amaona zimene makolofe timakonda kumvera, kuonera kapena kuwerenga ndipo amatsatira zimenezo kuposa malangizo amene timawapatsa.” Koma ana akaona kuti mumasankha bwino zosangalatsa, nawonso amachita zomwezo.​—Aroma 2:21-24. w15 11/15 1:12-14

Lachitatu, July 26

Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo.​—Sal. 32:8.

Masiku ano, gulu la Yehova limatilimbikitsa kuti tizilalikira m’malo opezeka anthu ambiri monga m’madepoti, m’malo oimika magalimoto komanso m’misika. Kodi mumachita mantha kulalikira m’malo oterewa? Ngati ndi choncho, mungachite bwino kupemphera komanso kuganizira zimene woyang’anira woyendayenda wina ananena. Iye anati: “Timaona kuti utumiki uliwonse watsopano umatipatsa mwayi wosonyeza kuti ndife okhulupirika ndiponso kuti timafunitsitsa kutumikira Yehova m’njira iliyonse imene watipempha.” Kuchita utumiki uliwonse ngakhale umene sutisangalatsa kwenikweni kumatithandiza kuti tizidalira kwambiri Yehova ndiponso kukhala naye pa ubwenzi wolimba. (2 Akor. 12: 9,10) Abale ndi alongo ambiri amakonda kusonyeza anthu webusaiti yathu ya jw.org. Webusaitiyi ikuthandiza anthu ambiri, ngakhale a kumadera akutali, kuti amve uthenga wabwino. w15 11/15 5:12, 13, 15

Lachinayi, July 27

Chitsulo chimanola chitsulo chinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.​—Miy. 27:17.

Takhala tikukumana ndi mavuto ambiri pomasulira Baibulo la Dziko Latsopano m’zilankhulo zina kuchokera ku Chingelezi. Mwachitsanzo, mu Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi, anagwiritsa ntchito mawu achiheberi akuti “Sheol” pa Mlaliki 9:10 komanso pamavesi ena, potsatira zimene Mabaibulo enanso achingelezi anachita. Vesi limeneli linkati: “Kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Sheoli kumene ukupitako.” Koma omasulira Mabaibulo m’zilankhulo zina anaona kuti sangagwiritse ntchito mawuwa chifukwa anthu ambiri sakuwadziwa ndipo angaone ngati ndi dzina la malo enieni. Pa chifukwa chomwechi, amene anagwira ntchito yokonzanso Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi, lomwe linatuluka mu 2013, anauzidwa kuti akhoza kungomasulira tanthauzo la mawu akuti “Sheol,” komanso mawu ofanana nawo achigiriki akuti “Hades.” Choncho mawuwa anawamasulira kuti “Manda,” omwe ndi mawu olondola komanso osavuta kumva. M’Baibuloli anachotsamonso mawu achikale ndipo anayesetsa kuti likhale lomveka bwino komanso losavuta kuwerenga. Komanso anaonetsetsa kuti likhale lolondola. Anatsatiranso zimene omasulira m’zilankhulo zina anachita pomasulira Baibulo ndipo izi zinathandiza kwambiri. w15 12/15 2:10, 12

Lachisanu, July 28

Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka. Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa. Yehova adzamuteteza ndi kumusunga ali wamoyo.​—Sal. 41:1,2.

Tikadwala, Mulungu angatilimbikitse, angatipatse nzeru komanso angatithandize ngati mmene anachitira ndi atumiki ake akale. Komabe tikudziwa kuti polemba mawu a mulemba lalerowa, Davide sankatanthauza kuti anthu amene amachita zinthu moganizira ovutika, sangafe. M’malomwake, ankangotanthauza kuti Mulungu amawathandiza anthu oterewa. Koma kodi amawathandiza bwanji? Davide anati, ‘Yehova adzawachirikiza pamene akudwala ndi kuwasamalira bwino kwambiri.’ (Sal. 41:3) Munthu amene amachita zinthu moganizira ovutika ayenera kudziwa kuti Mulungu amaona zabwino zimene amachitazo ndiponso kukhulupirika kwake. Komanso Mulungu amatithandiza chifukwa ndi amene anapanga thupi lathu m’njira yoti lizitha kuchira. w15 12/15 4:7

Loweruka, July 29

Kumbukirani amene ali m’ndende.​—Aheb. 13:3.

Apa sikuti Paulo ankangonena za munthu wina aliyense amene ali kundende. Koma ankanena za Akhristu amene anamangidwa chifukwa chotumikira Mulungu. Pamene ankalemba mawu amenewa, nayenso n’kuti atakhala m’ndende zaka pafupifupi 4. (Afil. 1:12-14) Iye anayamikira abale chifukwa chomusonyeza chifundo pamene anali m’ndende. (Aheb. 10:34) Akhristu achiheberi ankakhala kutali ndipo sakanatha kuthandiza Paulo pamene anali kundende. Ndiye kodi akanamukumbukira bwanji? Akanatha kumupempherera kuti Mulungu amuthandize. (Aheb. 13:18, 19) Masiku anonso sitingathe kuthandiza abale athu onse amene ali m’ndende ngati mmene abale apafupi angawathandizire. Koma tingasonyeze kuti timawamvera chisoni komanso kuwakonda tikamapempha Yehova mochokera pansi pa mtima kuti awathandize. w16.01 1:13, 14

Lamlungu, July 30

Mzimuwo umachitira umboni limodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu.​—Aroma 8:16.

Mulungu analenga anthu ndi cholinga choti akhale padziko lapansi osati kumwamba. (Gen. 1:28; Sal. 37:29) Koma Yehova wasankha anthu ena kuti apite kumwamba kukakhala mafumu ndi ansembe. Choncho munthu akadzozedwa amasintha mmene amaganizira, mmene amaonera zinthu ndipo chiyembekezo chake chimasinthanso. (Aef. 1:18) Koma kodi munthu amadziwa bwanji kuti wadzozedwa? Zimene Paulo anauza Akhristu a ku Roma, omwe anali “oitanidwa kukhala oyera,” zingatithandize kuyankha funsoli. Iye anawauza kuti: “Simunalandire mzimu wa ukapolo woyambitsanso mantha, koma munalandira mzimu wakuti mukhale ana, umene timafuula nawo kuti: ‘Abba, Atate!’” (Aroma 1:7; 8:15) Choncho mwachidule tingati Mulungu akadzoza munthu, amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera n’kumuthandiza kuti atsimikize zoti wasankhidwa kudzalamulira nawo mu Ufumu.​—1 Ates. 2:12. w16.01 3:8, 9

Lolemba, July 31

Musamalowerere mu nkhani za eni.​—1 Ates. 4:11.

Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza odzozedwa? Tizipewa kulowerera nkhani zimene sizikutikhudza. (2 Ates. 3:11) Mwachitsanzo, si bwino kuwafunsa mafunso monga lakuti, ‘Kodi munadziwa bwanji kuti mwadzozedwa?’ Tisamaganizenso kuti makolo, achibale komanso mwamuna kapena mkazi wa munthu wodzozedwa nayenso ndi wodzozedwa. Munthu sadzozedwa potengera banja limene wachokera. (1 Ates. 2:12) Tizipewanso kufunsa mwamuna kapena mkazi wa munthu wodzozedwa mafunso okhudza mmene amamvera akaganizira kuti sadzakhala limodzi ndi mnzakeyo m’Paradaiso. M’malo mowafunsa mafunso amene angawakhumudwitse, tiyenera kukhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova ‘adzatambasula dzanja lake ndi kukhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.’ (Sal. 145:16) Tikamachita zinthu moyenera ndi odzozedwa timapewanso kusocheretsedwa ndi “abale onyenga,” amene amati ndi odzozedwa.​—Agal. 2:4, 5; 1 Yoh. 2:19. w16.01 4:10, 11

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena