Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es17 tsamba 98-108
  • October

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • October
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
  • Timitu
  • Lamlungu, October 1
  • Lolemba, October 2
  • Lachiwiri, October 3
  • Lachitatu, October 4
  • Lachinayi, October 5
  • Lachisanu, October 6
  • Loweruka, October 7
  • Lamlungu, October 8
  • Lolemba, October 9
  • Lachiwiri, October 10
  • Lachitatu, October 11
  • Lachinayi, October 12
  • Lachisanu, October 13
  • Loweruka, October 14
  • Lamlungu, October 15
  • Lolemba, October 16
  • Lachiwiri, October 17
  • Lachitatu, October 18
  • Lachinayi, October 19
  • Lachisanu, October 20
  • Loweruka, October 21
  • Lamlungu, October 22
  • Lolemba, October 23
  • Lachiwiri, October 24
  • Lachitatu, October 25
  • Lachinayi, October 26
  • Lachisanu, October 27
  • Loweruka, October 28
  • Lamlungu, October 29
  • Lolemba, October 30
  • Lachiwiri, October 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2017
es17 tsamba 98-108

October

Lamlungu, October 1

Amene anawasankhiratu ndi amenenso anawaitana.​—Aroma 8:30.

Yehova anayamba kusankha odzozedwa Yesu ataukitsidwa ndipo zikuoneka kuti Akhristu onse a m’nthawi ya atumwi anali odzozedwa. Kuchokera nthawi imeneyo kudzafika kumayambiriro kwa masiku otsiriza, anthu ambiri amene ankati ndi otsatira a Yesu anali Akhristu onyenga. Yesu ananena kuti anthuwa anali ngati “namsongole.” Komabe pa nthawiyo, Yehova anapitiriza kudzoza anthu ena ndipo Yesu anati amenewa anali ngati “tirigu.” (Mat. 13:24-30) M’masiku otsiriza ano, Yehova wakhalanso akusankha anthu oti akhale m’gulu la 144,000. Ngati Mulungu wasankha kudzoza anthu ena m’masiku otsiriza kapena kumapeto kwake, tiyenera kungovomereza podziwa kuti nthawi zonse amachita zinthu mwanzeru. (Yes. 45:9; Dan. 4:35; Aroma 9:11, 16) Tiyenera kusamala kuti tisakhale ngati antchito amene anayamba kudandaula chifukwa cha malipiro amene mbuye wawo anawapatsa. Anthuwo anadandaula chifukwa analandira malipiro ofanana ndi a anthu amene anayamba ntchito mochedwa.​—Mat. 20:8-15. w16.01 4:15

Lolemba, October 2

Tenga Isaki mwana wako mmodzi yekhayo, mwana wako amene umamukonda kwambiriyo, ndipo muyende ulendo wopita ku Moriya. Kumeneko ukamupereke nsembe yopsereza paphiri limene ndidzakuuza.​—Gen. 22:2.

N’zoona kuti Mulungu satipempha kuchita zinthu ngati zimenezi masiku ano. Komabe amafuna kuti tizimumvera ngakhale pamene tikuona kuti n’zovuta kapena sitikumvetsa chifukwa chake. Kodi ndi zinthu ziti zimene Mulungu amafuna kuti tizichita, zomwe inuyo mumaona kuti ndi zovuta? Mwachitsanzo, anthu ena amavutika kulalikira. Mwina ndi amanyazi ndipo zimawavuta kulalikira kwa anthu osawadziwa. Pomwe ena zimawavuta kuti asachite nawo zinthu zina akakhala kusukulu kapena kuntchito poopa kuoneka osiyana. (Eks. 23:2; 1 Ates. 2:2) Kodi inunso nthawi zina mumaona kuti zimene Yehova akufuna kuti muchite ndi zovuta ngati zimene anauza Abulahamu? Ngati ndi choncho, nkhani ya Abulahamuyi ingakuthandizeni. Tikamaganizira kwambiri za chikhulupiriro cha anthu okhulupirika akale, tingayambe kuwatsanzira komanso kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova.​—Aheb. 12:1, 2. w16.02 1:3, 14

Lachiwiri, October 3

Sauli anauza mwana wake Yonatani ndi atumiki ake onse kuti akufuna kupha Davide.​—1 Sam. 19:1.

Yonatani atadziwa kuti Sauli akufuna kupha Davide, anafunika kusankha kuti akhala wokhulupirika kwa ndani. Iye anali atachita pangano ndi Davide komanso ankafuna kuti azimvera bambo ake. Komabe Yonatani ankadziwa kuti Mulungu ankathandiza Davide osati Sauli. Choncho anakhala wokhulupirika kwa Davide. Ndiyeno anamuchenjeza kuti akabisale ndipo kenako anauza Sauli zinthu zabwino zokhudza iyeyo. (1 Sam. 19:1-6) Ifenso tisamalole kuti mtundu wathu, sukulu yathu kapena timu yathu yamasewera zikhale zofunika kwambiri kwa ife moti n’kutilepheretsa kukhala okhulupirika kwa Yehova. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mnyamata wina dzina lake Henry amene amakonda kwambiri masewera enaake. Iye ankaimira sukulu yake pa masewerawa ndipo ankafunitsitsa kuti sukulu yawoyo ipambane. Henry anati: “Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kukonda kwambiri masewerawa komanso sukulu yanga kuposa kutumikira Mulungu. Tinkasewera Loweruka ndi Lamlungu lililonse moti ndinkasowa nthawi yolalikira ndiponso yosonkhana. Choncho ndinasankha kuti ndisiye kusewera mu timu ya sukulu yathu.”​—Mat. 6:33. w16.02 3:10, 12

Lachitatu, October 4

Anthu ako adzadzipereka mofunitsitsa.​—Sal. 110:3.

Monga wachinyamata, pali zinthu zingapo zimene zingakuthandizeni kudziwa ngati mukufunadi kubatizidwa. Mwachitsanzo, mapemphero anu angasonyeze ngati mukufunadi kutumikira Yehova. Munthu amene ali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova amapemphera pafupipafupi ndipo amamuuza zakukhosi kwake. (Sal. 25:4) Nthawi zambiri Yehova amayankha mapemphero athu pogwiritsa ntchito Mawu ake. Choncho mukamaphunzira Baibulo mwakhama mumasonyezanso kuti mukufuna kutumikira Yehova ndi mtima wonse komanso kukhala naye pa ubwenzi wolimba. (Yos. 1:8) Ndiyeno mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndimauza Yehova zakukhosi kwanga? Kodi ndimaphunzira Baibulo nthawi zonse?’ Komanso ngati banja lanu limachita Kulambira kwa Pabanja, mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndimasangalala kuchita nawo zimenezi?’ Zimene mungayankhe pa mafunsowa zingakuthandizeni kudziwa ngati mukufunadi kubatizidwa. w16.03 1:11, 13

Lachinayi, October 5

Kuchokera kwa iye, thupi lonselo limakula podzimanga lokha mwachikondi.​—Aef. 4:16.

Timasangalala kwambiri tikamawerenga Buku Lapachaka n’kuona lipoti lofotokoza mmene ntchito yathu ikuyendera padziko lonse. Komanso timaoneka kuti ndife ogwirizana tikhala pa msonkhano wadera, wachigawo komanso wamayiko. Pamisonkhanoyi timamvetsera nkhani zolimbikitsa za m’Baibulo komanso kuonera masewero ndi zitsanzo. Zonsezi zimatithandiza kuti tizitumikira Yehova ndi mtima wathu wonse. Timakhalanso ogwirizana ndi abale ndi alongo athu padziko lonse tikapezeka pa Chikumbutso. (1 Akor. 11:23-26) Timachita mwambowu pa Nisani 14, dzuwa litalowa. Tikamachita mwambowu timasonyeza kuti timayamikira zimene Yehova anatichitira komanso timamvera lamulo la Yesu. Choncho kutatsala milungu ingapo kuti Chikumbutso chichitike, timaitanira anthu kumwambo wofunikawu. Patokha sitingathe kulalikira anthu onse. Koma tikamalalikira mogwirizana, timathandiza anthu mamiliyoni ambiri kuti ayambe kutumikira Yehova. w16.03 3:4, 6, 7

Lachisanu, October 6

Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.​—Mat. 3:17.

Abale amene akuphunzitsidwa kuti azitumikira mu mpingo, ayenera kuthandizidwa kuti azitsatira mfundo za m’Baibulo. Tiyerekeze kuti mkulu wapempha m’bale kuti ayeretse kanjira kopita ku Nyumba ya Ufumu. Mwina angakambirane naye lemba la Tito 2:10 n’kumufotokozera kuti ntchitoyo idzakometsera “chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu.” Angamufotokozerenso mmene ntchitoyo ingathandizire anthu achikulire mumpingo. Mukamakambirana mwa njira imeneyi, zidzathandiza munthuyo kugwira ntchitoyo ndi mtima wofuna kuthandiza anthu osati mongotsatira malamulo. Iye adzasangalala kwambiri poona kuti ntchito yake yathandiza abale ndi alongo. Komanso mkulu ayenera kuyamikira munthu amene akumuthandizayo ngati wayesetsa kutsatira zimene akumuphunzitsa. Kodi zimenezi n’zothandiza bwanji? Kuyamikira munthu kuchokera pansi pa mtima kuli ngati kuthirira mbewu kuti zikule bwino. w15 4/15 2:7, 8

Loweruka, October 7

Ambuye adzandipulumutsa ku choipa chilichonse.​—2 Tim. 4:18.

Kodi munakumanapo ndi vuto lalikulu n’kumaona kuti palibe mtengo wogwira? Mwina simukupeza ntchito, mumanyozedwa kusukulu, muli ndi matenda enaake kapena zinthu zina zikukudetsani nkhawa. N’kutheka kuti munapempha thandizo kwa anthu ena koma sanakuthandizeni. Kunena zoona, si mavuto onse amene anthu angathe kutithandiza. Kodi ndi nzeru kutsatira malangizo akuti tizikhulupirira Yehova pa nthawi ngati imeneyi? (Miy. 3:5, 6) Inde. Tikutero chifukwa chakuti pali umboni wa m’Baibulo wosonyeza kuti Yehova amathandiza pa mavuto ngati amenewo. Choncho tikakumana ndi vuto lalikulu tisamakwiye. Tiziona kuti tapeza mwayi wosonyeza kuti timakhulupirira Yehova ndiponso woti tione akutithandiza. Umu ndi mmene Paulo ankaonera mavuto ake. Mukatero ubwenzi wanu ndi Yehova udzalimba kwambiri chifukwa choti mwayamba kumukhulupirira ndi mtima wonse. w15 4/15 4:3-5

Lamlungu, October 8

Mulungu wa nthawi ino wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira.​—2 Akor. 4:4.

Satana amadziwa kuti Yehova ndi wachikondi, choncho amachita zinthu mwachinyengo pofuna kuti anthu asiye kumvera Mulungu. (1 Yoh. 4:8) Amapusitsa anthu kuti asamazindikire “zosowa zawo zauzimu.” (Mat. 5:3) Iye “wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira, kuti asaone kuwala kwa uthenga wabwino waulemerero wonena za Khristu, yemwe ali chifaniziro cha Mulungu.” Yehova amafuna kuti anthu ‘azidzipereka kwa iye yekha.’ (Eks. 20:5) Ndiyeno Satana amagwiritsa ntchito chipembedzo chonyenga pofuna kupusitsa anthu. Iye amasangalala akaona anthu akulambira zinthu zina monga makolo akale kapena zinthu za m’chilengedwe. Anthu ena amene amaona kuti akulambira bwinobwino Mulungu amapusitsidwa n’kumakhulupirira zinthu zabodza komanso miyambo yachabechabe. Anthu oterewa ndi omvetsa chisoni chifukwa akufanana ndi amene Yehova anawauza kuti: “N’chifukwa chiyani mukuvutika kugwirira ntchito zinthu zimene sizikhutitsa? Tcherani khutu kwa ine . . . kuti moyo wanu usangalale kwambiri ndi zakudya zamafuta.”​—Yes. 55:2. w15 5/15 1:14, 15

Lolemba, October 9

Idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza chidendene.​—Gen. 3:15.

Abele ayenera kuti ankaiganizira kwambiri nkhaniyi ndipo ankadziwa kuti winawake ayenera ‘kuvulazidwa chidendene’ kuti anthu akhalenso angwiro ngati mmene Adamu ndi Hava analili poyamba. Ankakhulupirira kwambiri malonjezo a Yehova ndipo izi zinathandiza kuti Yehovayo alandire nsembe yake. (Gen. 4:3-5; Aheb. 11:4) Nayenso Nowa anali ndi chikhulupiriro ndipo anapulumuka Chigumula. (Aheb. 11:7) Madzi ataphwera, iye anasonyeza chikhulupiriro chake popereka nsembe ya nyama. (Gen. 8:20) Iye ayenera kuti ankakhulupiriranso zoti tsiku lina anthu adzamasulidwa ku uchimo ndi imfa. Pambuyo pa Chigumula, zinthu zinavutanso chifukwa chakuti Nimurodi anayamba kuchita zinthu zosemphana ndi cholinga cha Yehova. Koma Nowa anakhalabe ndi chikhulupiriro komanso chiyembekezo. (Gen. 10:8-12) N’kutheka kuti mtima wake unkakhala m’malo akaganizira zoti anthu adzamasulidwa ku uchimo ndi imfa. Panopa nthawi yomasulidwayi yatsala pang’ono ndipo nafenso tikhoza kumaona m’maganizo mwathu mmene zinthu zidzakhalire pa nthawiyo.​—Aroma 6:23. w15 5/15 3:4, 6

Lachiwiri, October 10

Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.​—Miy. 12:25.

Kupanda kusamala, kuda nkhawa kwambiri kukhoza kutidwalitsa kapena kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Choncho tizidalira Yehova ndiponso kukumbukira mawu a mulemba lalerowa. Anthufe timasangalala tikamva mawu olimbikitsa kuchokera kwa anthu amene amatimvetsa. Choncho tikakhala ndi vuto tikhoza kuchepetsa nkhawa ngati tifotokozera makolo athu, mkazi kapena mwamuna wathu kapena munthu wina amene angatithandize kudziwa maganizo a Yehova pa nkhaniyo. Tiyenera kudziwa kuti Yehova ndi amene amamvetsa nkhawa zathu kuposa aliyense. Paja Baibulo limati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afil. 4:6, 7) Tisamade nkhawa kwambiri chifuwa tingathandizidwe ndi Akhristu anzathu, akulu, kapolo wokhulupirika, angelo, Yesu ndiponso Yehova. w15 5/15 4:16, 17

Lachitatu, October 11

Panalinso mwamuna wina amene anakhala akudwala zaka 38.​—Yoh. 5:5.

Chakumpoto kwa kachisi wa ku Yerusalemu kunali dziwe lotchedwa Betesida. Anthu ambirimbiri odwala ndiponso olumala ankapita kumeneko chifukwa ankakhulupirira kuti akalowa m’dziweli madzi akuwinduka, angachiritsidwe. Chifukwa chomvera chisoni anthu, Yesu anayandikira munthu wina wolumala yemwe anali atadwala zaka zambiri kuposa zaka zimene Yesu anakhala padziko lapansi. (Yoh. 5:6-9) Yesu anafunsa munthuyo ngati akufuna kuchira. Munthuyo anayankha kuti ankafuna kuchira koma analibe munthu womuthandiza kulowa m’dziwelo. Iye ayenera kuti ankamvetsa chisoni pamene ankanena zimenezi. Kenako Yesu anamuuza kuti achite zinthu zooneka ngati zosatheka. Anati anyamule machira ake azipita. Munthuyo anachitadi zimenezi ndipo anayamba kuyenda. Zimenezi zikusonyeza bwino kuti Yesu amakondadi anthu ndipo adzawathandiza m’dziko latsopano. Nkhaniyi ikusonyezanso kuti Yesu ankafufuza anthu ovutika. Ifenso tikamalalikira tiyenera kufufuza anthu omwe akudandaula chifukwa cha mavuto a m’dzikoli. w15 6/15 2:8-10

Lachinayi, October 12

Muzipemphera motere.​—Mat. 6:9.

Yesu anayamba pempheroli ndi mawu akuti “Atate wathu” osati “Atate wanga.” Zimenezi zikutikumbutsa kuti tili m’gulu la abale ambiri omwe amakondana. (1 Pet. 2:17) Umenewutu ndi mwayi waukulu kwambiri. Akhristu ena asankhidwa ndi Mulungu kuti akhale ana ake ndiponso kuti apite kumwamba. Iwo ndi oyenereradi kunena kuti Yehova ndi “Atate” wawo. (Aroma 8:15-17) Koma Akhristu amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli anganenenso kuti Yehova ndi “Atate” wawo. Tikutero chifukwa chakuti Yehova ndi amene anawapatsa moyo ndipo amawapatsanso zinthu zonse zofunika. M’tsogolomu, iwonso adzakhala ana enieni a Mulungu. Izi zidzachitika akadzakhala angwiro komanso akadzadutsa bwinobwino mayesero omaliza. (Aroma 8:21; Chiv. 20:7, 8) Makolo ayenera kuphunzitsa ana awo kupemphera ndiponso kuwathandiza kuona kuti Yehova ndi Atate wawo wachikondi kwambiri. Kuthandiza ana kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova n’kofunika kwambiri kuposa kuwapatsa mphatso iliyonse. w15 6/15 4:4-6

Lachisanu, October 13

Mutilanditse kwa woipayo.​—Mat. 6:13.

Kuti tichite zinthu mogwirizana ndi pemphero lakuti “mutilanditse kwa woipayo,” tiyenera kupewa kukhala ‘mbali ya dziko la Satanali.’ Choncho tiyenera kupewa ‘kukonda dziko kapena zinthu za m’dzikoli.’ (Yoh. 15:19; 1 Yoh. 2:15-17) Koma kuchita zimenezi si kophweka. Tidzasangalala kwambiri Yehova akadzayankha pempheroli n’kuchotsa Satana ndi dziko loipali. Tisaiwale kuti Satana akudziwa zoti wangotsala ndi nthawi yochepa. Iye ndi wokwiya kwambiri ndipo akuchita zonse zimene angathe kuti asokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Choncho tiyenera kupemphera nthawi zonse kuti Yehova atilanditse kwa woipayo. (Chiv. 12:12, 17) Kodi mukulakalaka kukhala m’dziko lopanda Satana? Ngati zili choncho, pitirizani kupemphera kuti Mulungu ayeretse dzina lake ndiponso chifuniro chake chichitike padzikoli. Muzipemphanso Yehova kuti akuthandizeni kupeza zofunika pa moyo ndiponso kulimbitsa ubwenzi wanu ndi iye. Tiyeni tonse tiziyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi pemphero la Ambuye.​—Mat. 6:9-13. w15 6/15 5:12, 17, 18

Loweruka, October 14

Kudzakhala chisautso chachikulu.​—Mat. 24:21.

Sitikudziwa zonse zimene zidzachitike pa nthawi ya chisautso koma n’kutheka kuti padzafunika kusiya zinthu zina. Paja Akhristu oyambirira anafunika kusiya chuma chawo komanso kupirira mavuto osiyanasiyana kuti apulumuke. (Maliko 13:15-18) Kodi ifeyo tidzalolera kusiya zinthu zathu kuti tikhale okhulupirika kwa Mulungu? Kodi tidzamvera malangizo alionse amene tidzapatsidwe? Pa nthawiyo, atumiki a Yehova okhulupirika okha adzakhala ngati mneneri Danieli chifukwa adzapitiriza kulambira Yehova zinthu zitafika povuta. (Dan. 6:10, 11) Nthawi imeneyi sidzakhala yolalikira ‘uthenga wabwino wa ufumu.’ Nthawi yochita zimenezi idzakhala itatha chifukwa “mapeto” adzakhala atafika. (Mat. 24:14) Atumiki a Yehovafe tiyenera kuti pa nthawiyo tizidzalengeza uthenga wachiweruzo woopsa. Mwina tizidzauza anthu kuti dziko loipa la Satanali latsala pang’ono kutheratu. w15 7/15 2:3, 8, 9

Lamlungu, October 15

Sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.​—Yoh. 17:16.

Anthu amadana nafe chifukwa chakuti sitilowerera nawo m’zochitika za dzikoli. Koma sitiyenera kudabwa chifukwa Yesu ananeneratu kuti zimenezi zidzachitika. Anthu ambiri amene amatitsutsa samvetsa chifukwa chake sitilowerera m’zochitika za m’dzikoli. Koma ife timadziwa kuti nkhaniyi ingasonyeze ngati tili okhulupirika kwa Mulungu kapena ayi. Ndiyeno kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova, tiyenera kukhala olimba mtima. (Dan. 3:16-18) N’zoona kuti aliyense akhoza kuyamba kuopa anthu. Koma achinyamata ndi amene amavutika kwambiri kuchita zinthu zosiyana ndi anzawo. Choncho makolo ayenera kuwathandiza kudziwa zochita ngati atauzidwa kuti aimbe nawo nyimbo yafuko kapena achite zinthu zina zosonyeza kukonda kwambiri dziko lawo. Akhoza kukambirana zimenezi pa Kulambira kwa Pabanja kuti anawo adziwe bwino nkhaniyi n’cholinga choti azitha kuyankha molimba mtima. Ayenera kuwathandizanso kuti azifotokoza zimene amakhulupirira momveka bwino komanso mwaulemu. (Aroma 1:16) Makolo angachitenso bwino kulankhula ndi aphunzitsi a ana awo nkhani ngati zimenezi. w15 7/15 3:15, 16

Lolemba, October 16

Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha.​—Yoh. 3:16.

Yehova anasonyeza chikondi chosaneneka potumiza Yesu kuti akhale dipo n’cholinga choti “tipeze moyo kudzera mwa iye.” (1 Yoh. 4:9) Pofotokoza za mphatso imeneyi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Khristu anafera anthu osapembedza Mulungu pa nthawi yoikidwiratu. Pakuti n’chapatali kuti munthu wina afere munthu wolungama. Zoonadi, mwina wina angalimbe mtima kufera munthu wabwino. Koma Mulungu akuonetsa chikondi chake kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.” (Aroma 5:6-8) Zimene Yesu anachitazi zinathandiza kuti anthu akhale ndi mwayi wogwirizana ndi Mulungu. Dipo limasonyeza kuti Yehova amakonda kwambiri anthu. Ngati tikuyembekezera kudzakhala padzikoli, tiyenera kupitiriza kutumikira Mulungu mokhulupirika. Tisamakayikirenso kuti moyo umene adzatipatse m’dziko latsopano udzakhala wosangalatsa kwambiri. Zonsezi zikusonyeza kuti dipo ndi umboni waukulu kwambiri wakuti Mulungu amatikonda. w15 8/15 1:13, 15

Lachiwiri, October 17

Musadzimvere chisoni.​—Neh. 8:10.

Kukhala m’dziko latsopano n’kumalamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu kudzakhala kosangalatsa kwambiri. N’zoona kuti zinthu zikhoza kusintha pa moyo wathu koma tiyenera kuchita zonse zimene tingathe pomvera gulu la Yehova ndiponso kugwira ntchito yake. Mwachitsanzo, abale ndi alongo ena ku Beteli ya ku United States anapemphedwa kuti apite kukachita utumiki wina. Oyang’anira oyendayenda ena anapemphedwanso kuti akachite upainiya wapadera mwina chifukwa cha uchikulire kapena pa zifukwa zina. Onsewa akusangalala ndipo Yehova akuwadalitsa. Ifenso tiyenera kukhala okhutira, kupempha Yehova kuti atithandize komanso kuchita zonse zimene tingathe pomutumikira. Tikatero tidzakhala osangalala ndipo Yehova adzatidalitsa. (Miy. 10:22) Mwina tikaganizira za m’dziko latsopano timalakalaka kudzakakhala kwinakwake. Koma n’kutheka kuti tidzapemphedwa kukakhala kumene sitinkaganizirako. Koma kaya pa nthawiyo adzatiuza kuti tikakhale kuti kapena tigwire ntchito iti, sitikukayikira kuti tidzakhala oyamikira ndiponso osangalala. w15 8/15 3:8

Lachitatu, October 18

[Nowa] anali wopanda cholakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake.​—Gen. 6:9.

Nowa ankakhala m’dziko lomwe linali litaipa kwambiri, koma sanalole kuti anthu oipa a m’dzikolo akhale anzake apamtima. Iye ndi banja lake lonse ankagwira ntchito zimene Mulungu anawapatsa monga kumanga chingalawa. Nowa analinso “mlaliki wa chilungamo.” (2 Pet. 2:5) Ankalalikira, kumanga chingalawa ndiponso kucheza ndi banja lake. Zonsezi zinkamuthandiza kuti azisangalatsa Mulungu. Chifukwa cha zimenezi, Nowa ndi banja lake anapulumuka. Tiyenera kuyamikira kwambiri zimene iwo anachita chifukwa pakanapanda iwowo sitikanabadwa. Nawonso Akhristu oyambirira amene ankamvera Mulungu sankagwirizana ndi anthu oipa ndipo anapulumuka pamene Yerusalemu anawonongedwa mu 70 C.E.​—Luka 21:20-22. w15 8/15 4:17, 18

Lachinayi, October 19

[Pali] nthawi yoseka . . . ndi nthawi yodumphadumpha mosangalala.​—Mlal. 3:4.

Pali zosangalatsa zina zimene si zabwino ndipo zina tikazichita nthawi yaitali kwambiri sizithandiza. Kodi chikumbumtima chathu chingatithandize bwanji kusankha bwino zosangalatsa? Malemba amanena kuti tizipewa “ntchito za thupi” monga ‘zinthu zodetsa, khalidwe lotayirira, kupembedza mafano, kuchita zamizimu, udani, ndewu, nsanje, kupsa mtima, mikangano, kugawikana, magulu ampatuko, kaduka, kumwa mwauchidakwa ndiponso maphwando aphokoso.’ Paulo ananena kuti “anthu amene amachita zimenezi sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (Agal. 5:19-21) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi chikumbumtima changa chimandiuza kuti ndizipewa masewera achiwawa, olimbikitsa mtima wampikisano kapena wokonda dziko lathu? Nanga chimandichenjeza ndikafuna kuonera filimu yosonyeza zolaula kapena yolimbikitsa zinthu monga chiwerewere, kuledzera ndi kukhulupirira mizimu?’ w15 9/15 2:11, 12

Lachisanu, October 20

Ine ndikudziwa bwino, inu Yehova, kuti munthu wochokera kufumbi alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.​—Yer. 10:23.

Baibulo limatiuza kuti Mulungu sanalenge anthufe m’njira yoti tizisankha tokha zabwino ndi zoipa. Munthu akanyalanyaza mfundo imeneyi amakumana ndi mavuto aakulu. Choncho tiyenera kutsogoleredwa ndi Mulungu kuti tizikhala mwamtendere ndiponso mosangalala. Yehova watiphunzitsa mfundo yofunika imeneyi chifukwa choti amatikonda. Bambo wachikondi amafunitsitsa kuti zinthu ziziyenda bwino pa moyo wa ana ake. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti anthu ambiri sadziwa za zinthu zimene zichitike m’tsogolomu ndipo amatanganidwa ndi zinthu zosakhalitsa. (Sal. 90:10) Ifeyo tili ndi mwayi chifukwa Atate wathu wakumwamba watilonjeza tsogolo labwino kwambiri. Izi zimathandiza kuti tizikhala osangalala. w15 9/15 4:10, 11

Loweruka, October 21

Sikugwa mame kapena mvula zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditalamula.​—1 Maf. 17:1.

M’nthawi ya Aisiraeli, anthu a mitundu ina anali ndi mwayi woona komanso kumva mmene Mulungu anathandizira Aisiraeliwo. Mwachitsanzo, Yehova anapulumutsa anthu ake ku Iguputo komanso kwa mafumu ena ambiri. (Yos. 9:3, 9, 10) Adani a Aisiraeli anagonjetsedwa chifukwa chakuti sankafuna kuvomereza kuti Mulungu akuwamenyera nkhondo Aisiraeliwo. Ahabu, yemwe anali mfumu yoipa, analinso ndi mwayi woona dzanja la Mulungu. Ahabu anaona moto ukugwa kuchokera kumwamba n’kupsereza nsembe ya Eliya. Kenako Eliya ananena kuti Yehova athetsa chilala chimene chinaliko ndipo anauza Ahabu kuti: “Tsetserekani kuti chimvula chisakutsekerezeni.” (1 Maf. 18:22-45) Ngakhale kuti Ahabu anaona zonsezi, sanavomereze kuti Yehova ndi amene ankazichititsa. Zitsanzo ngati zimenezi zikusonyeza kuti tiyenera kukhala tcheru kuti tizizindikira mphamvu za Yehova. w15 10/15 1:4, 5

Lamlungu, October 22

Wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.​—Agal. 3:11.

Tisamakayikire kuti zinthu zizitiyendera bwino tikamatsatira malangizo a Mulungu. Timafunika kukhulupirira Yehova chifukwa ndi amene angatithandize kwambiri. Paulo ananena kuti Mulungu ndi “amene angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza, malinga ndi mphamvu yake imene ikugwira ntchito mwa ife.” (Aef. 3:20) Atumiki a Yehovafe timachita zonse zimene tingathe potumikira Mulungu. Koma timadziwanso kuti pali zinthu zina zimene sitingakwanitse patokha. Choncho timayamikira kwambiri kuti Mulungu akutithandiza ndiponso kutidalitsa. Koma kodi Mulungu angawonjezere chikhulupiriro chathu masiku ano? Baibulo limanena kuti akhoza kuchita zimenezi ngati “tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake.” (1 Yoh. 5:14) Yehova amasangalala ndi anthu amene amamukhulupirira ndi mtima wonse. Iye adzayankha tikamapempha kuti atiwonjezere chikhulupiriro. Ndiyeno chikhulupiriro chathu chikalimba, tidzakhala “oyenerera ufumu wa Mulungu.”​—2 Ates. 1:3, 5. w15 10/15 2:16-18

Lolemba, October 23

Tisatengeke pang’onopang’ono n’kusiya chikhulupiriro.​—Aheb. 2:1.

Kuganizira kwambiri za Yehova ndi Yesu kumathandiza kuti tikhale Akhristu odalirika komanso tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. (Aheb. 5:14; 6:1) Ngati sitipeza mpata wochita zimenezi, ubwenzi wathu ndi Yehova ukhoza kuyamba kusokonekera mpaka kufika potheratu. (Aheb. 3:12) Yesu anasonyeza kuti munthu sangasunge Mawu a Mulungu ngati Mawuwo sanamufike pamtima. Zingakhale zosavuta kuti munthu wotereyu atengeke ndi ‘nkhawa, chuma ndi zosangalatsa za moyo uno ndipo zipatso zake sizikhwima.’ (Luka 8:14, 15.) Choncho tiyeni tisasiye kuganizira kwambiri Mawu a Mulungu. Izi zidzatithandiza kutsatira kwambiri makhalidwe a Yehova. (2 Akor. 3:18) Tili ndi mwayi waukulu wophunzira za Mulungu komanso kutsanzira makhalidwe ake mpaka muyaya.​—Mlal. 3:11. w15 10/15 4:13, 14

Lachiwiri, October 24

Dziwa nzeru kuti upindule. Ukazipeza, udzakhala ndi tsogolo labwino.​—Miy. 24:14.

N’zosachita kufunsa kuti makolonu mumafunitsitsa kuti ana anu akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Nayenso Mulungu amafuna kuti muzilera ana anu “m’malangizo [ake] ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Choncho nthawi zonse muyenera kuchita zinthu zothandiza ana anu kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova. Paja makolo amaonetsetsa kuti ana awo azipita kusukulu chifukwa chodziwa ubwino wake. N’chimodzimodzinso ndi kuwaphunzitsa za Yehova. Makolo achikondi amaonetsetsa kuti ana awo azikhala nawo pa kulambira kwa pabanja komanso kuti azipita kumisonkhano yampingo ndiponso ikuluikulu. Zimenezi n’zofunika kwambiri chifukwa zingawathandize kudzapulumuka. Choncho muziyesetsa kuthandiza ana anu kuti azisangalala pophunzira za Yehova ndiponso azizindikira kuti iye angawaphunzitse kukhala anzeru. Yesu anathandiza ophunzira ake kuti azilalikira mwakhama. Inunso muzithandiza ana anu achinyamata kuti azikonda kulalikira ndiponso kuphunzitsa Mawu a Mulungu. w15 11/15 2:6

Lachitatu, October 25

Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu. Mutu wa mkazi ndi mwamuna, ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.​—1 Akor. 11:3.

Yehova anasankha mwamuna kuti akhale mutu wa banja. Koma amafuna kuti mwamunayo azitsogolera banja lake mwachikondi osati mwankhanza. Ngakhale kuti mwamuna ndi mutu wa mkazi wake, Baibulo limati ayenera ‘kumupatsa ulemu.’ (1 Pet. 3:7) Mwamuna angachite zimenezi poganizira zofuna za mkaziyo ndiponso kumulola kuti azisankha zochita pa zinthu zina. Baibulo limanena kuti: “Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu monga mmene Khristu anakondera mpingo n’kudzipereka yekha chifukwa cha mpingowo.” (Aef. 5:25) Lembali likusonyeza kuti Yesu ankakonda ophunzira ake moti analolera kuwafera. Mwamuna akamatsanzira Yesu potsogolera mkazi wake mwachikondi, zimakhala zosavuta kuti mkaziyo azimukonda, kumulemekeza ndiponso kumumvera.​—Tito 2:3-5. w15 11/15 4:6, 7

Lachinayi, October 26

Ayuda olankhula Chigiriki anayamba kudandaula za Ayuda olankhula Chiheberi.​—Mac. 6:1.

Chikhristu chitafalikira, anthu a Mulungu ambiri ankalankhula Chigiriki osati Chiheberi. Tikutero chifukwa chakuti mabuku a Maliko, Luka komanso Yohane, omwe amafotokoza zimene Yesu anaphunzitsa ndiponso kuchita, analembedwa ndiponso kufalitsidwa m’Chigiriki. Makalata a mtumwi Paulo ndiponso mabuku ena analembedwanso m’Chigiriki. Anthu amene analemba Malemba Achigiriki akafuna kugwira mawu Malemba Achiheberi, nthawi zambiri ankatenga mawuwo m’Baibulo limene linamasuliridwa m’Chigiriki. (la Septuagint) Mawu amenewa amapezekabe m’Baibulo ngakhale kuti amasiyana pang’ono ndi mawu a m’Malemba Achiheberi oyambirira. Choncho Yehova analola kuti mawu ena a anthu amene anamasulira Baibulo lachigirikili, apezeke m’Mawu ake. Izi zikusonyeza kuti Mulungu sakondera chilankhulo kapena chikhalidwe chinachake.​—Mac. 10:34. w15 12/15 1:8, 9

Lachisanu, October 27

Inu Yehova, tsegulani milomo yangayi, kuti pakamwa panga patamande inu.​—Sal. 51:15.

Anthufe timakonda kulankhula, komabe Baibulo limanena kuti pali nthawi ina imene tiyenera ‘kukhala chete.’ (Mlal. 3:7) Mwachitsanzo ena akamalankhula, tiyenera kukhala chete posonyeza kuti tikuwalemekeza. (Yobu 6:24) Tiyeneranso kupewa kulankhula nkhani zachinsinsi. (Miy. 20:19) Komanso ena akatikhumudwitsa, ndi bwino kukhala chete ndipo izi zimasonyeza kuti ndife anzeru. (Sal. 4:4) Komabe Baibulo limanenanso kuti pali “nthawi yolankhula.” (Mlal. 3:7) Tiyerekeze kuti mnzanu wakupatsani mphatso yamtengo wapatali, kodi mungangoisunga osaigwiritsa ntchito? N’zodziwikiratu kuti mungaigwiritse ntchito bwino posonyeza kuti mukuyamikira. N’chimodzimodzinso ndi mphatso yolankhula imene Yehova anatipatsa. Tingasonyeze kuti timaiyamikira tikamaigwiritsa ntchito bwino. Tingachite zimenezi potamanda Mulungu, polimbikitsa anzathu komanso pouza ena mmene tikumvera kapena zimene tikufuna. w15 12/15 3:4, 5

Loweruka, October 28

Usamangomwa madzi okha, koma uzimwanso vinyo pang’ono, chifukwa cha vuto lako la m’mimba ndi kudwaladwala kwako kuja.​—1 Tim. 5:23.

Masiku ano Akhristu alibe “mphatso za kuchiritsa.” (1 Akor. 12:9) Koma abale ndi alongo ena amene akufuna kutithandiza akhoza kutipatsa malangizo okhudza mankhwala. N’zoona kuti malangizo ena angakhale othandiza. Mwachitsanzo, Paulo anapereka malangizo othandiza kwa Timoteyo pamene ankavutika m’mimba chifukwa choti madzi akuderalo sanali abwino. Koma izi n’zosiyana kwambiri ndi kukakamiza Akhristu anzathu kuti agwiritse ntchito mtundu winawake wa mankhwala, kudya zakudya zinazake kapena kupewa kudya zinthu zina. N’kutheka kuti zinthuzi sizingawathandize ndipo nthawi zina zikhoza kuwapweteka. Mwachitsanzo, Akhristu ena anganene kuti: ‘Mankhwala amenewa ndi othandiza kwambiri. Akutiakuti aja anali ndi vuto ngati lanuli ndipo anachira atamwa mankhwalawa.’ Koma tizikumbukira kuti ngakhale mankhwala odziwika bwino akhoza kukhala ndi mavuto ake.​—Miy. 27:12. w15 12/15 4:13

Lamlungu, October 29

Khristu anafera machimo kamodzi kokha basi. Munthu wolungamayo anafera anthu osalungama.​—1 Pet. 3:18.

Tonse ndife ochimwa ndipo timayembekezera kufa. (Aroma 5:12) Koma chifukwa chotikonda, Yehova anakonza kuti Yesu abwere padzikoli n’cholinga choti “alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.” (Aheb. 2:9) Choncho Yehova anakonza zoti adzathetseretu imfa. (Yes. 25:7, 8; 1 Akor. 15:22, 26) Aliyense amene amakhulupirira Yesu adzalandira moyo wosatha. Anthu ena adzakhala ndi moyo wosangalala komanso wamtendere padziko lapansi pano n’kumalamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo odzozedwa adzapita kumwamba kukalamulira limodzi ndi Yesu. (Aroma 6:23; Chiv. 5:9, 10) Koma kodi ndi madalitso ena ati amene ndi mbali inanso ya mphatsoyi? Mulungu adzaukitsa akufa, adzathetsa matenda onse komanso dzikoli lidzakhala paradaiso. (Yes. 33:24; 35:5, 6; Yoh. 5:28, 29) Madalitso onsewa ndi mbali ya mphatso yaulere imene Mulungu watipatsa. N’zodziwikiratu kuti tonsefe timakonda Yehova ndiponso Mwana wake chifukwa chotipatsa mphatsoyi.​—2 Akor. 9:15. w16.01 2:5, 6

Lolemba, October 30

Anthu inu muyenera kubadwanso.​—Yoh. 3:7.

Mkhristu asanadzozedwe, amasangalala kuti adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Amalakalaka kudzaona Yehova atakonza dzikoli n’kuchotsapo zinthu zonse zoipa. Komanso amaganizira mmene adzasangalalire akamadzalandira achibale ake omwe anamwalira. Mwina amaganiziranso kuti adzamanga nyumba yabwino n’kumakhalamo komanso azidzadya zipatso zomwe adzabzale. (Yes. 65:21-23) Koma akadzozedwa zonsezi zimasintha. Sizisintha chifukwa chakuti sakusangalalanso kukhala ndi moyo padziko lapansi kapena pongofuna kuthawa mavuto padzikoli. Si chifukwanso chakuti amayamba kuona kuti moyo wosatha padziko lapansili udzakhala wotopetsa kapena chifukwa chongofuna kukaona zina kumwamba. Koma amasintha chifukwa chakuti Mulungu akamudzoza ndi mzimu wake, mzimuwo umamuthandiza kusintha chiyembekezo chake ndiponso mmene amaganizira. w16.01 3:11, 13

Lachiwiri, October 31

Pamene tikugwira naye ntchito limodzi, tikukudandauliraninso kuti musalandire kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kuphonya cholinga cha kukoma mtimako.​—2 Akor. 6:1.

Yehova ndi wamkulu m’chilengedwe chonse, ndi Mlengi wa zinthu zonse komanso ali ndi nzeru ndiponso mphamvu zopanda malire. Yobu anazindikira zimenezi moti Yehova atamufunsa zokhudza zimene analenga, anayankha kuti: “Ndadziwa kuti inu mumatha kuchita zinthu zonse, ndipo palibe zimene simungakwanitse.” (Yobu 42:2) Yehova angathe kuchita chilichonse chimene akufuna popanda wina kumuthandiza. Komabe kuyambira kale, amapereka mwayi kwa ena kuti agwire naye ntchito limodzi pokwaniritsa cholinga chake. Yehova analenga Mwana wake, Yesu, asanalenge china chilichonse. Kenako analola kuti Mwana wakeyo agwire naye ntchito yolenga zinthu zina zonse. (Yoh. 1:1-3, 18) Choncho Yehova anapatsa Yesu ntchito yoti agwire komanso anauza ena zimene Yesuyo anachita. Izi zikusonyeza kuti amaona kuti Mwana wakeyu ndi wofunika kwambiri.​—Akol. 1:15-17. w16.01 5:1, 2

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena