Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es17 tsamba 88-97
  • September

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • September
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
  • Timitu
  • Lachisanu, September 1
  • Loweruka, September 2
  • Lamlungu, September 3
  • Lolemba, September 4
  • Lachiwiri, September 5
  • Lachitatu, September 6
  • Lachinayi, September 7
  • Lachisanu, September 8
  • Loweruka, September 9
  • Lamlungu, September 10
  • Lolemba, September 11
  • Lachiwiri, September 12
  • Lachitatu, September 13
  • Lachinayi, September 14
  • Lachisanu, September 15
  • Loweruka, September 16
  • Lamlungu, September 17
  • Lolemba, September 18
  • Lachiwiri, September 19
  • Lachitatu, September 20
  • Lachinayi, September 21
  • Lachisanu, September 22
  • Loweruka, September 23
  • Lamlungu, September 24
  • Lolemba, September 25
  • Lachiwiri, September 26
  • Lachitatu, September 27
  • Lachinayi, September 28
  • Lachisanu, September 29
  • Loweruka, September 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
es17 tsamba 88-97

September

Lachisanu, September 1

[Abulahamu] ananyamuka ulendo wopita kumalo amene Mulungu woona anamuuza.​—Gen. 22:3.

Abulahamu anauza antchito ake amene anayenda nawo kuti: “Inu tsalani pano ndi buluyu, ine ndi mwana wangayu tikupita uko kukalambira, tikupezani.” (Gen. 22:5) Kodi apa Abulahamu ankatanthauza chiyani? Kodi ankanamiza antchito akewo kuti Isaki abweranso, pomwe ankadziwa kuti akukamupereka nsembe? Ayi, Baibulo limatithandiza kudziwa zimene Abulahamu ankaganiza. (Aheberi 11:19.) Iye “anadziwa kuti Mulungu ali ndi mphamvu zomuukitsa [Isaki] kwa akufa.” Izi zikusonyeza kuti Abulahamu ankakhulupirira kuti akufa adzaukitsidwa. Paja Yehova anachititsa kuti iyeyo ndi Sara abereke mwana ngakhale kuti anali atakalamba kwambiri. (Aheb. 11:11, 12, 18) Abulahamu ankadziwa kuti palibe zimene Yehova sangakwanitse kuchita. Choncho sankakayikira kuti ngakhale atapereka mwana wakeyo nsembe, Yehova amuukitsa kuti akwaniritse zonse zimene analonjeza. N’chifukwa chake Abulahamu anatchedwa ‘tate wa onse okhala ndi chikhulupiriro.’​—Aroma 4:11. w16.02 1:3, 13

Loweruka, September 2

Chifukwa cha dzina lake lalikulu, Yehova sadzasiya anthu ake.​—1 Sam. 12:22.

Sauli anali mfumu yosankhidwa ndi Mulungu. Koma pa nthawi ina anayamba kuchita zinthu zosakhulupirika ndipo Yehova sankasangalalanso naye. (1 Sam. 15:17-23) Komabe Yehova sanamuchotse pampando nthawi yomweyi. Choncho pa nthawiyi Aisiraeli ankavutika kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu chifukwa munthu amene anali “pampando wachifumu wa Yehova,” ankachita zoipa. (1 Mbiri 29:23) Koma Yonatani anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Nafenso tingasonyeze kuti ndife okhulupirika kwa Yehova tikamamvera akuluakulu a boma pa zinthu zoyenera. Tingachite zimenezi ngakhale kuti nthawi zina sachita zabwino. Mwachitsanzo, olamulira akhoza kukhala achinyengo, koma tiyenera kuwalemekezabe chifukwa Yehova amafuna kuti tizichita zimenezi. (Aroma 13:1, 2) Komanso timasonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova tikamamvera anthu amene Yehova wawapatsa udindo.​—1 Akor. 11:3; Aheb. 13:17. w16.02 3:5, 6, 8

Lamlungu, September 3

Anthu ako adzadzipereka mofunitsitsa.​—Sal. 110:3.

Baibulo limati anthu a Mulungu, ngakhale achinyamata, “adzadzipereka mofunitsitsa” kuti amutumikire. Choncho munthu amene akuganiza zobatizidwa ayenera kutsimikizira kuti akufunadi ndi mtima wonse kubatizidwa. Munthuyo ayenera kudzifufuza bwinobwino kuti adziwe zimenezi. Kudzifufuza n’kofunika makamaka kwa achinyamata amene anakulira m’banja la Mboni. N’kutheka kuti mwaona anzanu kapena achibale anu akubatizidwa. Komabe muyenera kusamala kuti musaganize kuti muyenera kubatizidwa chifukwa choti mwakwanitsa zaka zinazake kapena chifukwa choti anzanu onse akubatizidwa. Ndiye kodi mungatani kuti mukhale ndi maganizo oyenera pa nkhani imeneyi? Muyenera kuganizira kwambiri chifukwa chake munthu amabatizidwa. w16.03 1:11, 12

Lolemba, September 4

Aliyense wakumva anene kuti: “Bwera!” Aliyense wakumva ludzu abwere. Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere.​—Chiv. 22:17.

Akhristufe tili ndi ntchito yaikulu yolalikira “uthenga wabwino” padziko lonse mapeto asanafike. Koma kuti zimenezi zitheke, tiyenera kugwira ntchitoyi mogwirizana. (Aef. 4:16) Kuti tithe kulalikira anthu ambiri, tiyenera kugwira ntchito yathuyi mwadongosolo. N’chifukwa chake gulu limatipatsa malangizo kudzera kumpingo. Malangizowa amathandiza kuti anthu a Mulungu padziko lonse azigwira ntchitoyi mogwirizana. Msonkhano wokonzekera utumiki ukatha, timapita kukalalikira uthenga wa Ufumu kwa anthu a mitundu yonse. Timathandiza anthu kuti amve uthengawu polankhula nawo komanso powapatsa mabuku athu. Kodi inuyo mumagwira nawo ntchito yapadera yoitanira anthu kumsonkhano, ku Chikumbutso kapena yowauza anthu uthenga winawake? Mukamachita zimenezi, mumakhala kuti mukugwirizana ndi abale ndi alongo padziko lonse pogwira ntchito yolalikira uthenga umenenso angelo amalengeza.​—Chiv. 14:6. w16.03 3:4, 5

Lachiwiri, September 5

Mipukutu inafunyululidwa.​—Chiv. 20:12.

Baibulo limati m’dziko latsopano Yehova adzatipatsa malangizo kudzera m’mipukutu. M’mipukutuyi muyenera kuti mudzakhala zimene Yehova adzafune kuti anthu onse, kuphatikizapo oukitsidwa, azidzachita pa nthawiyo. Mipukutu imeneyi idzatithandizanso kuti tidzamudziwe bwino Yehova. Komanso tidzamvetsa bwino zimene Mawu a Mulungu amanena ndipo zimenezi zidzathandiza kuti tizidzakondana komanso kulemekezana kwambiri m’Paradaiso. (Yes. 26:9) Nthawi imeneyo tidzaphunzira zinthu zambiri motsogoleredwa ndi Mfumu yathu, Yesu Khristu. Tikadzamvera ‘zolembedwa m’mipukutu’ n’kukhalabe okhulupirika pa mayesero omaliza, Yehova adzalemba mayina athu ‘mumpukutu wa moyo’ ndipo sadzachotsedwamonso. Zimenezi zikusonyeza kuti adzatipatsa moyo wosatha. w16.03 4:19, 20

Lachitatu, September 6

Chiyembekezo changa ndinu, Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, ndimadalira inu kuyambira pa unyamata wanga.​—Sal. 71:5.

Akulu ena omwe amakonda kuphunzitsa ena anafotokoza kuti m’pofunika kuyamba kuphunzitsa achinyamata adakali aang’ono. Ndi bwino kuwapatsa ntchito zina mumpingo zogwirizana ndi msinkhu wawo. Kuphunzitsa achinyamatawa kungawathandize kukhala ndi zolinga isanafike nthawi yomwe angasokonezedwe ndi zinthu zina. (Sal. 71:17) Akulu angathandizenso wachinyamata kuti azifuna kutumikira mu mpingo, akamamuuza zoyenera kuchita ndiponso zifukwa zake. Mukamufotokozera chifukwa chogwirira ntchitoyo, mumasonyeza kuti mukutsanzira Yesu. Mwachitsanzo, Yesu asanauze ophunzira ake ntchito yoti agwire, anawauza chifukwa chake ayenera kumvera. Iye anati: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” Kenako ananena kuti: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse.”​—Mat. 28:18, 19. w15 4/15 2:5, 6

Lachinayi, September 7

Ambuye anaima pafupi ndi ine ndi kundipatsa mphamvu . . . Ndiponso ndinapulumutsidwa m’kamwa mwa mkango.​—2 Tim. 4:17.

Ku Roma, zinali zoopsa kwambiri munthu akangodziwika kuti ndi Mkhristu. Akhristu ananamiziridwa kuti awotcha mzinda wa Roma mu 64 C.E. Pa nthawiyi, Akhristu ankazunzidwa koopsa. Imeneyi ndi nthawi yomwe mtumwi Paulo anamangidwa kachiwiri ku Roma. Kodi zikanatheka kuti Akhristu anzake amupulumutse? Mwina mtumwi Paulo ankaona kuti palibe amene angamuthandize popeza analembera Timoteyo kuti: “Pamene ndinali kudziteteza koyamba pa mlandu wanga, palibe amene anakhala kumbali yanga. Onse anandisiya ndekha.” (2 Tim. 4:16) Komabe iye anazindikira kuti akhoza kupeza thandizo. Ankakhulupirira kuti Yehova amuthandiza kupirira mayesero alionse. N’chifukwa chake anapitiriza kulemba kuti: “Ambuye adzandipulumutsa ku choipa chilichonse.” (2 Tim. 4:18) Apatu zikuonetseratu kuti Paulo anazindikira kuti Yehova ndi Yesu amatithandiza pamene tikuona kuti palibiretu mtengo wogwira. w15 4/15 4:1-3

Lachisanu, September 8

Idzaphwanya mutu wako.​—Gen. 3:15.

Pamene Yesu ankabadwa, Satana ankadziwa kuti mwanayu adzakhala Mesiya. Kodi Satana akanaganiza kuti kupha mwanayo ikanakhala nkhanza? Ayi. Iye sadandaula akachita zoipa moti mwamsanga anayamba mapulani ofuna kumupha. Ndiye kodi chinachitika n’chiyani? Mfumu Herode anakwiya koopsa pamene okhulupirira nyenyezi anamuuza kuti akufuna kuona “mfumu ya Ayuda imene yabadwa.” (Mat. 2:1-3, 13) Iye anakonza zoti aphe ana onse aamuna osapitirira zaka ziwiri ku Betelehemu ndi madera ena. (Mat. 2:13-18) Yesu anapulumuka chiwembuchi. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti Satana ndi wotani? N’zoonekeratu kuti Satana salemekeza moyo wa munthu ndipo samvera chisoni ana. Iye ndi “mkango wobangula” ndipo tiyenera kusamala naye.​—1 Pet. 5:8. w15 5/15 1:10, 12, 13

Loweruka, September 9

Sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezowo. Koma anawaona ali patali.​—Aheb. 11:13.

Yehova anatilenga ndi luso loona m’maganizo mwathu zinthu zimene sitinazione. Zimenezi zimatithandiza kuchita zinthu mwanzeru komanso kuyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo. Yehova amadziwa zomwe zidzachitike ndipo Baibulo limatithandiza kudziwa zam’tsogolo. Choncho timatha kuona zinthuzo m’maganizo mwathu n’kumakhulupirira kuti zidzachitikadi. (2 Akor. 4:18) Nthawi ina Hana ankaganizira zinthu zenizeni zimene zingachitike atapereka mwana wake Samueli kuti azikatumikira pachihema. Kuganizira kwambiri zimenezi kunamuthandiza kuti asasinthe maganizo. (1 Sam. 1:22) Tikamaona m’maganizo mwathu zimene Mulungu walonjeza ndiye kuti tikuganizira zinthu zimene zidzachitikadi. (2 Pet. 1:19-21) N’zosakayikitsa kuti atumiki akale a Yehova ankaona m’maganizo mwawo zimene Mulungu anawalonjeza. w15 5/15 3:1-3

Lamlungu, September 10

Zinthu zamtengo wapatali za munthu wachuma . . . m’maganizo mwake zili ngati mpanda woteteza.​—Miy. 18:11.

Anthu ena amaganiza kuti akhoza kusangalala ngati atasiya kutumikira Yehova mwakhama n’kupeza chuma chambiri. Yesu anapereka fanizo la ‘munthu amene anadziunjikira yekha chuma, koma amene sanali wolemera kwa Mulungu.’ (Luka 12:16-21) Zimene munthuyo anachita sizinamuthere bwino. Koma tikaunjika ‘chuma kumwamba’ n’kumachita zimene Yehova amafuna, iye amasangalala ndipo ifenso timakhala osangalala. (Mat. 6:20; Miy. 27:11) Ubwenzi wathu ndi Yehova uli ngati chuma choposa chuma chilichonse padzikoli. Taganizirani za nkhawa imene tingakhale nayo ngati tikufunitsitsa “kudziunjikira chuma padziko lapansi.” (Mat. 6:19) Yesu anapereka fanizo posonyeza kuti “nkhawa za moyo wa m’nthawi ino ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma” zingatilepheretse kutumikira Mulungu.​—Mat. 13:18, 19, 22. w15 5/15 4:15, 16

Lolemba, September 11

Khamu la anthulo linadabwa kuona osalankhula akulankhula, olumala akuyenda ndiponso akhungu akuona.​—Mat. 15:31.

Yesu anatha kuchita zodabwitsa zambirimbiri chifukwa cha mphamvu yochokera kwa Mulungu. Sikuti anachiritsa akhate okha. Anachiritsa anthu odwala matenda alionse komanso olumala. Yesu ankachiritsa anthu onsewa popanda kupempha anthu abwinobwino kuti apereke ziwalo kwa odwalawo. Anthuwo ankachira nthawi yomweyo ndipo ena ankawachiritsa ali kutali. (Yoh. 4:46-54) Kodi zodabwitsa zimene Yesu anachitazi zikusonyeza chiyani? Zikusonyeza kuti Yesu, yemwe akulamulira kumwamba, ali ndi mphamvu zochiritsa komanso mtima wofuna kuchita zimenezi. Tikaganizira zimene Yesu ankachitira anthu sitikayikira kuti m’dziko latsopano lemba la Salimo 72:13 lidzakwaniritsidwa. Paja lembali limati: “[Yesu] adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka.” Yesu adzachiritsadi anthu onse ovutika chifukwa chakuti ali ndi mtima wofuna kuwathandiza. w15 6/15 2:6

Lachiwiri, September 12

Dzina lanu liyeretsedwe.​—Mat. 6:9.

Anthu ambiri amadziwa bwino mawu a m’pemphero la Ambuye. Tikamalalikira timakonda kugwiritsa ntchito pempheroli pothandiza anthu kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma limene lidzathetse mavuto padzikoli. Nthawi zina timagwiritsa ntchito pempheroli pothandiza anthu kudziwa kuti Mulungu ali ndi dzina ndipo liyenera kuyeretsedwa. (Mat. 6:9) Kodi Yesu ankatanthauza kuti tiyenera kuloweza pempheroli n’kumatchula mawu ake ndendende tikamapemphera? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti asananene pempheroli ananena kuti: “Iwe popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza.” (Mat. 6:7) Pa nthawi ina, ananenanso pempheroli koma anasintha mawu ena. (Luka 11:1-4) Choncho Yesu ankangofuna kutithandiza kudziwa zimene tingatchule m’pemphero. M’pake kuti pempheroli limatchedwanso kuti pemphero lachitsanzo. w15 6/15 4:1, 2

Lachitatu, September 13

Amene akuyesa kuti ali chilili asamale kuti asagwe.​—1 Akor. 10:12.

Yehova amatipatsa mphamvu ya mzimu woyera kuti itithandize kupewa mayesero. Iye amagwiritsanso ntchito Mawu ake ndiponso mpingo potichenjeza. Mwachitsanzo, amanena kuti tiyenera kupewa kugwiritsa ntchito nthawi, ndalama kapena mphamvu zathu pofufuza chuma kapena zinthu zosafunika kwenikweni. M’bale wina dzina lake Espen ndi mkazi wake Janne kale ankachita upainiya koma panopa ali ndi ana awiri. M’baleyo anati: “Popeza sitingachite zambiri mu utumiki, timapempha Yehova kuti azitithandiza kuti tisalowe m’mayesero. Timapempha kuti atithandize kukhalabe naye pa ubwenzi wolimba komanso kuti tizichita khama mu utumiki.” Kuonera zolaula ndi vuto lina limene lafika poipa masiku ano. Ena amayamba kuonera zolaulazi chifukwa chakuti sadziletsa akayamba kuganizira zinthu zoipa. Koma pali abale ndi alongo ambirimbiri amene amapeweratu zimenezi ndipo inunso mukhoza kukwanitsa.​—1 Akor. 10:13. w15 6/15 5:15, 16

Lachinayi, September 14

Mafumu a dziko lapansi, nduna, akuluakulu a asilikali, olemera, amphamvu, kapolo aliyense ndi mfulu aliyense, anabisala m’mapanga ndi m’matanthwe a m’mapiri.​—Chiv. 6:15.

Kodi chidzachitike n’chiyani pambuyo poti zipembedzo zonyenga zawonongedwa? Uwu udzakhala mpata woti aliyense asonyeze zimene zili mumtima mwake. Anthu ambiri adzafuna kuti atetezedwe ndi mabungwe a m’dzikoli omwe ali ngati ‘matanthwe a m’mapiri.’ Koma anthu a Yehova adzathawira kumalo achitetezo ophiphiritsa amene Yehova adzawakonzere. Pamene chisautso chinaimitsidwa mu 66 C.E. sinali nthawi yoti Ayuda onse alowe Chikhristu. Koma inali nthawi yoti Akhristu achite zinthu mogwirizana ndi malangizo amene anapatsidwa. Ndi mmene zidzakhalirenso masiku a chisautso chachikulu akadzafupikitsidwa. Sikuti anthu ambiri adzayamba kutumikira Yehova. Koma udzakhala mpata woti Akhristu asonyeze kuti amakonda Yehova ndiponso athandize abale a Khristu.​—Mat. 25:34-40. w15 7/15 2:7

Lachisanu, September 15

Zili bwino ngati wina, chifukwa cha chikumbumtima chake kwa Mulungu, akupirira zowawa ndi kuvutika popanda mlandu.​—1 Pet. 2:19.

Kodi inuyo mumavutika ndi mtima wa tsankho chifukwa cha kumene munakulira? Kapena kodi mumakonda kwambiri dziko kapena dera lanu? Akhristu sayenera kulola zinthu ngati zimenezi kuti zisokoneze mgwirizano wawo ndi anthu ena. Ndiyeno kodi mungatani ngati mukuona kuti muli ndi kamtima koipidwa ndi anthu amene mukusiyana nawo mayiko, chikhalidwe, chilankhulo kapena mtundu? Ndi bwino kuganizira mmene Yehova amaonera nkhani ya tsankho kapena yokonda kwambiri dziko linalake. Mwina mungafufuze nkhani zimenezi m’mabuku athu n’kumaziphunzira. Ndiyeno muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala ndi maganizo ake pa nkhaniyi. (Aroma 12:2) Tikutero chifukwa chakuti mtumiki wa Yehova aliyense ayenera kudziwa kuti nthawi zina anthu ena angafune kuti iye achite zinthu zosemphana ndi zimene amakhulupirira. Izi zikhoza kuchitika kuntchito, kusukulu, kunyumba kapena kwina kulikonse. Zikatero sitiyenera kuopa kuchita zinthu zosiyana ndi ena. w15 7/15 3:14, 15

Loweruka, September 16

Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wake, ali m’mimba mwa chinsomba.​—Yona 2:1.

Yehova amamvetsera tikamamuuza mavuto athu. Iye amatimvetsa ngakhale pamene zikuoneka kuti palibe munthu aliyense amene akumvetsa mavuto athuwo. Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amatikonda kwambiri. Tingaphunzire zambiri pa mapemphero amene analembedwa m’Baibulo. Choncho nthawi zina tingachite bwino kukambirana mapempherowa pa Kulambira kwa Pabanja. Kuganizira zimene atumiki akale ananena pouza Yehova za mumtima mwawo, kungathandize kuti mapemphero athu akhale abwino. Mwachitsanzo, mungakambirane zimene Yona ananena pochonderera Yehova ali m’mimba mwa chinsomba. (Yona 1:17; 2:1-10) Kapena mungakambiranenso pemphero lochokera pansi pa mtima limene Solomo anapereka potsegulira kachisi. (1 Maf. 8:22-53) Mungaganizirenso zinthu zothandiza zimene Yesu ananena m’pemphero lachitsanzo. (Mat. 6:9-13) Koma chofunika kwambiri n’chakuti “zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”​—Afil. 4:6, 7. w15 8/15 1:11, 12

Lamlungu, September 17

Muziwagonjera.​—Aheb. 13:17.

Zidzakhala zosangalatsa pamene Yehova azidzatitsogolera kuti tikongoletse dzikoli, tiphunzitse anthu oukitsidwa komanso tithandize pokwaniritsa cholinga chake. Koma kodi pa nthawiyo tidzalolera kugwira ntchito imene sitisangalatsa? Kodi tidzagonjera n’kumaigwira mosangalala? Mwina tayankha kale kuti, inde. Koma funso ndi lakuti, kodi panopa tayamba kale kugonjera malangizo amene gulu la Yehova limapereka? Ngati timatero, ndiye kuti tikukonzekera moyo wa m’dziko latsopano. Tingakonzekerenso moyo wa m’dziko latsopano poyesetsa kukhala ndi mtima womvera ndiponso wokhutira ndi zimene tili nazo. Ngati masiku ano timamvera amene akutitsogolera n’kumagwira mosangalala ntchito zatsopano zimene tapatsidwa, ndiye kuti tidzateronso m’dziko latsopano. w15 8/15 3:6, 7

Lolemba, September 18

Akazi ake [osalambira Yehova] anali atapotoza mtima wake moti iye anali kutsatira milungu ina. . . . Chotero Solomo anayamba kuchita zinthu zimene zinali zoipa m’maso mwa Yehova.​—1 Maf. 11:4, 6.

Akazi a Solomo osalambira Yehova anamuchititsa kuti ayambe kuchita zinthu mopanda nzeru n’kusiya kutumikira Mulungu mokhulupirika. (1 Maf. 11:1-6) Choncho Akhristu amene akufuna kukwatirana ndi munthu wosalambira Yehova ayenera kuiganizira bwino nkhaniyi. Koma bwanji ngati munthu wayamba kutumikira Yehova atakwatirana kale ndi munthu wosalambira Yehova? Baibulo limati: “Inu akazi, muzigonjera amuna anu kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu.” (1 Pet. 3:1) N’zoona kuti malangizowa ndi opita kwa akazi koma amathandizanso mwamuna amene wayamba kutumikira Yehova atakwatira kale mkazi wosalambira Yehova. Apa mfundo ndi yakuti tiziyesetsa kukhala mwamuna kapena mkazi wabwino n’kumatsatira malangizo a Mulungu onena za ukwati. Pali anthu ambiri amene ayamba kutumikira Yehova ataona kuti mwamuna kapena mkazi wawo wayamba kuchita bwino chifukwa chotsatira mfundo za m’Malemba. w15 8/15 4:15, 16

Lachiwiri, September 19

Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.​—Miy. 14:15.

Pali matenda ena amene alibe mankhwala. Choncho tiyenera kusamala tikamva ena akuchemerera mankhwala enaake koma alibe umboni woti ndi othandizadi. Paulo analemba kuti: “Tikhalebe oganiza bwino.” (1 Ates. 5:6) Kuganiza bwino kungatithandizenso kuti tisamangoganizira za thanzi lathu mpaka kufika poiwala zinthu zina zokhudza kulambira. Tikayamba kuganizira kwambiri za thanzi lathu tikhoza kusiyanso kuganizira zofuna za ena. (Afil. 2:4) Tisamaiwale kuti m’dzikoli sitingapeweretu matenda. Tizikumbukiranso kuti kutumikira Yehova n’kofunika kwambiri kuposa chinthu china chilichonse. (Afilipi 1:10) Pa nkhani ngati za mankhwala aliyense ayenera kusankha yekha zochita kuti patsogolo asadzaimbe mlandu anthu ena. w15 9/15 2:8, 10

Lachitatu, September 20

Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu. Zimenezi zinditsogolere.​—Sal. 43:3.

Yehova ndi “Mulungu wachoonadi.” (Sal. 31:5) Iye amatikonda kwambiri ndipo amasangalala kutitsogolera pomulambira ndiponso pa moyo wathu wonse. Kodi Yehova wasonyeza kuti amatikonda potiphunzitsa zinthu ziti? Choyamba, Yehova watithandiza kuti timudziwe bwino. Mwachitsanzo, watiuza dzina lake lomwe limapezeka m’Baibulo m’malo ambiri kuposa dzina lina lililonse. Izi zimasonyeza kuti akufunitsitsa kukhala nafe pa ubwenzi. (Yak. 4:8) Iye amatithandizanso kudziwa makhalidwe ake. Mwachitsanzo, tikamayang’ana chilengedwe timaona kuti Yehova ndi wamphamvu komanso wanzeru. (Aroma 1:20) Baibulo limasonyezanso kuti iye ndi wachilungamo ndiponso wachikondi. Mulungu ali ngati bambo wamphamvu, wanzeru, wachilungamo ndiponso wachikondi. Choncho n’zosavuta kukhala naye pa ubwenzi. w15 9/15 4:8, 9

Lachinayi, September 21

Dzanja la Yehova lidzadziwika kwa atumiki ake.​—Yes. 66:14.

Anthu ambiri amaganiza kuti Mulungu saona zimene iwo amachita. Ena amakhulupirira kuti Mulungu alibe nazo ntchito zimene zikutichitikira. Mwachitsanzo, mu November 2013 mphepo yamkuntho itawononga zinthu zambiri mumzinda wina waukulu m’dziko la Philippines, meya wa mzindawu anati: “Zikuoneka kuti Mulungu kunalibe pa nthawi ya ngoziyi.” Palinso anthu ena amene amachita zinthu ngati kuti Mulungu sakuwaona. (Yes. 26:10, 11; 3 Yoh. 11) Iwo ali ngati anthu amene mtumwi Paulo anawafotokoza ponena kuti: ‘Sanafune kumudziwa Mulungu molondola.’ Anthuwo “anadzazidwa ndi zosalungama zonse, kuipa konse, kusirira konse kwa nsanje, ndi uchimo wonse.” (Aroma 1:28, 29) Mosiyana ndi anthu amenewa, ifeyo timadziwa kuti Yehova amaona zonse zimene timachita. Koma tingachite bwino kudzifunsa kuti, Kodi ndimaona kuti Yehova amandiganizira ineyo? w15 10/15 1:1-3

Lachisanu, September 22

Ine ndikuonetsa chikhulupiriro changa mwa ntchito.​—Yak. 2:18.

Kulalikira ndi njira imodzi imene tingasonyezere kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba. Munthu amene amagwira ntchito imeneyi amakhulupirira kuti Mulungu adzawononga dziko loipali pa nthawi yake ndipo “sadzachedwa.” (Hab. 2:3) Choncho kuti tidziwe ngati chikhulupiriro chathu n’cholimba kapena ayi tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri? Kodi ndikuchita zonse zimene ndingathe pa ntchitoyi? Kodi ndimayesetsa kupeza njira zowonjezera zimene ndimachita mu utumiki?’ (2 Akor. 13:5) ‘Tikamalengeza poyera chikhulupiriro chathu kuti tipulumuke’ timasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba. (Aroma 10:10) Timasonyezanso kuti tili ndi chikhulupiriro tikamapirira mavuto a m’dzikoli. Kaya tili ndi mavuto monga matenda, nkhawa kapena umphawi, tiyenera kukhulupirira kuti Yehova ndi Yesu adzatithandiza pa nthawi yoyenera. (Aheb. 4:16) Tingasonyeze kuti timakhulupirira Yehova tikamapemphera kuti azitithandiza. w15 10/15 2:12-14

Loweruka, September 23

Mzimu woyera. . . udzakukukumbutsani zonse zimene ndinakuuzani.​—Yoh. 14:26.

Ngati taletsedwa kukhala ndi Baibulo, tikhoza kuganizira malemba amene tikuwakumbukira kapena nyimbo za Ufumu zimene tinaloweza. (Mac. 16:25) Mzimu woyera ungatithandize kuti tizikumbukira zinthu zabwino zimene tinaphunzira. Tingasankhe masiku ena pa mlungu kuti tiziwerenga Baibulo motsatira ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Koma masiku ena tingamawerenge mabuku monga Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane n’kumaganizira zimene Yesu ankaphunzitsa ndi kuchita. (Aroma 10:17; Aheb. 12:2; 1 Pet. 2:21) Tilinso ndi buku limene limafotokoza mwatsatanetsatane zimene Yesu anachita ali padzikoli. Bukuli lingatithandize kuti tizimvetsa bwino nkhani zimene zinalembedwa m’mabuku a m’Baibulo onena za Yesu.​—Yoh. 14:6. w15 10/15 4:11, 12

Lamlungu, September 24

Ndakutchani mabwenzi, chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.​—Yoh. 15:15.

Atumwi ankaona kuti Yesu anali Ambuye wawo komanso mnzawo wapamtima. Kale, nthawi zambiri munthu sankauza akapolo ake zakukhosi kwake. Koma Yesu ankakonda ophunzira ake ndipo ankacheza nawo. Iye ankawauza maganizo ake ndiponso mmene akumvera mumtima mwake. Ankamvetseranso ophunzirawo akamamufotokozera zimene akuganiza komanso mmene akumvera. (Maliko 6:30-32) Izi zinathandiza kuti Yesu azigwirizana kwambiri ndi atumwiwo komanso kuti iwo akhale okonzeka kudzagwira ntchito yomwe anadzapatsidwa. Yesu ankakonda kwambiri ophunzira ake ndipo ankafuna kuti iwo azisangalala potumikira Yehova mwakhama. Choncho ankawalimbikitsa kuti azikonda kwambiri ntchito yolalikira ndipo anawauza kuti adzawathandiza.​—Mat. 28:19, 20. w15 11/15 2:3, 5

Lolemba, September 25

Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.​—Mat. 22:39.

Chikondi ndi khalidwe lalikulu kwambiri la Yehova Mulungu. (1 Yoh. 4:16) Poyamba, iye analenga Yesu ndipo anakhala naye kumwamba kwa zaka zosawerengeka. Kumwambako, Yesu anaphunzira makhalidwe a Mulungu monga chikondi. (Akol. 1:15) Ndiyeno pa moyo wake wonse kumwamba ndiponso padzikoli, iye wakhala akutsanzira Yehova posonyeza chikondi. Choncho sitikukayikira kuti ulamuliro wa Yehova ndi Yesu udzakhalabe wachikondi mpaka kalekale. Munthu wina atafunsa Yesu za lamulo lalikulu kwambiri, iye anayankha kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba. Lachiwiri lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’” (Mat. 22:37-39) Yesu ananena kuti tiyenera kukonda kwambiri Yehova ndi anzathu. Izi zikusonyeza kuti chikondi n’chofunika kwambiri. w15 11/15 4:1-3

Lachiwiri, September 26

Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.​—Aroma 15:4.

Yehova anayamba kulankhula ndi anthu m’zilankhulo zinanso kuwonjezera pa Chiheberi. Anthu a Mulungu atachoka ku ukapolo wa ku Babulo, ena ankalankhula Chiaramu. Mwina n’chifukwa chake Mulungu anachititsa kuti Danieli, Yeremiya komanso Ezara alembe mbali zina za mabuku awo m’Chiaramu. Alekizanda Wamkulu atayamba kulamulira m’madera ambiri, anthu a m’maderawo anayamba kulankhula Chigiriki. Ayuda ambiri anayambanso kulankhula chilankhulochi ndipo izi zinachititsa kuti Malemba Achiheberi amasuliridwe m’Chigiriki. Baibulo limene linamasuliridwa m’Chigirikili (Septuagint) linali loyamba kumasuliridwa kuchokera m’Malemba oyambirira. Pomasulira Baibuloli, ena ankamasulira liwu ndi liwu pomwe ena ankangomasulira mfundo za m’malembawo. Ayuda komanso Akhristu amene ankalankhula Chigiriki ankalemekeza Baibuloli ndipo ankaliona kuti ndi Mawu a Mulungu. w15 12/15 1:4-6

Lachitatu, September 27

Tangoganizani mmene kamoto kakang’onong’ono kamayatsira nkhalango yaikulu.​—Yak. 3:5.

Lemba la Yakobo 3:6 limati: “Lilimenso ndi moto.” Apa lilime likuimira zimene timalankhula. Mofanana ndi moto, zimene timalankhula zikhoza kuyambitsa mavuto aakulu. Paja Baibulo limanenanso kuti: “Imfa ndiponso moyo zili mu mphamvu ya lilime.” (Miy. 18:21) Koma sitisiya kugwiritsa ntchito moto chifukwa choopa kuwotcha zinthu. Choncho sitiyeneranso kusiyiratu kulankhula poopa kuti tingalankhule zinthu zolakwika. Chofunika ndi kukhala osamala. Moto tikamaugwiritsa ntchito mosamala, tikhoza kuphikira, kuwotha ndiponso kuunikira. N’chimodzimodzinso lilime lathu. Tikhoza kuligwiritsa ntchito potamanda Mulungu komanso polimbikitsa anthu ena. (Sal. 19:14) Kaya timalankhula ndi pakamwa kapena ndi manja, tiyenera kukumbukira kuti kulankhula ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu. Choncho, tiyenera kugwiritsa ntchito mphatsoyi polimbikitsa ena osati kuwakhumudwitsa.​—Yak. 3:9, 10. w15 12/15 3:1-3

Lachinayi, September 28

Luka, dokotala wokondedwa, akuti moni nonse.​—Akol. 4:14.

Luka anali dokotala ndipo ayenera kuti ankathandiza Paulo ndiponso anthu ena amene ankayenda nawo, akadwala. (Agal. 4:13) Zimene ankachitazi n’zogwirizana ndi zimene Yesu ananena kuti: ‘Odwala amafuna dokotala.’ (Luka 5:31) Baibulo silinena kuti Luka anaphunzira kuti ntchito yaudokotala komanso anaphunzira liti. Koma limatiuza kuti Paulo anapereka moni wa Luka kwa Akhristu a ku Kolose. Choncho n’kutheka kuti Luka anaphunzira ntchito yakeyi kufupi ndi ku Kolose, kusukulu ina ya mumzinda wa Laodikaya. Kaya Luka anaphunziradi ntchito yake kumeneko kapena ayi, zimene tikudziwa n’zakuti sankangopereka malangizo okhudza mankhwala koma anali dokotala weniweni. Umboni wa zimenezi ndi mawu okhudza zachipatala amene anagwiritsa ntchito m’buku la Machitidwe ndiponso mu Uthenga Wabwino. Komanso anafotokoza kwambiri mmene Yesu anachiritsira anthu. w15 12/15 4:11, 12

Lachisanu, September 29

Tikuyamika Mulungu chifukwa cha mphatso yake yaulere, imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.​—2 Akor. 9:15.

Yehova anasonyeza kuti amatikonda kwambiri pamene anatumiza Mwana wake padzikoli. (Yoh. 3:16; 1 Yoh. 4:9, 10) Mtumwi Paulo ananena kuti pochita zimenezi, Mulungu anatipatsa ‘mphatso yaulere imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.’ Paulo ankadziwa kuti zonse zimene Mulungu analonjeza zidzakwaniritsidwa chifukwa cha nsembe ya Yesu. (2 Akor. 1:20) Ndiye ponena kuti ‘mphatso yaulere,’ ankatanthauza zinthu zonse zabwino zimene Mulungu angatipatse kudzera mwa Yesu. Mphatsoyi ndi yaikulu kwambiri moti anthufe sitingathe kuifotokoza bwinobwino. Ndiye kodi tiyenera kumva bwanji tikaganizira za mphatsoyi? Nanga tingasonyeze bwanji kuti timaiyamikira? Mwina tingaone kuti tiyenera kuganiza zosintha zimene timachita pa moyo wathu n’kuyamba kuchita zabwino. N’kuthekanso kuti ingatichititse kukhala ndi mtima wopatsa, kusonyeza ena chikondi komanso kukhululukira amene atilakwira. Musaiwale kuti zimene Yehova anatichitira ndi zazikulu kwambiri kuposa zimene aliyense angatichitire.​—1 Pet. 3:18. w16.01 2:1, 2, 4, 5

Loweruka, September 30

Mphepo imawombera kumene ikufuna, ndipo munthu amamva mkokomo wake, koma sadziwa kumene ikuchokera ndi kumene ikupita. N’chimodzimodzinso aliyense wobadwa mwa mzimu.​—Yoh. 3:8.

Munthu akadzozedwa angamadzifunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu wasankha ineyo?’ Mwinanso angamadzione kuti ndi wosayenera kupatsidwa udindo wodzalamulira ndi Yesu. Komabe sikuti amakayikira zoti wadzozedwa. Amasangalala komanso amayamikira Yehova chifukwa chomupatsa mwayiwu. Amamva ngati mmene Petulo ankamvera pamene anati: “Atamandike Mulungu amenenso ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, pakuti mwachifundo chake chachikulu, anatibereka mwatsopano kuti tikhale ndi chiyembekezo cha moyo mwa kuukitsidwa kwa Yesu Khristu. Anatibereka kuti tikhale ndi cholowa chosawonongeka, chosadetsedwa ndiponso chosasuluka. Cholowa chimenechi anasungira inuyo kumwamba.” (1 Pet. 1:3, 4) Mkhristu aliyense wodzozedwa akawerenga mawu amenewa amadziwiratu kuti Atate wake wakumwamba akulankhula ndi iyeyo. w16.01 3:11, 12

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena