August
Lachiwiri, August 1
Kodi Woweruza wa dziko lonse lapansi sadzachita cholungama?—Gen. 18:25.
Abulahamu ankamvera Yehova ngakhale pa zinthu zazing’ono ndipo izi zinathandiza kuti ubwenzi wawo ukhale wolimba. Ankamasuka kuuza Yehova za mumtima mwake moti ankatha kumufunsa mafunso omwe ankamuthetsa nzeru. Mwachitsanzo, atamva kuti Mulungu awononga mzinda wa Sodomu ndi wa Gomora anada nkhawa kuti mwina anthu abwino akhoza kuwonongedwanso. N’kutheka kuti ankadera nkhawa Loti yemwe ankakhala ku Sodomu. Choncho Abulahamu anafunsa Mulungu mafunso okhudza zimenezi. Koma anafunsa modzichepetsa kwambiri komanso mosonyeza kuti ankakhulupirira zoti Mulungu ndi “Woweruza wa dziko lonse lapansi.” Yehova anayankha Abulahamu moleza mtima n’kumuthandiza kuona kuti iye ndi Mulungu wachifundo, amaona mumtima ndipo poweruza sangawononge anthu olungama. (Gen. 18:22-33) Kunena zoona zimene Abulahamu ankadziwa zokhudza Yehova ndiponso zimene anakumana nazo pa moyo wake zinamuthandiza kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehovayo. w16.02 1:11, 12
Lachitatu, August 2
Yehova akhale pakati pa iwe ndi ine, ndi pakati pa ana ako ndi ana anga mpaka kalekale.—1 Sam. 20:42.
Tonsefe timaona kuti kukhulupirika ndi khalidwe lofunika kwambiri. Yonatani ndi chitsanzo chabwino pa nkhaniyi chifukwa anali wokhulupirika kwa Davide. Koma kodi n’chifukwa chiyani anali wokhulupirika kwa Davide m’malo momuchitira nsanje? Yonatani analinso wokhulupirika kwa Yehova. Iye ankaona kuti kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndi kofunika kuposa chilichonse. Ndipotu onsewa anachita zinthu mogwirizana ndi pangano lawo lakuti: “Yehova akhale pakati pa iwe ndi ine, ndi pakati pa ana ako ndi ana anga mpaka kalekale.” Ifenso tiziyesetsa kukhala okhulupirika kwa achibale athu, anzathu ndiponso abale ndi alongo mumpingo. (1 Ates. 2:10, 11) Koma chofunika kwambiri, tizikhala okhulupirika kwa Yehova chifukwa ndi amene anatipatsa moyo. (Chiv. 4:11) Tikamachita zimenezi timakhala osangalala. Koma tiyenera kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu ngakhale pamene takumana ndi mavuto.—w16.02 3:3, 4
Lachinayi, August 3
Danieli anatsimikiza mumtima mwake kuti sadzidetsa.—Dan. 1:8.
Wachinyamata wolimba mwauzimu nthawi zonse amayesetsa kutsatira zimene amakhulupirira. Mwachitsanzo, iye sachita zinthu ngati Mkhristu akakhala ku Nyumba ya Ufumu koma n’kumachita zinthu ngati anthu a m’dzikoli akakhala kusukulu. Satengekanso ndi makhalidwe oipa koma amakhalabe wokhulupirika ngakhale atakumana ndi mayesero. (Aef. 4:14, 15) Kaya ndife achikulire kapena achinyamata, tonsefe timalakwitsa nthawi zina. (Mlal. 7:20) Komabe ngati mukufuna kubatizidwa, muyenera kuganizira zimene mumachita kuti muone ngati mukuyesetsa kutsatira mfundo za Yehova. Mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndakhala ndikutsatira bwinobwino zimene Mulungu amafuna? Kodi ndimatani ndikakumana ndi mayesero? Nanga kodi ndimasonyeza kuti ndimatha kusiyanitsa zoyenera ndi zosayenera? Kodi ndingatani ngati anthu a m’dzikoli atandiuza kuti ndili ndi luso ndipo ndikhoza kuchita zinazake zaphindu? Kodi nthawi zonse ‘ndimazindikira chifuniro cha Yehova,’ ngakhale pamene ndakumana ndi mayesero?’—Aef. 5:17. w16.03 1:7-9
Lachisanu, August 4
Masiku amenewo adzakhala masiku a chisautso chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu analenga kudzafika nthawi imeneyo.—Maliko 13:19.
Tikukhala ‘m’masiku otsiriza,’ ndipo posachedwapa kuchitika chisautso chachikulu choti sichinachitikepo. (2 Tim. 3:1) Komanso, Satana ndi ziwanda zake anaponyedwa padzikoli ndipo izi zikuchititsa kuti anthufe tizivutika. (Chiv. 12:9, 12) Kuwonjezera pamenepa, tikugwira ntchito imene Yesu anatilamula yoti tizilalikira kwa anthu a mitundu yonse komanso a zilankhulo zonse. Kuti Mulungu apitirize kutidalitsa, tiyenera kutsatira kwambiri malangizo amene timalandira kudzera mumpingo wachikhristu. Tikamamvera malangizo amene Mulungu akutipatsa panopa, zidzakhalanso zosavuta kuti tidzamvere malangizo pa nthawi ya “chisautso chachikulu,” chomwe chidzawononge dziko la Satanali. (Mat. 24:21) Chisautso chachikulu chikadzatha, tidzakhala m’dziko latsopano ndipo Satana sadzasocheretsanso anthu. Choncho tidzafunikanso malangizo atsopano. w16.03 4:16, 18
Loweruka, August 5
Mu utsiwo, munatuluka dzombe.—Chiv. 9:3.
Chakumapeto kwa nthawi ya atumwi, mtumwi Yohane anaona masomphenya a angelo 7 ndipo mngelo aliyense analiza lipenga. Pamene mngelo wa 5 analiza lipenga lake, Yohane anaona “nyenyezi” itagwa kuchokera kumwamba. Nyenyeziyo inali ndi kiyi ndipo inatsegula dzenje lolowera kuphompho. Ndiyeno utsi unatuluka kuchokera m’phomphomo ndipo mu utsiwo munatulukanso dzombe. Komabe dzombelo silinadye zomera koma linavulaza ‘anthu amene analibe chidindo cha Mulungu pamphumi pawo.’ (Chiv. 9:1-4) M’nthawi ya Mose, dzombe linawononga kwambiri zomera ku Iguputo. (Eks. 10:12-15) Choncho Yohane ayenera kuti ankadziwa kuti dzombe ndi loopsa. Dzombe limene Yohane anaona linkaimira Akhristu odzozedwa amene akhala akulalikira uthenga woti zipembedzo zonyenga zidzawonongedwa. Panopa pali Akhristu ambiri omwe adzakhale padziko lapansi amene akugwira ntchitoyi mogwirizana ndi odzozedwa. Uthenga womwe amalalikira wathandiza anthu ambiri kuti atuluke m’zipembedzo zonyenga komanso asiye kutsogoleredwa ndi Satana. w16.03 3:3
Lamlungu, August 6
Tsegulani maso anga kuti ndione zinthu zodabwitsa za m’chilamulo chanu.—Sal. 119:18.
Kodi mkulu angadziwe bwanji ngati mfundo za m’Malemba zikuthandiza m’bale amene akumuphunzitsa? Mwina angamufunse kuti: “Kodi inuyo mutadzipereka kwa Yehova munasintha zinthu ziti?” Funso limeneli lingapangitse kuti akambirane mfundo zomwe zingathandize m’baleyo kudziwa zoyenera kuchita kuti azitumikira Yehova ndi moyo wake wonse. (Maliko 12:29, 30) Pambuyo pokambirana mfundo ngati zimenezi akhoza kupemphera naye. Ndiyeno m’pempherolo angapemphe Yehova kuti amupatse mzimu woyera kuti umuthandize kuphunzira zinthu zatsopano. M’baleyo akhoza kusangalala kumva pemphero la mkuluyo losonyeza kuti amamuganizira kwambiri. Poyamba kumuphunzitsa, mkuluyo ayenera kukambirana naye nkhani zina za m’Baibulo zimene zingamuthandize kukhala ndi mtima wofuna kutumikira, kukhala wodalirika komanso wodzichepetsa. (1 Maf. 19:19-21; Neh. 7:2; 13:13; Mac. 18:24-26) Makhalidwe amene tatchulawa ali ngati manyowa othandiza m’baleyo kuti ayambe mwamsanga kukonda kwambiri Yehova komanso kudziwa malemba amene ‘angamutsegule m’maso kuti aone ‘zinthu zodabwitsa’ za m’Mawu a Mulungu. w15 4/15 2:3, 4
Lolemba, August 7
Yandikirani Mulungu.—Yak. 4:8.
Kulankhula ndi Yehova nthawi zonse kumalimbitsa ubwenzi wathu. Kodi tingalankhule naye bwanji? Tingalankhule naye popemphera kwa iye. (Sal. 142:2) Yehova amalankhula nafe tikamawerenga Mawu ake ndiponso kuwaganizira mozama. (Yes. 30:20, 21) Mukamamuuza Yehova zonse zimene zili mumtima mwanu, simudzavutika kudziwa kuti wakuyankhani. Mapemphero anu akamayankhidwa, m’pamene Yehova amakhala mnzanu weniweni. Choncho kuti muyandikire kwambiri Yehova, muyenera kumuuza zonse za mumtima mwanu. Tiyenera kuyesetsa kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova kwa moyo wathu wonse. Ngati tikufuna kuti Yehova atiyandikire, tiyenera kuyamba ifeyo. Choncho tiyeni tiziyesetsa kulankhulana ndi Yehova powerenga Mawu ake komanso popemphera nthawi zonse. Tikatero ubwenzi wathu ndi Yehova udzalimba kwambiri ndipo tidzatha kupirira vuto lililonse limene tingakumane nalo. w15 4/15 3:3, 14, 16
Lachiwiri, August 8
Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.—1 Pet. 5:8.
Lembali likutithandiza kumvetsa bwino zimene Satana amachita. Ngakhale kuti dziko lonse lili m’manja mwake, iye akulusirabe anthu ambiri. Satana wakhala akufunitsitsa kumeza atumiki a Yehova kuyambira m’nthawi ya atumwi mpaka masiku ano. Mkango wolusa sumvera chisoni nyama ndipo ukaipha sudandaula kapena kudziimba mlandu. Choncho Satana sachita chisoni ndi anthu omwe akufuna kuwameza. Mwachitsanzo, Satana sankadandaula pamene Aisiraeli ankachita chiwerewere ndiponso dyera. Ndipo kodi mukuganiza kuti Satana anamva bwanji ataona zimene zinachitikira Zimiri chifukwa chochita chiwerewere kapena Gehazi chifukwa cha dyera? Iye ayenera kuti anasangalala kwambiri.—Num. 25:6-8, 14, 15; 2 Maf. 5:20-27. w15 5/15 1:8, 9
Lachitatu, August 9
Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.—Yak. 4:7.
Kodi tingagonjetse bwanji Satana? Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ngati inu mudzapirire, mudzapeza moyo.” (Luka 21:19) Kaya anthu atichitire zotani, tsogolo lathu likhoza kukhalabe lowala. Palibe amene angatilande ubwenzi wathu ndi Yehova pokhapokha ngati titalolera tokha. (Aroma 8:38, 39) Kodi atumiki a Yehova akamwalira ndiye kuti Satana wapambana? Ayi ndithu. Pajatu Yehova adzawaukitsa. (Yoh. 5:28, 29) Tiyeneranso kudziwa kuti Satana ndi amene alibe tsogolo labwino. Dziko loipali likadzawonongedwa, iye adzaponyedwa m’phompho kwa zaka 1,000. (Chiv. 20:1-3) Kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu, Satana adzamasulidwa kwa kanthawi kuti ayese anthu angwiro komaliza kenako adzaphedwa. (Chiv. 20:7-10) Inuyo muli ndi tsogolo labwino koma Satana alibiretu tsogolo. Yesetsani kulimbana naye ndiponso kulimbitsa chikhulupiriro chanu. (1 Pet. 5:9) N’zotheka kugonjetsa Satana. w15 5/15 2:1, 18
Lachinayi, August 10
Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.—Miy. 22:3.
Munthu wanzeru amadziwa kuti maganizo athu ali ngati moto. Moto umatithandiza kuti tiphike komanso kuchita zinthu zina. Koma ngati sitisamala, umatha kuwotcha nyumba n’kupha anthu. N’chimodzimodzi ndi maganizo. Zimene timaganiza zikhoza kutithandiza kutsanzira Yehova. Koma munthu amene amakonda kuganizira zinthu zoipa tsiku lina akhoza kuchitadi zinthuzo n’kusokoneza ubwenzi wake ndi Yehova. (Yak. 1:14, 15) Kumbukirani chenjezo limene Yesu anapereka pa nkhani yoganizira zachiwerewere. Iye anati: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.”—Mat. 5:28. w15 5/15 4:11, 12, 14
Lachisanu, August 11
Zinthu zimene zinali kundisangalatsa, zinali zokhudzana ndi ana a anthu.—Miy. 8:31.
Polalikira, Yesu ankachita zodabwitsa zambiri zosonyeza kuti amakonda anthu. Pa nthawi ina, anakumana ndi munthu womvetsa chisoni kwambiri. (Maliko 1:39, 40) Munthuyo ankadwala khate. Luka anasonyeza kuti matendawo anali atafika poipa chifukwa analemba kuti munthuyo anali “wakhate thupi lonse.” (Luka 5:12) Wodwalayo ataona Yesu, “anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi ndi kum’pempha, kuti: ‘Ambuye, ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.’” Munthuyo ankadziwa kuti Yesu ali ndi mphamvu yomuchiritsa koma ankafuna kudziwa ngati akufunitsitsa kuchita zimenezi. Kodi Yesu anamuyankha bwanji? Anatambasula dzanja lake n’kumukhudza kenako anamulankhula motsimikiza, koma mokoma mtima kuti: “Ndikufuna. Khala woyera.” Nthawi yomweyo khate la munthuyo linatha. (Luka 5:13) Apatu Yesu anasonyezeratu kuti amakonda kwambiri anthu.—Luka 5:17. w15 6/15 2:3-5
Loweruka, August 12
Wodzipatula . . . amachita zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.—Miy. 18:1.
Ngati mungalimbe mtima n’kuuzako Akhristu anzanu zinthu zoipa zimene mukuganiza, zidzakuthandizani kusiya kuganizira zoipazo. (Aheb. 3:12, 13) Kukambirana zimenezi ndi Akhristu omwe amadziwa zinthu zambiri kungakuthandizeni kuzindikira mavuto anu. Mukatero mudzatha kukonza mavutowo ndipo ubwenzi wanu ndi Yehova udzalimba. Akulu akhoza kutithandiza kwambiri tikawauza vuto lathu. (Yak. 5:13-15) Tiyenera kupempha ena kuti atithandize ngati tili ndi vuto loonera zolaula. Tikazengereza kupempha thandizo, maganizo oipa angakule ndipo tsiku lina tikhoza kuchita chiwerewere. Zimenezi zidzakhumudwitsa anthu ena ndiponso kunyozetsa Yehova. Mtima wofuna kusangalatsa Mulungu ndiponso kukhalabe mumpingo, walimbikitsa Akhristu ambiri kupempha thandizo n’kutsatira malangizo.—Yak. 1:15; Sal. 141:5; Aheb. 12:5, 6. w15 6/15 3:15-17
Lamlungu, August 13
Aneneri azidzachita manyazi pa tsiku limenelo. Azidzachita manyazi ndi masomphenya awo pamene akulosera. Sadzavalanso chovala chapadera chaubweya kuti anamize anthu.—Zek. 13:4.
Babulo Wamkulu akamadzawonongedwa, kodi anthu ake onse adzaphedwa? Ayi. Atsogoleri ena adzasiya zipembedzo zawo n’kukanitsitsa zoti anali m’zipembedzozo. (Zek. 13:5, 6) Nanga n’chiyani chidzachitikire atumiki a Mulungu pa nthawiyo? Yesu anati: “Kunena zoona, masikuwo akanapanda kufupikitsidwa, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwawo, masikuwo adzafupikitsidwa.” (Mat. 24:22) Mu 66 C.E., nthawi ya chisautso ‘inafupikitsidwa.’ Ndiyeno Akhristu odzozedwa, kapena kuti anthu ‘osankhidwa,’ amene anali mu Yerusalemu komanso m’madera ozungulira anathawa. Nawonso masiku a chisautso chachikulu ‘adzafupikitsidwa’ chifukwa cha anthu ‘osankhidwa.’ Yehova sadzalola kuti “nyanga 10” ziwononge anthu ake. (Chiv. 17:16) Choncho chisautsocho chidzaimitsidwa kwa kanthawi. w15 7/15 2:5, 6
Lolemba, August 14
Woyesayo anabwera.—Mat. 4:3.
Munthu aliyense angasankhe yekha kukopeka ndi mayeserowo kapena ayi. (Mat. 6:13; Yak. 1:13-15) Yesu anakana mayesero onse ochokera kwa Mdyerekezi pogwiritsa ntchito malemba oyenerera. Apatu Yesu anasonyeza kuti Mulungu ndi woyenera kulamulira. Koma Satana sanasiyire pomwepo. Anangomudikira kaye “kufikira nthawi ina yabwino.” (Luka 4:13) Satana anachita zonse zimene akanatha kuti alepheretse Yesu kukhala wokhulupirika koma Yesu sanalole. Koma Satana amayesabe Akhristu onse ndipo inuyo muli m’gulu loyesedwalo. Popeza nkhani yokhudza ulamuliro wa Mulungu sinathe, Yehova amalola kuti Satana azigwiritsa ntchito dzikoli potiyesa. Koma sitinganene kuti Mulungu ndi amene amatilowetsa m’mayesero. Iye amatikhulupirira kwambiri ndipo amafunitsitsa kutithandiza. Komabe amalemekeza ufulu wathu wosankha ndipo satikakamiza kuti tizimumvera. Choncho amalola kuti tisankhe tokha kumumvera kapena kukopeka ndi mayesero. Kuti tisagonje poyesedwa, tiyenera kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova ndiponso kupemphera mosalekeza. w15 6/15 5:13, 14
Lachiwiri, August 15
Sitikuchita chilichonse chokhumudwitsa, kuti utumiki wathu usapezedwe chifukwa.—2 Akor. 6:3.
Akhristu ayenera kudziphunzitsa kuti azisankha zochita mwanzeru pa nkhani zimene zingasiyanitse anthu. (Aroma 14:19) Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Mirjeta anachokera m’dziko limene linkatchedwa Yugoslavia ndipo anaphunzitsidwa kuti anthu a ku Serbia ndi oipa. Kenako anaphunzira kuti Yehova alibe tsankho koma Satana ndi amene amayambitsa zosankhana mitundu. Zitatero, anayamba kuyesetsa kuti asamakhale ndi tsankho. Koma kenako m’dera limene ankakhala munayambika zipolowe chifukwa cha tsankho. Izi zinachititsa kuti mlongoyu ayambenso kuipidwa ndi anthu a ku Serbia moti zinkamuvuta kwambiri kuti aziwalalikira. Koma iye anazindikira kuti ayenera kuyesetsa kusintha chifukwa tsankho lakelo silikanatha palokha. Iye anapempha Yehova kuti amuthandize kuthetsa vutoli. Mlongoyu anati: “Ndazindikira kuti kuchita khama pa ntchito yolalikira n’kothandiza kwambiri. Ndikakhala mu utumiki ndimayesetsa kuona anthu mmene Yehova amawaonera ndipo izi zandithandiza kuti ndizikonda aliyense.” w15 7/15 3:11-13
Lachitatu, August 16
Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.—2 Mbiri 16:9.
Taganizirani zimene Yehova anachitira Mfumu Yehosafati ya ku Yuda. Pa nthawi ina, Yehosafati anagwirizana ndi Mfumu Ahabu ya ku Isiraeli kuti apitire limodzi ku nkhondo. Aneneri onyenga 400 ananamiza Ahabu kuti akapambana nkhondoyo. Koma mneneri wa Yehova, dzina lake Mikaya, ananena kuti akagonjetsedwa. Ahabu anaphedwa pa nkhondoyo ndipo Yehosafati anapulumukira m’kamwa mwa mbuzi. Yehosafati atabwerera ku Yerusalemu anadzudzulidwa chifukwa chogwirizana ndi mfumu yoipayo. Ngakhale zinali choncho, Yehu mwana wa Haneni anauza Yehosafati kuti: “Pali zinthu zabwino zimene zapezeka mwa inu.” (2 Mbiri 18:4, 5, 18-22, 33, 34; 19:1-3) N’zoona kuti Yehosafati anachita zinthu zosayenera koma Yehova anakumbukirabe zabwino zimene anachita. (2 Mbiri 17:3-10) Nafenso nthawi zina timachita zinthu zosayenera. Koma nkhani ya Yehosafatiyi ikutitsimikizira kuti Yehova adzapitirizabe kutikonda tikamayesetsa ndi mtima wonse kuchita zinthu zomusangalatsa. w15 8/15 1:8, 9
Lachinayi, August 17
Uwalamule kuti azichita zabwino, . . . kuti agwire mwamphamvu moyo weniweniwo.—1 Tim. 6:18, 19.
Kodi tingakonzekere bwanji moyo wa m’dziko latsopano? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tiyerekezere kuti tikufuna kusamukira m’dziko lina. Mwina pokonzekera tingayambe kuphunzira chilankhulo ndi chikhalidwe cha m’dzikolo. Mwina tingayesenso kudya chakudya cha kumeneko. Pokonzekera, tingayesetse kuchita zinthu ngati kuti tasamukira kale m’dzikolo. N’chimodzimodzi ndi moyo wa m’dziko latsopano. Tiyenera kuyamba panopa kukonzekera, poyesetsa kumvera Mulungu komanso kuchita zinthu zimene tizidzachita m’dziko latsopanolo. M’dziko la Satanali, anthu ambiri safuna kuuzidwa zochita ndipo zotsatira zake zimakhala zoipa kwambiri. Kusamvera Mulungu kwayambitsa mavuto osaneneka. (Yer. 10:23) Timalakalaka kwambiri nthawi imene anthu onse azidzamvera Mulungu wathu wachikondi. w15 8/15 3:4, 5
Lachisanu, August 18
Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira, chifukwa ndinu osiyana.—2 Akor. 6:14.
Anthu amene akufuna kukwatira kapena kukwatiwa ayenera kusankha bwino. Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti azikwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye.” Izi zikutanthauza kuti ayenera kukwatirana ndi munthu wobatizidwa amene amatsatira mfundo za m’Baibulo. (1 Akor. 7:39) Mkhristu akatsatira malangizowa amasankha munthu amene angagwirizane naye ndiponso angamuthandize polambira Yehova mokhulupirika. Yehova amadziwa zinthu zimene zingathandize atumiki ake ndipo malangizo amene amapereka pa nkhani ya ukwati sasintha. Kumbukirani zimene analangiza Mose kuti auze Aisiraeli zokhudza anthu a mitundu ina amene sankamulambira. Iye anati: “Usadzachite nawo mgwirizano wa ukwati. . . . Pakuti adzapatutsa ana ako aamuna kuti asanditsatire ndipo adzatumikira ndithu milungu ina.”—Deut. 7:3, 4. w15 8/15 4:12, 13
Loweruka, August 19
Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti, kuti mukhale opanda cholakwa ndi osakhumudwitsa ena.—Afil. 1:10.
Kodi chikumbumtima chathu tingachiphunzitse bwanji? Tiyenera kuphunzira Baibulo nthawi zonse, kuganizira kwambiri zimene timawerenga ndiponso kupempha Yehova kuti atithandize kuzigwiritsa ntchito. Apa n’zoonekeratu kuti pamafunika zambiri osati kungowerenga kuti tidziwe malamulo ndi mfundo zina. Tiyenera kuphunzira n’cholinga choti tidziwe bwino Yehova, makhalidwe ake, zimene amakonda ndiponso zimene amadana nazo. Tikatero chikumbumtima chathu chimayamba kuzindikira mosavuta zimene Yehova amafuna. Pamapeto pake, timayamba kuona zinthu mmene iye amazionera. Komabe ngati sitikumvetsa zimene Mkhristu mnzathu wasankha mogwirizana ndi chikumbumtima chake, tisafulumire kumuweruza kapena kumukakamiza kuti asinthe. N’kutheka kuti akufunikira kuphunzitsabe chikumbumtima chake kapena mwina chikumbumtima chakecho chimamutsutsa pa zinthu zambiri.—1 Akor. 8:11, 12. w15 9/15 2:4, 8, 10
Lamlungu, August 20
Dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.—Sal. 115:16.
Zikuoneka kuti dziko lapansi lokhali ndi limene Mulungu analilenga kuti likhale ndi zinthu zonse zofunika pa moyo. Iye anaonetsetsanso kuti likhale lokongola, losangalatsa ndi lotetezeka. (Yes. 45:18) Umenewutu ndi umboni wakuti Yehova amatikonda kwambiri. (Yobu 38:4, 7; Sal. 8:3-5) Koma Yehova amadziwanso kuti anthufe timafunikira zinthu zina kuti tizikhala osangalala. Mwana amamva bwino akaona kuti makolo ake amamukonda ndiponso kumusamalira. Ndiyeno Yehova analenga anthu m’chifanizo chake. (Gen. 1:27) Choncho timatha kuzindikira kuti iye amatikonda ndiponso ifeyo tikhoza kumukonda. Paja Yesu ananenanso kuti timakhala osangalala tikakhala pa ubwenzi ndi Yehova. (Mat. 5:3) Iye ndi Atate wathu wachikondi ndipo “amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale.”—1 Tim. 6:17; Sal. 145:16. w15 9/15 4:6, 7
Lolemba, August 21
Pali njira yooneka ngati yowongoka kwa munthu, koma mapeto ake ndi imfa.—Miy. 14:12.
Munthu wina amene analemba masalimo ankakonda kwambiri Yehova komanso kumudalira ndipo anati: “Yembekezera Mulungu, ndipo ndidzamutamanda pakuti iye ndiye mpulumutsi wanga wamkulu. Inu Mulungu wanga, ine ndataya mtima. N’chifukwa chake ndakumbukira inu.” (Sal. 42:5, 6) Kodi inunso mumakonda kwambiri ndiponso kudalira Mulungu? N’kutheka kuti mwayankha kuti inde, koma mwina mukhoza kumudalira kwambiri kuposa mmene mumachitira panopa. Paja Baibulo limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.” (Miy. 3:5, 6) Yehova ndi amene anayamba kutikonda ndipo watiphunzitsa mmene tingamusonyezere chikondi. (1 Yoh. 4:19) Tiyeni nthawi zonse tiziganizira chitsanzo chake pa nkhaniyi. Tiziyesetsanso kusonyeza kuti timamukonda ‘ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, maganizo athu onse ndi mphamvu zathu zonse.’—Maliko 12:30. w15 9/15 5:17-19
Lachiwiri, August 22
Ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikira Yehova.—Yos. 24:15.
Tikamagwira ntchito yolalikira timathandiza anthu ena kukhala ndi chikhulupiriro komanso timalimbitsa chikhulupiriro chathu. Mofanana ndi Akhristu oyambirira, tikamalalikira timayamba kukhulupirira kwambiri Yehova ndiponso kulankhula molimba mtima nthawi zonse. (Mac. 4:17-20; 13:46) Chikhulupiriro chathu chimalimba tikaona kuti Yehova akutithandiza ndiponso kuyankha mapemphero athu. Izi n’zimene zinachitikira Kalebe ndi Yoswa. Iwo anakhulupirira kwambiri Yehova pamene anapita kukazonda Dziko Lolonjezedwa. Chikhulupiriro chawo chinapitiriza kulimba ataona kuti Yehova ankawatsogolera pa moyo wawo wonse. M’pake kuti Yoswa anauza Aisiraeli ndi mtima wonse kuti: “Pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe.” Kenako anadzanena kuti: “Tsopano opani Yehova ndi kum’tumikira mosalakwitsa ndiponso mokhulupirika.” (Yos. 23:14; 24:14) Ifenso tikaona mmene Yehova akutithandizira tingayambe kumukhulupirira kwambiri.—Sal. 34:8. w15 10/15 2:10, 11
Lachitatu, August 23
Ezara anakonza mtima wake.—Ezara 7:10.
Ngati mumalemba mfundo zikuluzikulu zimene mumamva pa misonkhano, mungamaziwerenge n’kumaganizira zimene mukuphunzira. Mukhozanso kumaganizira nkhani zopezeka m’magazini atsopano komanso m’mabuku amene timalandira pa msonkhano wachigawo. Mukamawerenga Buku Lapachaka, mungachite bwino kuganizira kaye nkhani imene mwawerengayo. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti mumvetse bwino nkhani zonse zimene mwawerenga komanso kuti zikufikeni pamtima. Mukamawerenga nkhani inayake, muzidula mizere kunsi kwa mfundo zazikulu kapena kulemba notsi zimene mungagwiritse ntchito pa ulendo wobwereza, ulendo waubusa kapena pokamba nkhani. Choncho, tikamaganizira zimene tawerenga, nkhaniyo ingatifike pamtima ndipo tingathokoze Yehova chifukwa cha zimene taphunzirazo. w15 10/15 4:9, 10
Lachinayi, August 24
Yesu anali kukulabe m’nzeru ndi mu msinkhu. Ndipo Mulungu ndi anthu anapitiriza kukondwera naye.—Luka 2:52.
Makolo amasangalala kwambiri mwana wawo akabatizidwa. Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Berenice ali ndi ana 4 ndipo onsewo anabatizidwa asanakwanitse zaka 14. Iye anati: “Tinasangalala kwambiri kuona kuti ana athu akufuna kutumikira Yehova. Koma tinkadziwanso kuti anawo akamakula azikumana ndi mavuto ambiri.” Katswiri wina wodziwa za kaganizidwe ka ana ananena kuti makolo sayenera kuona kuti nthawi imene achinyamata akukula amakhala ovuta kapena achibwana. Ayenera kudziwa kuti nthawi imeneyi amaganiza kwambiri, amafuna kusonyeza kuti ali ndi luso lochita zinthu zina paokha komanso amafunitsitsa kucheza ndi anzawo. Komabe pa nthawiyi, angayambenso kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ngati mmene Yesu anachitira ali wachinyamata. Akhozanso kusankha kudzipereka kwa Yehova ndiponso kumumvera. Angawonjezerenso luso lolalikira n’kumafunitsitsa kuchita zambiri potumikira Mulungu. w15 11/15 2:1, 2
Lachisanu, August 25
Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.—Mat. 6:10.
Ufumu wa Mesiya ndi boma limene Mulungu wakhazikitsa ndipo umasonyezanso kuti iye amatikonda kwambiri. Yehova wasankha Yesu kuti akhale mfumu ndipo m’pomveka chifukwa chakuti Mwana wakeyu amakonda kwambiri anthu ndipo ndi woyeneradi kukhala Mfumu. (Miy. 8:31) Yehova wasankhanso anthu 144,000 kuti akalamulire ndi Yesu kumwamba. Iwo akamaukitsidwa amakumbukira mmene moyo wa anthu umakhalira. (Chiv. 14:1) Yesu ali padzikoli ankaphunzitsa kwambiri za Ufumu umenewu ndipo anauza ophunzira ake kuti azipempha Ufumuwu komanso madalitso amene udzabweretse. Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa mu 1914. Kuchokera nthawi imeneyo, pakhala ntchito yosonkhanitsa anthu ena okalamulira limodzi ndi Yesu komanso a “khamu lalikulu” amene adzapulumuke pa mapeto n’kudzakhala m’dziko latsopano.—Chiv. 7:9, 13, 14. w15 11/15 3:16, 18
Loweruka, August 26
Tamvera, ndikufuna ndikulankhule.—Yobu 42:4.
Mtumwi Yohane ananena za Yesu kuti ndi “Mawu” komanso “woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.” (Yoh. 1:1; Chiv. 3:14) Yehova ankamuuza Yesu maganizo ake ndiponso mmene ankamvera mumtima mwake. (Yoh. 1:14, 17; Akol. 1:15) Komanso nthawi ina mtumwi Paulo ananena za ‘malilime a angelo.’ Pamenepa, ankanena za chilankhulo cha angelo chomwe ndi chapamwamba kuposa cha anthu. (1 Akor. 13:1) Angelo ndiponso anthu, alipo ambirimbiri koma Yehova amawadziwa bwino onsewa. Nthawi iliyonse anthu ambiri amapemphera kwa Yehova m’zilankhulo zosiyanasiyana. Komabe Yehova amatha kumvetsera mapemphero onsewo kwinaku akulankhulanso ndi angelo ake. Mulungu ndi wapamwamba kwambiri kuposa anthu, n’chifukwa chake amakwanitsa kuchita zimenezi. (Yes. 55:8, 9) N’zoona kuti Yehova akhoza kulankhula m’njira yapamwamba kwambiri. Koma akamalankhula ndi anthu amanena zinthu m’njira yosavuta kumva, n’cholinga choti anthuwo amve zimene akufuna. w15 12/15 1:1, 2
Lamlungu, August 27
Dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.—Yes. 11:9.
M’mayiko ambiri, Mabaibulo ndi odula ndiponso osowa. Choncho anthu a m’mayikowo akalandira Baibulo amaona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali. Mwachitsanzo, abale ena a ku Rwanda ananena kuti: “Anthu ambiri amene ankaphunzira Baibulo ndi abale ndi alongo, ankachedwa kusintha zinthu pa moyo wawo. Anthuwa analibe Baibulo chifukwa sakanakwanitsa kugula Mabaibulo a tchalitchi chawo. Komanso ankavutika kumvetsa mavesi ena. Zimenezi zinkachititsa kuti azichedwa kuyamba kutumikira Yehova.” Koma zinthu zinasintha pamene Baibulo la Dziko Latsopano linatuluka m’zilankhulo zawo. Banja lina la ku Rwanda komweko, lomwe lili ndi ana 4 achinyamata linati: “Tikuthokoza kwambiri Yehova ndiponso kapolo wokhulupirika chifukwa chotipatsa Baibuloli. Ndife osauka ndipo sitikanakwanitsa kugulira aliyense Baibulo. Koma panopa aliyense walandira lake. Tsiku lililonse timawerenga Baibulo pamodzi posonyeza kuyamikira zimene Yehova watichitira.” w15 12/15 2:15, 16
Lolemba, August 28
Inu Yehova, ndikomereni mtima. Ndichiritseni, pakuti ndakuchimwirani.—Sal. 41:4.
N’kutheka kuti apa Davide ankanena za zimene anapempha Yehova pamene Abisalomu ankafuna kulanda ufumu wake. Pa nthawiyo, n’kuti akudwala kwambiri moti sakanatha kulimbana ndi mwana wakeyo. Ankadziwa kuti akukumana ndi mavuto amenewa chifukwa cha tchimo limene anachita ndi Bati-seba. (2 Sam. 12:7-14) Davide ankadziwanso kuti Mulungu anamukhululukira ndipo ankakhulupirira kuti amuthandiza pamene akudwala. Koma sikuti ankapempha Mulungu kuti amuchiritse mozizwitsa. Nkhaniyi imasonyeza kuti ankangopempha Mulungu kuti amuthandize ngati mmene Mulunguyo akanathandizira anthu amene amaganizira onyozeka. Iye ankafuna kuti Mulungu azimusamalira pamene “akudwala pabedi lake.” (Sal. 41:3) Popeza Davide anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, anamupempha kuti amulimbikitse komanso kumuthandiza kuti thupi lake lizigwira ntchito bwino kuti achire. (Sal. 103:3) Ifenso tikadwala tingapemphe Yehova kuti atichitire zimenezi. w15 12/15 4:8, 9
Lachiwiri, August 29
Munalandira mzimu wakuti mukhale ana, umene timafuula nawo kuti: “Abba, Atate!”—Aroma 8:15.
Akhristu amene asankhidwa ndi Mulungu safunikira umboni wina wowatsimikizira kuti adzozedwa. Yehova amawathandiza kuti asamakayikire ngakhale pang’ono za zimenezi. Mtumwi Yohane anauza Akhristu odzozedwa kuti: “Munadzozedwa ndi woyerayo, ndipo nonsenu ndinu odziwa choonadi.” Anawonjezeranso kuti: “Mulungu anakudzozani ndi mzimu ndipo mzimu umenewo udakali mwa inu. Chotero simukufunikira wina aliyense kuti azikuphunzitsani, koma popeza kuti munadzozedwadi moona osati monama, chifukwa cha kudzozedwako, mukuphunzitsidwa zinthu zonse. Monga mmene mwaphunzitsidwira, pitirizani kukhala ogwirizana naye.” (1 Yoh. 2:20, 27) N’zoona kuti odzozedwa amafunikira kuphunzitsidwa mfundo za m’Baibulo ngati mmene zilili ndi Akhristu ena onse. Koma safunikira kuti munthu wina awatsimikizire zoti adzozedwa. Zili choncho chifukwa mzimu wa Mulungu umawathandiza kudziwa zimenezi. w16.01 3:9, 10
Lachitatu, August 30
Mukhale okhutira ndi zimene muli nazo.—Aheberi 13:5.
Tikamakhulupirira kwambiri Yehova, timaona zinthu moyenera ndipo timakhutira ndi zimene tili nazo. (1 Tim. 6:6-8) Timazindikiranso kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ndiponso kugwirizana ndi abale ndi alongo athu ndi kofunika kwambiri kuposa chilichonse. Munthu amene ndi wansanje, wadyera, wokonda kudandaula komanso kupezera ena zifukwa zimamuvuta kuti azikondana ndi abale ake. Koma munthu wokhutira ndi zimene ali nazo sachita zimenezi ndipo amakonda kugawana zinthu ndi ena. (1 Tim. 6:17-19) Komanso tikamakhulupirira Yehova timachita zinthu molimba mtima tikakumana ndi mavuto. (Aheb. 13:6) Izi zimatithandiza kuti tiziona zinthu moyenera, tizikonda abale athu komanso tiziwalimbikitsa. (1 Ates. 5:14, 15) Ngakhale pa nthawi ya chisautso chachikulu, tidzatha ‘kuimirira chilili ndi kutukula mitu yathu’ podziwa kuti Yehova atipulumutsa.—Luka 21:25-28. w16.01 1:16, 17
Lachinayi, August 31
Yehova amadziwa anthu ake.—2 Tim. 2:19.
Kwa zaka zambiri m’mbuyomu, chiwerengero cha anthu amene ankadya zizindikiro pa Chikumbutso chinkatsika. Koma pa zaka zingapo zapitazi, taona kuti chiwerengerochi chayambanso kukwera. Kodi tiyenera kudandaula ndi zimenezi? Ayi. Tiyeni tione zifukwa zake zina. Abale amene amawerenga anthu omwe adya zizindikiro pa Chikumbutso, sangadziwe amene ndi wodzozedwadi. Pa gulu la anthu amene adya zizindikirowo pamakhalanso ena amene sayenera kudya. Ena amene amadya zizindikiro, pakapita nthawi amasiya. Palinso ena amene saganiza bwino chifukwa cha matenda ndipo amadya zizindikiro poganiza kuti adzozedwa. Choncho sitikudziwa chiwerengero cholondola cha odzozedwa enieni amene atsala padzikoli. Komanso Baibulo silinena kuti padzikoli padzakhala odzozedwa angati chisautso chachikulu chikamadzayamba. w16.01 4:12-14